Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaika Kutumikira Yehova pa Malo Oyamba?

Kodi Mumaika Kutumikira Yehova pa Malo Oyamba?

 Kodi Mumaika Kutumikira Yehova pa Malo Oyamba?

“Pakamwa panga padzanena za chilungamo chanu, padzanena za chipulumutso chanu tsiku lonse.”​—SAL. 71:15.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

N’chifukwa chiyani Nowa, Mose, Yeremiya ndiponso Paulo anasankha kuika kutumikira Yehova patsogolo?

Kodi ndi mafunso ati amene angakuthandizeni kusankha zimene mudzachita pa moyo wanu?

N’chifukwa chiyani mukufunitsitsa kuika kutumikira Yehova pa malo oyamba?

1, 2. (a) Kodi munthu amene wadzipereka kwa Yehova amakhala atalonjeza chiyani? (b) Kodi kukambirana zimene Nowa, Mose, Yeremiya ndi Paulo anasankha kungatithandize bwanji?

MUNTHU amene wadzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa, wachita chinthu chachikulu kwambiri. Kusankha kudzipereka kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu kwambiri pa moyo wa munthu. Zili ngati munthuyo akulonjeza kuti: ‘Yehova, ine ndikufuna kuti muzindiyang’anira pa zochita zanga zonse. Ndine mtumiki wanu. Ndikufuna kuti muzindiuza zoyenera kuchita, zoyenera kuika pa malo oyamba, komanso mmene ndingagwiritsire ntchito chuma changa ndi maluso anga.’

2 Ngati ndinu Mkhristu wodzipereka ndiye kuti munalonjeza Yehova zimenezi. Munachita bwino kwambiri kusankha zinthu mwanzeru. Popeza kuti munasankha Yehova kukhala wokuyang’anirani, kodi muyenera kugwiritsa ntchito bwanji nthawi yanu? Zitsanzo za Nowa, Mose, Yeremiya ndiponso mtumwi Paulo zingatithandize kuyankha funsoli. Aliyense ankatumikira Yehova ndi mtima wonse. Zimene iwowa ankakumana nazo n’zofanana ndi zimene timakumana nazo masiku ano. Zimene anasankha kuika pa malo oyamba zingatithandize kuonanso bwino ngati timagwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru.​—Mat. 28:19, 20; 2 Tim. 3:1.

CHIGUMULA CHISANACHITIKE

3. Kodi masiku athu ano akufanana bwanji ndi nthawi ya Nowa?

3 Yesu anasonyeza kuti nthawi yathu ikufanana ndi nthawi ya Nowa. Iye anati: “Monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire. . . . Anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa,  kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo.” (Mat. 24:37-39) Masiku ano, anthu ambiri sazindikira kufunika kwa nthawi imene tikukhalamoyi. Iwo amanyalanyaza machenjezo amene atumiki a Mulungu amalengeza. Mofanana ndi nthawi ya Nowa, masiku ano anthu ena amafika ngakhale ponyoza maganizo akuti Mulungu adzaweruza anthu. (2 Pet. 3:3-7) Kodi Nowa ankagwiritsa ntchito bwanji nthawi yake m’dziko loipalo?

4. Kodi Nowa atapatsidwa ntchito ndi Yehova, ankagwiritsa ntchito bwanji nthawi yake ndipo n’chifukwa chiyani?

4 Nowa atauzidwa zimene Mulungu adzachite ndiponso atapatsidwa ntchito, anamanga chingalawa chopulumutsira anthu ndi nyama. (Gen. 6:13, 14, 22) Nowa ankachenjezanso anthu za chiweruzo cha Yehova. Mtumwi Petulo ananena kuti Nowa anali “mlaliki wa chilungamo.” (Werengani 2 Petulo 2:5.) Zimenezi zikusonyeza kuti Nowa anayesetsa kuthandiza anthu kuti asinthe chifukwa moyo wawo unali pa ngozi. Kodi Nowa ndi banja lake akanachita bwino kugwiritsa ntchito nthawi yawo poyesetsa kukhala ndi bizinezi yaikulu kapena kukhala moyo wotsogola ndiponso wapamwamba? Ayi. Popeza ankadziwa zam’tsogolo, iwo sanafune kusokonezedwa ndi zinthu ngati zimenezi.

ZIMENE KALONGA WA KU IGUPUTO ANASANKHA

5, 6. (a) Kodi Mose ayenera kuti ankaphunzitsidwa kuti adzachite chiyani? (b) N’chifukwa chiyani Mose anakana kukhalabe kalonga ku Iguputo?

5 Tiyeni tsopano tikambirane chitsanzo cha Mose. Iye anakulira m’nyumba yachifumu ku Iguputo ndipo mwana wa Farao anamulera monga mwana wake. Monga kalonga, iye anaphunzitsidwa “nzeru zonse za Aiguputo.” (Mac. 7:22; Eks. 2:9, 10) N’kutheka kuti anamuphunzitsa zimenezi n’cholinga choti adzagwire ntchito zothandiza Farao. Iye akanatha kukhala munthu wapamwamba m’boma lamphamvu kwambiri pa nthawi imeneyo. Akanathanso kukhala ndi zinthu zonse zabwino ndiponso zosangalatsa zimene munthu wotere ankakhala nazo. Kodi Mose ankaona kuti zinthu zimenezi n’zofunika?

6 Mose ali mwana, makolo ake om’bereka anamuphunzitsa za Yehova. Choncho ayenera kuti ankadziwa zimene Yehova analonjeza makolo ake akale, omwe ndi Abulahamu, Isaki ndiponso Yakobo. Mose ankakhulupirira malonjezo amenewo. Ayenera kuti ankaganizira kwambiri za tsogolo lake ndiponso za kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Ndiyeno kodi anatani itafika nthawi yoti asankhe kukhalabe kalonga wa ku Iguputo kapena kapolo wachiisiraeli? Mose anasankha “kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mochita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.” (Werengani Aheberi 11:24-26.) Iye anatsatira malangizo a Yehova a mmene angagwiritsire ntchito moyo wake. (Eks. 3:2, 6-10) N’chifukwa  chiyani Mose anasankha kuchita zimenezi? Anatero chifukwa chokhulupirira malonjezo a Mulungu. Ankadziwa kuti zimene angachite ku Iguputo zilibe tsogolo. Pasanapite nthawi yaitali, Mulungu analanga Aiguputo ndi miliri 10. Kodi anthu odzipereka kwa Yehova masiku ano akuphunzirapo chiyani pamenepa? M’malo moika maganizo pa ntchito kapena zosangalatsa za m’dzikoli, tiziika maganizo athu pa Yehova ndi kumutumikira.

YEREMIYA ANKADZIWA ZIMENE ZINALI KUTSOGOLO

7. Kodi nthawi imene Yeremiya ankakhala ikufanana bwanji ndi nthawi yathu ino?

7 Nayenso mneneri Yeremiya ankaika kutumikira Yehova patsogolo. Yehova anauza Yeremiya, monga mneneri wake, kulalikira uthenga wachiweruzo kwa anthu opanduka ku Yerusalemu ndiponso Yuda. Nthawi ya Yeremiya inali yofanana ndi nthawi yathu ino. Iye ankakhalanso “m’masiku otsiriza.” (Yer. 23:19, 20) Ankadziwa bwinobwino kuti dziko limene ankakhala liwonongedwa.

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani Baruki ankafunika kuthandizidwa kuti asinthe maganizo? (b) Kodi tiyenera kuika chiyani pa malo oyamba tikamaganizira zam’tsogolo?

8 Kodi Yeremiya anapewa kuchita chiyani chifukwa cha zimene ankakhulupirira? Iye sanaganize zopanga maziko m’dziko limene linatsala pang’ono kuwonongedwa. Kuchita zimenezi kukanakhala kosathandiza. Koma pa nthawi ina, mlembi wa Yeremiya dzina lake Baruki sankaona zinthu moyenera. Choncho Mulungu anauzira Yeremiya kuuza mlembi wakeyu kuti: “Taona! Zimene ndamanga, ndikuzigwetsa, ndipo zimene ndabzala, ndikuzizula. Ndichita zimenezi m’dziko lonse. Koma iwe, ukufunafunabe zinthu zazikulu. Leka kuzifunafuna. Anthu onse ndikuwagwetsera tsoka ndipo iwe ndidzakupatsa moyo wako monga chofunkha chako kulikonse kumene ungapite.”​—Yer. 45:4, 5.

9 Sitikudziwa bwinobwino “zinthu zazikulu” zimene Baruki ankafunafuna. * Chimene tikudziwa n’chakuti zinthuzi zinali zopanda tsogolo ndipo zinali zoti ziwonongedwa pamene Ababulo ankawononga Yerusalemu mu 607 B.C.E. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Kuti tipeze zinthu zofunika pa moyo timafunika kuganizira zam’tsogolo. (Miy. 6:6-11) Koma kodi ndi nzeru kutaya nthawi komanso mphamvu zambiri kuti tipeze zinthu zosakhalitsa? N’zoona kuti gulu la Yehova limapitiriza kumanga Nyumba za Ufumu zatsopano, nthambi ndiponso zinthu zina zokhudza Ufumu. Koma zinthu zimenezi zili ndi tsogolo chifukwa chakuti cholinga chake n’kupititsa patsogolo ntchito ya Ufumu. Anthu a Yehova angachitenso bwino kuika pa malo oyamba zinthu zokhudza Ufumu akamaganizira zam’tsogolo. Kodi inuyo mukuona kuti ‘mukufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo cha Yehova’?​—Mat. 6:33.

“NDIMAZIYESA MULU WA ZINYALALA”

10, 11. (a) Kodi n’chiyani chimene Paulo ankaona kuti n’chofunika kwambiri asanakhale Mkhristu? (b) N’chifukwa chiyani Paulo anasintha?

10 Pomaliza, tiyeni tikambirane za Paulo. Iye asanakhale Mkhristu, anachita zinthu zimene zinkaoneka ngati zingamuthandize m’tsogolo. Iye anaphunzitsidwa zamalamulo achiyuda ndi mmodzi wa aphunzitsi otchuka kwambiri. Iye anali kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzake ambiri. (Mac. 9:1, 2; 22:3; 26:10; Agal. 1:13, 14) Koma Paulo anasintha atazindikira kuti Yehova sakudalitsanso mtundu wa Ayuda.

11 Paulo anazindikira kuti kupita patsogolo m’Chiyuda n’kopanda ntchito pa maso pa Yehova ndipo kunalibe tsogolo. (Mat. 24:2) Paulo, yemwe poyamba anali Mfarisi, anaona kuti  mfundo zokhudza zolinga za Mulungu zimene anaphunzira ndiponso mwayi womutumikira ndi zamtengo wapatali. Iye anafika poona kuti zimene poyamba ankaganiza kuti ndi zofunika zinali “mulu wa zinyalala.” Paulo anasiya kutsatira Chiyuda ndipo anadzipereka kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino pa moyo wake wonse.​—Werengani Afilipi 3:4-8, 15; Mac. 9:15.

KODI NDI ZINTHU ZITI ZIMENE MUMAZIIKA PATSOGOLO?

12. Kodi Yesu atabatizidwa ankachita chiyani?

12 Nowa, Mose, Yeremiya, Paulo ndiponso anthu ena ambiri anagwiritsa ntchito nthawi yawo ndi mphamvu zawo potumikira Mulungu. Iwo ndi zitsanzo zabwino kwambiri kwa ife. Koma Yesu ndi mtumiki wa Yehova amene ndi chitsanzo chabwino kwambiri kuposa onse. (1 Pet. 2:21) Atabatizidwa, Yesu anagwiritsa ntchito moyo wake wonse padziko lapansi kuti alalikire uthenga wabwino ndiponso kulemekeza Yehova. Mkhristu amene amaona kuti Yehova ndi womuyang’anira amadziwa kuti kumutumikira kuyenera kukhala patsogolo pa chinthu china chilichonse. Kodi ife timaona choncho? Kodi tingatani kuti tiwonjezere zimene timachita mu utumiki popanda kunyalanyaza zinthu zina zofunika?​—Werengani Salimo 71:15; 145:2.

13, 14. (a) Kodi Akhristu onse odzipereka kwa Yehova akulimbikitsidwa kuchita chiyani? (b) Kodi anthu a Mulungu amamva bwanji akamachita upainiya?

13 Kwa zaka zambiri, gulu la Yehova lakhala likulimbikitsa Akhristu mobwerezabwereza kuti apemphere n’kuona ngati angakwanitse kuchita upainiya. Pa zifukwa zosiyanasiyana, atumiki ena okhulupirika sangakwanitse kuchita upainiya n’kumapereka maola 70 pa mwezi. (1 Tim. 5:8) Nanga bwanji inuyo? Kodi simungakwanitsedi kuchita upainiya?

14 Taganizirani mmene anthu ambiri a Mulungu anasangalalira m’mwezi wa March chaka chino pamene tinkakonzekera Chikumbutso. Apainiya othandiza anapatsidwa mwayi wosankha kupereka maola 30 kapena 50. (Sal. 110:3) Anthu mamiliyoni ambiri anachita upainiya wothandiza ndipo mipingo yambiri inasangalala kwadzaoneni. Kodi mungakonze mapulogalamu anu kuti muzichita upainiya nthawi ndi nthawi n’kumasangalala? Dzuwa likamalowa tsiku lililonse, Mkhristu amene akuchita upainiya amasangalala kunena kuti, “Yehova ndachita zonse zimene ndikanatha mu utumiki wanu.”

15. Kodi achinyamata ayenera kukhala ndi maganizo otani pa nkhani ya maphunziro?

15 Ngati mwatsala pang’ono kumaliza sukulu, mukhoza kuona kuti mudakali ndi thanzi labwino komanso mulibe maudindo ambiri. Kodi munaganizirapo zochita upainiya wokhazikika? N’zosachita kufunsa kuti alangizi a kusukulu amaona kuti ndi bwino kuchita maphunziro apamwamba kuti mudzagwire ntchito ya ndalama zambiri. Koma vuto ndi lakuti iwo amangoganizira za ndalama ndi za moyo uno umene si wokhalitsa. Koma ngati mutasankha kuchita utumiki wa nthawi zonse, mudzachita zinthu zimene zidzakupindulitsani mpaka muyaya. Mukatero, ndiye kuti mudzatsatira chitsanzo chabwino kwambiri cha Yesu ndipo mudzasangalala. Mudzakhalanso wotetezeka. Izi zidzasonyezanso kuti mukufunitsitsa kuchita zinthu mogwirizana ndi kudzipereka kwanu kwa Yehova.​—Mat. 6:19-21; 1 Tim. 6:9-12.

16, 17. Kodi Mkhristu ayenera kudzifunsa mafunso ati okhudza kutumikira Yehova?

16 Akhristu ambiri masiku ano amagwira ntchito maola ambiri kuti apeze zofunika pa banja lawo. Koma ena amagwira ntchito maola opitirira muyeso. (1 Tim. 6:8) Dzikoli limatichititsa kuganiza kuti sitingakhale bwinobwino popanda zinthu zamakono zimene  zikugulitsidwa panopa. Koma Akhristu oona salola kuti dziko la Satanali liziwauza zoyenera kuika patsogolo. (1 Yoh. 2:15-17) Anthu amene apuma pa ntchito angachitenso bwino kuganizira za upainiya. Akatero, adzasonyeza kuti amaika kutumikira Yehova patsogolo.

17 Atumiki a Yehova onse ayenera kudzifunsa kuti: Kodi cholinga changa chachikulu pa moyo n’chiyani? Kodi ndimaika patsogolo zinthu za Ufumu? Kodi ndimatsanzira Yesu pa nkhani ya kudzimana zinthu zina? Kodi ndikutsatira malangizo a Yesu oti ndizimutsatira nthawi zonse? Kodi ndingasinthe mapulogalamu anga n’cholinga choti ndizichita zambiri pa ntchito yolalikira za Ufumu kapena kuchita zinthu zina zauzimu? Ngati sindingawonjezere zimene ndimachita mu utumiki, kodi ndikuyesetsabe kukhala munthu wodzimana komanso wodzipereka?

‘AMALIMBITSA ZOLAKALAKA ZATHU KUTI TICHITE ZIMENE IYE AMAKONDA’

18, 19. Kodi mungachite bwino kupempherera nkhani iti ndipo n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kungasangalatse Yehova?

18 Zimakhala zosangalatsa kwambiri tikamaona anthu a Mulungu akuchita khama. Koma anthu ena amene akhoza kuchita upainiya alibe mtima wofuna kuuchita kapena amakayikira zoti angakwanitse. (Eks. 4:10; Yer. 1:6) Kodi iwowo angachite chiyani? Angachite bwino kupempherera nkhaniyi. Paulo anauza Akhristu anzake kuti Yehova “amachita zinthu m’njira imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.” (Afil. 2:13) Choncho ngati simulakalaka kuwonjezera utumiki wanu, muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kulakalaka komanso kukwanitsa kuchita zimenezi.​—2 Pet. 3:9, 11.

19 Nowa, Mose, Yeremiya, Paulo ndiponso Yesu anali anthu odzipereka kwambiri. Iwo ankagwiritsa ntchito nthawi ndiponso mphamvu zawo kuti alengeze machenjezo a Yehova. Iwo sanalole kuti zinthu zina ziwasokoneze kutumikira Yehova. Mapeto a dzikoli ayandikira kwambiri. Choncho tonsefe amene tadzipereka kwa Mulungu tiyenera kupitiriza kuchita chilichonse chimene tingathe kutsatira zitsanzo zabwino zimene zili m’Malemba. (Mat. 24:42; 2 Tim. 2:15) Tikamachita zimenezi, timasangalatsa Yehova ndipo iye amatidalitsa kwambiri.​—Werengani Malaki 3:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Onani buku lakuti Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya, tsamba 104 mpaka 106.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Anthu ananyalanyaza zimene Nowa anawachenjeza

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi mwaganiza mofatsa n’kuona ngati mungachite upainiya?