Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dzikoli Lidzatha Bwanji?

Kodi Dzikoli Lidzatha Bwanji?

“Simuli mu mdima ayi, kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingachitire kwa mbala.”—1 ATES. 5:4.

1. N’chiyani chingatithandize kukhalabe maso ndiponso kupirira mayesero?

POSACHEDWAPA, padzikoli pachitika zinthu zoopsa. Maulosi a m’Baibulo amene akukwaniritsidwa akutsimikizira zimenezi. Choncho tiyenera kukhalabe maso. Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Mawu a mtumwi Paulo amatilimbikitsa kuika “maso athu pa zinthu zosaoneka.” Tiyenera kuganizira kwambiri za mphoto yathu ya moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padziko lapansi. Polemba mawuwa, Paulo ankalimbikitsa Akhristu anzake kuganizira zinthu zosangalatsa zimene adzapeze chifukwa chokhala okhulupirika. Kuchita zimenezi kukanawathandiza kupirira poyesedwa komanso pozunzidwa.—2 Akor. 4:8, 9, 16-18; 5:7.

2. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti chiyembekezo chathu chikhale cholimba? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino komanso yotsatira?

2 Pali mfundo yofunika kwambiri m’malangizo a Paulo amenewa. Kuti chiyembekezo chathu chikhale cholimba, tiyenera kuganizira zinthu zam’tsogolo osati zimene tikuziona panopa. Tiyenera kuganizira zinthu zofunika kwambiri zomwe panopa n’zosaoneka. (Aheb. 11:1; 12:1, 2) Tiyeni tikambirane zinthu 10 zimene zidzachitike m’tsogolo zomwe zikugwirizana kwambiri ndi chiyembekezo chathu cha moyo wosatha. *

N’CHIYANI CHIDZACHITIKE DZIKOLI LISANATHE?

3. (a) Kodi pa 1 Atesalonika 5:2, 3, Paulo anati chidzachitike n’chiyani m’tsogolo? (b) Kodi atsogoleri andale adzachita chiyani ndipo mwina adzachita limodzi ndi ndani?

3 M’kalata yake yopita kwa Atesalonika, Paulo anatchula chinthu chimodzi chimene chidzachitike m’tsogolo. (Werengani 1 Atesalonika 5:2, 3.) Iye ananena za “tsiku la Yehova.” “Tsiku la Yehova” lotchulidwa pa lembali lidzayamba pamene zipembedzo zonyenga zidzawonongedwa ndipo lidzatha nkhondo ya Aramagedo ikadzamenyedwa. Koma tsikuli lisanayambe, olamulira a dzikoli azidzanena kuti: “Bata ndi mtendere!” Zimenezi zikhoza kunenedwa nthawi imodzi kapena nthawi zingapo. N’kutheka kuti ponena zimenezi azidzaganiza kuti atsala pang’ono kuthetsa mavuto akuluakulu a dzikoli. Kodi atsogoleri a zipembedzo adzanena nawo zimenezi? Popeza kuti iwo amalowerera m’zinthu za dzikoli, n’zotheka kuti adzanena nawo. (Chiv. 17:1, 2) Akamadzatero, adzakhala akutsanzira aneneri onyenga akale a ku Yuda. Ponena za aneneriwo, Yehova anati akunena kuti: “‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ pamene kulibe mtendere.”—Yer. 6:14; 23:16, 17.

4. Mosiyana ndi anthu ena, kodi timadziwa chiyani?

4 Sitikudziwa anthu onse amene adzanena nawo kuti “Bata ndi mtendere!” Koma chomwe tikudziwa n’chakuti akangonena mawuwa, tsiku la Yehova liyamba. N’chifukwa chake Paulo anati: “Abale simuli mu mdima ayi, kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingachitire kwa mbala. Pakuti inu nonse ndinu ana a kuwala.” (1 Ates. 5:4, 5) Mosiyana ndi anthu ena, timadziwa kuti zinthu zimene zikuchitika zikukwaniritsa maulosi a m’Malemba. Kodi ulosi wokhudza kunena kuti “Bata ndi mtendere!” udzakwaniritsidwa bwanji? Panopa sitikudziwa, choncho tiyeni tingodikira. Tiyeni tiyesetse ‘kukhalabe maso ndiponso kukhala oganiza bwino.’—1 Ates. 5:6; Zef. 3:8.

“MFUMUKAZI” IMENE SIKUDZIWA TSOGOLO LAKE

5. (a) Kodi “chisautso chachikulu” chidzayamba bwanji? (b) Kodi ndi “mfumukazi” iti imene sikudziwa tsogolo lake?

5 Kodi ndi chinthu chinanso chiti chimene chidzachitike? Paulo anati: “Pamene azidzati: ‘Bata ndi mtendere!’ chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo.” ‘Chiwonongeko chodzidzimutsachi’ chidzayamba ndi kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu,” yemwe akuimira zipembedzo zonse zonyenga. “Babulo Wamkulu” amatchedwanso “hule.” (Chiv. 17:5, 6, 15) Kuwonongedwa kwa zipembedzo zonse zonyenga, kuphatikizapo matchalitchi amene amati ndi achikhristu, kudzakhala chiyambi cha “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21; 2 Ates. 2:8) Anthu ambiri adzadabwa kwambiri ndi zimenezi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti pa nthawiyo, huleli lidzakhala likudzionabe ngati “mfumukazi” imene ‘sidzalira ngakhale pang’ono.’ Koma ‘mfumukaziyi’ idzazindikira kuti sinkadziwa za tsogolo lake. Zidzakhala ngati yawonongedwa “m’tsiku limodzi” lokha.—Chiv. 18:7, 8.

6. Kodi ndani adzawononga zipembedzo zonyenga?

6 Mawu a Mulungu amanena kuti huleli  lidzawonongedwa ndi “chilombo” cha “nyanga 10.” Kuphunzira buku la Chivumbulutso kwatithandiza kudziwa kuti chilombochi chikuimira bungwe la United Nations. “Nyanga 10” zikuimira maulamuliro onse andale amene amathandiza “chilombo chofiira kwambiri” chimenechi. * (Chiv. 17:3, 5, 11, 12) Kodi hulelo lidzawonongedwa bwanji? Mayiko amene ali m’bungwe la United Nations adzalanda chuma cha hulelo, kusonyeza kuipa kwake, kulisakaza komanso “kulinyeketsa ndi moto.” Tingati adzaliwonongeratu.—Werengani Chivumbulutso 17:16.

7. N’chiyani chidzachititse “chilombo” kuukira hule?

7 Ulosi wa m’Baibulo umasonyezanso zimene zidzachititse “chilombo” kuwononga hule. Zikuoneka kuti Yehova adzaika “maganizo ake” m’mitima ya olamulira andale n’cholinga choti awononge hulelo. (Chiv. 17:17) Zipembedzo zimalimbikitsa nkhondo osati mgwirizano. Choncho mwina mayiko adzaganiza kuti akawononga zipembedzo, zinthu ziyamba kuyenda bwino. Olamulira akamadzathana ndi zipembedzozi azidzaganiza kuti akukwaniritsa “maganizo awo amodzi.” Koma zoona zake n’zakuti iwo adzakhala chida cha Mulungu chowonongera zipembedzo zonse zonyenga. Apatu zinthu zidzasintha mosayembekezereka moti mbali imodzi ya dziko la Satana idzawononga inzake. Satana sadzakhalanso ndi mphamvu yolepheretsa zimenezi.—Mat. 12:25, 26.

ANTHU A MULUNGU ADZAUKIRIDWA

8. Kodi “Gogi wa kudziko la Magogi” adzachitira chiyani atumiki a Yehova?

8 Zipembedzo zonyenga zikadzawonongedwa, atumiki a Yehova azidzaoneka kuti “akukhala mwabata” komanso “m’midzi yopanda mipanda.” (Ezek. 38:11, 14) Kodi n’chiyani chidzachitikire atumiki a Yehova amene azidzaoneka ngati osatetezeka? Zikuoneka kuti iwo adzaukiridwa koopsa ndi “mitundu yambiri ya anthu.” Mawu a Mulungu amati kumeneku kudzakhala kuukiridwa ndi “Gogi wa kudziko la Magogi.” (Werengani Ezekieli 38:2, 15, 16.) Kodi tiyenera kuopa zimenezi?

9. (a) Kodi Akhristu ayenera kuganizira kwambiri za chiyani? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani panopa kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu?

9 Kudziwiratu za kuukira kumeneku sikuyenera  kutidetsa nkhawa. Sitiyenera kuganizira kwambiri za kupulumuka koma za mmene Yehova adzayeretsere dzina lake ndiponso kusonyeza kuti iye ndi woyenera kulamulira. Pajatu Yehova ananena maulendo 60 kuti: “Mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.” (Ezek. 6:7) Choncho tikulakalaka kwambiri nthawi imene ulosi wa Ezekieli umenewu udzakwaniritsidwe. Ndipo sitikayika kuti “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.” (2 Pet. 2:9) Panopa tikufunika kulimbitsa kwambiri chikhulupiriro chathu n’cholinga choti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova zivute zitani. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kupemphera, kuphunzira Baibulo, kusinkhasinkha ndiponso kulalikira uthenga wa Ufumu. Tikamatero, chiyembekezo chathu cha moyo wosatha chimakhala cholimba ngati “nangula.”—Aheb. 6:19; Sal. 25:21.

MITUNDU YONSE YA ANTHU IDZAM’DZIWA YEHOVA

10, 11. Kodi n’chiyani chidzayambitse Aramagedo? Nanga n’chiyani chidzachitike pa nkhondoyi?

10 Kodi ndi zinthu zoopsa ziti zimene zidzayambike atumiki a Yehova akadzaukiridwa? Yehova adzagwiritsa ntchito Yesu ndi magulu ankhondo a kumwamba kuti apulumutse anthu ake. (Chiv. 19:11-16) Imeneyo idzakhala ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,’ kapena kuti Aramagedo.—Chiv. 16:14, 16.

11 Ezekieli analemba mawu a Yehova onena za nkhondo imeneyi. Iye anati: “‘Ndidzamubweretsera [Gogi] lupanga m’madera anga onse a m’mapiri kuti limuwononge,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.’” Anthu amene ali kumbali ya Satana adzasokonezeka chifukwa cha mantha n’kuyamba kuukirana. Kenako nayenso Satana adzakumana ndi zokhoma. Yehova ananena za Gogi kuti: “Ndidzamugwetsera . . . moto ndi sulufule. Ndidzagwetsa zimenezi pa iyeyo, pagulu lake la asilikali ndi pa mitundu yambiri ya anthu amene adzakhale kumbali yake.” (Ezek. 38:21, 22) Kodi zotsatira zake zidzakhala zotani?

12. Kodi anthu onse adzazindikira chiyani?

12 Anthu adzazindikira kuti amene akuwagonjetsa ndi Yehova. Mofanana ndi Aiguputo amene ankathamangira Aisiraeli pa Nyanja Yofiira, magulu a Satana adzathedwa nzeru n’kunena kuti: “Yehova akuwamenyera nkhondo.” (Eks. 14:25) Anthu onse adzam’dziwadi Yehova. (Werengani Ezekieli 38:23.) Kodi zinthu zimenezi zichitikadi posachedwa?

SIPADZAKHALANSO ULAMULIRO WINA WAMPHAMVU PADZIKO LONSE

13. Kodi tikudziwa chiyani zokhudza mbali yachisanu ya chifaniziro chimene Danieli anafotokoza?

13 Ulosi wina wa m’buku la Danieli umatithandiza kudziwa kuti kwatsala nthawi yochepa kuti chisautso chachikulu chiyambe. Danieli anafotokoza za chifaniziro chooneka ngati munthu, chopangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana. (Dan. 2:28, 31-33) Chifanizirochi chimaimira maulamuliro amphamvu amene alamulira motsatizana, omwe alowerera m’zochitika za anthu a Mulungu m’mbuyomu ndiponso masiku ano. Maulamuliro ake ndi Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi, Roma ndiponso wina womaliza, womwe ndi wa masiku ano. Ulosi wa Danieli umasonyeza kuti ulamuliro womalizawu ukuimiridwa ndi mapazi ndiponso zala za chifanizirochi. Pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, mayiko a Britain ndi United States anayamba kugwirizana kwambiri. Choncho mbali yachisanu ya chifanizirochi ikuimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Popeza mapazi ali kumapeto kwa chifanizirochi ndiye kuti sipadzakhalanso ulamuliro wina  wamphamvu padziko lonse. Mapazi ndi zala zapangidwa ndi chitsulo chosakanizidwa ndi dongo. Zimenezi zimaimira kuti ulamuliro wa Britain ndi America si wamphamvunso kwenikweni.

14. Kodi ndi ulamuliro uti umene udzakhala wamphamvu Aramagedo ikamadzayamba?

14 Ulosi womwewu umanena za mwala wodulidwa kuphiri. Mwalawu ukuimira Ufumu wa Mulungu ndipo unadulidwa kuphiri, lomwe likuimira ulamuliro wa Yehova. Zimenezi zinachitika mu 1914. Mwalawu watsala pang’ono kuphwanya mapazi a chifanizirochi. Pa Aramagedo, mapazi ndiponso mbali zonse za chifaniziro chimenechi zidzaphwanyidwa. (Werengani Danieli 2:44, 45.) Choncho ulamuliro wa Britain ndi America udzakhalabe wamphamvu padziko lonse pamene Aramagedo izidzayamba. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kuona ulosi umenewu ukukwaniritsidwa. * Koma kodi Yehova adzamuchita chiyani Satana?

ZIMENE ZIDZACHITIKIRE MDANI WAMKULU WA MULUNGU

15. Kodi n’chiyani chidzachitikire Satana ndi ziwanda zake Aramagedo ikadzatha?

15 Choyamba, Satana adzaona dziko lakeli likuwonongedwa mpaka kutheratu. Kenako idzafika nthawi yoti nayenso aone zokhoma. Mtumwi Yohane anafotokoza zimene zidzachitike. (Werengani Chivumbulutso 20:1-3.) Yesu Khristu, yemwe ndi “mngelo” wokhala ndi “kiyi wa paphompho,” adzagwira Satana ndi ziwanda zake n’kuwaponya m’phompho kuti akhale m’menemo zaka 1,000. (Luka 8:30, 31; 1 Yoh. 3:8) Ichi chidzakhala chiyambi cha kuphwanya mutu wa njoka. *Gen. 3:15.

16. Kodi n’chiyani chidzachitikire Satana akadzaponyedwa “m’phompho”?

16 Kodi ‘phompho’ limene Satana ndi ziwanda zake adzaponyedwa n’chiyani? Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘phompho’ pa Chivumbulutso 20:1-3 akutanthauza “malo akuya kwambiri” ndipo akhoza kutanthauzanso dzenje lopanda malire. Choncho palibe aliyense amene angafikeko kupatulapo Yehova ndiponso mngelo wokhala ndi “kiyi wa paphompho.” M’phomphomo, Satana adzakhala ngati wafa ndipo sadzatha ‘kusocheretsa mitundu ya anthu.’ “Mkango wobangula” uja sudzatha kuchita chilichonse.—1 Pet. 5:8.

ZIMENE ZIDZACHITIKE NTHAWI YAMTENDERE ISANAFIKE

17, 18. (a) Kodi takambirana zinthu ziti zimene zidzachitike m’tsogolo? (b) Kodi zinthu zimenezi zikadzachitika, moyo udzakhala wotani?

17 Kutsogoloku tikuyembekezera zinthu zoopsa komanso zochititsa chidwi. Tidzaona mmene anthu adzafuulire kuti “Bata ndi mtendere!” Kenako tidzaona Babulo Wamkulu akuwonongedwa, Gogi wa ku Magogi akuukira anthu a Yehova ndiponso nkhondo ya Aramagedo. Nayenso Satana ndi ziwanda zake adzaponyedwa m’phompho. Izi zikadzachitika, sipadzakhalanso zoipa zilizonse ndipo tidzayamba moyo wina watsopano. Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu udzayamba ndipo tidzakhala ndi “mtendere wochuluka.”—Sal. 37:10, 11.

18 Takambirana zinthu zisanu zimene zidzachitike. M’nkhani yotsatira tidzakambirana zinthu zinanso zimene tikuyembekezera.

^ ndime 2 Tikambirana zinthu 10 zimenezi m’nkhani ino komanso yotsatira.

^ ndime 6 Onani buku lakuti, Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Ayandikira, tsamba 251 mpaka 258.

^ ndime 14 Lemba la Danieli 2:44 limanena za “kuthetsa maufumu ena onsewo.” Apa akunena za maufumu omwe akuimiridwa ndi mbali zosiyanasiyana za chifanizirochi. Koma ulosi wina m’Baibulo umanena kuti “mafumu a dziko lonse lapansi” adzasonkhanitsidwa kuti alimbane ndi Yehova pa “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chiv. 16:14; 19:19-21) Choncho maufumu a m’chifanizirocho komanso maufumu onse a padziko lapansi adzawonongedwa pa Aramagedo.

^ ndime 15 Adzamalizitsa kuphwanya mutu wa njoka zikadzatha zaka 1,000 zimenezi. Pa nthawiyi, Satana ndi ziwanda zake adzaponyedwa “m’nyanja yamoto ndi sulufule.”—Chiv. 20:7-10; Mat. 25:41.