Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizani Ena Kuti Ayenerere Maudindo

Thandizani Ena Kuti Ayenerere Maudindo

 Thandizani Ena Kuti Ayenerere Maudindo

“Aliyense amene waphunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake.”​—LUKA 6:40.

1. Kodi Yesu asanapite kumwamba anachita chiyani kuti asonkhanitse anthu amene anadzakhala mpingo waukulu?

KUMAPETO kwa uthenga wabwino wa Yohane kuli mawu akuti: “Ndipo pali zinthu zinanso zambiri zimene Yesu anachita. Zikanakhala kuti zonse zinalembedwa mwatsatanetsatane, ndikuganiza kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana m’dzikoli.” (Yoh. 21:25) Yesu anachita utumiki wake padziko lapansi kwa nthawi yochepa koma anachita zinthu zambiri. Zina mwa zinthu zimene anachita zinali kufufuza amuna, kuwaphunzitsa ndiponso kuwasonkhanitsa kuti adzatsogolere gulu la Mulungu iye akapita kumwamba. Pamene ankapita kumwamba m’chaka cha 33 C.E., iye anali atayala maziko a mpingo umene pasanapite nthawi anthu ake anawonjezeka n’kukwana masauzande.​—Mac. 2:41, 42; 4:4; 6:7.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani amuna ambiri mu mpingo afunika kuyesetsa kuti ayenerere maudindo? (b) Kodi m’nkhani ino tikambirana chiyani?

2 Masiku ano pali ofalitsa Ufumu oposa 7 miliyoni m’mipingo yoposa 100,000. Choncho pakufunika amuna ambiri oti azitsogolera pa zinthu zauzimu mu mpingo. Popeza m’mipingo mukufunika akulu ambiri, anthu amene akuyesetsa kuti ayenerere udindo umenewu ndi ofunika kuwayamikira chifukwa “akufuna ntchito yabwino.”​—1 Tim. 3:1.

3 Komabe, kuyenerera pa udindo umenewu sikuchitika pakokha. Maphunziro akudziko kapena  zimene munthu wakhala akuchita pa moyo sizichititsa kuti munthu ayenerere ntchito imeneyi. Kuti munthu agwire bwino ntchito imeneyi ayenera kukhala woyenera mwauzimu. Munthu ayenera kukhala ndi makhalidwe ofotokozedwa m’Baibulo osati luso kapena zinthu zina zimene wakhala akuchita. Kodi amuna mu mpingo angathandizidwe bwanji kuti ayenerere udindo? Yesu ananena kuti: “Aliyense amene waphunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake.” (Luka 6:40) M’nkhani ino tikambirana mmene Mphunzitsi Waluso Yesu Khristu anathandizira ophunzira ake kuti ayenerere maudindo akuluakulu. Tionanso zimene tikuphunzira pa chitsanzo chake.

“Ndakutchani Mabwenzi”

4. Kodi Yesu anawasonyeza bwanji ophunzira ake kuti anali bwenzi lawo lapamtima?

4 Yesu ankachita zinthu ndi ophunzira ake monga mabwenzi ake osati ngati anthu otsika. Iye ankacheza nawo, kuwafotokozera maganizo ake ndiponso ‘ankawadziwitsa zonse zimene anamva kwa Atate wake.’ (Werengani Yohane 15:15.) Tangoganizirani mmene iwo anasangalalira pamene Yesu anawayankha funso lawo lakuti: ‘Kodi chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?’ (Mat. 24:3, 4) Iye ankauzanso otsatira ake zimene zili m’maganizo ndi mumtima mwake. Usiku woti aperekedwa, Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane n’kupita m’munda wa Getsemane. Kumeneko iye anapemphera mochonderera chifukwa chovutika kwambiri mumtima mwake. Atumwi atatuwa ayenera kuti sanamve zimene Yesu ankanena koma anadziwa kuti zinthu zafika povuta. (Maliko 14:33-38) Taganiziraninso mmene ophunzira atatuwo anamvera ataona Yesu atasandulika. (Maliko 9:2-8; 2 Pet. 1:16-18) Kugwirizana kwawo ndi Yesu kunathandiza kwambiri ophunzirawo kuti akhale olimba mtima pogwira ntchito yofunika kwambiri imene anapatsidwa pambuyo pake.

5. Tchulani njira zimene akulu achikhristu angathandizire ena.

5 Mofanana ndi Yesu, akulu achikhristu amamasuka ndi anthu ndipo amawathandiza. Iwo amacheza ndi Akhristu anzawo n’cholinga choti akhale nawo pa ubwenzi wabwino. Akulu amazindikira kuti pali nkhani zina zomwe ndi zachinsinsi zimene sayenera kulankhula kwa ena, koma sikuti amayenera kukhala achinsinsi pa chilichonse. Iwo amakhulupirira abale awo ndipo amatha kuwafotokozera zinthu zokhudza choonadi zimene aziphunzira kuchokera m’Baibulo. Akulu samaona mtumiki wothandiza yemwe ndi wachinyamata kuti ndi wotsika. M’malomwake amaona kuti ndi m’bale wauzimu amene akhoza kusamalira bwino maudindo mu mpingo.

“Ndakupatsani Chitsanzo”

6, 7. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani kwa ophunzira ake ndipo zimenezi zinawathandiza bwanji?

6 Ngakhale kuti ophunzira a Yesu ankaona kuti zinthu zauzimu n’zofunika, nthawi zina chikhalidwe chawo ndiponso mmene anakulira zinkasokoneza mmene ankaonera zinthu. (Mat. 19:9, 10; Luka 9:46-48; Yoh. 4:27) Komabe sikuti Yesu ankangokhalira kuwapatsa uphungu kapena kuwakalipira. Yesu sankawaumiriza kuchita zinthu zomwe zinali zovuta ndipo sankawapempha kuchita zinthu zomwe iyeyo sakanatha kuchita. Koma iye ankawaphunzitsa powapatsa chitsanzo.​—Werengani Yohane 13:15.

7 Kodi Yesu anawasiyira chitsanzo chotani ophunzira ake? (1 Pet. 2:21) Iye ankakhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti athe kutumikira ena popanda chododometsa. (Luka 9:58) Yesu anali wodzichepetsa ndipo nthawi zonse ankaphunzitsa zinthu zochokera m’Malemba. (Yoh. 5:19; 17:14, 17) Anali wochezeka ndiponso wachifundo. Iye ankachita chilichonse chifukwa chachikondi. (Mat. 19:13-15; Yoh. 15:12) Zimene Yesu anali kuchita zinathandiza kwambiri ophunzira ake. Mwachitsanzo, Yakobo sanachite mantha pamene anaopsezedwa ndipo anatumikira Mulungu molimba mtima mpaka pamene anaphedwa. (Mac. 12:1, 2) Nayenso Yohane anatsanzira Yesu mokhulupirika kwa zaka zoposa 60.​—Chiv. 1:1, 2, 9.

8. Kodi akulu angakhale bwanji chitsanzo chabwino kwa achinyamata ndiponso kwa anthu ena?

8 Akulu omwe ndi odzipereka, odzichepetsa  ndiponso achikondi amapereka chitsanzo chabwino kwa achinyamata mu mpingo. (1 Pet. 5:2, 3) Komanso akulu omwe amasonyeza chitsanzo chabwino pa chikhulupiriro, kuphunzitsa, makhalidwe achikhristu ndiponso mu utumiki, amasangalala kudziwa kuti chitsanzo chawo chimathandiza ena.​—Aheb. 13:7.

Yesu Atawapatsa Malangizo, Anawatumiza Kukalalikira

9. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu anaphunzitsa ophunzira ake ntchito yolalikira?

9 Yesu atalalikira mwakhama kwa zaka pafupifupi ziwiri anatumiza atumwi ake 12 kuti akalalikire. Koma asananyamuke anawapatsa malangizo. (Mat. 10:5-14) Pa nthawi ina Yesu akufuna kudyetsa khamu la anthu mozizwitsa, anauza ophunzira ake kuti asonkhanitse anthu m’magulumagulu ndi kuwapatsa chakudya. (Luka 9:12-17) Choncho Yesu anaphunzitsa ophunzira ake powapatsa malangizo omveka bwino ndiponso osavuta kuwatsatira. Kaphunzitsidwe kameneka komanso mphamvu ya mzimu woyera zinathandiza atumwi kuti atsogolere bwino ntchito yolalikira imene inachitika m’chaka cha 33 C.E ndiponso m’zaka zotsatira.

10, 11. Kodi akulu limodzi ndi anthu ena mumpingo angathandize bwanji ena kuchita utumiki wosiyanasiyana?

10 Masiku ano, munthu amayamba kulandira malangizo auzimu pamene wayamba kuphunzira Baibulo. Tingafunike kumuthandiza kuti aziwerenga bwino. Ndipo pamene tikupitiriza kuphunzira naye Baibulo tiyenera kumamuthandizabe. Komanso pamene wayamba kubwera ku misonkhano, amayamba kudziwa zambiri akalembetsa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kukhala wofalitsa wosabatizidwa ndiponso kuchita zinthu zina. Pambuyo pobatizidwa angamathandize zinthu monga kukonza Nyumba ya Ufumu. Kenako m’baleyo angathandizidwe kudziwa zofunika kuchita kuti ayenerere kukhala mtumiki wothandiza.

11 Mkulu akamapatsa m’bale wobatizidwa zochita, amamufotokozera mmene zinthu zimayendera m’gulu la Mulungu komanso kumupatsa malangizo ofunika. M’bale amene akumuphunzitsayo ayenera kudziwa zimene akufunikira kuchita. Ngati akuvutika kuchita zimene akumuuza, mkulu wachikondi sangofikira kuganiza kuti m’baleyo sangakwanitse udindowo. M’malomwake angachite bwino kumuthandiza zimene ayenera kusintha ndi kumufotokozeranso zimene ayenera kuchita. Akulu amasangalala akaona anthu akusintha chifukwa cha thandizo lawo.​—Mac. 20:35.

Munthu “Womvera Malangizo ndi Wanzeru”

12. N’chiyani chinachititsa kuti malangizo a Yesu akhale ogwira mtima?

12 Yesu ankathandizanso ophunzira ake powapatsa malangizo ogwirizana ndi mavuto awo. Mwachitsanzo, iye anadzudzula Yakobo ndi Yohane chifukwa chofuna kuitanitsa moto kuchokera kumwamba kuti unyeketse Asamariya amene sanamulandire. (Luka 9:52-55) Komanso pamene mayi a Yakobo ndi Yohane anapita kwa Yesu kukapempha kuti ana awo akhale ndi maudindo apamwamba mu Ufumu, Yesu anauza abale akewo mosapita m’mbali kuti: “Kunena zokhala kudzanja langa lamanja ndi lamanzere, si ine wopereka mwayi umenewo, koma Atate wanga adzaupereka kwa amene anawakonzera.” (Mat. 20:20-23) Nthawi zonse Yesu ankapereka malangizo omveka bwino, othandiza komanso ogwirizana ndi mfundo za Mulungu. Iye anathandiza ophunzira ake kuganizira mfundo zimenezi. (Mat. 17:24-27) Komabe Yesu ankaganizira zimene ophunzira ake angakwanitse kuchita ndipo sankayembekezera kuti azichita zinthu mwangwiro. Iye ankawalangiza chifukwa chowakonda.​—Yoh. 13:1.

13, 14. (a) Kodi ndani amafunika malangizo? (b) Perekani chitsanzo cha malangizo amene mkulu angapereke kwa munthu yemwe sakupita patsogolo mwauzimu.

13 Munthu aliyense amene akuyesetsa kuti akhale ndi maudindo mumpingo pa nthawi inayake amafuna malangizo a m’Malemba. Lemba la Miyambo 12:15 limanena kuti: “Womvera malangizo ndi wanzeru.” M’bale wina wachinyamata ananena kuti, “Vuto langa lalikulu linali kulimbana ndi kupanda ungwiro kwanga. Koma malangizo amene m’bale wina yemwe ndi mkulu  anandipatsa anandithandiza kuti ndikhale ndi maganizo oyenera pa nkhani imeneyi.”

14 Mkulu akaona kuti khalidwe linalake likulepheretsa munthu wina kukula mwauzimu, amayesa kumuthandiza ndi mzimu wofatsa. (Agal. 6:1) Nthawi zina munthu angafunike kupatsidwa malangizo chifukwa cha khalidwe lake. Mwachitsanzo, ngati m’bale wina ndi wamphwayi, mkulu angamuthandize kudziwa kuti Yesu anali wakhama polalikira za Ufumu ndipo iye ndi amene analamula otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu. (Mat. 28:19, 20; Luka 8:1) Ngati m’bale akuoneka kuti akulakalaka zinthu zapamwamba, mkulu angamuthandize kuona mmene Yesu anathandizira ophunzira ake kuti apewe mtima wofuna kulamulira ena. (Luka 22:24-27) Nanga bwanji ngati m’bale ali ndi vuto losakhululukira anzake? Mwina mkulu angamuthandize ndi fanizo la kapolo amene sanakhululukire mnzake amene anabwereka tindalama tochepa ngakhale kuti iye anakhululukiridwa ngongole yaikulu. (Mat. 18:21-35) Ngati munthu wina angafunike malangizo, akulu angachite bwino kumuthandiza mwamsanga.​—Werengani Miyambo 27:9.

Muzichita Zinthu Zokuthandizani Kuti Muyenerere Maudindo

15. Kodi banja lingathandize bwanji mwamuna kuti azitumikira ena?

15 N’zoona kuti akulu amayesetsa kuthandiza amuna kuti ayenerere maudindo koma anthu ena akhoza kuthandizanso. Mwachitsanzo, banja la munthu amene akufuna kukhala ndi maudindo liyenera kumuthandiza kuti ayenerere udindowo. Ngati ndi mkulu kale, mkazi komanso ana ake akhalidwe labwino angamuthandizenso. Kuti mkulu azisamalira bwino udindo wake m’pofunika kuti banja lakelo lizidziwa kuti nthawi ina azichita zinthu zina mu mpingo. Iye amasangalala kwambiri banja lake likamadzimana n’cholinga choti iye athe kusamalira bwino maudindo ake. Timayamikira kwambiri kudzimana kumene mabanja amenewa amasonyeza.​—Miy. 15:20; 31:10, 23.

16. (a) Kuti munthu ayenerere udindo winawake, kodi ndani ayenera kuchita khama kwambiri? (b) Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti ayenerere udindo mu mpingo?

16 Akulu amathandiza munthu kuti ayenerere udindo, koma amene ayenera kuchita khama kwambiri ndi munthuyo. (Werengani Agalatiya 6:5.) Sikuti m’bale amafunika kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu kuti azitha kuthandiza ena kapena kuti azilalikira mwakhama. Komabe kuti munthu ayenerere maudindo mu mpingo ayenera kuyesetsa kukwaniritsa zimene Malemba amanena. (1 Tim. 3:1-13; Tito 1:5-9; 1 Pet. 5:1-3) Choncho ngati munthu akufuna kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu, ayenera kuona mbali zimene afunikira kusintha kuti apite patsogolo mwauzimu. Kuti zimenezi zitheke, ayenera kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo mwakhama, kusinkhasinkha kwambiri, kupemphera mochokera pansi pamtima ndiponso  kulalikira mwakhama. Akamachita zimenezi, ndiye kuti akukwanitsa kuchita zimene Paulo anauza Timoteyo kuti: “Ukhale ndi chizolowezi chochita zinthu zokuthandiza kuti ukhalebe wodzipereka kwa Mulungu.”​—1 Tim. 4:7.

17, 18. Kodi Mkhristu yemwe ndi wobatizidwa angachite chiyani ngati nkhawa, kudzikayikira kapena maganizo osafuna kutumikira zikumulepheretsa kuti ayenerere udindo mu mpingo?

17 Bwanji ngati munthu sakuyesetsa kuti ayenerere chifukwa cha nkhawa kapena kudzikayikira? Iye angachite bwino kuganizira zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu amatichitira. Yehova “amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.” (Sal. 68:19) Choncho Atate wathu wakumwamba angathandize m’bale kukwaniritsa udindo wake mu mpingo. M’bale amene si mtumiki wothandiza kapena mkulu angachite bwino kuganizira mfundo yakuti pakufunika amuna ambiri omwe ndi okhwima mwauzimu oti atumikire m’gulu la Mulungu. Kuganizira mfundo zimenezi kungathandize m’bale kuti ayesetse kuthetsa maganizo odzikayikira. Angapempherere mzimu woyera kuti umuthandize kuti akhale ndi makhalidwe amene mzimu woyerawo umatulutsa monga mtendere ndi kudziletsa. Makhalidwe amenewa amathandiza kuti munthu asamade nkhawa kapena kudzikayikira. (Luka 11:13; Agal. 5:22, 23) Tingakhale otsimikiza kuti Yehova amadalitsa anthu onse amene akuyesetsa ndi zolinga zabwino kuti akhale ndi maudindo.

18 Bwanji ngati munthu sakuyesetsa kuti akhale ndi udindo chifukwa chakuti alibe maganizo ofuna kutumikira? N’chiyani chingathandize m’bale wotereyu? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu amachita zinthu m’njira imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.” (Afil. 2:13) Mulungu amathandiza munthu kukhala ndi mtima wofuna kutumikira ndipo mzimu wa Yehova umalimbikitsa munthu kuchita utumiki wopatulika. (Afil. 4:13) Kuwonjezera pamenepo, Mkhristu angapemphe Mulungu kuti amuthandize kuchita zoyenera.​—Sal. 25:4, 5.

19. Kodi mfundo yoti mumpingo mudzakhala “abusa 7, inde atsogoleri 8” ikutanthauza chiyani?

19 Yehova amadalitsa anthu amene amachita khama pophunzitsa ena. Amadalitsanso anthu amene amayesetsa kuti akhale ndi maudindo mumpingo. Malemba amatitsimikizira kuti pakati pa anthu a Mulungu padzakhala “abusa 7, inde atsogoleri 8.” Mawu amenewa akuimira chiwerengero chokwanira cha amuna oyenerera amene adzaikidwe kuti azitsogolera m’gulu la Yehova. (Mika 5:5) N’zosangalatsa kwambiri kuti amuna ambiri achikhristu akuthandizidwa kuti ayenerere maudindo ndipo zimenezi zimachititsa kuti Yehova atamandidwe.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzira ake kuti adzatumikire ena?

• Kodi akulu angatsanzire bwanji Yesu pothandiza amuna mu mpingo kuti ayenerere maudindo?

• Kodi anthu a m’banja la munthu angamuthandize bwanji kuti ayenerere maudindo?

• Kodi m’bale angatani kuti ayenerere udindo?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 31]

Kodi munthu amene mumaphunzira naye Baibulo mungamuthandize bwanji kuti akule mwauzimu?

[Chithunzi patsamba 32]

Kodi abale angachite chiyani kuti ayenerere udindo?