Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Lipoti la Msonkhano Wapachaka

Palidi Mgwirizano Ndiponso Mapulani Abwino

Palidi Mgwirizano Ndiponso Mapulani Abwino

NTHAWI zonse misonkhano yapachaka ya Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania imakhala yosangalatsa zedi. Zimenezi zinaoneka pa msonkhano wa nambala 127 umene unachitika Loweruka pa October 1, 2011. Alendo ochokera m’mayiko osiyanasiyana anasonkhana ku Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ku Jersey City, ku New Jersey m’dziko la United States.

M’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhani yoyamba n’kulandira anthu. Iye anauza anthu ochokera kumayiko 85 amene anasonkhana kuti ali pa mgwirizano wapadera kwambiri padziko lonse. Mgwirizano umenewu umathandiza anthu kumva uthenga wathu ndipo umalemekeza Yehova. Nkhani ya mgwirizano inkatchulidwatchulidwa pa msonkhanowu.

NKHANI YABWINO YOCHOKERA KU MEXICO

Mbali yoyamba ya msonkhanowu inasonyeza kuti anthu a Yehova ndi ogwirizana. Nthambi za mayiko 6 a ku Central America zinaphatikizidwa ndi nthambi ya ku Mexico. M’bale Baltasar Perla, wa kunthambi ya Mexico, anafunsa abale ena atatu a kunthambiyo mmene ntchito yoyang’anira mayiko onsewo ikuyendera. Anthu ena a kumayikowa anapita kukatumikira kunthambi ya ku Mexico. Chifukwa cha zimenezi, tsopano kunthambiyo kuli anthu ochokera kumayiko osiyanasiyana ndiponso azikhalidwe zosiyanasiyana. Abale ndi alongo akusangalala kukumana ndi anthu ochokera m’mayiko ena ndipo pali kulimbikitsana kwabasi. Zili ngati Mulungu wanyamula chilabala n’kufufuta malire a mayikowo.

Ataphatikiza nthambizi, mpingo uliwonse wa kumayiko 6 amenewa unalumikizidwa ku Intaneti n’cholinga choti uzilemberana maimelo ndi ofesi ya nthambi ya ku Mexico. Zimenezi zathandiza ofalitsa kuti asamadzimve ngati ali kutali ndi gulu la Yehova.

LIPOTI LOCHOKERA KU JAPAN

M’bale James Linton wa kunthambi ya ku Japan anafotokoza mavuto amene abale anakumana nawo chifukwa cha chivomezi ndi kusefukira kwa madzi mu March 2011. Abale ambiri anaferedwa ndipo katundu wawo anawonongeka. Mboni zina zinawathandiza popereka nyumba zoposa 3,100 ndiponso magalimoto ambirimbiri. Abale a m’komiti yomanga anatumiza anthu kuti akakonze nyumba za abale. Anthuwo anadzipereka kugwira ntchito mosalekeza. Anthu oposa 1,700 anadzipereka kukagwira ntchito kulikonse kumene kunkafunika thandizo. Abale ndi alongo okwana 575 anathandiza nawo kukonza Nyumba za Ufumu ndipo ena a iwo anachokera ku United States.

Panakonzedwa zoti abale amene anakhudzidwa ndi tsokali atonthozedwe ndiponso kulimbikitsidwa mwauzimu. Akulu oposa 400 anapita kukalimbikitsa abalewa. Bungwe Lolamulira linasonyeza kuti limawaganiziranso pamene abale awiri oyendera nthambi ochokera kulikulu lathu anapita kuderali kuti akawalimbikitse. Abale akuderali analimbikitsidwanso chifukwa chakuti abale ndi alongo padziko lonse anasonyeza kuti amawaganizira.

 MILANDU IMENE YATIYENDERA BWINO

Anthu anali tcheru pamene M’bale Stephen Hardy wochokera kunthambi ya Britain anayamba kukambirana ndi abale ena za milandu yaposachedwapa imene yatiyendera bwino. Mwachitsanzo, boma la France linalamula kuti tilipire msonkho wa ndalama zokwana madola 82 miliyoni a ku United States. Koma Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula kuti zimenezi zinali zolakwika. Khotili linanena kuti boma la France linaphwanya Gawo 9 la pangano la mayiko a ku Ulaya lonena za ufulu wa zipembedzo. Linasonyeza kuti Mboni za Yehova zinadandaula za nkhaniyi osati pofuna kuzemba msonkho. Khotili linati: “Kukana kuvomereza chipembedzo chinachake, kuyesa kuchithetsa ndiponso kuchitsutsa mwachipongwe ndi zinthu zimene zimasemphana ndi ufulu wa mu Gawo 9 la panganoli.”

Khotili linaweruzanso motikomera mlandu wa ku Armenia. Kuyambira mu 1965, khotili linkaganiza kuti pangano la mayiko a ku Ulaya silipatsa munthu mwayi wokana ngati boma likumuumiriza kulowa usilikali. Koma akuluakulu a khotili anagamula kuti panganoli limapatsa munthu ufulu wokana usilikali ngati amakhulupirira mwamphamvu kuti ntchitoyi ndi yotsutsana ndi chipembedzo chake. Chifukwa cha chigamulochi maboma a Armenia, Azerbaijan ndi Turkey ayenera kuperekanso ufuluwu.

NTCHITO YOMANGA

M’bale Guy Pierce wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhani yotsatira. Iye ananena kuti anthu onse amene anasonkhana ankafunitsitsa kudziwa za ntchito yomanga ku New York. Iye anaonetsa anthu vidiyo yosonyeza zimene zikuchitika ku Wallkill ndiponso ku Patterson. Pa vidiyoyo anasonyezanso zimene akufuna kuchita kumalo atsopano ku Warwick ndiponso ku Tuxedo. Ku Wallkill, akumanga nyumba yogona ya zipinda zoposa 300 ndipo mwina itha mu 2014.

Panopa akukonza zoti amange nyumba zina kumalo a maekala 248 ku Warwick. M’bale Pierce ananena kuti, “Ngakhale kuti sitikudziwa maganizo a Yehova pa nkhani ya malo a ku Warwick, tikupitiriza kukonza malowa n’cholinga choti tisamutsireko likulu lathu la Mboni za Yehova.” Pa nthawi yomanga, tizidzasunga makina ndiponso zipangizo zathu ku Tuxedo. Malo amenewa ali pa mtunda wa makilomita 10 kuchokera ku Warwick ndipo ndi aakulu maekala 50. M’baleyu ananenanso kuti, “Tikalandira chilolezo, tiyamba kumanga ndipo tikufuna kumaliza pasanathe zaka zinayi. Kenako tidzagulitsa nyumba zonse za ku Brooklyn.”

M’bale Pierce anafunsa kuti, “Kodi Bungwe Lolamulira lasiya kuganiza kuti chisautso chachikulu chayandikira?” Iye anayankha kuti, “Iyayi. Chisautso chachikulu chikabwera tikumangabe nyumbazo, zikhalanso bwino kwabasi.”

SAMALANI NDI MKANGO WOBANGULA

Kenako M’bale Stephen Lett, yemwenso ali m’Bungwe Lolamulira, anafotokoza za lemba la 1 Petulo 5:8. Lembali limati: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” M’bale Lett ananena kuti fanizo la Petulo limeneli ndi labwino kwambiri chifukwa Mdyerekezi amafanana ndi mkango m’njira zingapo.

Mikango ndi yamphamvu ndiponso imathamanga kwambiri kuposa anthu. Nayenso Satana sitingalimbane naye podalira mphamvu zathu. Timafunika kuthandizidwa ndi Yehova. (Yes. 40:31) Mikango imasaka mu mdima. Nayenso Satana amagwira anthu amene ali mu mdima mwauzimu. Mikango imakonda kupha nyama zofatsa monga agwape kapena tiana ta mbidzi timene tili m’tulo. Satananso alibe chifundo ndipo angakonde kutipha. Mkango ukapha nyama n’kudya, simungaizindikirenso nyamayo. Nawonso  anthu amene amagwidwa ndi Satana amasinthiratu moti “makhalidwe awo amakhala oipa kwambiri kuposa poyamba.” (2 Pet. 2:20) Choncho tiyenera kulimbana ndi Satana mwamphamvu n’kumatsatira kwambiri mfundo za m’Baibulo.—1 Pet. 5:9.

MUZIYAMIKIRA MALO ANU M’NYUMBA YA YEHOVA

Amene anakamba nkhani yotsatira anali M’bale Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira. Iye anati, “Tonsefe tili ndi malo m’nyumba ya Yehova.” Nyumba imeneyi ndi kachisi wauzimu wa Mulungu yemwe akuimira dongosolo loti tizilambira Yehova movomerezeka chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. Aliyense ayenera kuyamikira malo ake chifukwa ndi amtengo wapatali. Mofanana ndi Davide, timafuna kukhala “m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo [wathu].”—Sal. 27:4.

Pofotokoza lemba la Salimo 92:12-14, M’bale Herd anafunsa kuti, “Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti zinthu zizitiyendera bwino?” Iye anayankha kuti: “M’paradaiso wauzimu, Mulungu amatilimbikitsa, kutiteteza ndiponso kutitsitsimula ndi choonadi. Tiyenera kumuthokoza kwambiri.” Kenako M’bale Herd analimbikitsa omvera kuti: “Tiyeni tizisangalala kukhala m’nyumba ya Yehova osati kwa nthawi yochepa koma kwamuyaya.”

AKHRISTU AMALEMEKEZA MAWU A MULUNGU

M’nkhani yotsatira, M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira anafotokoza kuti kuyambira kale, Akhristu oona akhala akulemekeza Mawu a Mulungu. Nthawi ya atumwi, iwo anadalira Mawu a Mulungu pothetsa nkhani ya mdulidwe. (Mac. 15:16, 17) Koma m’zaka za m’ma 100, anthu ena amene anaphunzitsidwa nzeru za Agiriki anayamba kudalira nzeruzo m’malo modalira Malemba. Kenako ena anayamba kuphunzitsa maganizo a akuluakulu a tchalitchi komanso a mafumu achiroma osati Baibulo. Umu ndi mmene ziphunzitso zina zonyenga zinayambira.

M’bale Splane ananena kuti Yesu anasonyeza m’fanizo lake kuti kuyambira nthawi ya atumwi, padziko lapansi padzakhalabe odzozedwa enieni n’cholinga choti azichitira umboni choonadi. (Mat. 13:24-30) Sitingatchule motsimikiza kuti anthu ake ndi akutiakuti. Koma kwa zaka zonsezi pakhala anthu amene ankatsutsa ziphunzitso ndiponso zinthu zina zosemphana  ndi Malemba. Ena mwa iwo ndi mkulu wa mabishopu dzina lake Agobard wa ku Lyons. Iye anakhalapo m’zaka za m’ma 800. M’zaka za m’ma 1100 kunali Peter wa ku Bruys, Henry wa ku Lausanne ndiponso Valdès (kapena kuti Waldo). M’zaka za m’ma 1300 kunali John Wycliffe. M’zaka za m’ma 1500 kunali William Tyndale ndipo m’zaka za m’ma 1800 kunali Henry Grew ndi George Storrs. Masiku ano, Mboni za Yehova zimatsatira kwambiri mfundo za m’Baibulo ndipo zikhulupiriro zawo zonse zimachokera m’Mawu a Mulungu. N’chifukwa chake Bungwe Lolamulira lasankha lemba la Yohane 17:17 kukhala lemba la chaka cha 2012. Lembali limati: “Mawu anu ndiwo choonadi.”

KUSINTHA KOKHUDZA SUKULU ZOPHUNZITSA BAIBULO

M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira analengeza kusintha kokhudza amishonale ndiponso apainiya apadera. Kuyambira pa September 2012, mayiko ena adzayamba kukhala ndi Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja. Komanso cholinga cha Sukulu ya Giliyadi chasintha. Kuyambira mu October 2011, amene akupita ku Giliyadi ndi amishonale omwe sanapiteko, apainiya apadera, oyang’anira oyendayenda kapena atumiki a pa Beteli. Omaliza maphunziro a Giliyadi azitumizidwa kukathandiza kumaofesi a nthambi, m’ntchito yoyang’anira dera kapena m’mipingo ya m’mizinda ikuluikulu yokhala ndi anthu ambiri.

Apainiya apadera ndi amene azitumizidwa kumadera a kumidzi kumene kuli ofalitsa ochepa kapena kulibiretu. Kuyambira pa January 1, 2012, ena mwa omaliza Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira ndiponso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja akhala akuikidwa monga apainiya apadera akanthawi n’kutumizidwa kumadera a kumidzi. Iwo amapatsidwa mwayi woti achite upainiya wapadera chaka chimodzi. Akachita bwino amawapatsa mwayi wa chaka chinanso. Akachita zimenezi kwa zaka zitatu, akhoza kuikidwa monga apainiya apadera a nthawi zonse.

Msonkhano wapachaka wa 2011 unali wosangalatsa kwambiri. Gulu la Yehova likuyesetsa kuti tizilalikira m’madera ambiri padziko lonse ndiponso kuti tizigwirizana kwambiri. Tikudziwa kuti Yehova adzadalitsa zimenezi ndipo zidzalemekeza dzina lake.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 18, 19]

TINACHEZANSO NDI ALONGO ASANU

Pa msonkhanowu, anafunsa alongo asanu amene amuna awo anali m’Bungwe Lolamulira koma anamwalira. Alongo ake ndi Marina Sydlik, Edith Suiter, Melita Jaracz, Melba Barry, ndiponso Sydney Barber. Iwo anafotokoza mmene anaphunzirira choonadi ndiponso kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Aliyense anafotokoza zinthu zosaiwalika pa moyo wake, zinthu zosangalatsa zokhudza amuna awo ndiponso madalitso amene analandira potumikira nawo. Pomaliza, omvera anaimba nyimbo yoyenera kwambiri ya nambala 86 yakuti “Akazi Okhulupirika Ndiponso Alongo Achikhristu.”

[Zithunzi]

(Pamwamba) Daniel ndi Marina Sydlik; Grant ndi Edith Suiter; Theodore ndi Melita Jaracz

(M’munsi) Lloyd ndi Melba Barry; Carey ndi Sydney Barber

[Mapu patsamba 16]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Nthambi 6 zinaphatikizidwa kuti ziziyang’aniridwa ndi nthambi ya ku Mexico

MEXICO

GUATEMALA

HONDURAS

EL SALVADOR

NICARAGUA

COSTA RICA

PANAMA

[Chithunzi patsamba 17]

Pulani ya likulu lathu ku Warwick, New York