Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumasangalala ndi “Mwayi Wopereka Nawo Mphatso Zachifundo”?

Kodi Mumasangalala ndi “Mwayi Wopereka Nawo Mphatso Zachifundo”?

 Kodi Mumasangalala ndi “Mwayi Wopereka Nawo Mphatso Zachifundo”?

AKHRISTU oyambirira a ku Filipi ankadziwika kuti anali owolowa manja popereka zinthu zothandiza pa kulambira koona. M’kalata youziridwa imene anawalembera, Paulo ananena kuti: “Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira za inu. Ndimachita zimenezi m’pembedzero langa lililonse limene ndimapereka mosangalala chifukwa cha nonsenu. Ndimamuyamika chifukwa cha chopereka chanu chimene mwakhala mukupereka ku uthenga wabwino, kuchokera pa tsiku loyamba mpaka pano.” (Afil. 1:3-5) Paulo ankakumbukira bwino mtima wochereza umene Lidiya pamodzi ndi a m’banja lake anamusonyeza. Anthu a m’banjali atabatizidwa, anachonderera kuti Paulo limodzi ndi anzake, omwe anali kugwira nawo ntchito yolalikira, azikhala m’nyumba mwawo.​—Mac. 16:14, 15.

Ndiyeno pasanapite nthawi mpingo watsopano wa ku Filipi unatumizira mphatso Paulo kawiri pamene anali kuchezera Akhristu a ku Tesalonika. Kuti akam’peze Paulo, anafunika kuyenda mtunda  wa makilomita 160. (Afil. 4:15, 16) Patapita zaka zingapo, Akhristu a ku Filipi ndi a ku Makedoniya anali pa mavuto komanso pa “umphawi wadzaoneni,” koma atamva kuti Akhristu anzawo a ku Yerusalemu akuzunzidwa anafuna kuwathandiza. Paulo ananena kuti iwo ‘anachita malinga ndi zimene akanatha komanso zoposa pamenepo.’ Ponena za Akhristuwo iye analemba kuti: “Anapitiriza kutipempha mochokera pansi pa mtima ndiponso mochonderera kwambiri, kuti tiwapatse mwayi wopereka nawo mphatso zachifundo.”​—2 Akor. 8:1-4; Aroma 15:26.

Kwa zaka pafupifupi 10 kuchokera pamene Afilipi anakhala Akhristu, iwo anapitirizabe kusonyeza mzimu wopatsa umenewu. Atamva kuti Paulo ali m’ndende ku Roma, iwo anatuma Epafurodito kuti anyamule zinthu akamupatse. Epafurodito anayenda mtunda wa makilomita 1,287 kuti akafike ku Roma komwe Paulo anali. Akhristu a ku Filipi amenewa, anali ofunitsitsa kuthandiza Paulo n’cholinga choti iye apitirize kulimbikitsa abale ndiponso kulalikira ngakhale pamene anali m’ndende.​—Afil. 1:12-14; 2:25-30; 4:18.

Masiku ano Akhristu oona amaona kuti ndi mwayi kupereka zinthu zothandiza pa ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Iwo amagwiritsa ntchito nthawi yawo, mphamvu zawo ndiponso ndalama zawo kuti athandize pa ntchito zokhudza Ufumu. Bokosi lili m’munsili likusonyeza zinthu zina zimene mungachite kuti muthandize pa ntchito imene Mulungu watipatsayi.

[Bokosi pamasamba 22, 23]

NJIRA ZIMENE ENA AMAPEREKERA

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amachita bajeti, kapena kuti amaika padera ndalama zoti aziponya m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Ntchito ya Padziko Lonse.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira ntchito ya m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha ndalama zimene mukufuna ku Accounting Office, Watch Tower Society, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu. Mukamatumiza macheke ku adiresi yomwe ili pamwambayi, musonyeze kuti ndalamazo zipite ku “Watch Tower.” Mungathenso kupereka zinthu ngati ndolo, mphete, zibangili, kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Potumiza zinthu zimenezi, mulembe kalata yachidule yofotokoza kuti zimene mukutumizazo ndi mphatso basi.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mphatso za ndalama, pali njira zinanso zoperekera zinthu popititsa patsogolo ntchito ya Ufumu padziko lonse. Zina mwa njirazi ndi izi:

Inshuwalansi: Mungalembetse kuti Watch Tower Society ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena ndalama za penshoni.

Maakaunti Akubanki: Mukhoza kuikiza m’manja mwa Watch Tower Society maakaunti anu akubanki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pa ntchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira, a Watch Tower Society adzatenge zinthu zimenezi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya: Mungapereke masheya amene muli nawo m’kampani ku Watch Tower Society monga mphatso basi.

Malo ndi Nyumba: Mungapereke mphatso monga malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe, kapena ngati ili nyumba yoti mukukhalamo, mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo. Musanakonze zopereka malo kapena nyumba iliyonse, lankhulani kaye ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu.

Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ndi boma kuti Watch Tower Society idzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, ngati inuyo mutamwalira.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatso zimenezi, lankhulani ndi a ku Accounting Office pa telefoni kapena alembereni kalata pa adiresi imene ili pansipa kapenanso mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

Accounting Office

Watch Tower Society

P. O. Box 30749

Lilongwe 3

Malawi

Telefoni: 01 762111