Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mudzapeza Mphoto Chifukwa cha Ntchito Yanu”

“Mudzapeza Mphoto Chifukwa cha Ntchito Yanu”

 “Mudzapeza Mphoto Chifukwa cha Ntchito Yanu”

CHITHUNZICHI chikusonyeza Mfumu Asa itafika kuchigwa limodzi ndi asilikali ake. Iye ankatsogolera asilikaliwo pochokera kumapiri a ku Yudeya. Komano atangoona chigulu cha asilikali oti amenyane nawo, iye anaima modabwa komanso kuchita mantha. Asilikaliwo ndi a ku Itiyopiya ndipo ayenera kuti akwana 1 miliyoni. Koma asilikali a Asa ali ngati theka la adaniwo.

Kodi n’chiyani chimene Asa ankaganizira kwambiri pa nthawiyi? Kodi ankaganizira malangizo oti auze akuluakulu a asilikali ake? Kodi ankaganiza zolimbikitsa asilikali akewo? Kapena kodi ankaganiza zolembera kalata banja lake? Ayi. Iye anaganiza zopemphera.

Tisanakambirane pemphero lake komanso zimene zinachitika, tiyeni tikambirane za Asayo. N’chifukwa chiyani anaganiza zopemphera? Kodi anali ndi zifukwa zomveka zochitira zimenezi? Kodi nkhani ya Asa ikusonyeza bwanji kuti Yehova amadalitsa zochita za atumiki ake?

MBIRI YA ASA

Asa anayamba kulamulira mu 977 B.C.E. Nthawi imeneyi n’kuti Isiraeli ndi Yuda atagawikana kukhala maufumu awiri kwa zaka 20. Pa nthawiyi, kulambira konyenga kunali ponseponse mu Yuda. Nawonso anthu a maudindo mu ufumuwu ankalambira milungu ya ku Kanani imene ankati ndi yobereketsa. Ponena za Mfumu Asa, Baibulo limati: “Anachita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake.” Iye “anachotsa maguwa ansembe achilendo, anagwetsa malo okwezeka, anaphwanya zipilala zopatulika ndi kudula mizati yopatulika.” (2 Mbiri 14:2, 3) Asa anachotsanso m’Yuda monse “mahule aamuna a pakachisi” amene ankagonana ndi amuna anzawo polambira milungu yawo. Koma pali zinanso zimene Asa anachita. Iye analimbikitsanso anthu kuti “afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatira chilamulo” chake.—1 Maf. 15:12, 13; 2 Mbiri 14:4.

Yehova ataona kuti Asa walimbikitsa kulambira koona, anamudalitsa kuti akhale pa mtendere kwa zaka zambiri. N’chifukwa chake mfumuyi inati: “Tafunafuna Yehova Mulungu wathu. Tam’funafuna ndipo watipatsa mpumulo pakati pa adani athu onse otizungulira.” Mwayi umenewu utapezeka, anthu anayamba kumanga mipanda yolimba m’mizinda ya ku Yuda. Baibulo limati: “Iwo anamangadi ndipo zinthu zinawayendera bwino.”—2 Mbiri 14:1, 6, 7.

KU NKHONDO

Asa ankadziwa kuti Mulungu amadalitsa anthu amene amachita zinthu zosonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro. N’chifukwa chake Asa anapemphera kwa Yehova pa nthawi imene ankafuna kumenyana ndi gulu la asilikali, lomwe linali lalikulu kuposa gulu lina lililonse lotchulidwa m’Malemba. M’pemphero lake, Asa anachonderera Yehova kuti amuthandize. Iye ankadziwa kuti Mulungu akhoza kumuthandiza kugonjetsa adani ngakhale atakhala ambiri kapena amphamvu. Asa ankadziwa kuti zotsatira za nkhondoyo zidzakhudza dzina la Yehova. Choncho anapemphera kuti: “Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu, ndipo tabwera m’dzina lanu kudzamenyana ndi khamuli. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu. Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.” (2 Mbiri 14:11) Zinali ngati akunena kuti: ‘Yehova, Aitiyopiyawatu akukuyambani dala. Choncho musalole kuti dzina lanu  linyozeke. Zoona anthu ofookawa agonjetse anthu odziwika ndi dzina lanu?’ Atatero, “Yehova anagonjetsa Aitiyopiyawo pamaso pa Asa ndi Ayuda, ndipo Aitiyopiyawo anayamba kuthawa.”—2 Mbiri 14:12.

Masiku ano, anthu a Yehova ali ndi adani ambiri amphamvu. Koma sitimenyana nawo ndi zida zenizeni. Nkhondo yathu ndi yauzimu ndipo cholinga chathu ndi kulemekeza Yehova. Tikudziwa kuti Yehova adzathandiza anthu onse okhulupirika amene amamenya nkhondoyi. Mwina tikuyesetsa kuti ife kapena banja lathu tisatengere makhalidwe oipa a dzikoli. Apo ayi, mwina tikulimbana ndi zofooka zathu. Kaya tikulimbana ndi mavuto otani, tingalimbikitsidwe ndi pemphero la Asa. Iye anapambana chifukwa Yehova anamuthandiza. Ifenso tikadalira Mulungu, adzatithandiza kuthana ndi vuto lina lililonse. Iye ndi wamphamvu kwambiri kuposa munthu aliyense kapena chinthu chilichonse.

MAWU OLIMBIKITSA KOMANSO CHENJEZO

Mneneri Azariya anapita kukakumana ndi Asa pamene anali kubwerera ku nkhondo. Mneneriyu anauza Asa mawu olimbikitsa komanso kumuchenjeza. Iye anati: “Tamverani Mfumu Asa ndi anthu onse a fuko la Yuda ndi Benjamini. Yehova akhala nanu inuyo mukapitiriza kukhala naye. Mukamufunafuna iye adzalola kuti mum’peze, koma mukamusiya nayenso adzakusiyani. . . . Khalani olimba mtima ndipo musagwe ulesi, pakuti mudzapeza mphoto chifukwa cha ntchito yanu.”—2 Mbiri 15:1, 2, 7.

Mawu amenewa akhoza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Amasonyeza kuti Yehova sadzatisiya ngati timutumikirabe mokhulupirika. Tikamamupempha kuti atithandize, timadziwa kuti atimvera. Azariya anati: “Khalani olimba mtima.” Nthawi zambiri timafunika kulimba mtima kwambiri kuti tichite zinthu zolondola. Koma tingakwanitse kuchita zimenezi Yehova akatithandiza.

Agogo a Asa, omwe dzina lawo linali Maaka, anapanga “fano lonyansa kwambiri lopembedzera mzati wopatulika.” Choncho Asa anafunika kugwira ntchito yovuta kwambiri yochotsa agogo akewo pa udindo wawo monga “mayi wa mfumu.” Koma iye anachita zimenezi ndiponso anatentha fano lawolo. (1 Maf. 15:13) Asa anadalitsidwa chifukwa chochita zinthu zolondola molimba mtima. Ifenso tiyenera kumvera Yehova ndiponso malamulo ake mokhulupirika. Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale kuti achibale athu si okhulupirika kwa Mulungu. Tikatero, Yehova adzatidalitsa.

Njira imodzi imene Yehova anadalitsira Asa inali yakuti iye anaona Aisiraeli ambiri ochokera ku ufumu wakumpoto, womwe unali wopanduka, akubwera ku Yuda. Iwo anabwera chifukwa choona kuti Yehova anali kuthandiza Asa. Aisiraeliwo ankakonda kwambiri kulambira koona moti anasankha kusamuka m’nyumba zawo kuti akakhale limodzi ndi atumiki a Yehova. Asa limodzi ndi anthu onse mu Yuda ‘anachita pangano loti adzafunafuna Yehova ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse.’ Zotsatira zake zinali zakuti Mulungu “analola kuti amupeze. [Ndipo] Yehova anapitiriza kuwapatsa mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulira.” (2 Mbiri 15:9-15) Ifenso timasangalala kwambiri tikaona anthu okonda chilungamo akuyamba kulambira Yehova.

Koma mneneri Azariya anachenjezanso Asa. Iye  anati: “Mukamusiya [Yehova] nayenso adzakusiyani.” Ifeyo tisalole kuti zimenezi zitichitikire chifukwa zotsatira zake n’zoopsa. (2 Pet. 2:20-22) Malemba sanena chifukwa chimene Yehova anachenjezera Asa koma zimene tikudziwa n’zakuti mfumuyi sinamvere.

“MWACHITA ZOPUSA”

M’chaka cha 36 cha ulamuliro wa Asa, Mfumu Basa ya Isiraeli inapita kukaukira Yuda. Basa anamanga mpanda wolimba kwambiri kuzungulira mzinda wa Rama womwe unali pa mtunda wa makilomita 8 kumpoto kwa Yerusalemu. Mwina anachita zimenezi kuti anthu ake asamapite ku Yuda kukatumikira Yehova ndi Mfumu Asa. M’malo mopemphanso Yehova kuti amuthandize, Asa anapempha anthu. Anatumiza mphatso kwa mfumu ya Siriya n’cholinga choti imuthandize pa nkhondoyi. Asilikali a Siriya atalowerera, Basa anabwerera.—2 Mbiri 16:1-5.

Izi zinakwiyitsa Yehova moti anatumiza mneneri Haneni kwa Asa. Popeza Mulungu anamuthandiza kugonjetsa Aitiyopiya, Asa anayenera kudziwa kuti “maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” Mwina Asa analandira malangizo olakwika kapena ankaona kuti Basa ndi asilikali ake sanali oopsa kwenikweni moti akanangothana nawo yekha. Sitikudziwa mmene zinalili. Koma mfundo ndi yakuti, Asa anayamba kudalira nzeru za anthu m’malo modalira Yehova. Haneni anati: “Mwachita zopusa pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.”—2 Mbiri 16:7-9.

Asa atamva mawu amenewa, anapsa mtima n’kumanga mneneri Haneni m’matangadza. (2 Mbiri 16:10) Mwina Asa anaganiza kuti, ‘Ndakhala wokhulupirika kwa zaka zambirimbiri choncho sayenera kundilankhula chonchi.’ Kodi Asa anali atasiya kuganiza bwino chifukwa choti anali atakalamba? Baibulo silinena chilichonse pa nkhaniyi.

M’chaka cha 39 cha ulamuliro wake, Asa anadwala kwambiri matenda a mapazi. Baibulo limati: “Koma ngakhale pamene anali kudwala, iye anafunafuna ochiritsa osati Yehova.” Zikuoneka kuti nthawi imeneyo ubwenzi wa Asa ndi Yehova unali wosalimba. Asa anamwalira m’chaka cha 41 cha ulamuliro wake ndipo mwina anali asanasinthe.—2 Mbiri 16:12-14.

Zikuoneka kuti Yehova amakumbukira makhalidwe abwino a Asa komanso zimene anachita polimbikitsa kulambira koona osati zolakwa zake. Asa sanasiye kutumikira Yehova. (1 Maf. 15:14) Kodi tikuphunzira chiyani pa moyo wa Asa? Tiyenera kukumbukira mmene Yehova anatithandizira m’mbuyomu. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kuona kufunika kopempha Yehova kuti atithandizenso tikakumana ndi mavuto ena. Tisamaganize kuti ngati tatumikira Yehova kwa zaka zambiri sitifunikira malangizo a m’Malemba. Kaya tamutumikira nthawi yaitali bwanji, Yehova adzatilangiza tikalakwitsa. Kuti tipindule, tiyenera kumvetsera malangizowo modzichepetsa. Chofunika kwambiri n’chakuti ngati tipitiriza kutumikira Atate wathu wa kumwamba mokhulupirika, iye adzapitiriza kutithandiza. Maso a Yehova amayang’ana padziko lonse kuti aone anthu amene ndi okhulupirika kwa iye. Iye amagwiritsa ntchito mphamvu zake powathandiza. Yehova anachita zimenezi ndi Asa ndipo akhoza kuchitanso zomwezo ndi ife.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Yehova amapereka mphoto kwa anthu amene amamenya nkhondo yauzimu

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Pamafunika kulimba mtima kuti tichite zokondweretsa Yehova