Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musalole Kuti Matenda Akulandeni Chimwemwe

Musalole Kuti Matenda Akulandeni Chimwemwe

 Musalole Kuti Matenda Akulandeni Chimwemwe

TIYEREKEZE kuti mwadzuka m’mawa koma mukuona kuti zinthu sizikuyenda ayi. Mukuyenera kuzunzikanso ndi matenda komanso kuvutika maganizo. Mwina mungamamve ngati Yobu amene anati: “moyo wanga wasankha . . . imfa m’malo mwa mafupa angawa.” (Yobu 7:15) Kodi mungamve bwanji zimenezi zitakuchitikirani kwa zaka zambiri?

Izi ndi zimene zinachitikira Mefiboseti, mwana wa Jonatani yemwe anali mnzake wa Mfumu Davide. Mefiboseti ali ndi zaka zisanu ‘anagwetsedwa n’kulumala.’ (2 Sam. 4:4) Nthawi ina ananamiziridwa kuti wapandukira mfumu ndiponso analandidwa chuma chake. Mosakayikira zimenezi zinamuwawa mumtima. Koma iye anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopirira kulumala, kunenezedwa ndiponso kukhumudwitsidwa. Iye sanalole kuti zimenezi zimulande chimwemwe chake.​—2 Sam. 9:6-10; 16:1-4; 19:24-30.

Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi mtumwi Paulo. Pa nthawi ina, analemba za “munga m’thupi” umene ankazunzika nawo. (2 Akor. 12:7) Munga umenewu uyenera kuti unali vuto linalake m’thupi lake kapena anthu amene ankatsutsa zoti iye ndi mtumwi. Kaya vutolo linali lotani, linapitirira ndithu ndipo ankafunika kupirira.​—2 Akor. 12:9, 10.

Atumiki a Yehova ena masiku ano amavutika ndi matenda osachiritsika kapena kuvutika maganizo. Mwachitsanzo, Magdalena ali ndi zaka 18, anapezeka ndi matenda amene amachititsa kuti thupi la munthu liziwonongedwa ndi asilikali achitetezo a m’thupi mwake momwe. Iye anati: “Ndinachita mantha kwambiri. Matenda anga anayamba kuipiraipira ndipo ndinkavutika kwambiri ndi m’mimba, zilonda za m’kamwa ndiponso matenda a chithokomiro.” Koma Izabela amavutika ndi matenda amene anthu ambiri sangaone kuti akudwala. Iye anati: “Ndakhala ndikudwala matenda ovutika maganizo kuyambira ndili mwana. Izi zachititsa kuti nthawi zina ndizikhala ngati ndakomoka, ndizipuma mobanika ndiponso ndizivutika ndi m’mimba. Nthawi zambiri ndimakhala wofooka kwambiri.”

Dziwani Kuti Pali Zimene Simungathe Kuchita

Matenda kapena kulumala zikhoza kusintha kwambiri moyo wanu. Zinthu zimenezi zikakuchitikirani, ndi bwino kufatsa phee n’kuona zimene mungakwanitse ndi zimene simungathe kuchita. Koma kuchita zimenezi si kophweka. Magdalena anati: “Matenda anga akungoipiraipirabe. Nthawi zambiri ndimatopa kwambiri moti ndikagona sindifuna kudzuka. Popeza sindidziwa zomwe zindichitikire chifukwa cha matenda angawa, zimandivuta kupanga mapulani akutsogolo. Chimene chimandiwawa kwambiri n’chakuti sindithanso kuchita zimene ndinkachita mu utumiki wa Yehova.”

Nayenso Zbigniew akufotokoza kuti: “Chaka chilichonse thupi langa limakhala likufooka ndiponso kuwonongeka chifukwa cha matenda a nyamakazi. Nthawi zina thupi langa limatupa moti ndimalephera kugwira tintchito  ting’onoting’ono. Zimenezi zimandikhumudwitsa kwambiri.”

Zaka zingapo m’mbuyomu, Barbara anapezeka ndi chotupa mu ubongo. Iye anati: “Thupi langa lasintha kwambiri. Ndimakhala wofooka kwambiri, mutu umandipweteka pafupipafupi ndipo ndimavutika kuika maganizo anga pa zinthu. Chifukwa cha mmene matendawa akundifoolera, ndinayenera kuzindikira kuti panopa pali zinthu zina zimene sindingakwanitse kuchita.”

Anthu onse amene tawatchulawa ndi atumiki a Yehova odzipereka. Choncho iwo amaona kuti kuchita chifuniro chake ndi chinthu chofunika kwambiri. Iwo amakhulupirira Mulungu ndi mtima wonse ndipo iye amawathandiza.​—Miy. 3:5, 6.

Kodi Yehova Amathandiza Bwanji?

Tiyenera kupewa maganizo akuti munthu akamavutika ndiye kuti Mulungu sakusangalala naye. (Maliro 3:33) Taganizirani zimene zinachitikira Yobu ngakhale kuti anali “wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima.” (Yobu 1:8) Mulungu sayesa aliyense ndi zoipa. (Yak. 1:13) Matenda onse, kaya ndi osachiritsika kapena a maganizo, tinawalandira kuchokera kwa makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava.​—Aroma 5:12.

Koma Yehova ndi Yesu sadzasiya anthu olungama. (Sal. 34:15) Makamaka pa nthawi imene tikuvutika kwambiri m’pamene timaona umboni wakuti Mulungu ndi ‘pothawirapo pathu ndiponso malo athu achitetezo.’ (Sal. 91:2) Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe achimwemwe pamene tikupirira mavuto aakulu amene atigwera?

Pemphero: Mofanana ndi atumiki a Mulungu akale amene anali okhulupirika muyenera kutulira Atate wathu wakumwamba nkhawa zanu. (Sal. 55:22) Mukatero, mudzapeza “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” Mtendere umenewu “udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” (Afil. 4:6, 7) Magdalena amadalira kwambiri Mulungu ndipo amakonda kupemphera. Izi zimamuthandiza kupirira matenda ake. Iye anati: “Kuuza Yehova zakukhosi kwanga kumandithandiza kuti mtima wanga ukhale m’malo ndiponso kuti ndizikhalabe wosangalala. Panopa ndimadziwa bwino tanthauzo la kudalira Yehova tsiku lililonse.”​—2 Akor. 1:3, 4.

 Poyankha mapemphero anu, Yehova angakupatseni mphamvu kudzera mwa mzimu woyera, Mawu ake ndiponso Akhristu anzathu. Sitingayembekezere kuti Yehova atichotsera matenda athu m’njira yozizwitsa. Koma tiyenera kumudalira kuti atipatse nzeru ndi mphamvu zofunika kuti tipirire vuto lililonse. (Miy. 2:7) Iye akhoza kukuthandizani kwambiri pokupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa.”​—2 Akor. 4:7.

Anthu a m’banja lanu: Chikondi chimene anthu a m’banja lanu amasonyeza chingakuthandizeni kupirira matenda. Koma muyenera kukumbukira kuti anthu a m’banja lanu nawonso amavutika. Iwo amafuna thandizo ngati mmene inunso mumafunira. Ngakhale zili choncho, iwo akhoza kukuthandizani pa nthawi ya mavuto. Kupemphera limodzi kungakuthandizeni kuti mtima wanu uzikhala m’malo.​—Miy. 14:30.

Ponena za mwana wake wamkazi ndi alongo achitsikana a mu mpingo, mlongo wina dzina lake Barbara ananena kuti: “Amandithandiza kwambiri mu utumiki. Khama lawo limandisangalatsa kwambiri.” Zbigniew amaona kuti mkazi wake amamuthandiza kwambiri. Iye anati: “Mkazi wanga amagwira ntchito zonse zapakhomo. Amandiveka ndiponso kundinyamulira chikwama tikamapita ku misonkhano ndiponso mu utumiki.”

Akhristu anzathu: Tikakhala ndi Akhristu anzathu timalimbikitsidwa kwambiri. Koma bwanji ngati simukwanitsa kupita ku misonkhano chifukwa cha matenda anu? Magdalena anati: “Mpingo umayesetsa kwambiri kujambula misonkhano n’kunditumizira kuti ndizimvetsera. Akhristu ena amaimba foni kuti adziwe thandizo limene ndikufuna. Amandilemberanso makalata olimbikitsa kwambiri. Ndimalimbikitsidwa kwambiri chifukwa chodziwa kuti iwo amandikumbukira ndiponso kundiganizira.”

Izabela amene amadwala matenda ovutika maganizo anati: “Mu mpingo ndili ndi ‘atate,’ ndi ‘amayi’ ambirimbiri amene amamvetsera ndikamalankhula ndipo amadziwa bwino mavuto anga. Panopa mpingo uli ngati banja langa ndipo umandithandiza kukhala ndi mtendere wa mumtima komanso kukhala wosangalala.”

Anthu amene akukumana ndi mavuto osiyanasiyana ayenera kupewa ‘kudzipatula.’ Iwo ayenera kudziwa kuti kucheza ndi anzawo mu mpingo n’kothandiza kwambiri. (Miy. 18:1)  Akhristu ena amalimbikitsidwa kwambiri akamacheza nawo. Ngati mukukumana ndi mavuto, mwina nthawi zina simungafune kuti abale ndi alongo ena adziwe zimene mukufunikira. Koma dziwani kuti Akhristu anzanu amasangalala mukamamasuka nawo ndi kuwauza zimene mukufuna. Mukatero, zimawathandiza kuti akusonyezeni ‘chikondi chopanda chinyengo.’ (1 Pet. 1:22) Muzikhala omasuka kuwauza kuti mukufuna kuti akutengeni popita ku misonkhano, kuyenda nawo mu utumiki kapena kukambirana nawo pamalo oduka mphepo. Tiziyamikira thandizo lawo komabe tiyenera kupewa kuwapanikiza.

Muziona zinthu moyenera: Chimene chingakuthandizeni kukhalabe osangalala ngakhale kuti mumadwaladwala ndi kuona zinthu moyenera. Kumangokhala wokhumudwa nthawi zonse kungachititse kuti mukhale ndi maganizo olakwika. Baibulo limanena kuti: “Mtima wa munthu ukhoza kupirira matenda, koma mtima wosweka ndani angaupirire?”​—Miy. 18:14.

Magdalena anati: “Ndimayesetsa kwambiri kuti ndisamangoganizira za mavuto anga. Ndimaonetsetsa kuti ndizisangalala masiku amene ndadzuka bwino. Ndimalimbikitsidwa kwambiri ndikamawerenga nkhani za anthu amene akhalabe okhulupirika ngakhale kuti amadwaladwala.” Izabela amalimbikitsidwa ndi mfundo yakuti Yehova amamukonda ndipo amamuona kuti ndi wamtengo wapatali. Iye anati: “Ndimaona kuti ndine munthu wofunika ndipo moyo wanga ndi wamtengo wapatali pamaso pa munthu winawake. Ndikuyembekezeranso zinthu zabwino kwambiri mtsogolo.”

Zbigniew anati: “Matenda anga andithandiza kukhala wodzichepetsa ndiponso womvera. Andithandizanso kukhala wozindikira, woganiza bwino ndiponso wotha kukhululuka ndi mtima wonse. Ndaphunziranso kutumikira Yehova mosangalala ndiponso mopanda kudzimvera chisoni. Ndipotu ndalimbikitsidwa kuti ndizipitabe patsogolo mwauzimu.”

Musaiwale kuti Yehova amaona kupirira kwanu. Amakumverani chisoni ndipo amakuganizirani kwambiri. Iye ‘sangaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.’ (Aheb. 6:10) Nthawi zonse muzikumbukira lonjezo limene Mulungu wapereka kwa anthu amene amamuopa. Iye anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”​—Aheb. 13:5.

Ngati nthawi zina mumakhumudwa, muyenera kukumbukira zinthu zabwino kwambiri zimene mukuyembekezera m’dziko latsopano. Posachedwapa mudzaona madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse padziko lapansi.

[Bokosi/​Zithunzi pamasamba 28, 29]

Amalalikirabe Ngakhale Kuti Amadwaladwala

“Sinditha kuyenda ndekha choncho ndimayenda ndi mkazi wanga kapena Akhristu ena mu utumiki. Ndimaloweza maulaliki osiyanasiyana ndiponso mavesi.”​—Jerzy, yemwe saona.

“Kuwonjezera pa kulalikira pa telefoni, ndimakonda kulemba makalata makamaka kwa anthu achidwi. Ndikagonekedwa m’chipatala, nthawi zonse ndimaika Baibulo ndi mabuku pafupi ndi bedi langa. Zimenezi zimandithandiza kuti ndiyambe kukambirana bwino ndi anthu.”​—Magdalena, yemwe ali ndi matenda amene amachititsa kuti thupi la munthu liziwonongedwa ndi asilikali achitetezo a m’thupi mwake momwe.

“Ndimakonda kulalikira khomo ndi khomo koma ndikaona kuti sindili bwino, ndimalalikira pa telefoni.”​—Izabela, yemwe ali ndi matenda a maganizo.

“Ndimakonda kuchita maulendo obwereza komanso kuthandiza pa maphunziro a Baibulo a anthu ena. Ndikadzuka bwino ndimakonda kulalikira kunyumba ndi nyumba.”​—Barbara, yemwe ali ndi chotupa mu ubongo.

“Ndimangonyamula kachikwama kopepuka ka magazini. Ndimangolalikira kanthawi kochepa pamene ndikuona kuti miyendo yanga sikupweteka kwambiri.”​—Zbigniew, yemwe ali ndi matenda a nyamakazi.

[Chithunzi patsamba 30]

Achinyamata ndi achikulire omwe akhoza kutilimbikitsa