Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

• Kodi Olivétan anali ndani ndipo n’chifukwa chiyani zimene anachita zili zochititsa chidwi?

Anali mnyamata wachifulenchi amene ankadziwikanso ndi dzina lakuti Pierre Robert. Pa nthawi imene anthu ankachoka m’tchalitchi cha katolika m’zaka za m’ma 1500, anamasulira Baibulo m’Chifulenchi. Iye anasankha kugwiritsa ntchito mawu akuti “woyang’anira” osati “bishopu” komanso mawu akuti “mpingo” osati “tchalitchi.” M’malo ena anamasulira dzina la Mulungu kuti “Yehova.”​—9/1, tsamba 18-20.

• Kodi Mulungu anatanthauza chiyani pouza Alevi kuti “Ine ndine gawo lanu”?

Fuko lililonse la Aisiraeli linalandira malo monga cholowa chawo koma Alevi sanalandire malo chifukwa Yehova anali “gawo” lawo. (Num. 18:20) Iwo anapatsidwa mwayi waukulu wotumikira Yehova pa udindo wapadera. Ndiyeno Yehova ankawasamalira powapatsa zofunikira pa moyo. Masiku anonso anthu amene amapititsa patsogolo zinthu za Ufumu amakhala otsimikizira kuti Yehova adzawapatsa zofunikira pamoyo.​—9/15, tsamba 7-813.

• Kodi timadziwa bwanji chaka chimene Yerusalemu anawonongedwa ndi Ababulo?

Akatswiri olemba mbiri amafotokoza zosiyanasiyana zokhudza ulamuliro wa Babulo ndi mafumu ake. Koma akatswiri ena amavomereza kuti Koresi Wachiwiri anagonjetsa Babulo m’chaka cha 539 B.C.E., chomwe ndi chaka chofunika kwambiri. Ndipo Ayuda anamasulidwa mu ukapolo n’kubwerera kwawo m’chaka cha 537 B.C.E. Baibulo limatiuza kuti Ayuda anakhala ku ukapolo zaka 70 choncho Yerusalemu anawonongedwa mu 607 B.C.E. (2 Mbiri 36:21, 22; Yer. 29:10; Dan. 9:1, 2)​—10/1, tsamba 26-31.

• Kodi n’chiyani chingathandize Mkhristu kudziwa ngati zosangalatsa zimene wasankha zili zabwino kapena zoipa?

Kuti munthu adziwe ngati zosangalatsa zimene wasankha ndi zabwino komanso zokondweretsa Mulungu, m’pofunika kudzifunsa kuti: Kodi zosangalatsazo n’zotani? Kodi ndizizichita liti? Kodi ndizichita ndi ndani?​10/15, tsamba 9-12.

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuchotsa mimba n’kulakwa?

Mulungu amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali ndipo amaonanso kuti mwana amene wangoyambika kumene m’mimba mwa mayi ake ndi munthu. (Sal. 139:16) M’Chilamulo, munthu amene wavulaza mwana wosabadwa ankaimbidwa mlandu choncho Mulungu amaona kuti kupha mwana wosabadwa n’chimodzimodzi kupha munthu. (Eks. 21:22, 23)​—11/1, tsamba 6.

• Kodi nkhani ya pa Miyambo7:6-23 ingatithandize bwanji kuti tipewe kuonera zolaula?

Nkhani imeneyi imanena za mnyamata amene anali kuyenda mumsewu wolowera kumene kunkakhala mkazi wachiwerewere. Iye anakopeka ndi mkaziyo. Masiku ano tiyenera kupewa malo a pa Intaneti amene amakhala ndi zithunzi zolaula ndipo ndi bwino kupemphera kwa Yehova tisanayambe kufufuza zinthu pa Intaneti.​—11/15, tsamba 9-10.

• Kodi tikudziwa bwanji kuti dzikoli silidzatha m’chaka cha 2012?

Anthu ambiri akukhulupirira kuti dziko litha mu 2012 chifukwa chakuti ndi pamapeto pa kalendala yakale ya anthu otchedwa a Maya. Koma zimenezi si zoona chifukwa chakuti Yehova analenga dzikoli kuti anthu akhalemo ndipo Baibulo limanena kuti dzikoli lidzakhalapobe mpaka kalekale. (Mlal. 1:4; Yes. 45:18)​—12/1, tsamba 10.

• Pa anthu amene analemba nawo Baibulo, kodi ndi ati amene analipo pa Pentekosite wa m’chaka cha 33 C.E.?

Zikuoneka kuti panali anthu 6 amene analemba nawo Malemba Achigiriki. Panali atumwi atatu omwe ndi Mateyu, Yohane ndi Petulo. Yakobo ndi Yuda omwe ndi azibale ake a Yesu analinso pomwepo. N’kutheka kuti mnyamata wina dzina lake Maliko analiponso.​—12/1, tsamba 22.