Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukuonetsa Ulemerero wa Yehova?

Kodi Mukuonetsa Ulemerero wa Yehova?

 Kodi Mukuonetsa Ulemerero wa Yehova?

“Tili ngati magalasi oonera amene amaonetsa ulemerero wa Yehova.”​—2 AKOR. 3:18.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Ngakhale kuti ndife ochimwa, kodi tingakwanitse bwanji kuonetsa ulemerero wa Yehova?

Kodi mapemphero athu ndiponso kupezeka pa misonkhano zingatithandize bwanji kuonetsa ulemerero wa Mulungu?

N’chiyani chingatithandize kupitiriza kuonetsa ulemerero wa Yehova?

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu akhoza kutsanzira makhalidwe a Yehova?

TONSEFE tinatengera zinazake kwa makolo athu. Choncho sitidabwa munthu wina akauza mwana wamwamuna kuti, ‘Umafanana kwambiri ndi bambo ako.’ Kapena munthu angauze mwana wamkazi kuti, ‘Ndikakuona umandikumbutsa mayi ako.’ Nthawi zambiri ana amatengera zimene makolo awo amachita. Koma nanga bwanji ifeyo? Kodi tikhoza kutsanzira Yehova, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba? Ngakhale kuti sitinamuonepo, tingadziwe makhalidwe ake amtengo wapatali tikamaphunzira Mawu ake, kuona zimene analenga ndiponso kusinkhasinkha zimene timawerenga m’Malemba. Makamaka tikamaganizira kwambiri mawu ndiponso zochita za Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, tikhoza kudziwa makhalidwe a Yehova. (Yoh. 1:18; Aroma 1:20) Choncho tingaone kuti n’zotheka kuonetsa ulemerero wa Yehova.

2 Adamu ndi Hava asanalengedwe, Mulungu ankadziwa kuti anthu adzatha kuchita chifuniro chake, kusonyeza makhalidwe ake ndiponso kumubweretsera ulemerero. (Werengani Genesis 1:26, 27.) Akhristufe tiyenera kuonetsa makhalidwe a Mulungu yemwe anatipanga. Tikamachita zimenezi, timakhala ndi mwayi waukulu kwambiri woonetsa ulemerero wa Mulungu. Kaya chikhalidwe chathu ndi chotani, kaya tachokera kudziko liti komanso kaya ndife ophunzira kwambiri kapena ayi, tikhoza kuonetsa ulemerero wa Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Mac. 10:34, 35.

3. Kodi nkhope za Akhristu zimaoneka bwanji akamatumikira Yehova?

3 Akhristu odzozedwa amaonetsa ulemerero wa Yehova. N’chifukwa chake mtumwi Paulo, yemwe analinso wodzozedwa, analemba kuti: “Tonsefe tili ndi nkhope zosaphimba ndipo tili ngati magalasi oonera amene  amaonetsa ulemerero wa Yehova. Pamene tikuonetsa ulemerero umenewu, timasintha n’kukhala ngati chifaniziro chake ndipo timaonetsa ulemerero wowonjezerekawonjezereka.” (2 Akor. 3:18) Pamene mneneri Mose ankatsika m’phiri la Sinai atanyamula miyala yolembapo Malamulo Khumi, nkhope yake inkawala chifukwa Yehova anali atalankhula naye. (Eks. 34:29, 30) Akhristu sanakumane ndi zimenezi ndipo nkhope zawo siziwala. Komabe, akamauza ena za Yehova, makhalidwe ake ndiponso cholinga chake chokhudza anthu, nkhope zawo zimaonetsa kuti ndi osangalala. Kaya ndife odzozedwa kapena a nkhosa zina, tili ngati magalasi oonera nkhope chifukwa chakuti timaonetsa ulemerero wa Yehova pa moyo wathu ndiponso mu utumiki. (2 Akor. 4:1) Kodi inuyo mukuonetsa ulemerero wa Yehova pochita zinthu zomusangalatsa ndiponso pochita khama m’ntchito yolalikira?

TIMAFUNITSITSA KUONETSA ULEMERERO WA YEHOVA

4, 5. (a) Kodi mofanana ndi Paulo, tikulimbana ndi chiyani? (b) Kodi uchimo umatikhudza bwanji?

4 Popeza kuti ndife atumiki a Yehova, timafuna kuchita zinthu zomulemekeza nthawi zonse. Komabe nthawi zambiri timalephera kuchita zimene timafuna. Nayenso Paulo anali ndi vuto limeneli. (Werengani Aroma 7:21-25.) Iye anafotokoza chifukwa chake tili ndi vutoli. Analemba kuti: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Tonse tinalandira uchimo kuchokera kwa Adamu ndipo uchimowo uli ngati mfumu yankhanza imene imatilamulira.​—Aroma 5:12; 6:12.

5 Kodi uchimo ndi chiyani? Ndi chilichonse chimene chimasemphana ndi makhalidwe a Yehova, zimene amakonda kapena zimene amafuna kwa ife. Munthu akachita tchimo amasokoneza ubwenzi wake ndi Mulungu. Uchimo umatilepheretsa kuchita zonse zimene tikufuna mofanana ndi woponya mivi yemwe walephera kulasa chinthu chimene akufuna. Nthawi zina timachimwa mwadala koma nthawi zina mosazindikira. (Num. 15:27-31) Uchimo uli ndi mphamvu kwambiri pa anthu ndipo umawalekanitsa ndi Mlengi. (Sal. 51:5; Yes. 59:2; Akol. 1:21) Choncho anthu ambiri amalephera kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso kukhala ndi mwayi wamtengo wapatali woonetsa ulemerero wa Mulungu. Ndiye n’zoonekeratu kuti uchimo ndi chilema chachikulu kwambiri chimene chikusautsa anthu kuposa chinthu china chilichonse.

6. Ngakhale kuti ndife ochimwa, kodi tingaonetse bwanji ulemerero wa Mulungu?

6 Ngakhale kuti ndife ochimwa, Yehova wasonyeza kuti ndi “Mulungu amene amapereka chiyembekezo.” (Aroma 15:13) Iye anapereka njira yothetsera uchimo pamene anapereka dipo la nsembe ya Yesu Khristu. Tikamakhulupirira nsembe imeneyi, timasiya kukhala “akapolo a uchimo” ndipo timatha kuonetsa ulemerero wa Yehova. (Aroma 5:19; 6:6; Yoh. 3:16) Tikamapitiriza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, timadalitsidwa panopa ndiponso m’tsogolo tidzakhala angwiro ndi kulandira moyo wosatha. Ngakhale kuti ndife anthu ochimwa, tili ndi mwayi wakuti Mulungu amaona kuti tikhoza kuonetsa ulemerero wake.

ZIMENE ZIMATITHANDIZA KUONETSA ULEMERERO WA MULUNGU

7. Kodi tiyenera kuvomereza chiyani kuti tithe kuonetsa ulemerero wa Mulungu?

7 Kuti tithe kuonetsa ulemerero wa Mulungu, tiyenera kuzindikira kuti ndife ochimwa. (2 Mbiri 6:36) Tiyenera kuvomereza kuti tili ndi zofooka ndiponso kulimbana nazo kuti tithe kuonetsa bwinobwino ulemerero wa Mulungu. Mwachitsanzo, ngati takhala tikuchita tchimo loonera zolaula tiyenera kuzindikira kuti tikufunikira thandizo lauzimu. Choncho tiyenera kupempha akulu kuti atithandize. (Yak. 5:14, 15) Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti tikufuna kuyamba kuonetsa ulemerero wa Mulungu. Nthawi zonse tiyenera kudzifufuza kuti tione ngati tikuchitadi zimene Yehova amafuna kuti tizichita. (Miy. 28:18; 1 Akor. 10:12)  Kaya zofooka zathu ndi zotani, tiyenera kuyesetsabe kulimbana nazo kuti tionetse ulemerero wa Mulungu.

8. Ngakhale kuti ndife anthu opanda ungwiro, kodi tiyenera kuchita chiyani?

8 Yesu anali munthu yekhayo amene anaonetsa ulemerero wa Mulungu mpaka kufa popanda kulakwitsa chilichonse. Koma ifeyo ndife anthu opanda ungwiro. Ngakhale zili choncho, tiyenera kuyesetsa kutsatira chitsanzo chake. (1 Pet. 2:21) Yehova samangoona kuti tikupita patsogolo koma amaonanso khama lathu poyesetsa kuonetsa ulemerero wake ndipo amadalitsa khamalo.

9. Kodi Baibulo limathandiza bwanji Akhristu amene amafunitsitsa kuchita zimene Mulungu amafuna?

9 Mawu a Yehova akhoza kutithandiza kudziwa mmene tingaonetsere bwino ulemerero wa Mulungu. Kuphunzira Malemba mozama ndiponso kusinkhasinkha zimene timawerenga m’Baibulo n’kofunika kwambiri. (Sal. 1:1-3) Kuwerenga Malemba tsiku ndi tsiku kungatithandize kukhala Akhristu oyenerera. (Werengani Yakobo 1:22-25.) Zimene timaphunzira m’Baibulo zimalimbitsa chikhulupiriro chathu ndiponso zimatithandiza kupewa machimo aakulu. Zimatithandizanso kuti tichite zinthu zimene zimasangalatsa Yehova.​—Sal. 119:11, 47, 48.

10. Kodi kupemphera kungatithandize bwanji kutumikira Yehova bwinobwino?

10 ‘Kulimbikira kupemphera’ kungatithandizenso kuonetsa ulemerero wa Mulungu. (Aroma 12:12) Tifunika kupemphera kwa Yehova kuti atithandize kumutumikira m’njira yoyenera. Tiyenera kumupempha kuti atipatse mzimu woyera, atithandize kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu, kulimbana ndi mayesero ndiponso kukhala ndi luso lotha “kufotokoza bwino mawu a choonadi.” (2 Tim. 2:15; Mat. 6:13; Luka 11:13; 17:5) Mofanana ndi mwana amene amadalira bambo wake, ifenso tiyenera kudalira Yehova yemwe ndi Atate wathu wakumwamba. Ngati titamupempha kuti atithandize kumutumikira bwino, tingakhulupirire kuti adzatithandizadi. Tisamaganize kuti mapemphero athu amamuvutitsa. Tikamapemphera tiyenera kumutamanda, kumuthokoza ndiponso kumupempha kuti atithandize, makamaka tikakhala pa mayesero. Tiyeneranso kumupempha kuti atithandize kumutumikira m’njira imene imalemekeza dzina lake loyera.​—Sal. 86:12; Yak. 1:5-7.

11. Kodi misonkhano yampingo imatithandiza bwanji kuonetsa ulemerero wa Mulungu?

11 Mulungu anapatsa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” udindo wosamalira nkhosa zake zamtengo wapatali. (Mat. 24:45-47; Sal. 100:3) Kapoloyu ndi wofunitsitsa kuthandiza Akhristu kuti azionetsa ulemerero wa Yehova. Misonkhano imatithandiza kusintha makhalidwe athu kuti tikhale Akhristu abwino. Izi zikufanana ndi zimene telala amachita posintha chovala kuti chizitikwana ndiponso kuti tizioneka bwino tikachivala. (Aheb. 10:24, 25) Koma kufika mochedwa kumachititsa kuti tiziphonya mfundo zina zauzimu zimene zingatithandize kukhala atumiki a Yehova abwino. Choncho tiyenera kufika pa misonkhano mofulumira.

TIYENI TIZITSANZIRA MULUNGU

12. Kodi tingatsanzire bwanji Mulungu?

12 Kuti tizikwanitsa kuonetsa ulemerero wa Yehova, tiyenera ‘kutsanzira Mulungu.’ (Aef. 5:1) Njira imodzi imene tingatsanzirire Yehova ndiyo kuyesetsa kuona zinthu ngati mmene iye amazionera. Kusachita zimenezi kungasonyeze kuti sitikulemekeza Mulungu ndipo kukhoza kutibweretsera mavuto. Popeza tikukhala m’dziko limene Satana Mdyerekezi akulamulira, tiyenera kuchita khama kwambiri kuti tizidana ndi zimene Yehova amadana nazo ndi kukonda zimene amakonda. (Sal. 97:10; 1 Yoh. 5:19) Tiyenera kukhulupirira ndi mtima wonse kuti njira yoyenera yotumikirira Mulungu ndiyo kuchita zonse ku ulemerero wake.​—Werengani 1 Akorinto 10:31.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kudana ndi tchimo ndipo zimenezi zingatithandize kupewa chiyani?

13 Yehova amadana ndi tchimo choncho  ifenso tiyenera kudana nalo. Tiyenera kuyesetsa kutalikirana ndi chilichonse chimene chingatipangitse kuchita tchimo. Mwachitsanzo, tiyenera kuyesetsa kupewa mpatuko. Tikutero chifukwa mpatuko ndi tchimo limene lingatilepheretse kuonetsa ulemerero wa Mulungu. (Deut. 13:6-9) Choncho sitiyenera kuyanjana ndi ampatuko kapena aliyense amene amati ndi m’bale koma amanyoza Mulungu. Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale kuti munthuyo ndi wachibale wathu. (1 Akor. 5:11) Kuyesa kutsutsa zonena za anthu ampatuko kapena amene amakonda kunena zoipa zokhudza gulu la Yehova sikungatithandize. Ndipo kuwerenga ngakhale pang’ono zimene amalemba m’mabuku kapena pa Intaneti n’kosayenera. Tikutero chifukwa chakuti kungawononge ubwenzi wathu ndi Yehova.​—Werengani Yesaya 5:20; Mateyu 7:6.

14. Tikamayesetsa kuonetsa ulemerero wa Mulungu, kodi tiyenera kukhala ndi khalidwe liti ndipo n’chifukwa chiyani?

14 Kukonda ena ndi njira yabwino kwambiri yotsanzirira Atate wathu wakumwamba. Tiyenera kukonda ena ngati mmene iye amachitira. (1 Yoh. 4:16-19) Tikamakondana, timasonyeza kuti ndifedi ophunzira a Yesu ndiponso atumiki a Yehova. (Yoh. 13:34, 35) Nthawi zina zimativuta kukonda anthu ena chifukwa cha kupanda ungwiro komabe tiyenera kuyesetsa kuwakonda nthawi zonse. Kuyesetsa kukhala ndi chikondi ndiponso makhalidwe ena abwino kungatithandize kuti tisachite zinthu zoipa kapena zokhumudwitsa ena.​—2 Pet. 1:5-7.

15. Kodi kukonda anthu ena kumatithandiza kuchita chiyani?

15 Tikakhala ndi chikondi, timafuna kuchitira anthu ena zinthu zabwino. (Aroma 13:8-10) Mwachitsanzo, kukonda mwamuna kapena mkazi wathu kumatithandiza kukhala wokhulupirika kwa iye. Kukonda akulu ndiponso kulemekeza ntchito yawo kungatithandize kumvera ndiponso kutsatira malangizo awo. Ana amene amakonda makolo awo amawamvera ndi kuwalemekeza. Iwo salankhula zowanyoza. Ngati timakonda anthu anzathu, sitiona kuti ndife ofunika kuposa iwowo ndipo sitingawalankhule mwachipongwe. (Yak. 3:9) Nawonso akulu amene amakonda nkhosa za Mulungu, amazisamalira mwachikondi.​—Mac. 20:28, 29.

16. Kodi kukonda Yehova ndiponso anthu ena kungatithandize bwanji mu utumiki wathu?

16 Tiyeneranso kusonyeza chikondi tikakhala mu utumiki. Ngakhale kuti anthu ena safuna kumva uthenga wathu, sitisiya kulalikira uthenga wabwino chifukwa timakonda kwambiri Yehova. Chikondi chimatilimbikitsa kukonzekera bwino tisanalowe mu utumiki ndiponso kuyesetsa kuphunzitsa Mawu a Mulungu mogwira mtima. Ngati timakondadi Mulungu ndiponso anthu ena, sitingaone kuti ntchito yolalikira za Ufumu ndi yotopetsa. M’malomwake, timaona kuti kugwira ntchitoyi ndi mwayi waukulu kwambiri ndipo timaigwira mosangalala.​—Mat. 10:7.

PITIRIZANI KUONETSA ULEMERERO WA YEHOVA

17. Popeza timadziwa kuti uchimo umatilepheretsa kuonetsa ulemerero wa Mulungu, kodi tiyenera kuchita chiyani?

17 Anthu ambiri m’dzikoli sadziwa kuopsa kwa tchimo, koma ife timadziwa. Zimenezi zimatithandiza kuzindikira kuti timafunikira kulimbana ndi chibadwa chathu chofuna kuchimwa. Kudziwa kuti ndife ochimwa kumatilimbikitsa kuphunzitsa chikumbumtima chathu kuti chizitithandiza kuchita zabwino tikayamba kuganiza zochita zoipa. (Aroma 7:22, 23) Ngakhale kuti ndife ofooka, Mulungu angatilimbitse kuti tizichita zabwino nthawi zonse.​—2 Akor. 12:10.

18, 19. (a) Kodi n’chiyani chimatithandiza kuti tipambane polimbana ndi Satana ndiponso ziwanda zake? (b) Kodi tiziyesetsa kuchita chiyani?

18 Ngati timafuna kuonetsa ulemerero wa Yehova, tiyeneranso kulimbana ndi Satana ndiponso ziwanda zake. Zida zankhondo zauzimu zimene Mulungu wapereka zimatithandiza  kupambana. (Aef. 6:11-13) Nthawi zonse Satana amayesetsa kulanda ulemerero womwe Yehova yekha ndi amene ayenera kulandira. Mdyerekezi amayesetsanso kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova. Koma zimamupweteka kwambiri akamaona anthu mamiliyoni opanda ungwiro akukhalabe okhulupirika kwa Mulungu ndiponso kumulemekeza. Choncho tiyeni tipitirize kutamanda Yehova ngati mmene zolengedwa zakumwamba zimachitira. Zimafuula kuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”​—Chiv. 4:11.

19 Choncho zivute zitani, tiyeni tiziyesetsa kuonetsa ulemerero wa Yehova nthawi zonse. Iye amasangalala kwambiri akamaona anthu okhulupirika akuyesetsa kumutsanzira ndiponso kuonetsa ulemerero wake. (Miy. 27:11) Tiyenera kukhala ndi maganizo ofanana ndi a Davide. Iye anaimba kuti: “Ndikukutamandani inu Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse, ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale.” (Sal. 86:12) Timalakalaka nthawi imene tidzatha kuonetsa ulemerero wa Yehova popanda kulakwitsa chilichonse ndiponso kumutamanda mpaka kalekale. Nthawi imeneyi idzafika ndipo anthu omvera adzasangalala kwambiri. Kodi panopa mukuonetsa ulemerero wa Yehova Mulungu ndiponso kukhala ndi chiyembekezo chochita zimenezi mpaka muyaya?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 27]

Kodi mukuonetsa ulemerero wa Yehova m’njira zimenezi?