Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Lolani Yehova Kukutsogolerani ku Ufulu Weniweni

Lolani Yehova Kukutsogolerani ku Ufulu Weniweni

 Lolani Yehova Kukutsogolerani ku Ufulu Weniweni

“[Muziyang’anitsitsa] m’lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu.”—YAK. 1:25.

KODI MUNGAFOTOKOZE?

Kodi ndi lamulo liti limene limabweretsa ufulu weniweni? Nanga ndani amapindula nalo?

Kodi tingatani kuti tipeze ufulu weniweni?

Kodi anthu amene amamvera Yehova adzapeza ufulu uti?

1, 2. (a) Kodi chikuchitika n’chiyani pa nkhani ya ufulu m’dzikoli ndipo chifukwa chiyani zikutero? (b) Kodi atumiki a Yehova akuyembekezera ufulu wotani?

MASIKU ano anthu ambiri ndi adyera, osamvera malamulo ndiponso achiwawa. (2 Tim. 3:1-5) Chifukwa cha zimenezi, maboma amapanga malamulo ambiri, amawonjezera apolisi ndiponso amaika m’malo osiyanasiyana makamera oonera zimene zikuchitika. M’mayiko ena, anthu amaonetsetsa kuti nyumba zawo ndi zotetezeka poika maalamu, maloko ambiri ndiponso mipanda yamagetsi. Ambiri safuna kutuluka usiku. Salolanso kuti ana awo azisewera okha panja ngakhale masana. N’zoonekeratu kuti ufulu ukucheperachepera ndipo zimenezi zipitirira.

2 M’munda wa Edeni, Satana ananena kuti anthu angakhale pa ufulu weniweni ngati atasiya kutsogoleredwa ndi Yehova. Limenelitu ndi bodza loopsa komanso lamkunkhuniza. Anthu ambiri akamanyalanyaza mfundo za Mulungu, dziko lonse limakhala pa mavuto. Mavuto amenewa amatikhudzanso atumiki a Yehovafe. Ngakhale zili choncho, tikuyembekezera nthawi imene anthu adzamasulidwa ku ukapolo wa uchimo ndi kuvunda. Pa nthawi imeneyo, anthu adzasangalala ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Panopa Yehova wayamba kale kukonzekeretsa anthu kuti adzakhale pa ufulu umenewu. Kodi akuchita bwanji zimenezi?

3. Kodi Yehova wapatsa Akhristu lamulo liti, ndipo tikambirana mafunso ati?

3 Yankho lake likupezeka pa zimene Yakobo ananena. Iye anatchula za ‘lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu.’ (Werengani Yakobo 1:25.) Mabaibulo ena amamasulira mawu a m’lembali kuti “lamulo langwiro limene limapatsa ufulu” (Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero)  ndiponso “m’lamulo langwiro, ndilo laufulu” (Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu). Nthawi zambiri, anthu amaganiza kuti malamulo amawachotsera ufulu osati kuwapatsa. Ndiyeno kodi ‘lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu’ n’chiyani? Kodi lamuloli limatipatsa bwanji ufulu?

LAMULO LIMENE LIMABWERETSA UFULU

4. Kodi ‘lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu’ n’chiyani? Nanga ndi ndani amene amapindula nalo?

4 ‘Lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu’ si Chilamulo cha Mose. Chilamulocho chinachititsa kuti machimo aonekere ndipo chinakwaniritsidwa ndi Khristu. (Mat. 5:17; Agal. 3:19) Ndiyeno kodi Yakobo ankanena za lamulo liti? Iye anali kunena za “chilamulo cha Khristu” chomwe chimatchedwanso kuti “lamulo la chikhulupiriro” ndiponso “lamulo la mfulu.” (Agal. 6:2; Aroma 3:27; Yak. 2:12) “Lamulo langwiro” limaphatikizapo zinthu zonse zimene Yehova amafuna kuti tizichita. Akhristu odzozedwa ndiponso “nkhosa zina” amapindula ndi lamulo limeneli.—Yoh. 10:16.

5. N’chifukwa chiyani lamulo laufulu si lolemetsa?

5 Mosiyana ndi malamulo amene mayiko ambiri amakhazikitsa, ‘lamulo langwiro’ ndi losavuta kumva ndipo si lolemetsa. Lamuloli lili ndi malamulo osavuta ndiponso mfundo zothandiza pa moyo wathu. (1 Yoh. 5:3) Yesu anati: “Goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:29, 30) Komanso ‘lamulo langwiro’ lilibe mndandanda wa zilango zomwe munthu angalandire akaswa malamulo ake. M’malomwake, linapangidwa chifukwa cha chikondi ndipo lalembedwa m’maganizo ndi m’mitima ya anthu osati pazolembapo zamiyala.—Werengani Aheberi 8:6, 10.

KODI ‘LAMULO LANGWIRO’ LIMABWERETSA BWANJI UFULU?

6, 7. Kodi cholinga cha mfundo za Yehova n’chiyani? Nanga lamulo la ufulu limatithandiza kuchita chiyani?

6 Yehova anapereka malamulo n’cholinga choti atithandize ndiponso kutiteteza. Mwachitsanzo, taganizirani za malamulo a chilengedwe a m’thupi. Thupi lathu likatiuza kumwa madzi kapena kudya, sitiona kuti tikuponderezedwa. Koma timayamikira malamulowo chifukwa timadziwa kuti amatithandiza kukhala athanzi. Mofanana ndi zimenezi, mfundo za Yehova zokhudza makhalidwe ndiponso kulambira, zomwe zili mu ‘lamulo langwiro’ la Khristu, zimatithandiza.

7 Lamulo la ufulu limatiteteza. Komanso limatithandiza kukwaniritsa zofuna zathu zonse zabwino popanda kudzipweteka kapena kusokoneza ufulu wa anthu ena. Kuti tikhale ndi ufulu weniweni wochita zinthu zonse zimene timalakalaka, zimene timalakalakazo ziyenera kukhala zabwino. Ziyenera kukhala zogwirizana ndi makhalidwe ndiponso mfundo za Yehova. Choncho tiyenera kuphunzira kukonda zimene Yehova amakonda ndiponso kudana ndi zimene amadana nazo. Lamulo la ufulu lingatithandize kuchita zimenezi.—Amosi 5:15.

8, 9. Kodi anthu amene amatsatira lamulo la ufulu amapindula bwanji? Perekani chitsanzo.

8 Popeza kuti ndife opanda ungwiro, timavutika kugonjetsa zilakolako zoipa. Komabe, tikamatsatira mokhulupirika lamulo la ufulu, timatha kukhala aufulu ngakhale panopa. Mwachitsanzo, munthu wina dzina lake Jay, amene anali atangoyamba kumene kuphunzira Baibulo, ankasuta fodya kwambiri. Koma ataphunzira kuti Mulungu amadana ndi kusuta, anayenera kusankha zochita. Anayenera kusankha kutsatira chilakolako cha thupi kapena kumvera Yehova. Iye anasankha mwanzeru. Anasankha kutumikira Mulungu ngakhale kuti ankavutika kwambiri ndi chibaba. Kodi anamva bwanji atasiya kusuta? Iye anati, “Ndinaona kuti tsopano ndine waufulu komanso wosangalala kwambiri.”

9 Jay anadzionera yekha kuti ufulu wa dzikoli, womwe umalola anthu kutsatira zofuna zathupi, umangowachititsa kukhala pa ukapolo.  Koma ufulu umene Yehova amapereka, womwe ndi kutsatira zofuna za mzimu, umatimasula ku ukapolo ndiponso kutibweretsera “moyo ndi mtendere.” (Aroma 8:5, 6) Kodi Jay anatha bwanji kuthana ndi vuto lake losuta fodya? Sanathane nalo yekha koma anathandizidwa ndi Mulungu. Iye anati: “Ndinkaphunzira Baibulo nthawi zonse, kupempha mzimu woyera kwa Mulungu ndiponso anthu mu mpingo ankandithandiza mwachikondi.” Zinthu zimenezi zingatithandizenso kuti tipeze ufulu weniweni. Tiyeni tione mmene zingatithandizire.

MUZIYANG’ANITSITSA M’MAWU A MULUNGU

10. Kodi ‘kuyang’anitsitsa’ m’lamulo la Mulungu kumatanthauza chiyani?

10 Lemba la Yakobo 1:25 limati: “Woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala polichita.” Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kuyang’anitsitsa’ amatanthauza “kuwerama kuti muonetsetse bwinobwino.” Kuchita zimenezi kumafuna kuyesetsa mwakhama. Ngati tikufuna kuti lamulo la ufulu litifike pa mtima ndi kusintha mmene timaganizira, tiyenera kuchita khama kuphunzira Baibulo, kupemphera ndiponso kusinkhasinkha zimene taphunzira.—1 Tim. 4:15.

11, 12. (a) Kodi Yesu anatsindika bwanji kufunika kotsatira choonadi pa moyo wathu? (b) Kodi zithunzi zili pamwambazi zikusonyeza kuti achinyamata ayenera kupewa chiyani?

11 Komanso tiyenera ‘kulimbikira’ kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kuti tizitsatira choonadi pa moyo wathu. Yesu analankhula zofanana ndi zimenezi kwa ophunzira ake ena. Iye anati: “Mukamasunga mawu anga  nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Buku lina limanena kuti mawu oti ‘kudziwa’ palembali amatanthauzanso kuyamikira kwambiri “chinthu chimene ‘tikudziwa’ chifukwa chakuti ndi chamtengo wapatali kapena chofunika kwambiri kwa ife.” Choncho ‘timadziwa’ bwino choonadi ngati timachitsatira pa moyo wathu. Pamenepo m’pamene tinganene kuti “mawu a Mulungu” ‘akugwira ntchito’ mwa ife. Mawuwo amatithandiza kusintha makhalidwe athu kuti afanane ndi a Atate wathu wakumwamba.—1 Ates. 2:13.

12 Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimadziwadi choonadi? Kodi ndimachitsatira pa moyo wanga? Kapena kodi ndimalakalakabe zinthu zina m’dzikoli zimene ndimaona kuti zingandipatse ufulu?’ Mlongo wina amene anakulira m’banja lachikhristu analemba kuti: “Mukakulira m’choonadi, mumangoona kuti Yehova alipo. Koma ine sindinkamudziwa kwenikweni. Sindinaphunzire kudana ndi zimene iye amadana nazo. Sindinkaona kuti zochita zanga zimamukhudza. Sindinkaonanso kufunika kopita kwa iye ndikakhala pa mavuto. Ndinkadalira nzeru zanga, koma kumeneku kunali kupusa chifukwa sindinkadziwa chilichonse.” N’zosangalatsa kuti mlongoyu anadzazindikira kuti maganizo ake anali olakwika ndipo anasintha. Iye anafika mpaka pochita upainiya wokhazikika.

MZIMU WOYERA UNGAKUTHANDIZENI KUPEZA UFULU

13. Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji kukhala ndi ufulu?

13 Lemba la 2 Akorinto 3:17 limati: “Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.” Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji kukhala ndi ufulu? Njira ina ndi yakuti umatithandiza kukhala ndi makhalidwe ofunika kuti tikhale ndi ufulu monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.” (Agal. 5:22, 23) Popanda makhalidwe amenewa, makamaka chikondi, anthu sangakhale ndi ufulu weniweni. Umboni wa zimenezi ukuonekera m’dzikoli. Chochititsa chidwi n’chakuti mtumwi Paulo atatchula makhalidwe amenewa, ananena kuti: “Palibe lamulo loletsa zinthu zoterezi.” Kodi iye anatanthauza chiyani? Anatanthauza kuti palibe lamulo limene lingalepheretse mzimu wa Mulungu kutulutsa makhalidwe amenewa mwa munthu. (Agal. 5:18) Lamulo lotero litakhalapo, silingagwire ntchito. Tikutero chifukwa chifuniro cha Yehova n’chakuti tiziwonjezerabe kusonyeza makhalidwe achikhristu mpaka muyaya.

14. Kodi mzimu wa dziko umachititsa bwanji anthu amene amaugonjera kukhala akapolo?

14 Anthu amene amatsogoleredwa ndi mzimu wa dziko ndiponso kuchita zilakolako za thupi, amaganiza kuti ali ndi ufulu. (Werengani 2 Petulo 2:18, 19.) Koma zimenezi si zoona. Anthu oterewa amafunikira malamulo ambirimbiri kuti asamachitirane zoipa. Paulo anati: “Lamulo siliikidwa chifukwa cha munthu wolungama. Limaikidwa chifukwa cha anthu osamvera malamulo, osalamulirika.” (1 Tim. 1:9, 10) Iwo ndi akapolo a uchimo ndipo amakakamizika “kuchita zofuna za thupi,” lomwe lili ngati wolamulira wankhanza. (Aef. 2:1-3) Anthu oterewa ali ngati tizilombo timene timalowa mu uchi chifukwa cholakalaka kuudya. Kenako amapezeka kuti akulephera kuchokamo.—Yak. 1:14, 15.

PEZANI UFULU MU MPINGO WACHIKHRISTU

15, 16. Kodi kukhala mu mpingo n’kofunika bwanji? Nanga ndi ufulu uti umene timakhala nawo mu mpingo?

15 Pamene munayamba kusonkhana ndi mpingo wachikhristu, sikuti munangosankha nokha ngati mmene mungachitire polowa gulu linalake lamasewera. Yehova ndi amene anakukokani kuti mukhale mu mpingo wake. (Yoh. 6:44) N’chiyani chinamuchititsa kukukokani? Kodi anaona kuti ndinu wolungama komanso  woopa Mulungu? Mwina mungayankhe kuti, “Mmmh, Ayi.” Nangano anaona chiyani? Iye anaona kuti muli ndi mtima umene ungamvere lamulo lake lobweretsa ufulu ndiponso umene ungalandire thandizo lake lokoma mtima. Ndiyeno mutafika mu mpingo, Yehova wakuphunzitsani Mawu ake, wakumasulani ku mabodza ndi zikhulupiriro za m’zipembedzo zonyenga komanso wakuthandizani kukhala ndi makhalidwe achikhristu. (Werengani Aefeso 4:22-24.) Izi zathandiza kuti mukhale m’gulu la anthu amene angatchedwe ‘afulu’ enieni.—Yak. 2:12.

16 Taganizirani izi. Kodi mumachita mantha mukakhala ndi anthu amene amakonda Yehova ndi mtima wonse? Kodi mumacheukacheuka? Mukamacheza ndi anthu ku Nyumba ya Ufumu, kodi mumayang’anitsitsa katundu wanu poopa kuti wina angakubereni? Ayi ndithu. Mumakhala omasuka ndiponso aufulu. Nanga mutakhala kuti muli pa zochitika za kudziko, kodi mungamve choncho? Ayi. Koma dziwani kuti ufulu umene tili nawo m’gulu la Mulungu ndi wochepa kwambiri tikayerekezera ndi umene ukubwera.

“UFULU WAULEMERERO WA ANA A MULUNGU”

17. Kodi ufulu wa anthu ukugwirizana bwanji ndi ‘kuonekera kwa ulemerero wa ana a Mulungu’?

17 Pofotokoza za ufulu umene Yehova adzapatse atumiki ake padziko, Paulo analemba kuti: “Chilengedwe chikudikira mwachidwi nthawi imene ulemerero wa ana a Mulungu udzaonekere.” Kenako anati: “Chilengedwecho chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:19-21) Mawu oti “chilengedwe” akunena za anthu amene ali ndi chiyembekezo chokhala padziko lapansi. Iwo adzapindula pamene ulemerero wa ana a Mulungu “udzaonekere.” Ulemererowu udzayamba kuonekera ‘anawa’ ataukitsidwira kumwamba. Udzaonekera akamadzathandiza Khristu kuchotsa zoipa zonse padziko ndiponso kupulumutsa “khamu lalikulu” kuti lilowe m’dziko latsopano.—Chiv. 7:9, 14.

18. Kodi ufulu wa anthu omvera uzidzawonjezereka bwanji ndipo udzafika pati?

18 Anthu amene adzapulumuke adzapeza ufulu winanso chifukwa Satana ndi ziwanda zake sadzawasokoneza. (Chiv. 20:1-3) Apa ndiye osanama, tidzamasuka kwabasi. Kenako, Khristu ndi olamulira anzake 144,000, omwenso ndi ansembe, adzapitiriza kumasula anthu. Iwo mwapang’onopang’ono adzagwiritsa ntchito nsembe ya dipo kuti uchimo wochokera kwa Adamu ndiponso kupanda ungwiro zitheretu. (Chiv. 5:9, 10) Anthu amene adzapambane mayesero omaliza adzapeza ufulu weniweni womwe umatchedwa “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” Ufuluwu ndi umene Yehova anawakonzera pachiyambi. Pa nthawiyo, sizidzakhalanso zovuta kuchita zofuna za Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti thupi lathu, mtima wathu komanso maganizo athu zidzakhala zangwiro ndipo tidzatha kutsanzira Mulungu bwinobwino.

19. Kodi masiku ano tiyenera kupitiriza kuchita chiyani kuti tidzapeze ufulu weniweni?

19 Kodi mumalakalaka “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu”? Ngati ndi choncho, pitirizani kulola kuti ‘lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu’ lizitsogolera maganizo ndi mtima wanu. Muziphunzira Malemba mwakhama. Muzitsatira choonadi pa moyo wanu ndipo muzichikonda kwambiri. Muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera. Muzilola kuti Yehova akuthandizeni kudzera mu chakudya chauzimu ndiponso mpingo wachikhristu. Kumbukirani kuti Satana anapusitsa Hava. Musalole kuti akupusitseninso n’kumaganiza kuti Mulungu amaletsa anthu kusangalala. Kunena zoona, Mdyerekezi angachite zinthu mochenjera kwambiri. Koma n’zotheka kupewa misampha yake chifukwa “tikudziwa bwino ziwembu zake.” M’nkhani yotsatira tidzakambirana zimenezi.—2 Akor. 2:11.

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 9]

Kodi ndimalakalakabe zinthu zina m’dzikoli zimene ndimaona kuti zingandipatse ufulu?

[Zithunzi patsamba 9]

Kodi ndimatsatira choonadi pa moyo wanga?