Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu?

 N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu?

“Inu ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu ndi wabwino. Unditsogolere.”​—SAL. 143:10.

1. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti munthu amatha kutsogoleredwa ndi mphamvu yosaoneka.

ANTHU ena akamayenda m’chipululu kapena panyanja, amagwiritsa ntchito kampasi kuti iwathandize kudziwa kumene akupita. Kampasi ndi kachipangizo kamene kamakhala ndi muvi umodzi wamaginito umene umaloza kumpoto. Chifukwa cha mphamvu yamaginito imene ili m’kachipangizoka komanso imene ili kumpoto kwenikweni ndi kum’mwera kwenikweni kwa dzikoli, muviwu umaloza kumpoto.

2, 3. (a) Kodi Yehova anagwiritsa ntchito mphamvu iti zaka zambiri m’mbuyomu? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kudalirabe mphamvu yosaoneka ya Mulungu kuti izititsogolera masiku ano?

2 Koma pali mphamvu ina yosaoneka yomwe iyenera kutitsogolera. Kodi mphamvu imeneyi n’chiyani? Mphamvu imeneyi ndi imene yafotokozedwa m’mavesi oyambirira a m’Baibulo. Ponena zimene Yehova anachita zaka zambirimbiri zapitazo, buku la Genesis limati: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Pamene ankachita zimenezi, iye anagwiritsa ntchito mphamvu yake chifukwa nkhaniyo imapitiriza kuti: “Ndipo mphamvu ya Mulungu inali kuyendayenda.” (Gen. 1:1, 2) Kodi mphamvu imeneyi inali chiyani? Inali mzimu woyera womwe Mulungu anagwiritsira ntchito polenga zinthu. Timayamikira Yehova chifukwa anagwiritsira ntchito mzimu wake woyera kuti tikhale ndi moyo komanso kuti pakhale zolengedwa zina zonse.​—Yobu 33:4; Sal. 104:30.

3 Popeza Yehova anatilenga pogwiritsa ntchito mphamvu yake ya mzimu woyera, kodi tiyenera kuyembekeza kuti mzimuwo uzititsogolerabe pa moyo wathu? Mwana wa Mulungu ankadziwa kuti tiyeneradi kutero chifukwa anauza ophunzira ake kuti: ‘Mzimu . . . udzakutsogolerani m’choonadi chonse.’ (Yohane 16:13) Kodi mzimu umenewu n’chiyani? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi mtima wofuna kutsogoleredwa ndi mzimu woyera?

Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?

4, 5. (a) Kodi anthu amene amakhulupirira Utatu amaganiza kuti mzimu woyera n’chiyani? (b) Kodi inuyo mungati mzimu woyera n’chiyani?

4 Nthawi zambiri anthu amene timawalalikira amakhala ndi maganizo olakwika pa nkhani ya mzimu woyera. Anthu amene amakhulupirira utatu amaganiza kuti mzimu nawonso ndi Mulungu ndipo ndi wofanana ndi Mulungu Atate. (1 Akor. 8:6) Koma chiphunzitso chimenechi n’chosiyana kwambiri ndi zimene Malemba amaphunzitsa.

5 Ndiyeno kodi mzimu woyera n’chiyani kwenikweni? Mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, mawu achiheberi akuti ruʹach anamasuliridwa kuti “mphamvu ya Mulungu” pa Genesis 1:2 ndipo pali mawu a m’munsi onena kuti: “Kapena kuti ‘mzimu wa Mulungu.’” M’mavesi ena mawu amenewa amamasuliridwanso kuti mphepo. (Yerekezerani ndi Gen 3:8; 8:1.) Mphepo sioneka koma timadziwa kuti ilipo chifukwa cha zimene imachita. N’chimodzimodzi ndi mzimu woyera womwe suoneka koma umagwira ntchito. Mzimu umenewu ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu imene amagwiritsa ntchito pa anthu kapena zinthu zina kuti akwaniritse cholinga chake. N’zosadabwitsa kuti mphamvu imeneyi ndi yochokera kwa Mulungu yemwe ndi woyera komanso Wamphamvuyonse.​—Werengani Yesaya 40:12, 13.

6. Kodi Davide anapempha chiyani kwa Yehova?

 6 Kodi Yehova angagwiritsirebe ntchito mzimu wake woyera kuti azititsogolera pa moyo wathu? Inde. Tikutero chifukwa chakuti iye analonjeza wamasalimo Davide kuti: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.” (Sal. 32:8) Kodi Davide ankafunadi kutsogoleredwa ndi Mulungu? Inde. Pajatu anapempha Yehova kuti: “Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu, pakuti inu ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu ndi wabwino. Unditsogolere.” (Sal. 143:10) Nafenso tiyenera kukhala ndi mtima wofuna kutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu. N’chifukwa chiyani tiyenera kutero? Pali zifukwa zinayi.

Sitingathe Kudzitsogolera

7, 8. (a) N’chifukwa chiyani si zotheka kukhala popanda kutsogoleredwa ndi Mulungu? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti n’zovuta kwambiri kuti tiyende tokhatokha m’dziko loipali.

7 Chifukwa choyamba chomwe tingafunire mzimu woyera kuti uzititsogolera n’chakuti sitingathe kudzitsogolera tokha. Kutsogolera munthu kumatanthauza kumusonyeza njira yolondola imene akufunika kudutsa. Yehova sanatilenge m’njira yoti tizitha kudzitsogolera tokha. Komanso chifukwa cha kupanda ungwiro, timalakwitsa zinthu zambiri tikamayesa kudzitsogolera tokha. Yeremiya analemba kuti: “Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yer. 10:23) Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho? Yeremiya anamva zimene Mulungu ananena zosonyeza kuti anthufe sitingathe kudzitsogolera. Pofotokoza za mmene ifeyo tilili kwenikweni, Yehova ananena kuti: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa. Ndani angaudziwe?”​—Yer. 17:9; Mat. 15:19.

8 Tiyerekeze kuti munthu wina akufuna kudutsa m’nkhalango yoopsa kapena kuti m’chipululu moti sanapitemo chiyambire. Kodi zingakhale zanzeru kupita yekha popanda munthu amene akudziwa dera limenelo komanso popanda kampasi? Ayi. Chifukwa ngati sakudziwa kumene akulowera komanso sakudziwa mmene angadzitetezere ku zinthu zoopsa, moyo wake ukhoza kukhala pangozi. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene amaganiza kuti akhoza kuchita zinthu bwinobwino m’dziko loipali popanda kutsogoleredwa ndi Mulungu. Kuti tithe kuyenda bwinobwino m’dziko loipali, tiyeneranso kupempha Yehova zimene Davide anamupempha kuti: “Mapazi anga ayendebe m’njira zanu, mmene sadzapunthwa ngakhale pang’ono.” (Sal. 17:5; 23:3) Kodi tingatani kuti Mulungu azititsogolera?

9. Malinga ndi chithunzi chimene chili patsamba 12, kodi mzimu wa Mulungu ungatitsogolere bwanji?

9 Ngati ndife odzichepetsa komanso odalira Yehova, iye adzatipatsa mzimu wake woyera kuti uzititsogolera. Kodi mphamvu imeneyi ingatithandize bwanji? Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mthandizi, amene ndi mzimu woyera, amene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse ndi kukukumbutsani  zonse zimene ndinakuuzani.” (Yoh. 14:26) Tikamapemphera ndi kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse ndiponso kuphunzira zimene Khristu ananena, mzimu woyera wa Mulungu ungatithandize kumvetsa nzeru zozama za Yehova. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tizichita chifuniro chake nthawi zonse. (1 Akor. 2:10) Komanso ngati takumana ndi mavuto mwadzidzidzi pa moyo wathu, mzimu wa Mulungu udzatithandiza kudziwa zochita. Mzimuwo udzatikumbutsa mfundo za m’Baibulo zomwe tinaphunzira ndipo udzatithandiza kuona mmene mfundozo zingatithandizire kusankha zinthu mwanzeru.

Yesu Ankatsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu

10, 11. Kodi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu ankayembekezera kuti mzimu woyera umuthandiza bwanji ndipo kodi chinachitika n’chiyani?

10 Chifukwa chachiwiri chimene tingafunire mzimu wa Mulungu kuti uzititsogolera n’chakuti Mulungu anatsogolera Mwana wake ndi mzimu womwewo. Asanabwere padziko lapansi, Mwana wobadwa yekha wa Mulunguyu ankadziwa bwino ulosi wakuti: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzeru, womvetsa zinthu, wolangiza, wamphamvu, wodziwa zinthu ndi woopa Yehova.” (Yes. 11:2) Yesu ankadziwa kuti akumana ndi mavuto padzikoli. Choncho mpake kuti ankafunikira kulandira mzimu woyera kuti umuthandize.

11 Mawu a Yehova anakwaniritsidwadi. Uthenga Wabwino wa Luka umanena zimene zinachitika Yesu atangobatizidwa. Timawerenga kuti: “Tsopano Yesu anachoka ku Yorodano atadzazidwa ndi mzimu woyera. Ndipo mzimuwo unamutenga ndi kumuyendetsa uku ndi uku m’chipululu.” (Luka 4:1) Ali m’chipululumo Yesu ankasala kudya, kupemphera ndiponso kusinkhasinkha. N’zodziwikiratu kuti Yehova anamulangiza ndiponso kumufotokozera zimene akumane nazo. Mphamvu ya Mulungu inkagwira ntchito m’maganizo ndi mumtima mwa Yesu ndipo ndi umene unkamutsogolera posankha zinthu. Izi n’zimene zinathandiza Yesu kuti azidziwa zochita pa nthawi iliyonse ndipo ankachita ndendende zimene Atate wake ankafuna.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha mzimu wa Mulungu kuti uzititsogolera?

12 Yesu ankadziwa kufunika kwa mzimu wa Mulungu pa moyo wake ndipo izi zinamuchititsa kuti alimbikitse ophunzira ake kupempha mzimuwo ndiponso kuulola kuti uziwatsogolera. (Werengani Luka 11:9-13.) N’chifukwa chiyani nafenso tiyenera kupempha mzimu woyera n’kuulola kuti uzititsogolera? Chifukwa chakuti ungasinthe kaganizidwe kathu kuti tikhale ndi maganizo amene Khristu ali nawo. (Aroma 12:2; 1 Akor. 2:16) Tikamalola mzimu wa Mulungu kutitsogolera, tikhoza kumaganiza ngati Khristu ndiponso kutengera chitsanzo chake.​—1 Pet. 2:21.

Mzimu wa Dziko Ukhoza Kutisocheretsa

13. Kodi mzimu wa dziko n’chiyani ndipo umachititsa anthu kukhala otani?

13 Chifukwa chachitatu chimene tingafunire mzimu wa Mulungu kuti uzititsogolera n’chakuti popanda mzimuwo tikhoza kusocheretsedwa  ndi mzimu woipa umene ukutsogolera anthu ambiri masiku ano. Dzikoli lili ndi mphamvu ina imene imachititsa anthu kuchita zosemphana ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. M’malo molimbikitsa anthu kukhala ndi maganizo a Khristu, mzimu wa dziko umachititsa anthu kutengera maganizo ndiponso zochita za Satana yemwe ndi wolamulira wa dzikoli. (Werengani Aefeso 2:1-3; Tito 3:3.) Munthu akalolera kutsogoleredwa ndi mzimu wa dzikoli n’kumachita ntchito za thupi, zotsatira zake zimakhala zoopsa ndipo zimachititsa kuti akhale wosayenera kulowa mu Ufumu wa Mulungu.​—Agal. 5:19-21.

14, 15. Kodi tingakane bwanji mzimu wa dzikoli?

14 Yehova watipatsa zinthu zonse zotithandiza kupewa mzimu wa dziko. Mtumwi Paulo anati: “Pitirizani kupeza mphamvu kuchokera kwa Ambuye ndiponso kuchokera ku mphamvu zake zazikulu . . . kuti musadzagonje m’tsiku loipa.” (Aef. 6:10, 13) Yehova amatipatsa mphamvu kudzera mu mphamvu yake ya mzimu woyera kuti Satana asatisocheretse. (Chiv. 12:9) Mzimu wa dziko ndi wamphamvu ndipo n’zosatheka kuupeweratu. Koma n’zotheka kuukana. Mzimu woyera ndi wamphamvu kwambiri kuposa mzimuwu ndipo ukhoza kutithandiza.

15 Ponena za anthu amene anasiya kukhulupirira Khristu kalelo, mtumwi Petulo ananena kuti: “Popeza anasiya njira yowongoka, asocheretsedwa.” (2 Pet. 2:15) Ndife oyamikira kwambiri kuti “sitinalandire mzimu wa dziko, koma mzimu wochokera kwa Mulungu.” (1 Akor. 2:12) Mothandizidwa ndi mzimu woyera komanso ngati tigwiritsa ntchito zinthu zonse zimene Yehova watipatsa kuti tiyende pa njira yoyenera, tikhoza kukana mzimu wa Satana umene uli m’dziko loipali.​—Agal. 5:16.

Mzimu Woyera Umatulutsa Makhalidwe Abwino

16. Kodi mzimu woyera ungatichititse kuti tikhale ndi makhalidwe ati?

16 Chifukwa chachinayi chimene tingafunire mzimu wa Mulungu kuti uzititsogolera n’chakuti mzimu woyera umatulutsa makhalidwe abwino kwambiri pa moyo wa anthu amene akutsogoleredwa nawo. (Werengani Agalatiya 5:22, 23.) Tonsefe timafuna kukhala anthu achikondi, achimwemwe komanso amtendere. Timafunanso kukhala anthu oleza mtima, okoma mtima ndiponso abwino. Timadziwa kuti zinthu zingakhale bwino kwambiri ngati tili ofatsa, odziletsa ndiponso tili ndi chikhulupiriro cholimba. Mzimu wa Mulungu umatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino amene ndi ofunika kwa ifeyo komanso kwa anthu a m’banja lathu ndiponso a ku mpingo. Kuti munthu ukhale ndi makhalidwe amene mzimuwu umatulutsa pamafunika kuchitabe khama ndipo palibe malire ochitira zimenezi.

17. Kodi tingatani kuti tizisonyeza kwambiri makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa?

17 Tingachite bwino kudzifufuza n’kuona ngati zolankhula komanso zochita zathu zimasonyeza kuti timatsogoleredwa ndi mzimu woyera komanso ngati tili ndi makhalidwe amene mzimuwu umatulutsa. (2 Akor. 13:5a; Agal. 5:25) Ngati taona kuti tilibe makhalidwe ena a mzimu woyera, tikufunika kuyesetsa kuti tikhale nawo ndiponso kudalira mzimu woyera kuti utithandize. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuphunzira khalidwe lililonse palokha pogwiritsira ntchito Baibulo komanso mabuku ena ofotokoza Baibulo. Tikatero tiyenera kuganizira mmene tingasonyezere khalidwelo pa zimene timachita tsiku ndi tsiku komanso kufufuza njira zosiyanasiyana zimene tingasonyezere kwambiri khalidwe limenelo. * Kuona mmene mzimu woyera umatithandizira pa moyo wathu komanso wa abale ndi alongo athu mu mpingo kumachititsa kuti timvetse chifukwa chake timafunika kutsogoleredwa ndi mzimu woyera.

Kodi Mumalola Mzimu wa Mulungu Kukutsogolerani?

18. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yolola mzimu wa Mulungu kutitsogolera?

18 Monga “mmisiri waluso” wa Mulungu pa ntchito yolenga zinthu, Yesu amadziwa bwino  mphamvu yamaginito imene kampasi imayendera. (Miy. 8:30; Yoh. 1:3) Komabe palibe vesi lililonse m’Baibulo lomwe limasonyeza kuti iye ankagwiritsa ntchito kampasi pamene anali padziko lapansi. Koma Baibulo limanena kuti pamene anali padziko lapansi Yesu ankatha kuona kuti mzimu woyera wa Mulungu ukugwira ntchito pa moyo wake. Iye anaulandira n’kuulola kuti uzimutsogolera kenako n’kumachita zinthu motsogoleredwa ndi mzimuwo. (Maliko 1:12, 13; Luka 4:14) Kodi inunso mumatero?

19. Kodi tingatani kuti mzimu woyera uzititsogolera pa moyo wathu?

19 Mzimu woyera umatsogolerabe maganizo ndi mitima ya anthu omwe amafuna kutsogoleredwa nawo. Ndiye kodi mungatani kuti mzimu woyera uzikutsogolerani? Muyenera kupemphera kwa Yehova nthawi zonse kuti akupatseni mzimu wake komanso kuti akuthandizeni kuti mulole kutsogoleredwa nawo. (Werengani Aefeso 3:14-16.) Muzisonyeza kuti mukufuna kutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu pophunzira Baibulo lomwe linalembedwa pogwiritsira ntchito mphamvu imeneyi ya mzimu woyera. (2 Tim. 3:16, 17) Muzimvera malangizo a nzeru a m’Baibulo komanso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kutsogoleredwa ndi mzimu woyera. Muyeneranso kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzatha kukutsogolerani bwino m’dziko loipali.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Kuti mumve zambiri zokhudza makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa werengani magazini awa: w07 7/15 mas. 24-25; w03 1/15 tsa. 11; w02 1/15 tsa. 17; w95 1/15 tsa. 16; w01 11/1 mas. 14-15; w03 7/1 tsa. 6; w01 1/1 tsa. 22; w03 4/1 mas. 15, 19-20; w03 10/15 tsa. 14.

Kodi Mwamvetsa Mfundo Zazikulu?

• Kodi mzimu woyera ungatithandize bwanji pa moyo wathu?

• Kodi ndi zifukwa zinayi ziti zimene timafunira mzimu wa Mulungu kuti uzititsogolera?

• Kodi tingatani kuti mzimu woyera uzititsogolera nthawi zonse?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Yesu ankatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu pa moyo wake

[Chithunzi patsamba 17]

Mzimu wa Mulungu umatsogolera maganizo ndi mitima ya anthu