Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Mbiri ya Moyo Wanga

“Kudzanja Lanu Lamanja Kuli Chimwemwe Mpaka Muyaya”

“Kudzanja Lanu Lamanja Kuli Chimwemwe Mpaka Muyaya”

Yosimbidwa ndi Lois Didur

Ndi kangati pa moyo wanu pamene munalankhulapo mawu akuti, ‘Ndikanadziwa si bwenzi nditachita zimenezi’? Ndakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 50 ndipo sindinaonepo ngakhale chinthu chimodzi chosasangalatsa chochokera m’dzanja lamanja la Yehova. Tadikirani ndikufotokozereni.

NDINABADWA m’chaka cha 1939 ndipo ndinakulira m’dera lakumidzi ku Saskatchewan m’dziko la Canada. Ndili ndi azichemwali anayi ndi mchimwene wanga mmodzi. Tinkakhala kufamu inayake ndipo moyo kumeneku unali wosangalatsa kwambiri. Tsiku lina Mboni za Yehova zinabwera kudzacheza ndi bambo anga ndipo ndinawafunsa ngati Mulungu ali ndi dzina. Iwo anandisonyeza dzina lakuti Yehova pa Salimo 83:18. Izi zinandichititsa kuti ndikhale ndi mtima wofuna kudziwa Mulungu ndiponso Mawu ake.

Pa nthawiyo ana tonse a kufamuyi tinkapita kusukulu ina ya m’mudzi yofika sitandade 8 ndipo tonse tinkaphunzira chipinda chimodzi. Sukuluyo inali kutali kwambiri ndipo tinkayenda pa hatchi kapena wapansi. Mabanja a m’deralo ndi amene ankasunga ndi kusamalira aphunzitsi. Ndiyeno chaka china, makolo anga ndi amene anayenera kusunga mphunzitsi wina dzina lake John Didur.

Sindinkadziwa kuti mphunzitsiyu nayenso ankakonda kwambiri Mawu a Mulungu. Bambo anga ankakonda chikomyunizimu ndipo tsiku lina ine ndinkalankhula zotamanda ulamuliro umenewu. Ndiyeno John anayankha chapansipansi kuti: “Palibe munthu woyenera kulamulira mnzake. Woyenera kulamulira ndi Mulungu basi.” Izi zinachititsa kuti tikambirane zinthu zambirimbiri zochititsa chidwi.

John anabadwa mu 1931 ndipo anali atamva mmene anthu anazunzikira pa nthawi ya nkhondo. Ku Korea kutabuka nkhondo mu 1950, iye anafunsa akuluakulu a chipembedzo chifukwa chimene ankamenyera nawo nkhondoyo. Onse ananena kuti n’kololeka kuti Akhristu azimenya nawo nkhondo. Kenako anadzafunsa  a Mboni za Yehova. Iwo anamufotokozera kuchokera m’Malemba mmene Akhristu oyambirira ankaonera nkhani imeneyi. John anabatizidwa mu 1955. Ine ndinabatizidwa chaka chotsatira. Tonsefe tinkadziwa kuti tikufuna kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse komanso mphamvu zathu zonse. (Sal. 37:3, 4) Mu July 1957, ndinakwatirana ndi John.

Nthawi zambiri misonkhano yachigawo inkachitika mu July pa deti limene tinakwatirana. Tinkasangalala kwambiri kukhala ndi anthu ambirimbiri amene ankalemekeza ukwati. Msonkhano wa mayiko umene tinapezekapo koyamba unachitika mu 1958. Tinanyamuka pa galimoto anthu asanu kuchokera ku Saskatchewan kupita kumzinda wa New York. Tinayenda ulendowu kwa mlungu umodzi ndipo kukada tinkagona mutenti. Titangofika ku Bethelehem, ku Pennsylvania m’bale wina amene tinakumana naye anatiuza kuti tikagone kwawo. Zimene anachitazi zinatithandiza kuti tikafike kumzinda wa New York tili aukhondo. Msonkhano umenewo unatithandiza kuona kuti munthu ukamatumikira Yehova umakhala wosangalala kwambiri. M’pake kuti wamasalimo analemba kuti: “Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe mpaka muyaya.”​—Sal. 16:11.

KUCHITA UPAINIYA

Ndiyeno mu 1959, tinkachita upainiya ndipo tinkakhala m’kakalavani kenakake pamwamba pa phiri lina ku Saskatchewan. Gawo lathu linali lalikulu kwambiri ndipo tikakhala paphirili tinkatha kuona mbali zambiri za gawoli.

Tsiku lina tinalandira kalata yosangalatsa yochokera ku ofesi ya nthambi. Nditangolandira ndinathamangira kumene John ankagwira ntchito. Pa nthawiyi anali akuyendetsa thalakitala. Inali kalata yotiuza kuti tikakhale apainiya apadera kutauni ya Red Lake ku Ontario. Popeza sitinkadziwa kumene kunali tauni imeneyi, tinayang’ana pamapu.

Kwathu kunali udzu wokhawokha koma uku kunali mitengo ikuluikulu komanso timatauni ting’onoting’ono pafupi ndi migodi. Tsiku loyamba pamene tinkafufuza malo ogona, kamtsikana kena kakang’ono kanamva tikukambirana ndi amayi ena oyandikana nawo nyumba. Kenako kamtsikanako kanathamanga n’kukauza mayi ake zoti tikufuna malo ogona ndipo anatipatsa. Kachipinda kamene tinagonako kanali kapansi kochita kukumba. Kutacha tinapitiriza kufunafuna nyumba ndipo tinapeza ya zipinda ziwiri koma yopanda madzi ndi mipando. Munali mbaula yokha basi. Kenako tinapita kushopu ina kumene ankagulitsa zinthu zogwiritsidwa kale ntchito kumene tinakagula zinthu zina zochepa.

Kumene kunali mpingo kunali kutali moti unali mtunda wokwana makilomita 209. Anthu ambiri amene ankagwira ntchito kumigodi anali ochokera ku Ulaya ndipo ankakonda kupempha kuti tiwapezere Baibulo la m’chinenero chawo. Patangopita nthawi yochepa tinapeza maphunziro a Baibulo opita patsogolo okwanira 30. Patangopita miyezi 6, mpingo waung’ono unakhazikitsidwa.

Ndiyeno mwamuna wa mayi wina amene tinkaphunzira naye anaitanitsa wansembe kuti adzaletse mayiyo kuphunzira nafe. Wansembeyo atafika ananena kuti tiyenera kumaphunzitsa za Utatu ndi zinthu zina. Mayiyo anamupatsa Baibulo lachikatolika kuti amusonyeze malemba otsimikizira zimene ankanenazo. Koma wansembeyo anangoponya Baibulolo patebulo, ndipo anakana kufotokoza chilichonse. Pamene ankatuluka m’nyumbamo, anauza banjalo m’chilankhulo cha Chiyukireniya kuti atithamangitse ndipo asadzatilandirenso. Sankadziwa kuti John amamva Chiyukireniya.

Ndiyeno patangopita nthawi yochepa chabe, tinasamuka ku Red Lake chifukwa John anauzidwa kuti akaphunzire ntchito yoyang’anira dera. Patangotha chaka chimodzi, John akukamba nkhani ya ubatizo pa msonkhano wachigawo, anaona kuti mwamuna uja anali pagulu la anthu okabatizidwa. Zimene wansembe uja  anachita zinamuthandiza kuti nayenso ayambe kuphunzira Baibulo.

KUTANGANIDWA NDI UTUMIKI WOYENDAYENDA

Pa nthawi imene tinali mu utumiki woyendayenda, tinasangalala kwambiri kukhala ndi mabanja osiyanasiyana. Tinkagwirizana kwambiri ndi anthu amene ankatisunga m’nyumba zawo. Nthawi ina m’nyengo yozizira tinkagona m’chipinda china mmene munalibe magetsi. Ndiyeno mlongo wina wachikulire ankalowa m’chipinda chathucho mwakachetechete m’mawa uliwonse kudzasonkha moto m’mbaula. Kenako pakangodutsa nthawi pang’ono ankatibweretsera madzi ofunda kuti tisambe. Ndinaphunzira zambiri kuchokera kwa mlongoyu makamaka mmene ankachitira zinthu.

Ntchito yoyendayenda inandithandiza kuyandikira kwambiri Yehova. Mlongo wina ankakhala kutauni ina yakutali kwambiri kumpoto m’dera limene tinkachitako utumiki woyendayenda ku Alberta. Kodi gulu la Yehova linkamuthandiza bwanji mlongo ameneyu yemwe ankakhala kwayekhayekhayu? Miyezi 6 iliyonse tinkapita kumeneku pa ndege ndipo kwa mlungu umodzi tinkalalikira ndiponso kuchita misonkhano ndi mlongoyu ngati mmene tinkachitira ndi mpingo waukulu. Izi zinkasonyezeratu kuti Yehova amasamalira nkhosa iliyonse mwachikondi.

Tinapitirizabe kulemberana makalata ndi anthu amene anatisunga m’nyumba zawo. Zimenezi zinandikumbutsa mphatso yoyambirira imene John anandipatsa yomwe inali kabokosi kokongola kodzaza ndi mapepala olembera makalata. Tinkasangalala kwambiri kulemberana makalata ndi mabwenzi athuwa pogwiritsa ntchito mapepala ngati amenewa. Mpaka pano ndimakakondabe kabokosi kameneka.

Tikutumikira kudera la ku Toronto, m’bale wina anaimba foni kuchokera ku Beteli n’kutifunsa ngati tingapite kukatumikira ku Beteliko. Iye amafuna kuti timuyankhe mawa lake ndipo tinamuyankhadi kuti tipita.

UTUMIKI WA PA BETELI

Kusintha kulikonse kwa utumiki kunatichititsa kuona kuti m’dzanja la Yehova muli chimwemwe. Izi zinapitirira ngakhale titapita ku Beteli m’chaka cha 1977. Tinkakhala ndi Akhristu ena odzozedwa ndipo izi zinatithandiza kuona kuti khalidwe lawo linali losiyana koma onse ankalemekeza kwambiri Mawu a Mulungu.

Moyo wa pa Beteli unali wosangalatsa kwambiri. Mwachitsanzo, zovala zathu zinkakhala m’madirowa osati musutikesi ndiponso tinkapita ku mpingo umodzi basi. Kuwonjezera pa utumiki wanga, ndinkasangalala kuyenda ndi alendo amene akufuna kuona malo pa Betelipo. Ndinkafotokoza ntchito zimene zinkachitika ndiponso kumva zimene abale amene abwera kudzaona malo ankanena. Ndinkayankhanso mafunso awo.

Zaka zinkadutsa mwamsanga kwabasi ndipo mu 1997 John anaitanidwa kuti apite ku Sukulu ya Abale a m’Makomiti a Nthambi ku Patterson, ku New York. Kenako anadzatifunsa ngati tingakonde kupita ku Ukraine. Anatiuza kuti tiganizire nkhaniyo mofatsa ndiponso tiipempherere. Madzulo a tsiku lomwelo tinaona kuti n’zotheka kupita kumeneko.

KUSAMUKIRA KU UKRAINE

Mu 1992 tinakachita msonkhano waukulu wa mayiko ku St. Petersburg ku Russia ndipo mu 1993 tinakachitanso wina ku Kiev m’dziko la Ukraine. Misonkhano imeneyi inatithandiza kukonda kwambiri abale a kum’mawa kwa Ulaya. Nyumba yoyambirira imene tinkakhala titafika ku Lviv m’dziko la Ukraine inali yosanja koma yachikalekale ndipo tinkakhala chipinda chapamwamba. Tikakhala pawindo tinkatha kuona dimba, tambala wofiira ndiponso matadzi ambirimbiri. Tinkangoona ngati tili kufamu ya ku Saskatchewan. M’nyumbayi tinkakhala anthu 12. M’mawa uliwonse tinkakwera galimoto kudutsa mumzinda kupita kukagwira ntchito ku Beteli.

Kodi tinkamva bwanji kukhala ku Ukraine? Zinali zosangalatsa kukhala pakati pa anthu amene anakumana ndi mavuto ambiri. Moti m’dzikoli iwo analetsedwa  kulalikira komanso ena anakhalapo m’ndende. Koma ngakhale kuti anakumana ndi zonsezi, iwo anali ndi chikhulupiriro cholimba. Tikawayamikira iwo ankangoyankha kuti, “Tinachita zonsezi chifukwa chokonda Yehova.” Iwo sankaona kuti asiyidwa. Ngakhale panopa umati ukathokoza munthu wina chifukwa chakuti wakuchitira zabwino, amangoyankha kuti, “Tizithokoza Yehova.” Iwo amatero chifukwa iye ndi amene amatipatsa zinthu zonse zabwino.

Anthu ambiri ku Ukraine akamapita ku misonkhano amakonda kuyenda wapansi choncho amakhala ndi nthawi yocheza ndi kulimbikitsana. Amayenda kwa ola lathunthu kapena kuposerapo. Ku Lviv kuli mipingo yoposa 50 ndipo mipingo 21 imasonkhana m’Nyumba ya Ufumu imodzi yokhala ndi zipindazipinda. Tsiku Lamlungu zimakhala zosangalatsa kuona magulumagulu a abale akubwera ku misonkhano.

Sitinachedwe kuzolowerana ndi abale ndi alongo a khalidwe labwino ndiponso okonda kuthandiza ena. Akaona kuti ndikuvutika kumva chilankhulo chawo ankaleza nane mtima kwambiri. Kungowaona umatha kuzindikira kuti iwo ndi anthu abwinodi.

Pa msonkhano wa mayiko umene unachitika mu 2003 ku Kiev panachitika chinthu china chimene chinasonyeza kuti abalefe timadalirana. Titapita kumalo ena okwerera sitima apansi pa nthaka, kamtsikana kena kanabwera n’kutiuza monong’ona kuti, “Inetu ndasochera. Agogo anga sindikuwaona.” Kamtsikanaka kanali kataona mabaji athu n’kudziwa kuti ndife Mboni za Yehova. Kanali kolimba mtima ndipo sikankalira. Ndiyeno mkazi wa woyang’anira dera amene tinali naye limodzi anakatenga n’kupita nako ku Dipatimenti ya Zotayika. Pasanapite nthawi yaitali kanakumana ndi agogo ake aja. Ndinachita chidwi ndi mmene kamtsikanaka kanasonyezera kuti pagulu la anthu ambiri kanadalira kwambiri Mboni.

Abale ochokera m’mayiko ambiri anabwera pa mwambo wopereka kwa Yehova nthambi ya Ukraine mu May 2001. Lamlungu m’mawa itangotha nkhani yapadera ku sitediyamu, chigulu cha abale chinabwera kudzaona malo a Beteli yatsopanoyo. Inali nthawi yosaiwalika. Ndinachita chidwi kwambiri kuona abale amenewa omwe ankachita zinthu mwadongosolo. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti kutumikira Mulungu n’kosangalatsa.

ZINTHU ZINASINTHA KWAMBIRI

Zinali zomvetsa chisoni kuti mu 2004 John anapezeka ndi matenda a khansa. Tinapita ku Canada kuti akalandire chithandizo. Chithandizo choyamba chinali champhamvu kwambiri moti anakhala milungu ingapo ali chikomokere m’chipinda cha anthu odwala mwakayakaya. Koma kenako anatsitsimuka. Ngakhale kuti sankatha kulankhula, maso ake ankasonyeza kuti akuyamikira abale omwe ankabwera kudzamuona.

Komabe iye sanachire ndipo anamwalira chakumapeto a 2004. Ndinkamva kuti mbali yaikulu ya thupi langa yachoka. Ine ndi John tinkasangalala kwambiri potumikira limodzi Yehova. Popeza ndinatsala ndekha, ndinafunika kusankha zoti ndichite. Ndiyeno ndinasankha zobwerera ku Ukraine. Ndimayamika kwambiri chifukwa cha chikondi chimene abale ndi alongo ku Beteli ndi ku mpingo amandisonyeza.

Sitinanong’onezepo bondo ngakhale pang’ono chifukwa cha zimene tinasankha. Takhala tikusangalala kwambiri limodzi ndi abale ndi alongo abwino kwambiri. Ndikudziwa kuti pali zinthu zambiri zokhudza ubwino wa Yehova zimene ndingaphunzire. Panopa ndikufunitsitsa kumutumikira kwamuyaya chifukwa ndatsimikiza kuti ‘kudzanja lake lamanja kuli chimwemwe.’

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Sitinanong’onezepo bondo ngakhale pang’ono chifukwa cha zimene tinasankha”

[Chithunzi patsamba 3]

Tsiku la ukwati wathu

[Chithunzi patsamba 4]

Ndili mpainiya wapadera ku Red Lake ku Ontario

[Chithunzi patsamba 5]

Ndili ndi John ku Ukraine mu 2002