Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Khalani Olimba Mtima Kwambiri Ndipo Muchite Zinthu Mwamphamvu’

‘Khalani Olimba Mtima Kwambiri Ndipo Muchite Zinthu Mwamphamvu’

 ‘Khalani Olimba Mtima Kwambiri Ndipo Muchite Zinthu Mwamphamvu’

“Iwe khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. . . . Yehova Mulungu wako ali nawe.”​—YOS. 1:7-9.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi Inoki ndi Nowa anasonyeza bwanji kulimba mtima?

Kodi akazi ena akale anapereka chitsanzo chotani pa nkhani ya chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima?

Kodi ndi achinyamata ati amene amakuchititsani chidwi pa nkhani ya kulimba mtima?

1, 2. (a) Kodi ndi khalidwe liti limene limafunika nthawi zina kuti munthu achite zinthu zabwino pa moyo wake? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

MUNTHU wolimba mtima sakhala wamantha ndipo samangoopa zilizonse. Iye amachita zinthu mwamphamvu. Nthawi zina pamafunika kulimba mtima kwambiri kuti munthu azichita zabwino pa moyo wa tsiku ndi tsiku.

2 M’Baibulo muli nkhani za anthu amene anasonyeza kulimba mtima pa nthawi zovuta kwambiri. Ena anasonyeza kulimba mtima pa zochitika zimene atumiki ambiri a Yehova amakumana nazo. Kodi tingaphunzire chiyani m’zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene anali olimba mtima? Kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima?

MBONI ZOLIMBA MTIMA M’DZIKO LOSAOPA MULUNGU

3. Kodi Inoki analosera chiyani zokhudza anthu osaopa Mulungu?

3 Panafunika kulimba mtima kuti munthu akhale mboni ya Yehova pakati pa anthu oipa Chigumula cha masiku a Nowa chisanachitike. Ngakhale zinali choncho, Inoki, “wa m’badwo wa 7 kuchokera kwa Adamu,” analosera molimba mtima kuti: “Taonani! Yehova anabwera ndi miyandamiyanda ya oyera ake, kudzapereka chiweruzo kwa onse, ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu chifukwa cha ntchito zawo zonyoza Mulungu zimene anazichita mosaopa Mulungu, komanso chifukwa cha zinthu zonse zonyoza koopsa zimene ochimwa osaopa Mulungu anamunenera.” (Yuda 14, 15) Inoki analankhula mawu akewa ngati kuti zinthuzo zachitika kale chifukwa zinali zosakayikitsa kuti ulosiwu udzakwaniritsidwa. Ndipo anthu onse osaopa Mulungu anawonongedwa pa Chigumula chimene chinachitika padziko lonse.

4. Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawi imene Nowa “anayenda ndi Mulungu”?

4 Chigumula chinachitika m’chaka cha 2370 B.C.E., patapita zaka 650 kuchokera pamene Inoki analosera. Kuchokera pa nthawi imene Inoki anamwalira kufika nthawi  ya chigumula, Nowa anabadwa kukula, n’kukhala ndi banja ndipo iye ndi ana ake aamuna anamanga chingalawa. Angelo oipa anavala matupi a anthu n’kudzagona ndi akazi okongola ndipo anabereka Anefili. Ndipo dziko lapansi linaipa kwambiri komanso linadzaza ndi chiwawa. (Gen. 6:1-5, 9, 11) Ngakhale kuti makhalidwe anali oipa choncho, “Nowa anayenda ndi Mulungu woona” ndipo anachitira umboni molimba mtima monga “mlaliki wa chilungamo.” (Werengani 2 Petulo 2:4, 5.) Tikufunikanso kulimba mtima kotereku masiku otsiriza ano.

ANASONYEZA CHIKHULUPIRIRO NDIPONSO KULIMBA MTIMA

5. Kodi Mose anasonyeza bwanji chikhulupiriro ndi kulimba mtima?

5 Mose ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya chikhulupiriro ndi kulimba mtima. (Aheb. 11:24-27) Kuyambira m’chaka cha 1513 mpaka mu 1473 B.C.E., Mulungu anamugwiritsira ntchito kutsogolera Aisiraeli kutuluka ku Iguputo ndiponso pa nthawi imene anali m’chipululu. Mose ankaona kuti sangakwanitse zimenezi koma anavomerabe. (Eks. 6:12) Iye ndi m’bale wake Aroni anapita mobwerezabwereza kukalankhula ndi Farao wa ku Iguputo yemwe anali wodzikuza ndiponso wosamva za ena. Iwo molimba mtima analengeza za miliri 10 imene Yehova ankafuna kubweretsa pofuna kuchititsa manyazi milungu ya Aiguputo ndi kupulumutsa anthu ake. (Ekisodo machaputala 7-12) Mose anasonyeza chikhulupiriro ndi kulimba mtima chifukwa chakuti Mulungu ankamuthandiza nthawi zonse. Ifenso tili ndi thandizo limeneli​—Deut. 33:27.

6. Ngati akuluakulu a boma akutifunsa mafunso, kodi n’chiyani chidzatithandiza kuchitira umboni molimba mtima?

6 Tifunika kukhala olimba mtima ngati Mose chifukwa Yesu anati: “Adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina. Koma akakuperekani kumeneko, musade nkhawa za mmene mukalankhulire kapena zimene mukanene. Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule, pakuti wolankhula simudzakhala inu panokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzera mwa inu.” (Mat. 10:18-20) Ngati akuluakulu a boma akutifunsa mafunso, mzimu wa Yehova udzatithandiza kuchitira umboni mwaulemu, ndi chikhulupiriro komanso molimba mtima.​—Werengani Luka 12:11, 12.

7. N’chiyani chinathandiza kuti Yoswa akhale wolimba mtima komanso kuti apambane?

7 Kuphunzira Chilamulo cha Mulungu nthawi zonse n’kumene kunathandiza Yoswa, amene analowa m’malo mwa Mose , kukhala wolimba mtima komanso kunalimbitsa chikhulupiriro chake. M’chaka cha 1473 B.C.E., Aisiraeli anali okonzeka kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Mulungu analamula Yoswa kuti: “Khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu.” Yehova ananenanso kuti Yoswa akatsatira Chilamulo adzachita zinthu mwanzeru ndipo adzapambana. Anamuuzanso kuti: “Usachite mantha kapena kuopa pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.” (Yos. 1:7-9) Mawu amenewatu ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri Yoswa. Mulungu analidi naye chifukwa iye anagonjetsa pafupifupi malo onse a Dziko Lolonjezedwa m’zaka 6 zokha. Anali atachita zimenezi pofika chaka cha 1467 B.C.E.

 AKAZI OKHULUPIRIKA AMENE ANALIMBA MTIMA

8. Kodi Rahabi anapereka chitsanzo chotani pa nkhani ya chikhulupiriro komanso kulimba mtima?

8 Kuyambira kale, akazi ambiri olimba mtima asonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Yehova. Mwachitsanzo, Rahabi wa ku Yeriko, yemwe anali hule, anakhulupirira Mulungu ndipo analimba mtima n’kubisa anthu awiri amene anatumizidwa ndi Yoswa kuti akazonde mzindawo. Kenako nthumwi za mfumu ya mzindawo zitafika anazinamiza kuti anthuwo alowera njira inayake. Iye ndi anthu a m’banja lake anapulumuka pamene Aisiraeli anagonjetsa mzinda wa Yeriko. Rahabi anasiya moyo wake wachiwerewere, n’kuyamba kulambira Yehova mokhulupirika ndipo anakhala kholo la Mesiya. (Yos. 2:1-6; 6:22, 23; Mat. 1:1, 5) Anadalitsidwa kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chake komanso kulimba mtima.

9. Kodi Debora, Baraki ndi Yaeli anasonyeza bwanji kulimba mtima?

9 Yoswa atamwalira m’chaka cha 1450 B.C.E., oweruza ndi amene anali kukhazikitsa chilungamo mu Isiraeli. Mfumu yachikanani dzina lake Yabini anapondereza Aisiraeli kwa zaka 20. Ndiyeno Mulungu anauzira mneneri wamkazi Debora kuti alimbikitse woweruza Baraki kumenyana ndi mfumuyo. Baraki anasonkhanitsa amuna okwana 10,000 paphiri la Tabori ndipo anali wokonzeka kumenyana ndi Sisera yemwe anali mkulu wa gulu la asilikali a Yabini. Pa nthawiyi n’kuti Sisera atafika kuchigwa cha Kisoni ndi asilikali ake komanso magaleta ankhondo okwana 900. Pamene Aisiraeli anafika kuchigwacho, Mulungu anagwetsa chimvula chomwe chinachititsa kuti kukhale matope okhaokha ndipo izi zinachititsa kuti magaleta a Akananiwo azilephera kuyenda. Asilikali a Baraki anapambana ndipo “gulu lonse la Sisera linaphedwa ndi lupanga.” Sisera anathawa n’kukabisala kwa Yaeli ndipo atagona, Yaeliyo anamupha. Mogwirizana ndi zimene Debora anauza Baraki m’mawu ake aulosi, “ulemerero” wa kupambana nkhondoyi unapita kwa mkazi wotchedwa Yaeli. Chifukwa chakuti Debora, Baraki ndiponso Yaeli anachita zinthu molimba mtima, dziko la Isiraeli “linakhala pa mtendere zaka 40.” (Ower. 4:1-9, 14-22; 5:20, 21, 31) Palinso amuna ndi akazi ena ambiri oopa Mulungu amene asonyeza chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima koteroko.

MAWU ATHU ANGALIMBITSE MTIMA ANTHU ENA

10. Perekani umboni wosonyeza kuti mawu athu angalimbitse mtima anthu ena.

10 Mawu athu akhoza kulimbitsa mtima atumiki anzathu. M’zaka za m’ma 1000 B.C.E., Mfumu Davide inauza mwana wake Solomo kuti: “Limba mtima, ugwire ntchitoyi mwamphamvu. Usaope kapena kuchita mantha chifukwa Yehova Mulungu, Mulungu wanga, ali ndi iwe. Sadzakutaya kapena kukusiya, kufikira ntchito yonse yokhudza utumiki wa nyumba ya Yehova itatha.” (1 Mbiri 28:20) Solomo anachita zinthu molimba mtima ndipo anamanga kachisi wa Yehova wokongola kwambiri ku Yerusalemu.

11. Kodi mawu a mtsikana wachiisiraeli wolimba mtima anathandiza bwanji munthu wina?

 11 M’zaka za m’ma 900 B.C.E., mtsikana wina wachiisiraeli analimba mtima kwambiri ndipo mawu ake anathandiza kuti munthu wina wodwala khate achiritsidwe. Iye anagwidwa ndi gulu la achifwamba ndipo anadzakhala kapolo wa Namani yemwe anali mkulu wa gulu la asilikali a Siriya. Mtsikanayu ankadziwa zinthu zozizwitsa zimene Elisa anachita mothandizidwa ndi Yehova. Choncho anauza mkazi wa Namani kuti ngati mwamuna wake angapite ku Isiraeli, mneneri wa Mulunguyo akhoza kumuchiritsa. Namani atapita ku Isiraeli anachiritsidwa mozizwitsa ndipo anayamba kulambira Yehova. (2 Maf. 5:1-3, 10-17) Ngati ndinu wamng’ono ndipo mumakonda Mulungu mofanana ndi mtsikana ameneyu, Yehova akhoza kukulimbitsani mtima kuti muchitire umboni kwa aphunzitsi, ana asukulu anzanu ndiponso kwa anthu ena.

12. Kodi anthu anatani atamva mawu a Mfumu Hezekiya?

12 Mawu osankhidwa bwino akhoza kulimbitsa mtima anthu pa nthawi ya mavuto. Pamene Asuri anaukira Yerusalemu m’zaka za m’ma 700 B.C.E., Mfumu Hezekiya inauza anthu ake kuti: “Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu. Musaope kapena kuchita mantha ndi mfumu ya Asuri ndi khamu lalikulu limene ili nalo, chifukwa ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi mfumuyo. Iyo ikudalira mphamvu za anthu, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kuti atithandize ndi kutimenyera nkhondo zathu.” Kodi anthu anatani atamva mawu a mfumuyi? Baibulo limati: “Pamenepo anthuwo anayamba kulimba mtima chifukwa cha mawu a Hezekiya.” (2 Mbiri 32:7, 8) Mawu ngati amenewa akhoza kutilimbitsa mtima ifeyo komanso Akhristu anzathu tikamazunzidwa.

13. Kodi Obadiya, yemwe ankayang’anira nyumba ya Mfumu Ahabu, anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yolimba mtima?

13 Nthawi zina timasonyeza kulimba mtima popewa kunena zinthu zina. M’zaka za m’ma 900 B.C.E., Obadiya, yemwe anali woyang’anira nyumba ya Ahabu, analimba mtima n’kubisa kuphanga aneneri a Yehova okwana 100. Iye anawagawa “m’magulu awiri, gulu lililonse aneneri 50.” Pa nthawiyi Mfumukazi Yezebeli inali italamula kuti aneneri onse a Yehova aphedwe. (1 Maf. 18:4) Mofanana ndi Obadiya yemwe ankaopa Mulungu, atumiki a Yehova okhulupirika a masiku ano amalimbanso mtima ndipo saulula zinthu zokhudza atumiki anzawo kwa anthu ozunza.

ESITERE ANALI MFUMUKAZI YOLIMBA MTIMA

14, 15. Kodi Mfumukazi Esitere inasonyeza bwanji chikhulupiriro ndi kulimba mtima ndipo zotsatira zake zinali zotani?

14 M’zaka za m’ma 400 B.C.E., Mfumukazi Esitere inasonyeza kuti inali ndi chikhulupiriro cholimba komanso inali yolimba mtima. Pa nthawiyo, munthu wina woipa dzina lake Hamani anakonza chiwembu choti Ayuda onse m’chigawo cholamulidwa ndi Ufumu wa Perisiya aphedwe. N’zosachita kufunsa kuti Ayuda anali ndi chisoni kwambiri, anasala kudya ndiponso anapemphera ndi mtima wonse. (Esitere 4:1-3) Mfumukazi Esitere nayonso inamva chisoni kwambiri ndi zimenezi. Ndiyeno Mordekai yemwe anali wachibale wa Esitere anam’tumizira kalata yofotokoza lamulo loti Ayuda aphedweyo ndipo anauza Esitere kuti akachonderere kwa mfumu m’malo mwa Ayuda anzakewo. Koma munthu aliyense wopita kwa mfumu asanaitanidwe ankaphedwa.​—Esitere 4:4-11.

15 Ndiyeno Mordekai anauza Esitere kuti: ‘Ngati iwe ukhala chete pa nthawi ino, thandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina. Koma ndani akudziwa? Mwina iwe wakhala mfumukazi kuti uthandize pa nthawi ngati imeneyi.’ Esitere analimbikitsa Mordekai kuti asonkhanitse Ayuda onse ku Susani ndipo asale kudya m’malo mwa iye. Ananenanso kuti: ‘Inenso ndisala kudya. Pamenepo, ngakhale kuti ndi zosemphana ndi lamulo, ndidzapita kwa mfumu, ndipo ngati n’kufa, ndife.’ (Esitere 4:12-17) Esitere anachitadi molimba mtima ndipo buku la m’Baibulo lokhala ndi dzina lake limasonyeza kuti Mulungu anapulumutsa anthu ake. Masiku ano, Akhristu odzozedwa ndi anzawo a nkhosa zina amasonyeza kulimba mtima kotereku akakumana ndi mavuto ndipo nthawi zonse “Wakumva pemphero” amakhala nawo.​—Werengani Salimo 65:2; 118:6.

 “LIMBANI MTIMA”

16. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani kwa achinyamata?

16 Pa nthawi ina, Yesu ali ndi zaka 12 anapezeka m’kachisi “atakhala pakati pa aphunzitsi. Anali kuwamvetsera ndi kuwafunsa mafunso.” Anthu “onse amene anali kumumvetsera anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.” (Luka 2:41-50) Ngakhale kuti Yesu anali wamng’ono, anali ndi chikhulupiriro komanso anali wolimba mtima moti ankafunsa mafunso aphunzitsi achikulirewa m’kachisi. Kuganizira chitsanzo cha Yesu chimenechi kungathandize achinyamata mu mpingo wachikhristu kugwiritsira ntchito mwayi umene ali nawo ‘woyankha aliyense amene wawafunsa za chiyembekezo chimene ali nacho.’​—1 Pet. 3:15.

17. N’chifukwa chiyani Yesu anauza ophunzira ake kukhala olimba mtima, nanga n’chifukwa chiyani ifenso tiyenera kukhala olimba mtima?

17 Yesu analimbikitsa anthu ena kukhala olimba mtima. (Mat. 9:2, 22) Iye anauza ophunzira ake kuti: “Taonani! Nthawi ikubwera, ndipo yafika kale. Mubalalika aliyense kupita kunyumba kwake, ndipo mundisiya ndekha. Koma sindikhala ndekha, chifukwa Atate ali ndi ine. Ndanena zimenezi kwa inu kuti mukhale mu mtendere chifukwa cha ine. M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.” (Yoh. 16:32, 33) Mofanana ndi otsatira a Yesu oyambirira, ifenso timadedwa ndi dzikoli komabe sitiyenera kukhala mbali ya dziko. Kuganizira za kulimba mtima kumene Mwana wa Mulungu anasonyeza kungatithandize ifenso kukhala olimba mtima ndiponso kusadetsedwa ndi dzikoli. Ngati iye analigonjetsa dziko, ifenso tingaligonjetse.​—Yoh. 17:16; Yak. 1:27.

PAULO ANAUZIDWA KUTI “LIMBA MTIMA”

18, 19. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro ndiponso kuti anali wolimba mtima?

18 Mtumwi Paulo anapirira mayesero ambiri. Pa nthawi ina Ayuda ku Yerusalemu anatsala pang’ono kumukhadzulakhadzula moti asilikali achiroma ndi amene anamupulumutsa. Ndiyeno usiku wake “Ambuye anaimirira pambali pake ndi kunena kuti: ‘Limba mtima! Pakuti wandichitira umboni mokwanira mu Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.’” (Mac. 23:11) Izi ndi zimene Paulo anachitadi.

19 Paulo mosaopa anadzudzula ‘atumwi apamwamba’ amene ankafuna kusokoneza mpingo wa ku Korinto. (2 Akor. 11:5; 12:11) Mosiyana ndi atumwi apamwambawa, Paulo anali ndi umboni wotsimikizira kuti iye analidi mtumwi. Iye anamangidwa, kumenyedwa, kuyenda m’misewu yoopsa komanso kukumana ndi zoopsa zina. Anavutika ndi njala, ludzu, kusagona komanso nkhawa imene ankakhala nayo akaganizira za Akhristu anzake. (Werengani 2 Akorinto 11:23-28.) Apatu Paulo anasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro cholimba komanso anali wolimba mtima ndipo zikuonekeratu kuti Mulungu anamupatsa mphamvu.

20, 21. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti tiyenera kukhala anthu olimba mtima. (b) Kodi tiyenera kukhala olimba mtima pa zochitika ziti ndipo sitiyenera kukayikira za chiyani?

20 Sikuti Akhristu onse adzazunzidwa kwambiri. Koma aliyense ayenera kukhala wolimba mtima kuti athane ndi mavuto amene amakumana nawo pa moyo wake. Mwachitsanzo, mnyamata wina ku Brazil anali m’gulu lina la zigawenga. Ndiyeno ataphunzira Baibulo anaganiza zosintha zinthu zina pa moyo wake. Koma vuto linali loti munthu aliyense wochoka m’gululo ankaphedwa. Iye anapemphera ndipo anagwiritsa ntchito malemba posonyeza mtsogoleri wa gululo zifukwa zimene akuchokera. Mnyamatayo anamulola kuchoka m’gululo popanda kulandira chilango chilichonse ndipo tsopano ndi wofalitsa Ufumu.

21 Timafunikanso kulimba mtima kuti tilalikire uthenga wabwino. Akhristu achinyamata amene ali pa sukulu amafunikanso kulimba mtima kuti akhalebe okhulupirika. Pamafunikanso kulimba mtima kuti tipemphe abwana athu chilolezo choti tikapezeka pa msonkhano wachigawo masiku onse. Apa tangotchula zinthu zochepa zofuna kuti tikhale olimba mtima. Kaya tikukumana ndi mavuto otani, Yehova adzamva ‘mapemphero athu achikhulupiriro.’ (Yak. 5:15) Iye adzatipatsa mzimu woyera kuti ‘tikhale olimba mtima ndiponso tizichita zinthu mwamphamvu.’

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 11]

Inoki analalikira molimba mtima m’dziko la anthu osaopa Mulungu

[Chithunzi patsamba 12]

Yaeli anachita zinthu molimba mtima ndiponso mwamphamvu