Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe Odzipereka

Khalanibe Odzipereka

 Khalanibe Odzipereka

“Lalikira mawu. Lalikira modzipereka.”​—2 TIM. 4:2.

KODI MUNGAFOTOKOZE?

N’chifukwa chiyani Akhristu oyambirira ankalalikira modzipereka?

Kodi tingatani kuti tikhalebe odzipereka?

N’chifukwa chiyani tiyenera kulalikira Ufumu modzipereka kwambiri masiku ano kuposa kale lonse?

1, 2. Kodi munthu angafunse mafunso ati pambuyo powerenga malangizo akuti, ‘lalikira modzipereka’?

ANTHU amene amagwira ntchito yopulumutsa anthu amaigwira modzipereka kwambiri komanso mwachangu. Mwachitsanzo, ogwira ntchito yozimitsa moto akaimbiridwa foni amathamanga podziwa kuti miyoyo ya anthu ili pa ngozi.

2 Cholinga cha Mboni za Yehovafe n’chakuti tithandize anthu kupulumuka. Choncho timaona kuti ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi yofunika kwambiri. Koma sizikutanthauza kuti tiyenera kuchita zinthu mopanikizika kwambiri. Ndiyeno kodi mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani pamene anapereka malangizo akuti: “Lalikira mawu. Lalikira modzipereka”? (2 Tim. 4:2) Kodi ifeyo tingatani kuti tizilalikira modzipereka? Nanga n’chifukwa chiyani tifunika kugwira ntchito yathu modzipereka komanso mwachangu?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KULALIKIRA MODZIPEREKA?

3. N’chiyani chidzachitikire anthu ngati amvetsera kapena kukana uthenga wa Ufumu?

3 Mukaganizira zimene zidzachitikire anthu chifukwa chomvetsera kapena kukana uthenga wabwino, mudzaona kuti m’pofunika kwambiri kudzipereka powauza uthengawu. (Aroma 10:13, 14) Mawu a Mulungu amati: “Ndikauza munthu woipa kuti: ‘Udzafa ndithu,’ ndiyeno iye n’kubwerera kusiya machimo akewo, n’kuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, . . . munthuyo adzakhalabe ndi moyo, sadzafa ayi. Palibe tchimo ngakhale limodzi mwa machimo onse amene anachita limene lidzakumbukiridwe ndi kumulanga nalo.” (Ezek. 33:14-16) Ndipo Baibulo limauza anthu amene amalalikira uthenga wa Ufumu kuti: “Ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.”​—1 Tim. 4:16; Ezek. 3:17-21.

4. Kodi panali kugwirizana kotani pakati pa kulalikira modzipereka ndi kuyamba kwa mpatuko nthawi ya atumwi?

 4 Kuti timvetse chifukwa chake Paulo anapereka malangizo amenewa kwa Timoteyo, tiyeni tione mfundo zina za m’mavesi oyandikana ndi 1 Timoteyo 4:2. Timawerenga kuti: “Lalikira mawu. Lalikira modzipereka, m’nthawi yabwino ndi m’nthawi yovuta. Dzudzula, tsutsa, dandaulira. Chita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambiri. Pakuti idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso chiphunzitso cholondola, koma mogwirizana ndi zilakolako zawo, adzadzipezera aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu. Iwo adzasiya kumvetsera choonadi, n’kutembenukira ku nkhani zonama.” (2 Tim. 4:2-4) Yesu ananeneratu kuti mpatuko udzayamba. (Mat. 13:24, 25, 38) Mpatuko utayandikira, kunali kofunika kwambiri kuti Timoteyo adzipereke ‘polalikira mawu’ ngakhale mu mpingo n’cholinga choti Akhristu asanyengedwe ndi ziphunzitso zonyenga zomwe zinkakopa anthu. Miyoyo ya anthu inali pa ngozi. Nanga bwanji masiku ano?

5, 6. Kodi tikakhala mu utumiki tikhoza kukumana ndi anthu amene amakhulupirira ziphunzitso ziti?

5 Panopa mpatuko wafika pachimake ndipo wafala kwambiri. (2 Ates. 2:3, 8) Kodi ndi ziphunzitso ziti zimene zimakomera anthu m’khutu masiku ano? Kumadera ambiri, anthu amalimbikitsa ena kukhulupirira chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Anthu amagwiritsa ntchito mfundo za sayansi kuti aphunzitse zimenezi koma kwenikweni chiphunzitsochi chili ngati chipembedzo chawo. Chimakhudza mmene iwo amaonera Mulungu ndiponso anthu ena. Chiphunzitso china chimene chafala kwambiri n’chakuti Mulungu satiganizira choncho palibe chifukwa choti tizimulambira. N’chifukwa chiyani ziphunzitsozi zimakopa kwambiri anthu mpaka kuwachititsa kugona mwauzimu? Chifukwa chakuti mfundo yake ndi imodzi yonena kuti, ‘Munthu akhoza kumachita chilichonse chimene akufuna chifukwa palibe amene angamuimbe mlandu.’ Uthenga umenewu ndi umene umakomera m’makutu anthu ambiri.​—Werengani Salimo 10:4.

6 Anthu amauzidwa zinthu zowakomera m’makutu m’njira zinanso. Anthu ena amene amapita kutchalitchi amasangalala akamaphunzitsidwa kuti, ‘Kaya achite zotani pa moyo wawo, Mulungu amawakondabe.’ Ansembe ndiponso abusa amalankhula zowakomera anthu m’khutu powauza kuti akamachita miyambo, Misa, zikondwerero ndiponso kulambira mafano adzadalitsidwa ndi Mulungu. Anthu amene amauzidwa zimenezi sadziwa kuti ali pa ngozi yaikulu. (Sal. 115:4-8) Koma ngati tingawathandize kudzuka ku tulo tawo tauzimu ndi kumvetsera uthenga wa m’Baibulo akhoza kudzasangalala ndi madalitso a Ufumu wa Mulungu.

TANTHAUZO LA KULALIKIRA MODZIPEREKA

7. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalalikira modzipereka?

7 Dokotala wabwino amene akuchita opaleshoni amaika maganizo ake onse pa ntchito yakeyo chifukwa chodziwa kuti moyo uli pa ngozi. Nafenso tikakhala mu utumiki tiyenera kuika maganizo athu onse pa ntchito yathuyo. Tingachite zimenezi poganizira nkhani, mafunso komanso zinthu zina zimene zingakope chidwi cha anthu amene timakumana nawo. Kudzipereka kungathandize munthu kusintha nthawi yomwe amalowera mu utumiki n’cholinga choti azitha kupeza anthu ambiri amene angamvetsere.​—Aroma 1:15, 16; 1 Tim. 4:16.

8. Kuti tidzipereke pa ntchito yathu tiyenera kuchita chiyani?

8 Kuti tidzipereke pa ntchito yathu tiyeneranso kuika zinthu zofunika pa malo oyamba. (Werengani Genesis 19:15.) Tiyerekeze kuti mwapita kuchipatala ndipo pambuyo pokuyezani dokotala akukuitanani mu ofesi yake n’kunena kuti: “Zinthutu sizili bwino. Muyenera kuchitapo kanthu mwamsanga pasanathe mwezi umodzi.” Kodi mungatuluke mu ofesimo nthawi yomweyo ngati munthu amene akupita kukazimitsa moto? Ayi. Mukhoza kulandira kaye malangizo amene  angakupatseni kenako n’kupita kunyumba kwanu kuti mukaiganizire bwino nkhaniyo n’kuona zoyenera kuchita.

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Paulo ankalalikira modzipereka ku Efeso?

9 Paulo ankadzipereka kwambiri polalikira uthenga wabwino. Tikhoza kuona zimenezi m’mawu amene anauza akulu a ku Efeso pofotokoza mmene analalikirira kuchigawo cha Asia. (Werengani Machitidwe 20:18-21.) Zikuoneka kuti kuyambira tsiku limene anafika kumeneko anatanganidwa kwambiri kulalikira uthenga wabwino kunyumba ndi nyumba. Ndiyeno kwa zaka ziwiri, “tsiku ndi tsiku anali kukamba nkhani m’holo pasukulu ya Turano.” (Mac. 19:1, 8-10) N’zodziwikiratu kuti Paulo ankachita zimenezi chifukwa chakuti anali wodzipereka. Malangizo akuti ‘tizilalikira modzipereka’ sayenera kutichititsa kuona kuti ntchito yathu yolalikira ndi yopanikiza. Komabe tiyenera kuona kuti ntchitoyi ndi yofunika kwambiri pa moyo wathu.

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira kuti Akhristu anadzipereka kwambiri zaka 100 zapitazo?

10 Kagulu kochepa ka Ophunzira Baibulo kamene kanakhalako isanafike 1914, kanalalikira uthenga wabwino. Zimene kaguluka kanachita zikusonyeza bwino tanthauzo la kukhala odzipereka. Ngakhale kuti anali anthu okwana masauzande ochepa okha, iwo anazindikira kuti kudzipereka pa ntchito yolalikira za Ufumu m’nthawi yawo kunali kofunika kwambiri. Iwo ankafalitsa nkhani za Baibulo m’manyuzipepala ambirimbiri ndiponso ankaonetsa filimu yotchedwa “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.” Izi zinathandiza kuti alalikire uthenga wabwino kwa anthu mamiliyoni ambiri. Kodi akanapanda kukhala odzipereka, ndi angati a ife amene akanamva uthenga wa Ufumu?​—Werengani Salimo 119:60.

SAMALANI KUTI MUSASIYE KUKHALA ODZIPEREKA

11. N’chiyani chachititsa anthu ena kuti asakhalenso odzipereka?

11 Pali zododometsa zambiri zimene zingachititse munthu kuyamba kuona ntchito yolalikira ngati yosafunika kwenikweni. Dziko la Satanali lingatichititse kuti tiziganizira kwambiri zofuna zathu ndiponso zinthu zina. (1 Pet. 5:8; 1 Yoh. 2:15-17) Anthu ena amene poyamba ankaika kutumikira Yehova pa malo oyamba m’moyo wawo, panopo si odziperekanso. M’nthawi ya atumwi, Mkhristu wina dzina lake Dema ankagwira ntchito ndi Paulo koma anasokonezedwa ndi dziko losaopa Mulunguli. M’malo mopitiriza kulimbikitsa m’bale wake pa nthawi yovuta, Dema anamusiya Paulo.​—Filim. 23, 24; 2 Tim. 4:10.

12. Kodi panopa tili ndi mwayi wotani, nanga m’tsogolo tidzakhala ndi mwayi wotani?

12 Kuti tikhalebe odzipereka tiyenera kudzimana zinthu zina zimene moyo wathu umafuna. Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti ‘tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo.’ (1 Tim. 6:18, 19) Inu mukudziwanso kuti tikadzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu tidzasangalala ndi zinthu zambirimbiri. Koma pakali pano, tili ndi mwayi wosayerekezeka wothandiza anthu kuti adzapulumuke pa nkhondo ya Aramagedo.

13. Popeza ndife Akhristu, kodi tingatani kuti tikhalebe odzipereka?

13 Popeza anthu ambiri m’dzikoli akugona mwauzimu, n’chiyani chingatithandize kuti tisasiye kukhala odzipereka? Ndi bwino kuganizira mfundo yakuti nafenso nthawi inayake tinali m’tulo tauzimu. Koma tinadzutsidwa ndipo malinga ndi mawu a Paulo tingati Khristu watiunika. Panopa tili ndi mwayi wonyamula kuwala. (Werengani Aefeso 5:14.) Pambuyo ponena za kuunikidwa ndi Khristu, Paulo analemba kuti: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu chifukwa masikuwa ndi oipa.” (Aef. 5:15, 16) Popeza masikuwa ndi oipa, tiyeneradi ‘kugwiritsa ntchito bwino nthawi’ n’cholinga choti tizichita zinthu zimene zingatithandize kukhala maso mwauzimu.

 TIKUKHALA M’NTHAWI YAPADERA KWAMBIRI

14-16. N’chifukwa chiyani tiyenera kulalikira Ufumu modzipereka kwambiri masiku ano kuposa kale?

14 Kuyambira kale, utumiki wachikhristu wakhala wofunika koma panopa ndi wofunika kwambiri kuposa kale lonse. Kuyambira mu 1914, chizindikiro chokhala ndi mbali zambiri chofotokozedwa m’Mawu a Mulungu chikukwaniritsidwa. (Mat. 24:3-51) Panopa miyoyo ya anthu ili pa ngozi kwambiri kuposa m’mbuyomu. Ngakhale kuti mayiko amphamvu agwirizana kuchepetsa zida zankhondo, akusungabe zida zanyukiliya zokwana pafupifupi 2,000 zomwe n’zotcheratchera pokonzekera nkhondo. Akuluakulu a maboma amanena kawirikawiri kuti zida zina zanyukiliya zasowa. Kodi mwina zigawenga n’zimene zikusowetsa zidazi? Anthu ena amanena kuti zigawenga zitati ziyambitse nkhondo anthu onse akhoza kupululuka. Komatu si nkhondo yokha imene ikuchititsa moyo wa anthu kukhala pa ngozi.

15 Lipoti la mu 2009 lochokera ku magazini ina ya zachipatala ndiponso yunivesite ina ya ku London linanena kuti: “Kusintha kwa nyengo ndi vuto limene likudetsa nkhawa kwambiri zaka za m’ma 2000 zino. Vuto limeneli likhala likuwonjezereka kwambiri ndipo likuchititsa kuti miyoyo ya anthu ambiri ikhale pa ngozi.” (The Lancet ndi University College London) Zotsatira zake zikhoza kukhala zoopsa kwambiri monga kusefukira kwa madzi, chilala, miliri, mphepo yamkuntho, nkhondo ndiponso kuwonongeka kwa zinthu zachilengedwe. Kunena zoona, nkhondo ndi masoka achilengedwe zikubwezeretsa chitukuko m’mbuyo.

16 Anthu ena amaganiza kuti “chizindikiro” chimenechi chidzakwaniritsidwa pa nthawi imene anthu adzaphulitse zida zanyukiliya. Koma anthu ambiri sadziwa zimene chizindikirochi chikuimira. Chizindikirochi chakhala chikuoneka kwa zaka zambiri tsopano ndipo izi zikusonyeza kuti ndi nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. Zikusonyezanso kuti mapeto a dongosolo lino ali pafupi kwambiri. (Mat. 24:3) Mbali zosiyanasiyana za chizindikirochi zikuonekera kwambiri masiku ano kuposa kale. Ino ndi nthawi yoti anthu adzuke ku tulo tauzimu ndipo utumiki wathu ndi umene ungawathandize kuti adzuke.

17, 18. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani chifukwa cha “nyengo” imene tikukhalamoyi? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingachititse anthu kusintha mmene amaonera uthenga wa Ufumu?

17 Kwangotsala kanthawi kochepa kwambiri koti tisonyeze kuti timakonda kwambiri Yehova komanso koti timalize ntchito yolalikira imene tapatsidwa m’masiku otsiriza ano. Zimene Paulo anauza Akhristu a ku Roma n’zothandiza kwambiri masiku ano. Iye anati: “Nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale mu ola lakuti mudzuke ku tulo, pakuti chipulumutso chathu chili pafupi kwambiri tsopano kusiyana ndi nthawi imene tinakhala okhulupirira.”​—Aroma 13:11.

18 Kukwaniritsidwa kwa zinthu zimene zinaloseredwa kuti zichitika masiku otsiriza kungathandize anthu kuti azindikire zosowa zawo zauzimu. Ena amazindikira kuti anthu akufunika thandizo akaona mmene maboma akulepherera kuthetsa mavuto a anthu monga kusokonekera kwa chuma, nkhondo zanyukiliya, upandu ndiponso kuwonongeka kwa chilengedwe. Ena amazindikira zosowa zawo zauzimu chifukwa cha mavuto a m’banja mwawo monga matenda, kutha kwa banja kapena imfa ya munthu amene amam’konda. Pamene tikulalikira timakhala ndi mwayi wothandiza anthu oterewa.

KUDZIPEREKA KUMATITHANDIZA KUCHITA ZAMBIRI MU UTUMIKI

19, 20. Kodi Akhristu ambiri asintha bwanji zinthu pa moyo wawo kuti akhale odzipereka?

19 Kudzipereka kwathandiza Akhristu ambiri kuwonjezera zimene amachita mu utumiki. Mwachitsanzo, banja lina la ku Ecuador linaganiza zoyamba kukhala moyo wosalira zambiri litamvetsera nkhani za pa msonkhano wapadera wa 2006, wakuti “Khalanibe ndi Diso la Kumodzi.” Iwo analemba zinthu zimene sankazifuna. Patangotha miyezi itatu linasamuka m’nyumba yokhala ndi zipinda zitatu zogona n’kukakhala m’nyumba yokhala ndi chipinda chimodzi  chogona. Iwo anagulitsa zinthu zina kuti alipire ngongole zawo zonse. Pasanapite nthawi yaitali anayamba upainiya wothandiza ndipo kenako atakambirana ndi woyang’anira dera anapita kukatumikira ku mpingo wina kumene kunalibe ofalitsa Ufumu ambiri.

20 M’bale wina wa ku North America analemba kuti: “Pamene ine ndi mkazi wanga tinkamvetsera msonkhano wapadera mu 2006 tinali titakhala m’choonadi kwa zaka 30. Popita kunyumba pambuyo pa msonkhano, tinakambirana zimene tingachite potsatira malangizo oti tiyenera kukhala moyo wosalira zambiri. (Mat. 6:19-22) Tinali ndi nyumba zitatu, magalimoto apamwamba, boti, ndiponso kalavani. Poopa kuoneka ngati Akhristu osaganiza bwino, tinaona kuti ndi bwino kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Mu 2008 tinayamba upainiya. Apa n’kuti mwana wathu wamkazi atayamba kale upainiya. Timasangalala kwambiri kutumikira limodzi ndi abale athu. Takwanitsanso kukalalikira kugawo limene kunalibe ofalitsa ufumu ambiri. Kuchita zambiri potumikira Yehova kwatithandizanso kumuyandikira kwambiri. Timasangalala koposa tikaona anthu akutseguka m’maso chifukwa chomvetsa choonadi cha m’Mawu a Mulungu.”

21. Kodi timalalikira modzipereka chifukwa chodziwa zinthu ziti?

21 Tikudziwa kuti posachedwapa “tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu” lifika padziko loipali. (2 Pet. 3:7) Popeza tikudziwa zimene Mawu a Mulungu amanena, timalalikira mwakhama za chisautso chachikulu chimene chikubwera komanso za dziko latsopano. Timaona kuti m’pofunika kwambiri kulalikira modzipereka n’cholinga choti tithandize anthu kukhala ndi chiyembekezo chenicheni. Tikamagwira ntchito imeneyi mwakhama komanso modzipereka timasonyeza kuti timakondadi Mulungu ndiponso anzathu.

[Mafunso]