Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukomera Mtima Munthu Wokwiya Kumathandiza

Kukomera Mtima Munthu Wokwiya Kumathandiza

 Kukomera Mtima Munthu Wokwiya Kumathandiza

GEORGE ndi Manon amakhala ku Netherlands ndipo tsiku lina, akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, anapeza mayi wina wachikulire dzina lake Rie. Mayiyu sanawalandire bwino. Anawauza kuti mwamuna wake woyamba ndiponso wachiwiri komanso mwana wake wamwamuna anali atamwalira. Analinso kudwala kwambiri nyamakazi. Ngakhale kuti ankaoneka kuti mtima wake unakhala m’malo pokambirana, iye sanali waubwenzi.

Kenako George anakambirana ndi Manon kuti adzapitenso kukamupatsa maluwa chifukwa chakuti mayiyo ankaoneka kuti akusungulumwa kwambiri komanso ndi wokwiya. Atachita zimenezi, mwininyumbayo anasangalala kwambiri. Koma pa nthawiyi, analibe mpata wokwanira ndipo anapangana zoti adzapitenso ulendo wina. George ndi Manon atapitanso pa tsiku limene anapangana, sanamupeze mayiyu. Anayesa maulendo angapo pa nthawi zosiyanasiyana koma osamupezabe. Anafika poganiza kuti mayiyu akungowazemba.

Tsiku lina George atapita, anam’peza. Mayiyo anapepesa n’kumuuza George kuti sankapezeka chifukwa choti anali kuchipatala. Ndiyeno mayiyo anati: “Ukudziwa zimene ndakhala ndikuchita kuyambira tsiku limene tinasiyana lija? Ndayambatu kuwerenga Baibulo.” Anacheza bwino kwambiri ndipo phunziro la Baibulo linayambika.

Rie anasintha ataphunzira Baibulo. Sanalinso wokwiya koma wosangalala ndiponso wokoma mtima. Iye sankatha kuchoka pakhomo koma ankalalikira kwa anthu onse obwera kudzamuona. Chifukwa cha matenda ake, iye sankapezeka pa misonkhano nthawi zonse koma ankasangalala kwambiri abale ndi alongo akapita kukamuona. Pa tsiku limene ankakwanitsa zaka 82, anapezeka pa msonkhano wadera ndipo anabatizidwa posonyeza kuti anadzipereka kwa Mulungu.

Patangopita miyezi ingapo kuchokera pa tsiku limene anamwalira, anthu anapeza ndakatulo imene analemba. M’ndakatuloyo analemba mavuto amene munthu wokalamba amakumana nawo chifukwa chosowa wocheza naye. Ndipo anatsindikanso kufunika kwa kukoma mtima. Manon anati, “Ndakatuloyo inandikhudza kwambiri ndipo ndikusangalala kuti Yehova anatithandiza kumukomera mtima.”

Chitsanzo cha Yehova n’chimene chimatilimbikitsa kukhala achikondi ndiponso okoma mtima. (Aef. 5:1, 2) Zinthu zidzatiyendera bwino mu utumiki ngati ‘tikusonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu mwa kukhala okoma mtima.’​—2 Akor. 6:4, 6.