Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumatani Ena Akakupemphani Malangizo?

Kodi Mumatani Ena Akakupemphani Malangizo?

 Kodi Mumatani Ena Akakupemphani Malangizo?

Kodi munayamba mwapemphedwapo kuti mupereke malangizo kwa anthu ena? Mwachitsanzo, kodi munafunsidwapo kuti: ‘Kodi nditani pamenepa? Kodi ndipite ku phwando limeneli? Kodi ndiyambe ntchito imeneyi? Kodi ndizicheza ndi munthu ameneyu kuti kenako ndidzakwatirane naye?’

Anthu ena akhoza kukufunsani moona mtima kuti muwathandize kusankha zochita. Angakufunseni kuti muwapatse malangizo okhudza ubwenzi wawo ndi anzawo, anthu a m’banja lawo kapenanso Yehova. Kodi powayankha mukhoza kugwiritsa ntchito chiyani? Kodi mumatani popereka malangizo kwa ena? Kaya nkhaniyo ikuoneka yaing’ono kapena yaikulu, lemba la Miyambo 15:28 limati: “Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe.” Tiyeni tione mmene mfundo zisanu zochokera m’Baibulo zotsatirazi zingatithandizire tikamapereka malangizo.

1 Muziyamba Mwaimvetsa Bwino Nkhaniyo.

“Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.”​MIY. 18:13.

Kuti tipereke malangizo othandiza tiyenera kumvetsa maganizo a munthu wofunsayo komanso mmene zinthu zilili pa moyo wake. Mwachitsanzo, ngati munthu wina atakuimbirani foni n’kukufunsani mapu a kunyumba kwanu, kodi mungafunikire kudziwa chiyani kuti mumuthandize? Kodi mungamufotokozere njira yoti adzere koma osadziwa malo amene iye ali pa nthawiyo? Ayi simungatero. N’chimodzimodzi ndi kupereka malangizo abwino. Muyenera kuganizira makhalidwe a munthu wofunsayo komanso mmene amaonera zinthu. Pangakhale zinthu zina zofunika kuziganizira musanayankhe. Ngati sitikudziwa bwinobwino mmene zinthu zilili, tikhoza kupereka malangizo amene angasokoneze kwambiri munthuyo.​—Luka 6:39.

Dziwani Zimene Wapeza Atafufuza. Ndi bwinonso kufunsa munthu amene akupempha malangizoyo kuti: “Kodi ukuganiza kuti ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene zingakuthandize?” “Kodi waona ubwino ndi kuipa kwa zimene ukufuna kusankha?” “Kodi wafufuza zotani pa nkhaniyi?” “Kodi anthu ena monga akulu, makolo kapena amene amakuphunzitsa Baibulo akuthandiza bwanji pa nkhaniyi?”

Mayankho ake angatithandize kudziwa zimene munthuyo wachita kale pofuna kudziwa zochita. Ifenso tidzapereka malangizo moganizira zimene ena anena kale. Tingathenso kuzindikira ngati munthuyo akungofuna malangizo ‘omukomera m’makutu.’​—2 Tim. 4:3.

  2 Musafulumire Kuyankha.

“Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.”​YAK. 1:19.

Nthawi zina tikhoza kufulumira kuyankha ndipo tingachite zimenezi ndi zolinga zabwino. Koma kodi kuchita zimenezi kungakhale kothandiza ngati sitinafufuze bwinobwino za nkhaniyo? Lemba la Miyambo 29:20 limati: “Kodi waona munthu wopupuluma m’mawu ake? Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa iyeyo.”

Muyenera kutsimikizira kuti zimene mukulankhula ndi zogwirizana ndi nzeru zochokera kwa Mulungu. Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi mwina ndayamba kuyendera maganizo ndiponso “mzimu wa dziko”?’ (1 Akor. 2:12, 13) Dziwani kuti kungokhala ndi zolinga zabwino si kokwanira. Mtumwi Petulo atadziwa mavuto amene Yesu ankayembekezera kukumana nawo, anamulangiza kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Petulo anachitazi? Ngakhale munthu amene ali ndi zolinga zabwino, ngati sangasamale, akhoza kulimbikitsa ‘maganizo a anthu osati a Mulungu.’ (Mat. 16:21-23) Choncho tiyenera kuganiza kaye tisanalankhule. Ndiponso zimene timadziwa n’zochepa kwambiri tikaziyerekezera ndi nzeru za Mulungu.​—Yobu 38:1-4; Miy. 11:2.

3 Modzichepetsa Gwiritsani Ntchito Mawu a Mulungu

“Sindichita kanthu mongoganiza ndekha. Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.”​YOH. 8:28.

Kodi mungayankhe kuti, “Ndikanakhala ine ndikanangochita zakutizakuti”? Kaya yankho la funsolo n’lodziwikiratu, muyenera kutengera chitsanzo cha Yesu pa nkhani ya kudzichepetsa. Iye anali wanzeru kuposa munthu aliyense koma ananena kuti: “Sindinalankhulepo zongoganiza pandekha, koma Atate . . . anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula.” (Yoh. 12:49, 50) Yesu ankaphunzitsa ndiponso kupereka malangizo mogwirizana ndi chifuniro cha Atate wake.

Mwachitsanzo, pa Luka 22:49 ophunzira a Yesu anamufunsa ngati zinali zoyenera kuti amenyane ndi amene anabwera kudzamugwira. Wophunzira wina anafika potema wina ndi lupanga. Nkhani imeneyi ikupezekanso pa Mateyu 26:52-54 ndipo ikusonyeza kuti ngakhale pamene zinthu zinavuta chonchi, Yesu anapeza nthawi yokambirana ndi wophunzira wakeyo zimene Yehova amafuna. Yesu ankadziwa mfundo zofotokozedwa pa Genesis 9:6 komanso ulosi wa pa Salimo 22 ndi Yesaya 53. Izi zinamuchititsa kupereka malangizo anzeru amene anapulumutsa miyoyo ya anthu komanso amene analemekeza Yehova.

  4 Muzifufuza M’mabuku Athu.

“Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?”​MAT. 24:45.

Yesu waika gulu la kapolo lodalirika kwambiri lomwe limapereka chakudya chauzimu. Ngati mwafunsidwa malangizo pa nkhani inayake yofunika kwambiri kodi mumapatula nthawi yofufuza m’mabuku ofotokoza Baibulo?

Tikhoza kupeza mfundo zomveka bwino ngati titafufuza mu zinthu monga mlozera nkhani wa m’magazini, buku la Watch Tower Publications Index komanso CD ya Watchtower Library. * Tiyeni tizigwiritsa ntchito chuma cha mtengo wapatali chimenechi. M’zinthu zimenezi mumakhala mitu ya nkhani imene ingathandize munthu kupeza mfundo zimene akufuna. Kodi inuyo muli ndi luso lothandiza anthu kuti azifufuza mfundo za m’Baibulo komanso kuona mmene angazigwiritsire ntchito pa moyo wawo? Masiku ano kuli magalimoto amakono okhala ndi makina othandiza madalaivala kudziwa malo amene ali komanso msewu umene ayenera kutenga kuti akafike komwe akupita. Mofanana ndi makinawa, zinthu zothandiza pofufuza zimene tatchulazi zingatithandize kudziwa njira yopita ku moyo wosatha.

Akulu ambiri athandiza ofalitsa kufufuza nkhani pogwiritsa ntchito zinthu zimenezi. Izi zimathandiza abale ndi alongo kuti azigwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba pochita zinthu. Kuwonjezera pa kuwathandiza kuthana ndi mavuto awo, izi zimawathandizanso kukhala ndi chizolowezi chofufuza komanso chodalira zinthu zauzimu zimene Yehova watipatsa. Pochita zimenezi, iwo “aphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikira kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.”​—Aheb. 5:14.

5 Pewani Kusankhira Ena Zochita.

“Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.”​—AGAL. 6:5.

Pomaliza munthu aliyense amafunika kusankha yekha malangizo oyenera kuwatsatira. Yehova amatipatsa ufulu wosankha kutsatira mfundo zake kapena ayi. (Deut. 30:19, 20) Pa nkhani zina, pamakhala mfundo za m’Baibulo zingapo zofunika kuziganizira ndipo wofunsa malangizoyo ndi amene ayenera kusankha zoyenera kutsatira. Pambuyo poganizira msinkhu wa munthu wofunsayo komanso nkhani imene tafunsidwayo tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ine ndi woyeneradi kuyankha funso limeneli?’ Nkhani zina zimafunika kusamaliridwa ndi akulu ndipo ngati wofunsayo ndi mwana wamng’ono, makolo ake ndi amene angamuthandize.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Panopa CD ya Watchtower Library ikupezeka m’zinenero 39 ndipo mabuku a Watch Tower Publications Index akupezeka m’zinenero 45.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 8]

Zimene Mungachite pa Nthawi ya Kulambira kwa Pabanja

Pophunzira Baibulo panokha mungachite bwino kufufuza mayankho a mafunso amene mwafunsidwa posachedwapa. Kodi ndi nkhani ziti komanso mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingathandize munthu amene wakufunsaniyo? Tiyerekeze kuti m’bale kapena mlongo wakufunsani ngati m’poyenera kuchita chibwenzi ndi munthu wina n’cholinga chodzakwatirana naye. Choyamba muyenera kufufuza mitu ya nkhani imene ikutchula mwachindunji nkhani zimenezi. Mwachitsanzo, mungafufuze mitu monga yonena za “Chibwenzi” kapena “Ukwati.” Ndiyeno mukhoza kuyang’ana timitu ting’onoting’ono kuti mupeze mfundo zoyenera. Mukapeza mutu wa nkhani muyenera kuona ngati alemba kuti “Onaninso . . . ” kuti mudziwe ngati pali nkhani zina zogwirizana ndi nkhani imene mukufufuza.

[Bokosi patsamba 9]

Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha zonse zimene amapereka kudzera mu gulu lake zomwe zimatithandiza kupereka komanso kulandira malangizo abwino kwambiri. Lemba la Mlaliki 12:11 limati: “Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga zobayira ng’ombe pozitsogolera, ndipo anthu amene amadzipereka kusonkhanitsa mawu anzeru, ali ngati misomali yokhomerera kwambiri. Mawuwo aperekedwa ndi m’busa mmodzi.” Mofanana ndi mmene “zisonga” zinkathandizira potsogolera nyama zokoka ngolo, malangizo a chikondi komanso omveka bwino angatsogolere anthu oona mtima kuyenda pa njira yoyenera. Kugwiritsa ntchito misomali kukhomera zinthu kumathandiza kuti zinthuzo zikhale zolimba. Nakonso kupereka malangizo abwino kwa ena kumathandiza chifukwa chakuti amalimbikitsidwa. Anthu anzeru “amadzipereka” kapena kuti kuyesetsa kwambiri “kusonkhanitsa mawu” amene amasonyeza nzeru za Yehova yemwe ndi “m’busa” wawo.

Tiyenera kutsanzira M’busa ameneyu pamene tikupereka malangizo. Ndi mwayi waukulu kumvetsera anthu akamatifotokozera mavuto awo ndiponso kuwapatsa malangizo. Ngati titatsatira mfundo za m’Baibulo, malangizo athu akhoza kukhala abwino komanso othandiza mpaka kalekale.