Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Anandiphunzitsa Kuchita Chifuniro Chake

Yehova Anandiphunzitsa Kuchita Chifuniro Chake

Yosimbidwa ndi Max Lloyd

Mu 1955, ine ndinali kutumikira kudziko la Paraguay ku South America. Tsiku lina, ine ndi mmishonale mnzanga tinali m’nyumba inayake ndipo gulu la anthu olusa linazungulira nyumbayo. Anthuwo amafuula kuti: “Mulungu wathu ali ndi ludzu. Akulakalaka magazi a alendo anuwo.” Kodi zinatheka bwanji kuti tikhale alendo kumeneku?

INE ndinakulira m’dziko la Australia ndipo uku ndi kumene Yehova anayamba kundiphunzitsa kuchita chifuniro chake. Mu 1938, mlongo wina anapatsa bambo anga buku. Pa nthawiyi, mayi ndi bambo anga sanali kusangalala ndi atsogoleri a chipembedzo, omwe ankati mbali zina za Baibulo ndi nthano chabe. Patatha chaka chimodzi, makolo anga anabatizidwa. Kuchokera nthawi imeneyo, kuchita chifuniro cha Yehova kunali chinthu chofunika kwambiri m’banja lathu. Kenako mchemwali wanga, dzina lake Lesley, anabatizidwa. Iye anali wamkulu kwa ine ndi zaka 5. Ndipo ine ndinadzabatizidwa mu 1940, ndili ndi zaka 9.

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itangoyamba, dziko la Australia linaletsa kusindikiza ndiponso kufalitsa mabuku a Mboni za Yehova. Ngakhale kuti ndinali wamng’ono, ndinaphunzira kufotokoza zimene ndimakhulupirira pongogwiritsa ntchito Baibulo lokha. Ndinkakonda kutenga Baibulo kusukulu kuti ndisonyeze anzanga chifukwa chake sindinkachitira saluti mbendera kapena kuchita zinthu zina zokhudza nkhondo za mayiko.—Eks. 20:4, 5; Mat. 4:10; Yoh. 17:16; 1 Yoh. 5:21.

Anthu ambiri kusukulu sankacheza nane chifukwa ankati ndine “kazitape wa Germany.” Masiku amenewo, ankaonetsa mafilimu kusukulu. Tisanayambe kuonera, aliyense ankafunika kuima n’kuimba nyimbo ya fuko. Anyamata awiri kapena atatu ankandikoka tsitsi kuti nanenso ndiimirire. Kenako ndinadzachotsedwa sukulu chifukwa chotsatira chikhulupiriro changa. Koma ndinapitiriza maphunziro ndili kunyumba.

CHOLINGA CHANGA CHINATHEKA

Cholinga changa chinali choti ndikadzakwanitsa zaka 14, ndiyambe upainiya. Koma ndinakhumudwa pamene makolo anga anandiuza kuti ndiyambe kaye ndapeza ntchito. Iwo anandiuza kuti ndizilipira lendi kunyumbako ndipo anati ndidzayambe upainiya ndikakwanitsa zaka 18. Tinkakanganakangana pa nkhani ya ndalama zimene ndinkalandira. Ine ndinkafuna kuti ndizisunga kuti ndidzachitire upainiya koma iwo ankandilanda.

Itafika nthawi yoti ndiyambe upainiya, makolo anga anandiuza kuti ankasunga kubanki ndalama zanga zonse zija. Ndiyeno anandipatsa  ndalama zonsezo kuti ndigule zovala komanso zinthu zina zokagwiritsa ntchito pochita upainiya. Cholinga chawo chinali kundithandiza kuti ndisamangodalira chithandizo cha ena. Panopa ndimaona kuti anandithandiza kwambiri.

Pamene ine ndi Lesley tinali ana, apainiya ankabwera kudzakhala kwathu ndipo tinkakonda kuyenda nawo mu utumiki. Loweruka ndi Lamlungu tinkangokhalira kulalikira kunyumba ndi nyumba, mumsewu ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Wofalitsa aliyense ankalimbikitsidwa kukwanitsa maola 60. Mayi athu ankakwanitsa maolawa pafupifupi mwezi uliwonse ndipo tingati anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri.

KUCHITA UPAINIYA KU TASMANIA

Ndinayamba upainiya kuchilumba china cha ku Australia chotchedwa Tasmania. Ndinkatumikira limodzi ndi mchemwali wanga ndi mwamuna wake. Koma kenako, anandisiya n’kupita ku kalasi ya nambala 15 ya Sukulu ya Giliyadi. Ndinali wamanyazi kwambiri ndipo aka kanali koyamba kuchoka kwathu. Ena ankati sinditha miyezi itatu. Koma pasanathe chaka, mu 1950, ndinaikidwa kukhala mtumiki wa gulu, amene panopa amatchedwa wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu. Kenako ndinayamba upainiya wapadera limodzi ndi m’bale wina.

Tinatumizidwa kutauni ina yakutali, kumene kunali migodi ndipo kunalibe Mboni. Tinafika kutauniyi pa basi madzulo ndipo tinagona mu hotelo ina yachikalekale. Kutacha, tinayamba kulalikira komanso tinkafunsa anthu ngati akudziwa kumene tingapeze nyumba yalendi. Dzuwa litatsala pang’ono kulowa, munthu wina anatiuza kuti m’nyumba ya m’busa pafupi ndi tchalitchi china simunkakhala anthu. Ndiye anatiuza kuti tikalankhulane ndi adikoni. Adikoniwo anatilandira bwino ndipo anatilola kukhala m’nyumbayo. Zinali zachilendo ndithu kuti tinkachokera m’nyumba ya m’busa kupita kukalalikira.

Anthu m’derali ankamvetsera bwino ndipo tinayambitsa maphunziro ambirimbiri. Kenako akuluakulu a tchalitchicho, amene ankakhala kulikulu, anamva kuti a Mboni akukhala m’nyumba ya m’busa. Ndiyeno anauza dikoniyo kuti atitulutsemo msangamsanga. Apa tinayambanso kusowa nyumba.

Tsiku lotsatira titalalikira mpaka masana, tinayambanso kusakasaka malo ogona. Tinaganiza zoti tikangogona musitediyamu. Tinabisa masutikesi athu musitediyamumo n’kupitiriza kulalikira. Mdima unayamba koma tinafuna kumaliza nyumba zinazake. Panyumba ina, munthu wina anatipatsa nyumba yaing’ono.

KUKHALA WOYANG’ANIRA DERA NDIPONSO KUPITA KU GILIYADI

Nditatumikira kumeneku kwa miyezi pafupifupi 8, ofesi ya nthambi ya ku Australia inandipempha kuti ndikhale woyang’anira dera. Ndinadabwa  kwambiri chifukwa pa nthawiyi ndinali ndi zaka 20 zokha. Anandiphunzitsa utumikiwu kwa milungu ingapo kenako ndinayamba kuyendera mipingo. Anthu amene anali aakulu kundiposa anali ambiri koma sankandiderera. Iwo ankalemekeza kwambiri utumiki wanga.

Popita ku mipingo, ndinkayenda mosiyanasiyana. Mlungu wina ndinkayenda pa basi, wina pa sitima kapena pa galimoto. Nthawi zina, ndinkakwezedwa njinga yamoto nditanyamula sutikesi ndi chikwama cha mu utumiki. Ndinkasangalala kwambiri kukhala kunyumba za abale ndi alongo. M’bale wina, yemwe anali mtumiki wa gulu, anafunitsitsa kuti ndifikire m’nyumba yake ngakhale kuti inali yosatha. M’nyumbayi ndinkagona kubafa koma tonse tinalimbikitsidwa kwambiri mlungu umenewo.

Mu 1953, ndinadabwanso nditauzidwa kuti ndidzaze fomu yoti ndikalowe kalasi ya nambala 22 ya Sukulu ya Giliyadi. Ndinasangalala kwambiri. Komabe ndinali ndi nkhawa chifukwa mchemwali wanga ndi mwamuna wake atamaliza maphunziro awo a Giliyadi pa July 30, 1950, anatumizidwa ku Pakistan. Koma pasanathe n’chaka chomwe, Lesley anadwala mpaka kumwalira. Choncho ndinkakayikira ngati makolo anga angakonde kuti ndipite kukatumikira kudziko lina pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Lesley anamwalira. Koma makolowo anati: “Pita ukatumikire Yehova kulikonse kumene akufuna.” Kuchokera pa nthawiyi, sindinawaonenso bambo anga chifukwa chakuti anamwalira mu 1957.

Ndiyeno ndinauyamba ulendo wa ku New York City. Ndinayenda milungu 6 pa sitima yapamadzi limodzi ndi Akhristu ena 5 a ku Australia. Pa ulendowu, tinkawerenga ndi kuphunzira Baibulo ndiponso kulalikira kwa anthu ena amene tinali nawo mu sitimayi. Tisanafike kumalo amene kunali sukuluyi, komwe ndi ku South Lansing, ku New York, tinachita nawo msonkhano wa mayiko ku sitediyamu ya Yankee mu July 1953. Kunafika anthu okwana 165,829.

M’kalasi yathu munali anthu 120 ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Sanatiuze kumene atitumize mpaka tsiku lomaliza maphunziro. Ndiyeno titauzidwa, aliyense anathamangira kulaibulale kukafufuza za dziko limene akupita. Ine ndinafufuza za dziko la Paraguay kumene ananditumiza. Ndinapeza kuti dzikoli linali ndi mavuto a zandale. Nditafika ku Paraguay, usiku wina ndinamva phokoso lalikulu. Kutacha ndinafunsa amishonale anzanga za phokosolo. Iwo anangoseka n’kunena kuti: “Uli ndi mwayi woona kusintha kwa boma.” Kenako anandiuza kuti ndiyang’ane kunja ndipo ndinaona asilikali ali mbwee.

ZOCHITIKA ZOSAIWALIKA

Tsiku lina ine ndi woyang’anira dera wina tinapita ku mpingo wakutali kukasonyeza anthu filimu ina yonena za gulu la Mboni za Yehova. Kuti tikafike, tinayenda maola pafupifupi 9. Poyamba tinakwera sitima, kenako ngolo yokokedwa ndi mahatchi kenako ya ng’ombe. Tinatenga zipangizo  zonse zokaonetsera filimuyo. Tsiku lotsatira, tinayenda m’nyumba za anthu kumafamu n’kumawaitana kuti abwere kudzaonera filimuyo madzulo. Kunabwera anthu pafupifupi 15.

Titaonetsa filimuyo kwa mphindi 20, tinauzidwa kuti tilowe m’nyumba msangamsanga. Tinanyamula kanema n’kulowa. Kenako tinangomva anthu akuchita phokoso, kuomba mfuti ndiponso kunena mobwerezabwereza kuti: “Mulungu wathu ali ndi ludzu. Akulakalaka magazi a alendo anuwo.” Alendo amene ankanenedwa tinali ine ndi mzangayo. Anthu amene ankaonera filimuyo analimbana ndi gululo kuti lisalowe m’nyumbamo mpaka linachoka. Koma linadzabweranso cha m’ma 3 koloko m’bandakucha likuomba mfuti n’kumanena kuti litidikirira munjira tikamabwerera kutauni.

Abale anadziwitsa mkulu wa apolisi za nkhaniyi ndipo iye anabwera masana ndi mahatchi awiri kuti atiperekeze pobwerera kutauni. M’njira ankati tikayandikira malo owirira, iye ankatulutsa mfuti ndi kutsogola kuti aone ngati pabisala anthu. Pa ulendowu, ndinaona kuti hatchi ndi yothandiza pa kayendedwe choncho ndinadzapeza yanga.

AMISHONALE ENANSO ANABWERA

Ngakhale kuti atsogoleri a zipembedzo ankayesetsa kutiletsa, tinkalalikirabe ndipo anthu ankamvetsera. Mu 1955, amishonale enanso asanu anabwera. Wina anali mlongo wa ku Canada dzina lake Elsie Swanson, yemwe anali atamaliza maphunziro a Giliyadi a kalasi ya nambala 25. Iye asanatumizidwe kutauni ina, tinatumikira limodzi ku ofesi ya nthambi. Elsie ankatumikira Yehova modzipereka kwambiri ngakhale kuti makolo ake sanali Mboni za Yehova ndipo sankamuthandiza kwenikweni. Tinakwatirana pa December 31, 1957. Kenako tinkakhala tokha kunyumba ya amishonale ina kum’mwera kwa Paraguay.

Tinalibe madzi m’nyumbayo koma kunali chitsime kuseri. Choncho m’nyumba mwathu tinalibe bafa, chimbudzi, ndiponso makina ochapira. Tinalibenso firiji moti chakudya china tinkayenera kugula tsiku ndi tsiku. Koma nthawi imeneyi inali yosangalatsa kwambiri chifukwa chakuti tinalibe nkhawa zambiri komanso tinkakhala bwino ndi abale ndi alongo.

Mu 1963, tinapita ku Australia kukaona mayi anga. Titangofika, iwo anayamba kudwala mtima. Zikuoneka kuti matendawo anayamba chifukwa anasangalala kwambiri pondiona pambuyo pa zaka 10. Nthawi itayandikira yoti tibwerere  ku Paraguay, tinavutika kusankha zochita. Tinkadzifunsa kuti, ‘Kodi tibwereredi ku Paraguay, komwe tinkakonda kwambiri? Kodi n’zoona kuti tisiye mayi anga kuchipatala kuti asamaliridwe ndi anthu ena?’ Titapemphera kwambiri, tinasankha kukhala kuti tisamalire mayi. Tinawasamalira komanso kupitiriza utumiki wa nthawi zonse mpaka pamene iwo anamwalira mu 1966.

Kwa zaka zambiri, tinali ndi mwayi wotumikira m’ntchito yoyang’anira dera ndiponso chigawo m’dziko la Australia. Komanso ndinali ndi mwayi wophunzitsa akulu mu Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Koma kenako zinthu zinasinthanso. Ndinapemphedwa kuti ndikhale mu Komiti ya Nthambi yoyamba ku Australia. Itafika nthawi yoti timange ofesi ya nthambi yatsopano, anandisankha kukhala woyang’anira m’komiti yomanga. Abale ambiri odziwa bwino ntchitoyi anathandiza kuti ofesi ya nthambi yokongola kwambiri imangidwe.

Kenako ndinapemphedwa kuti ndikhale mu Dipatimenti ya Utumiki imene imayang’anira ntchito yolalikira. Ndinapatsidwanso mwayi woyendera nthambi zosiyanasiyana kuti ndithandize ndiponso kulimbikitsa abale ndi alongo. M’mayiko ena, ndinalimbikitsidwa kwambiri kukumana ndi Akhristu amene anakhala zaka zambiri m’ndende chifukwa chomvera Yehova mokhulupirika.

UTUMIKI UMENE TIKUCHITA PANOPA

Nditangofika kuchokera ku ulendo woyendera nthambi mu 2001, ndinapeza kalata yondipempha kuti ndikatumikire ku Brooklyn, New York. Anandipempha kuti ndikhale m’Komiti ya Nthambi imene inali itangokhazikitsidwa kumene ku United States. Titapempherera nkhaniyi, ine ndi Elsie tinavomera mosangalala. Panopa tatumikira kuno ku Brooklyn kwa zaka zoposa 11.

Ndikusangalala kuti mkazi wanga amalolera chilichonse chimene Yehova watipempha. Panopa tili ndi zaka za m’ma 80 koma tidakali athanzi. Tikuyembekeza nthawi imene tidzaphunzitsidwa ndi Yehova kwamuyaya komanso pamene onse ochita chifuniro chake adzalandira madalitso ambiri.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Mlungu wina ndinkayenda pa basi, wina pa sitima kapena pa galimoto. Nthawi zina, ndinkakwezedwa njinga yamoto nditanyamula sutikesi ndi chikwama cha mu utumiki

[Mawu Otsindika patsamba 21]

Tikuyembekeza nthawi imene tidzaphunzitsidwa ndi Yehova kwamuyaya

[Zithunzi patsamba 18]

Kumanzere: Ndili woyang’anira dera ku Australia

Kumanja: Ndili ndi makolo anga

[Chithunzi patsamba 20]

Tsiku la ukwati wathu pa December 31, 1957