Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi ndizitani ngati ndili ndi funso lokhudza zimene ndinawerenga m’Baibulo kapena ngati ndikufuna kuti munthu andipatse malangizo pa vuto limene ndili nalo?

Lemba la Miyambo 2:1-5 limalimbikitsa tonsefe kupitiriza ‘kufufuza’ ndiponso kuzindikira zinthu ngati kuti tikufufuza “chuma chobisika.” Choncho m’pofunika kuti tiziyesetsa mwakhama kufufuza m’Baibulo mayankho a mafunso omwe tingakhale nawo. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

Buku lakuti Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu tsamba 33 mpaka 38 limafotokoza za “Mmene Mungafufuzire.” Limatchula zida zimene tingagwiritse ntchito zomwe “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka. (Mat. 24:45) Patsamba 36 pamafotokoza mmene tingagwiritsire ntchito namlozera wotchedwa “Watch Tower Publications Index” yemwe ali ndi mbali ziwiri zotilozera nkhani. Mbalizi ndi mlozera mawu komanso mlozera malemba. Izi zimathandiza kuti tizifufuza pogwiritsa ntchito mawu ofunika kwambiri m’nkhaniyo kapena mavesi a m’Baibulo ndipo munthu amapeza mndandanda wa mabuku amene afotokoza nkhaniyo. Muyenera kufufuza mofatsa mayankho kapena malangizo amene mukufufuza. Kumbukirani kuti mukufufuza “chuma chobisika” ndipo pangafunike nthawi ndiponso khama.

N’zoona kuti pali nkhani zina ndiponso malemba ena zimene sizinafotokozedwe mwachindunji. Zingathekenso kuti tinafotokoza lemba linalake, koma mwina sitinalifotokoze mogwirizana ndi funso limene inuyo muli nalo mmaganizo. Palinso nkhani zina za m’Baibulo zimene sitingazimvetse bwinobwino chifukwa chakuti mfundo zina sizinatchulidwe mwachindunji. Choncho sitingapeze yankho lachindunji la funso lililonse limene tingakhale nalo. Izi zikachitika tiyenera kupewa kufalitsa nkhani zimene sitingapeze yankho lake. Nkhani zoterozo “zimangoyambitsa mafunso ndipo siziphunzitsa anthu chilichonse chochokera kwa Mulungu chokhudza chikhulupiriro.” (1 Tim. 1:4; 2 Tim. 2:23; Tito 3:9) Dziwani kuti ofesi ya nthambi kapena likulu la mboni za Yehova padziko lonse silingapereke mayankho pa mafunso amene mabuku athu sanafotokozepo chilichonse. Tiyenera kudziwa kuti Baibulo lili ndi mfundo zokwanira zotitsogolera pa moyo wathu koma silifotokoza zinthu zina n’cholinga choti tizikhulupirira kwambiri Mulungu yemwe ndi Mlembi wake.​—Werengani buku lakuti Yandikirani kwa Yehova tsamba 185 mpaka 187.

Nanga bwanji ngati mwayesetsa kufufuza nkhani zokhudza vuto lanulo koma simukupezabe mfundo zokuthandizani? Mungachite bwino kukambirana ndi Mkhristu wina wodziwa bwino choonadi mwina mkulu. Iwo akhala akuphunzira choonadi kwanthawi ndithu ndipo amadziwa bwino zochitika pa moyo wa Akhristu. Musaiwalenso kupemphera kwa Yehova za vuto lanu ndipo muzimupempha kuti akupatseni mzimu woyera kuti mumvetse zinthu. Tikutero chifukwa chakuti ‘Yehova amapereka nzeru ndi kuzindikira.’​—Miy. 2:6; Luka 11:13.