Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zotheka Kukhala Osangalala M’banja Limene Wina Si Mboni

N’zotheka Kukhala Osangalala M’banja Limene Wina Si Mboni

 N’zotheka Kukhala Osangalala M’banja Limene Wina Si Mboni

“Ukudziwa bwanji, mwina ungapulumutse [mwamuna kapena mkazi] wako?”​—1 AKOR. 7:16.

PEZANI MAYANKHO A MAFUNSO AWA

Kodi Mkhristu angachite chiyani kuti alimbikitse mtendere m’banja limene wina ndi wosakhulupirira?

Kodi Mkhristu angathandize bwanji achibale ake osakhulupirira kuti ayambe kuphunzira choonadi?

Kodi ena angathandize bwanji Mkhristu mnzawo amene ali m’banja ndi osakhulupirira?

1. Kodi chingachitike n’chiyani ngati wina m’banja waphunzira choonadi?

PA NTHAWI ina, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’” (Mat. 10:1, 7) Uthenga wabwino umenewu umapereka mtendere ndi chimwemwe kwa anthu amene amaulandira moyamikira. Komabe Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti anthu ambiri adzatsutsa ntchito yawo yolalikira za Ufumu. (Mat. 10:16-23) Zimakhala zopweteka kwambiri munthu akamatsutsidwa ndi anthu a m’banja mwake amene amakana uthenga waufumu.​—Werengani Mateyu 10:34-36.

2. Kodi n’zotheka kukhala osangalala ngati anthu ena m’banja lathu si Mboni? Fotokozani.

2 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitingakhale osangalala ngati anthu ena m’banja lathu si Mboni? Ayi. Ngakhale kuti nthawi zina achibale angamatsutse kwambiri, zimenezi sizichitika nthawi zonse. Komanso sikuti anthu a m’banja lathu angatitsutse mpaka kalekale. Nthawi zambiri zimadalira mmene Mkhristuyo amachitira akamatsutsidwa kapena anthu akamasonyeza kuti alibe chidwi. Ndipotu Yehova amadalitsa amene ali okhulupirika kwa iye komanso amawathandiza kukhala osangalala ngakhale akumane ndi mavuto. Akhristu amawonjezera chimwemwe chawo (1) akamayesetsa kukhala mwamtendere m’banja mwawo ndiponso (2)  akamayesetsa ndi mtima wonse kuthandiza anthu a m’banja mwawo amene ndi osakhulupirira kuti aphunzire choonadi.

MUZIYESETSA KUKHALA MWAMTENDERE M’BANJA

3. N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kuyesetsa kukhala pa mtendere ndi anthu a m’banja mwake amene si Mboni?

3 Kuti mbewu ya chilungamo ibereke chipatso m’banja lathu m’pofunika kuti pakhomo pakhale mtendere. (Werengani Yakobo 3:18.) Mkhristu ayenera kuyesetsa mwakhama kuti m’banja mwake mukhale mtendere ngakhale kuti banja lakelo ndi losagwirizana pa kulambira koona. Kodi angachite bwanji zimenezi?

4. Kodi Akhristu angachite chiyani kuti azikhalabe ndi mtendere wa mumtima?

 4 Akhristu ayenera kukhalabe ndi mtendere wa mumtima. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kumapemphera mochokera pansi pa mtima kuti tikhale ndi “mtendere wa Mulungu” umene ndi wosayerekezeka. (Afil. 4:6, 7) Munthu amakhala wosangalala ndiponso amakhala ndi mtendere ngati akuphunzira za Yehova komanso kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba pa moyo wake. (Yes. 54:13) Kuyankha pa misonkhano ya mpingo ndi kuchita khama mu utumiki wakumunda n’zofunikanso kwambiri kuti tikhale ndi mtendere komanso chimwemwe. Mkhristu amene ali m’banja limene ena si Mboni angathe kuchita nawo zinthu zina mu mpingo. Mwachitsanzo, taganizirani za mlongo wina dzina lake Enza, * amene mwamuna wake amamutsutsa mwachiwawa. Iye amapita mu utumiki akamaliza ntchito zake zapakhomo. Enza anati, “Yehova amandidalitsa kwambiri nthawi iliyonse imene ndayesetsa kuuza ena uthenga wabwino.” Madalitso amenewa amabweretsa mtendere, chimwemwe komanso amachititsa munthu kukhala wokhutira.

5. Kodi Akhristu amene amakhala m’banja loti ena si Mboni amakumana ndi mavuto otani, nanga ndi kuti kumene angapeze thandizo?

5 Tiyenera kuyesetsa mochokera pansi pa mtima kuti tizikhala mwa mtendere ndi anthu a m’banja mwathu omwe si Mboni. Zimenezi zingakhale zovuta chifukwa chakuti nthawi zina iwo angafune kuti tichite zinthu zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo mokhulupirika anthu ena amene ndi osakhulupirira m’banja lathu sangasangalale. Komabe pamapeto pake zimenezi zidzathandiza kukhala ndi mtendere m’banja. Kusalolera ngakhale pa zinthu zimene sizikuphwanya mfundo za m’Malemba kumangoyambitsa mikangano yosayenera. (Werengani Miyambo 16:7.) Choncho tikakumana ndi mavuto, m’pofunika kuti tizifufuza malangizo a m’Malemba opezeka m’mabuku ofalitsidwa ndi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndiponso ochokera kwa akulu.​—Miy. 11:14.

6, 7. (a) N’chifukwa chiyani ena amatsutsa anthu a m’banja lawo akayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova? (b) Kodi wophunzira Baibulo kapena wa Mboni ayenera kuchita chiyani ngati anthu a m’banja lake ali otsutsa?

6 Kuti tikhale ndi mtendere m’banja tiyenera kudalira Yehova ndiponso kuyesetsa kumvetsa mmene anthu osakhulupirira m’banja lathu amamvera. (Miy. 16:20) Ngakhale anthu amene angoyamba kumene kuphunzira Baibulo angayesetse kuchita zimenezi. Anthu ena osakhulupirira saletsa mwamuna kapena mkazi wawo kuti aziphunzira Baibulo. Iwo angafike pozindikira kuti kuphunzira Baibulo kungathandize banja lawo. Koma ena angatsutse mwamphamvu kwambiri. Esther, yemwe panopa ndi Mboni, ananena kuti anakwiya kwambiri pamene mwamuna wake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye anati: “Ndinkataya mabuku ake kapena kuwaotcha kumene.” Howard, amene poyamba sankafuna kuti mkazi wake aziphunzira Baibulo, ananena kuti: “Amuna ambiri amaopa kuti akazi awo angapusitsidwe kuti alowe chipembedzo china. Chifukwa choopa zimenezi mwamuna angayambe kutsutsa kwambiri mkazi wake.”

7 Wophunzira Baibulo amene akutsutsidwa ndi mwamuna kapena mkazi wake ayenera kulimbikitsidwa kuti asasiye kuphunzira. Nthawi zambiri kukhala wofatsa komanso kulemekeza wosakhulupirirayo kungathandize kuthetsa vutoli. (1 Pet. 3:15) Howard anati: “Ndikusangalala kwambiri chifukwa choti mkazi wanga anali wodekha ndipo sanachite zinthu mopupuluma.” Mkazi wake anati: “Howard anandiuza kuti ndisiye kuphunzira Baibulo. Iye anati a Mboni akundipusitsa kuti ndisiye zimene ndinkakhulupirira. M’malo mokangana naye ndinkamuuza kuti mwina akunena zoona koma si mmene ineyo ndikuonera. Ndiyeno ndinamupempha kuti awerenge buku limene ndinkaphunzira. Atawerenga sanathe kutsutsa zimene bukulo linkanena. Zimenezi zinamukhudza kwambiri.” Ndi bwino kumakumbukira kuti munthu amene si Mboni amakhala  ndi nkhawa komanso amaona ngati akunyalanyazidwa pa nthawi imene mwamuna kapena mkazi wake akupita kukagwira ntchito zachikhristu. Choncho amafunika kusonyezedwa chikondi chachikulu kuti athetse maganizo amenewa.

ATHANDIZENI KUTI APHUNZIRE CHOONADI

8. Kodi mtumwi Paulo anapereka malangizo otani kwa anthu omwe mkazi kapena mwamuna wawo si Mboni?

8 Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti sayenera kuthetsa ukwati chifukwa chakuti mwamuna kapena mkazi wawo ndi wosakhulupirira. * (Werengani 1 Akorinto 7:12-16.) Kudziwa kuti nthawi ina mwamuna kapena mkazi wosakhulupirirayo angadzakhale Mkhristu kungathandize kuti wokhulupirirayo akhalebe ndi chimwemwe. Zitsanzo zomwe tikambirane zisonyeza kuti pamafunika kukhala osamala kwambiri pamene tikuyesa kuthandiza wosakhulupirirayo kuti aphunzire choonadi.

9. Kodi tiyenera kusamala ndi zinthu ziti pamene tikulankhula za choonadi ndi anthu osakhulupirira a m’banja lathu?

9 Poganizira zimene ankachita atangoyamba kuphunzira choonadi cha m’Baibulo, Jason anati, “Ndinkangofuna kuuza aliyense zimene ndinkaphunzira.” Wophunzira Baibulo akamasangalala ndi choonadi chimene waphunzira kuchokera m’Malemba, nthawi zonse amangofuna kuuza anthu ena. Ndipo amangofuna kuti achibale ake akhulupirire n’kuyamba kuphunzira choonadi nthawi yomweyo koma vuto ndi lakuti nthawi zina sizitheka. Kodi zimene Jason ankachita atayamba kuphunzira zinakhudza bwanji mkazi wake? Mkazi wake ankaona kuti Jason akungokhalira kulankhula za choonadi ndipo zinkamutopetsa. Mayi wina amene anayamba kuphunzira choonadi patapita zaka 18 kuchokera pamene mwamuna wake anayamba kuphunzira anati, “Ndinkafunika kuti ndiziphunzira pang’onopang’ono.” Ngati panopa mukuphunzira ndi munthu amene mwamuna kapena mkazi wake sakufuna kuphunzira Baibulo, mungachite bwino kumuthandiza kuti adziwe zoyenera kuchita ngati patabuka vuto kapena nkhani inayake. Muziyeserera kuchita zimenezi. Mose anati: “Malangizo anga adzagwa ngati mvula, mawu anga adzatsika ngati mame, ngati mvula yowaza pa udzu.” (Deut. 32:2) Mfundo za choonadi zimene timauza ena ziyenera kukhala ngati mvula yowaza osati ngati chimvula chamkuntho.

10-12. (a) Kodi ndi malangizo otani amene mtumwi Petulo anapereka kwa Akhristu amene mwamuna kapena mkazi wawo ndi wosakhulupirira? (b) Kodi wophunzira Baibulo wina anaphunzira bwanji kugwiritsa ntchito malangizo opezeka pa 1 Petulo 3:1, 2?

10 Mtumwi Petulo anapereka malangizo a m’Malemba kwa akazi achikhristu amene amuna awo ndi osakhulupirira. Iye anati: “Momwemonso inu akazi, muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu,  poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.” (1 Pet. 3:1, 2) Kumvera komanso kupereka ulemu waukulu kwa mwamuna wake, ngakhale kuti mwina amamuchitira nkhanza, kungathandize kuti mwamunayo aphunzire choonadi. Chimodzimodzinso ndi mwamuna wachikhristu. Iye ayenera kukhala mutu wachikondi komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Mulungu ngakhale pamene akutsutsidwa ndi mkazi wake.​—1 Pet. 3:7-9.

11 Pali zitsanzo zambiri masiku ano zosonyeza ubwino wotsatira malangizo a Petulo amenewa. Taganizirani zimene zinachitikira Selma. Iye atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, mwamuna wake Steve sanasangalale nazo. Steve anati: “Ndinkakwiya ndi kuchita nsanje.” Selma anati: “Mwamuna wanga anali wovuta kwambiri ngakhale ndisanayambe kuphunzira. Anali ndi mtima wapachala. Ndiyeno nditayamba kuphunzira Baibulo khalidweli linangowonjezereka.” Kodi chinawathandiza n’chiyani?

12 Selma saiwala zimene anauzidwa ndi mlongo amene ankaphunzira naye Baibulo. Selma anati: “Tsiku lina sindinkafuna kuphunzira Baibulo. Usiku wa tsiku limenelo Steve anali atandimenya pamene ndinali kumufotokozera mfundo inayake. Ndinali wokhumudwa komanso ndinkadzimvera chisoni. Nditamufotokozera mlongoyo zimene zinachitika ndiponso mmene ndinkamvera, iye anandiuza kuti ndiwerenge lemba la 1 Akorinto 13:4-7. Pamene ndinkawerenga lembali ndinkaganiza kuti, ‘Koma Steve sanandichitirepo zinthu zabwino ngati zimenezi.’ Ndiyeno mlongoyo anandithandiza kuti ndiganize mwa njira ina pondifunsa kuti, ‘Pa zinthu zimene zatchulidwazi, ndi zinthu ziti zimene iweyo umachitira mwamuna wako?’ Ndinayankha kuti, ‘Palibe, chifukwa mwamuna wanga ndi wovuta kwambiri.’ Modekha, mlongoyo anati, ‘Selma kodi ndi ndani pakati pa iweyo ndi Steve amene akufuna kukhala Mkhristu?’ Ndinazindikira kuti ndikufunika kusintha kaganizidwe kanga ndiye ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kumukonda kwambiri Steve. Pang’ono ndi pang’ono zinthu zinayamba kusintha.” Pambuyo pa zaka 17, Steve anaphunzira choonadi.

MMENE ENA ANGATHANDIZIRE

13, 14. Kodi ena mu mpingo angathandize bwanji Akhristu amene ali ndi mwamuna kapena mkazi wosakhulupirira?

13 Mofanana ndi mvula yogwa pang’onopang’ono, imene imanyowetsa nthaka ndi kukulitsa mbewu, anthu ambiri mu mpingo amathandiza Akhristu amene mwamuna kapena mkazi wawo ndi wosakhulupirira kuti azikhala achimwemwe. Elvina wa ku Brazil ananena kuti: “Chikondi chimene abale ndi alongo amandisonyeza n’chimene chinandithandiza kukhala wolimba m’choonadi.”

14 Anthu mu mpingo akamasonyeza chidwi ndiponso kukomera mtima achibale a Mkhristu mnzathu omwe ndi osakhulupirira, zimawathandiza kuti asinthe. Mwamuna wina wa ku Nigeria amene anaphunzira choonadi patapita zaka 13 kuchokera pamene mkazi wake anaphunzira anati: “Tsiku lina ndikuyenda ndi wa Mboni wina, galimoto  yake inawonongeka. Iye anafufuza a Mboni anzake m’mudzi wapafupi ndipo tinapatsidwa malo ogona. Anatisamalira bwino kwambiri ngati kuti tinadziwana kuyambira tili ana. Pamenepa ndinadzionera ndekha chikondi chachikhristu chimene mkazi wanga ankandiuza nthawi zonse.” Mkazi wina wa ku England amene anaphunzira choonadi patadutsa zaka 18 kuchokera pamene mwamuna wake anaphunzira anati: “A Mboni ankatiitanira kunyumba zawo kuti tikadye chakudya. Ndipo ankatilandira bwino kwambiri.” * Mwamuna winanso wa m’dziko lomwelo, amene anadzaphunzira patapita nthawi yaitali kuchokera pamene mkazi wake anakhala Mkhristu, anati: “Abale ndi alongo ankabwera kunyumba kwathu komanso nthawi zina ankatiitanira kunyumba zawo. Ndinaona kuti ndi anthu amene amasamala za ena. Zimenezi zinaonekera kwambiri pa nthawi imene ndinali m’chipatala. Iwo ankabwera kudzandiona.” Kodi ifenso tingapeze njira zosonyezera chidwi kwa achibale osakhulupirira a Akhristu anzathu?

15, 16. Kodi n’chiyani chingathandize Mkhristu kukhalabe wosangalala pamene anthu ena m’banja lake sakufuna kuphunzira choonadi?

15 Nthawi zina ngakhale kuti wokhulupirirayo angayesetse kusonyeza khalidwe labwino ndiponso kulalikira mwanzeru kwa mwamuna kapena mkazi wake, makolo kapena achibale ena, si onse amene amayamba kuphunzira choonadi. Ena angapitirize kukhala opanda chidwi ndiponso otsutsa kwambiri. (Mat. 10:35-37) Komabe Mkhristu akamapitiriza kusonyeza khalidwe losangalatsa Mulungu, pamakhala zotsatira zabwino. Mwamuna wina amene anali wosakhulupirira anati: “Mkhristu akayamba kusonyeza makhalidwe abwino sadziwa mmene mnzake wosakhulupirirayo akumvera m’maganizo ndi mumtima mwake. Choncho musataye mtima ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wosakhulupirira.”

16 Ngakhale wina m’banja atakhalabe wosakhulupirira, n’zotheka kuti wokhulupirirayo akhale ndi chimwemwe. Mlongo wina wakhala akuyesetsa kwa zaka 21 kuthandiza mwamuna wake kuti adziwe uthenga wa Ufumu koma mwamunayo sakusintha. Mlongoyo anati: “Ndimakhala wosangalala chifukwa choyesetsa kuchita zimene Yehova amasangalala nazo, kukhala wokhulupirika komanso kuchita khama kuti ndikhale wolimba mwauzimu. Ndimadzipereka kuchita zinthu zauzimu monga kuphunzira pandekha, kupezeka pa misonkhano, kulalikira ndiponso kuthandiza ena mu mpingo. Zimenezi zandithandiza kuyandikira kwambiri kwa Yehova ndiponso zateteza mtima wanga.”​—Miy. 4:23.

MUSATAYE MTIMA

17, 18. Kodi Mkhristu angatani kuti asataye mtima ngati anthu ena m’banja lake ndi osakhulupirira?

17 Ngati ndinu Mkhristu wokhulupirika ndipo anthu ena m’banja lanu ndi osakhulupirira, musataye mtima. Kumbukirani kuti “chifukwa cha dzina lake lalikulu, Yehova sadzasiya anthu ake.” (1 Sam. 12:22) Iye adzakhala nanu ngati mupitiriza kukhala okhulupirika kwa iye. (Werengani 2 Mbiri 15:2.) Choncho tiyenera ‘kusangalala mwa Yehova’ ndiponso ‘kulola kuti iye atitsogolere panjira yathu. Tiyeneranso kumudalira.’ (Sal. 37:4, 5) “Limbikirani kupemphera” ndipo muzikhala ndi chikhulupiriro kuti Atate wathu wakumwamba amene ndi wachikondi angakuthandizeni kupirira mavuto amtundu uliwonse.​—Aroma 12:12.

18 Muzipempha Yehova kuti akupatseni mzimu woyera n’cholinga choti ukuthandizeni kulimbikitsa mtendere m’banja lanu. (Aheb. 12:14) N’zotheka ndithu kulimbikitsa mtendere ndipo zimenezi zikhoza kuthandiza kwambiri anthu a m’banja lathu omwe ndi osakhulupirira. Tidzapeza chimwemwe komanso mtendere wa mumtima ndi m’maganizo tikamachita “zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akor. 10:31) N’zolimbikitsa kudziwa kuti tili ndi abale ndi alongo athu mu mpingo amene ndi ofunitsitsa kutithandiza mwachikondi pamene tikuyesetsa kulimbikitsa mtendere m’banja lathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Tasintha mayinawa.

^ ndime 8 Malangizo a Paulo saletsa anthu kupatukana mogwirizana ndi malamulo a boma ngati pali mavuto aakulu kwambiri. Aliyense ayenera kusankha yekha zochita pa nkhani imeneyi. Onani buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu,” tsamba 220 mpaka 221.

^ ndime 14 Malemba saletsa kudya chakudya limodzi ndi osakhulupirira.​—1 Akor. 10:27.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Muzisankha nthawi yabwino yofotokoza zimene mumakhulupirira

[Chithunzi patsamba 29]

Akhristu ena azisonyeza kuti amaganizira mwamuna kapena mkazi wosakhulupirira