Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu

Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu

 Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu

“[Pali] chiyembekezo cha moyo wosatha, chomwe Mulungu amene sanganame, analonjeza kalekale.”​—TITO 1:2.

TIBWEREZE

Kodi tikudziwa bwanji kuti kumwamba kumakhala chisangalalo wodzozedwa akakhalabe wokhulupirika mpaka pa mapeto pa moyo wake?

Kodi chiyembekezo chimene a nkhosa zina ali nacho n’chogwirizana bwanji ndi cha odzozedwa?

Tchulani ‘makhalidwe oyera’ komanso ‘ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu’ zimene tiyenera kusonyeza kuti tidzaone kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chathu?

1. Kodi chiyembekezo chimene Yehova watipatsa chingatithandize bwanji kupirira?

MTUMWI PAULO ananena kuti Yehova ndi “Mulungu amene amapereka chiyembekezo.” Ananenanso kuti Yehova akhoza ‘kutidzaza ndi chimwemwe chonse ndi mtendere wonse chifukwa cha kukhulupirira kwathu, kuti tikhale ndi chiyembekezo chachikulu mwa mphamvu ya mzimu woyera.’ (Aroma 15:13) Munthu akakhala ndi chiyembekezo chachikulu, amatha kupirira vuto lililonse limene wakumana nalo ndipo amachita zimenezi mosangalala komanso mwamtendere. Mofanana ndi Akhristu odzozedwa, a nkhosa zina amaona kuti chiyembekezo choterechi chili ngati ‘nangula wa miyoyo yawo ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika.’ (Aheb. 6:18, 19) Chiyembekezo chingatithandize kupirira mavuto amene timakumana nawo pa moyo komanso chimatithandiza kuti tisayambe kukayikira kapena kusowa chikhulupiriro.​—Werengani Aheberi 2:1; 6:11.

2. Kodi Akhristu masiku ano ali ndi ziyembekezo ziwiri ziti, ndipo n’chifukwa chiyani a “nkhosa zina” amachita chidwi ndi chiyembekezo chimene odzozedwa ali nacho?

2 M’nthawi ya mapeto ino, pali ziyembekezo ziwiri zimene Akhristu ali nazo. Akhristu ochepa a “kagulu ka nkhosa,” omwe ndi odzozedwa ndi mzimu, amayembekezera moyo wosafa kumwamba komwe akatumikire monga mafumu ndi ansembe limodzi ndi Khristu mu Ufumu wake. (Luka 12:32; Chiv. 5:9, 10) Akhristu ambirimbiri a “khamu lalikulu,” kapena kuti a “nkhosa zina,” amayembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi molamulidwa ndi Ufumu wa Mesiya. (Chiv. 7:9, 10; Yoh. 10:16) Koma a nkhosa zina sayenera kuiwala kuti iwo adzapulumuka pokhapokha ngati akuthandiza “abale” a Khristu, kapena kuti odzozedwa, amene adakali padziko lapansi. (Mat. 25:34-40) Akhristu odzozedwa adzalandira mphoto yawo ndipo nawonso a nkhosa zina adzalandira zimene akuyembekezera. (Werengani Aheberi 11:39, 40.) Choyamba, tiyeni tikambirane chiyembekezo chimene odzozedwa ali nacho.

 “CHIYEMBEKEZO CHA MOYO” CHA AKHRISTU ODZOZEDWA

3, 4. Kodi zimakhala bwanji kuti Akhristu odzozedwa abadwe mwatsopano kuti akhale ndi chiyembekezo cha moyo, nanga kodi chiyembekezo chimenechi n’chiyani?

3 Mtumwi Petulo analemba makalata awiri opita kwa Akhristu odzozedwa omwe iye ankawatchula kuti “osankhidwa ndi Mulungu.” (1 Pet. 1:1) Iye anafotokoza bwino za chiyembekezo chosangalatsa chimene a kagulu ka nkhosa ali nacho. M’kalata yake yoyamba, Petulo analemba kuti: “Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, pakuti mwachifundo chake chachikulu, anatibereka mwatsopano kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu. Anatibereka kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka. Cholowa chimenechi anasungira inuyo kumwamba, inuyo amene Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro. Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso, ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera mu nthawi ya mapeto. Pa chifukwa chimenechi, mukusangalala kwambiri.”​—1 Pet. 1:3-6.

4 Akhristu ochepa amene asankhidwa ndi Yehova kuti akalamulire limodzi ndi Khristu m’boma la Ufumu wakumwamba amabadwanso mwatsopano monga ana auzimu a Mulungu. Iwo amadzozedwa ndi mzimu woyera kuti atumikire monga mafumu ndi ansembe limodzi ndi Khristu. (Chiv. 20:6) Petulo ananena kuti kubadwa mwatsopanoku kumawapatsa mwayi wokhala ndi “chiyembekezo cha moyo” chomwe anachifotokoza kuti ndi “cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka” chomwe ‘awasungira kumwamba.’ N’zosadabwitsa kuti odzozedwa ‘amasangalala kwambiri’ chifukwa chokhala ndi chiyembekezo cha moyo chimenechi. Koma adzaona kukwaniritsidwa kwa chiyembekezochi akakhala okhulupirika.

5, 6. N’chifukwa chiyani Akhristu odzozedwa amafunika kuyesetsa kuti akhalebe ndi chiyembekezo chakumwamba?

5 M’kalata yake yachiwiri, Petulo analimbikitsa Akhristu odzozedwa ‘kuchita chilichonse chotheka kuti akhalebe okhulupirika n’cholinga choti apitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha.’ (2 Pet. 1:10) Iwo amafunika kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikhulupiriro, kudzipereka kwa Mulungu, kukonda abale ndiponso chikondi. Petulo anati: “Ngati zinthu zimenezi zili mwa inu ndipo zikusefukira, zidzakutetezani kuti musakhale ozilala kapena osabala zipatso.”​Werengani 2 Petulo 1:5-8.

6 Khristu ataukitsidwa anauza akulu obadwa ndi mzimu ku mpingo wa Filadefiya ku Asia Minor kuti: “Popeza unasunga mawu onena za kupirira kwanga, inenso ndidzakusunga pa ola la kuyesedwa, limene likubwera padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Ndidzakusunga pa ola limene likubwera kudzayesa okhala padziko lapansi. Ndikubwera mofulumira. Gwirabe mwamphamvu chimene uli nacho, kuti wina asakulande mphoto yako.” (Chiv. 3:10, 11) Mkhristu wodzozedwa akalephera kukhala wokhulupirika sayenerera kulandira “mphoto yosafwifwa, yaulemerero” imene analonjeza kuti adzaipereka kwa omwe adzakhala okhulupirika mpaka imfa.​—1 Pet. 5:4; Chiv. 2:10.

KULOWA MU UFUMU

7. Kodi Yuda analemba za chiyembekezo chosangalatsa chiti?

7 Cha m’ma 65 C.E., m’bale wake wa Yesu dzina lake Yuda analembera kalata Akhristu anzake odzozedwa omwe anawatchula kuti “oitanidwa.” (Yuda 1; yerekezerani ndi Aheberi 3:1.) Cholinga cha kalata yakeyi chinali kufuna kuwauza za chiyembekezo chosangalatsa cha chipulumutso chimene Akhristu onse amene aitanidwa kuti akalamulire mu Ufumu wakumwamba ali nacho. (Yuda 3) Ngakhale kuti iye anali ndi zina zofunika kwambiri zoti awauze kumapeto kwa kalata yake yachidule imene anawalembera, iye anatchula za chiyembekezo chomwe Akhristu odzozedwa ali nacho. Yuda anati: “Koma ponena za Mulungu amene angathe kukutetezani kuti musapunthwe, ndiponso kukuikani opanda chilema pamaso pa ulemerero wake ndi chisangalalo chachikulu, kwa  iyeyo, Mulungu yekhayo amenenso ndi Mpulumutsi wathu mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, kuchokera kalekale kufikira panopa, mpaka ku nthawi yonse yomka muyaya.”​—Yuda 24, 25.

8. Mogwirizana ndi mawu a pa Yuda 24, kodi ndi chiyani chikusonyeza kuti kumwamba kumakhala chimwemwe Mkhristu wodzozedwa akakhala wokhulupirika mpaka pa mapeto?

8 Komabe Mkhristu wodzozedwa aliyense amafunika kutetezedwa kuti asapunthwe n’kuwonongeka. Chiyembekezo chawo chofotokozedwa m’Baibulo n’chakuti Yesu Khristu adzawaukitsa ndi matupi auzimu n’kuwalola kuonekera pamaso pa Mulungu ndi chisangalalo chachikulu. Mkhristu wodzozedwa akamwalira ali wokhulupirika, zimakhala zosakayikitsa kuti ‘adzaukitsidwa ndi thupi lauzimu’ kapena kuti “losakhoza kuwonongeka . . .  mu ulemerero.” (1 Akor. 15:42-44) Ngati ‘kumwamba kumakhala chisangalalo chochuluka chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa,’ ndiye taganizirani za chisangalalo chimene chimakhala kumwamba pamene mmodzi wa abale ake a Khristu odzozedwa ndi mzimu, wamaliza mokhulupirika moyo wake wa padziko lapansi. (Luka 15:7) Yehova ndiponso angelo okhulupirika adzasangalala limodzi ndi Mkhristu wodzozedwa amene walandira mphoto yake ndi “chisangalalo chachikulu.”​Werengani 1 Yohane 3:2.

9. Kodi Akhristu okhulupirika odzozedwa amalowa bwanji “mwaulemerero” mu Ufumu wakumwamba, nanga chiyembekezo chimenechi chimakhudza bwanji odzozedwa amene adakali padziko lapansi?

9 Pa nkhani yofananayi, Petulo analembera Akhristu odzozedwa kuti akasunga chiyembekezo chimene ali nacho ndi kukhala okhulupirika, ‘adzawatsegulira khomo kuti alowe mwaulemerero mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wawo Yesu Khristu.’ (2 Pet. 1:10, 11) Iwo adzalowa kumwamba “mwaulemerero” ndipo adzaonetsa kwambiri makhalidwe achikhristu. Mawu akuti adzalowa “mwaulemerero” mwina akusonyeza kuti amene anagwira ntchito mwakhama kwambiri pa mpikisano wokalandira moyo adzadalitsidwa kwambiri. Iwo akamayang’ana kumbuyo, n’kuona mmene achitira mokhulupirika pa moyo wawo, mitima yawo imadzaza ndi chimwemwe komanso kuyamikira. N’zosakayikitsa kuti chiyembekezo chimenechi chimalimbikitsa kwambiri Akhristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi ‘kukonzekeretsa  maganizo awo kuti agwire ntchito mwamphamvu.’​—1 Pet. 1:13.

“MAZIKO A CHIYEMBEKEZO” CHA NKHOSA ZINA

10, 11. (a) Kodi nkhosa zina zili ndi chiyembekezo chotani? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chodzakhala kosatha padziko lapansi kukugwirizana bwanji ndi Khristu ndiponso ‘kuonekera kwa ana a Mulungu’?

10 Mtumwi Paulo analemba za chiyembekezo chosangalatsa chimene “ana a Mulungu” obadwa ndi mzimu amakhala nacho monga “olandira cholowa anzake” a Khristu. Kenako analemba za chiyembekezo chosangalatsa chimene Yehova wasungira anthu osawerengeka a nkhosa zina. Iye anati: “Pakuti chilengedwe [anthu] chikudikira mwachidwi nthawi imene ulemelero wa ana a Mulungu [odzozedwa] udzaonekere. Popeza chilengedwe chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake, osati mwa kufuna kwake koma kudzera mwa iye amene anachipereka, pa maziko a chiyembekezo chakuti chilengedwecho chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”​—Aroma 8:14-21.

11 Yehova anapatsa anthu maziko a chiyembekezo pamene analonjeza kuti adzawapulumutsa kwa “njoka yakale,” yomwe ndi Satana Mdyerekezi. Adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito “mbewu” yolonjezedwa. (Chiv. 12:9; Gen. 3:15) Yesu Khristu ndi mbali yoyamba ya “mbewu” imeneyi. (Agal. 3:16) Imfa ndiponso kuukitsidwa kwa Yesu zimatsimikizira kuti chiyembekezo chimene anthu ali nacho, chomasulidwa ku ukapolo wa uchimo ndi imfa, chidzathekadi. Kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chimenechi n’kogwirizana ndi “nthawi imene ulemelero wa ana a Mulungu udzaonekere.” Akhristu odzozedwa ndi mbali yachiwiri ya “mbewu.” Iwo ‘adzaonekera’ pamene adzathandize Khristu powononga dziko la Satana loipali. (Chiv. 2:26, 27) Izi zidzachititsa kuti nkhosa zina zotuluka m’chisautso chachikulu zipulumutsidwe.​—Chiv. 7:9, 10, 14.

12. Kodi kuonekera kwa Akhristu odzozedwa kudzathandiza bwanji anthu?

12 Koma kunena zoona, “chilengedwe” chidzapumuladi mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Pa nthawi imeneyi, “ana a Mulungu” aulemerero adzaonekeranso pamene adzagwiranso ntchito monga ansembe limodzi ndi Khristu ndipo adzathandiza anthu kupindula ndi nsembe ya dipo ya Yesu. Monga nzika za Ufumu wa Mulungu, anthu adzamasulidwa ku uchimo ndi imfa. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono, anthu omvera ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda.’ Ngati adzakhalabe okhulupirika kwa Yehova mkati mwa zaka 1,000 mpaka pamapeto pa mayesero omaliza, mayina awo adzalembedwa mu “mpukutu wa moyo.” Iwo adzalowa mu “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Chiv. 20:7, 8, 11, 12) Chimenechitu ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri.

CHIYEMBEKEZO CHATHU CHIKHALEBE CHA MOYO

13. Kodi n’chiyani chachititsa kuti tikhale ndi chiyembekezo ndipo Khristu adzaonekera liti?

13 Makalata awiri amene Petulo analemba mouziridwa ali ndi malangizo othandiza Akhristu odzozedwa komanso a nkhosa zina kuti chiyembekezo chawo chikhalebe cha moyo. Iye anawauza kuti chiyembekezocho ali nacho osati chifukwa cha ntchito zawo koma chifukwa cha kukoma mtima kwa Yehova. Analemba kuti: “Khalanibe oganiza bwino, ndipo ikani chiyembekezo chanu pa kukoma mtima kwakukulu kumene kudzafika kwa inu, Yesu Khristu akadzaonekera.” (1 Pet. 1:13) Khristu adzaonekera pamene adzabwera kudzapereka mphotho kwa otsatira ake okhulupirika komanso kudzapereka chiweruzo cha Yehova kwa anthu osaopa Mulungu.​—Werengani 2 Atesalonika 1:6-10.

14, 15. (a) Kuti tisunge chiyembekezo chathu chili chamoyo, kodi tiyenera kuganizira kwambiri za chiyani? (b) Kodi Petulo anapereka malangizo otani?

14 Kuti chiyembekezo chathu chikhalebe cha moyo, tiyenera kuganizira kwambiri za “tsiku la Yehova” tikamachita zinthu pa moyo wathu. Pa tsiku limeneli, “kumwamba” kumene kulipo, kapena kuti maulamuliro a anthu, adzawonongedwa limodzi ndi “dziko lapansi” kapena kuti anthu oipa. Nazonso “zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi” zidzawonongedwa. Ndiyeno Petulo analemba  kuti: “Ganizirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala. . . . Muzichita zimenezi poyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova, pamene kumwamba kudzapsa ndi moto n’kusungunuka, ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri n’kusungunuka.”​—2 Pet. 3:10-12.

15 “Kumwamba” ndi “dziko lapansi” zimene zidzawonongedwe zidzalowedwa m’malo ndi “kumwamba kwatsopano [boma la Ufumu wa Khristu] ndi dziko lapansi latsopano [anthu okhala pa dziko lapansi].” (2 Pet. 3:13) Kenako Petulo anapereka malangizo osapita m’mbali kuchokera pa ‘kuyembekezera’ kwathu kapena kuti kusunga chiyembekezo chathu cha dziko latsopano chili cha moyo. Iye analemba kuti: “Chotero okondedwa, pakuti mukuyembekezera zinthu zimenezi, chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga, opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.”​—2 Pet. 3:14.

TIZICHITA ZINTHU MOGWIRIZANA NDI CHIYEMBEKEZO CHATHU

16, 17. (a) Kodi tingasonyeze bwanji ‘khalidwe loyera’ komanso ndi ntchito ziti zimene zimasonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu? (b) Kodi chiyembekezo chathu chidzakwaniritsidwa bwanji?

16 Kuwonjezera pa kusunga chiyembekezo chathu chili chamoyo, tiyenera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chiyembekezo chathucho. Tiyenera kudzifufuza mokwanira kuti tidziwe kuti moyo wathu wauzimu ndi wotani. Kukhala ndi “khalidwe loyera” kukuphatikizapo ‘kukhala ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli.’ (2 Pet. 3:11; 1 Pet. 2:12) Tifunika ‘kumakondana.’ Izi zikutanthauza kuti tiyenera kuyesetsa kuchita zimene tingathe kuti tizigwirizana ndi abale athu mu mpingo ndiponso padziko lonse. (Yoh. 13:35) ‘Ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu’ zimatanthauza zinthu zimene zingalimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. Apa tikunena zinthu monga kupemphera, kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kuphunzira Mawu a Mulungu mozama, kulambira kwa pabanja ndiponso kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu.’​—Mat. 24:14.

17 Tonsefe timafuna kuchita zinthu zokondweretsa Yehova kuti adzatipulumutse dziko loipali likamadzawonongedwa. Apa m’pamene tidzaone kukwaniritsidwa kwa “chiyembekezo cha moyo wosatha chomwe Mulungu amene sanganame, analonjeza kalekale.”​—Tito 1:2.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 22]

Akhristu odzozedwa amabadwa mwatsopano kuti akhale ndi chiyembekezo cha moyo

[Chithunzi patsamba 24]

Yesetsani kuti banja lanu likhalebe ndi chiyembekezo cha moyo