Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khulupirirani Yehova, “Mulungu Amene Amatitonthoza M’njira Iliyonse”

Khulupirirani Yehova, “Mulungu Amene Amatitonthoza M’njira Iliyonse”

 Khulupirirani Yehova, “Mulungu Amene Amatitonthoza M’njira Iliyonse”

“Atamandike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.”​—2 AKOR. 1:3.

1. Kodi n’chiyani chimene munthu wina aliyense amafuna?

MUNTHU akangobadwa, amafuna kutonthozedwa. Mwana amalira kuti anthu adziwe kuti akufuna kusamaliridwa. Mwina amalira chifukwa chakuti akufuna kunyamulidwa kapena kuyamwa. Ngakhale munthu wamkulu amafunanso kutonthozedwa. Kwenikweni izi zimafunika tikakhala pa mavuto.

2. Kodi Yehova akuwalonjeza chiyani anthu omwe amamukhulupirira?

2 Nthawi zina anzathu ndi achibale athu angatitonthoze tikakumana ndi mavuto. Koma nthawi zina zinthu zimene zimativutitsa maganizo zimakhala zoti anthu anzathu sangakwanitse kutithandiza. Ndi Yehova yekha amene angatitonthoze pa vuto lililonse limene tingakumane nalo. Mawu ake amatitsimikizira kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.” (Sal. 145:18, 19) Amatitsimikiziranso kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.” (Sal. 34:15) Koma kuti Mulungu atithandize ndiponso kutitonthoza, tiyenera kumukhulupirira. Wamasalimo Davide anasonyeza zimenezi pamene anaimba kuti: “Yehova adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo kwa aliyense woponderezedwa, adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo m’nthawi za masautso. Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani, pakuti simudzasiya ndithu anthu okufunafunani, inu Yehova.”​—Sal. 9:9, 10.

3. Kodi Yesu anapereka fanizo lotani pofuna kuti timvetse mmene Yehova amakondera anthu ake?

3 Yehova amaona kuti anthu amene amamulambira ndi a mtengo wapatali. Yesu anafotokoza bwino zimenezi pamene anati: “Mpheta zisanu amazigulitsa makobidi awiri ochepa mphamvu, si choncho kodi? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imene imaiwalika kwa Mulungu. Ndipo ngakhale tsitsi lonse la m’mutu mwanu analiwerenga. Musachite mantha. Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” (Luka 12:6, 7) Kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova anauza anthu ake kuti: “Ine ndakukonda ndipo ndidzakukonda mpaka kalekale. N’chifukwa chake ndakukoka mwa kukoma mtima kwanga kosatha.”​—Yer. 31:3.

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malonjezo a Yehova?

4 Kukhulupirira Yehova ndiponso malonjezo ake n’kotonthoza pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto. Choncho tiyenera kukhulupirira Mulungu ngati mmene Yoswa anachitira. Iye ananena kuti: “Pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.” (Yos. 23:14) Ndipotu timadziwa kuti ngati tapanikizika ndi vuto linalake, “Mulungu ndi wokhulupirika” ndipo sadzasiya atumiki ake okhulupirika.​—Werengani 1 Akorinto 10:13.

5. Kodi tingatonthoze bwanji ena?

5 Mtumwi Paulo ananena kuti Yehova ndi  “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” Kutonthoza kumatanthauza kukhazika mtima pansi munthu amene akuda nkhawa kapena amene ali ndi chisoni. Choncho Yehova amakhazika mtima pansi kapena kuchepetsa nkhawa za munthu amene akuvutika maganizo. (Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Palibe munthu kapena chinthu chilichonse chimene chingalepheretse Atate wathu wakumwamba kutonthoza anthu amene amamukonda. Choncho ife timatha kutonthoza ena “m’masautso amtundu uliwonse” chifukwa chakuti “nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.” Izi zikusonyeza kuti Yehova amatha kutonthoza anthu kuposa wina aliyense.

Zimene Zingatithandize Tikakumana ndi Zokhumudwitsa

6. Kodi ndi zinthu ngati ziti zomwe zimachititsa kuti tifune kutonthozedwa?

6 Timafuna kutonthozedwa tikakumana ndi mavuto osiyanasiyana pa moyo wathu. Chimodzi mwa zinthu zimene zimachititsa kuti tikhale achisoni ndi imfa ya munthu amene timamukonda makamaka akakhala mwamuna, mkazi kapena mwana wathu. Munthu amene amasalidwa kapena kudedwa amafunanso kutonthozedwa. Matenda, ukalamba, umphawi, mavuto a m’banja kapena mavuto ena a m’dzikoli zimachititsa kuti anthu azifuna kutonthozedwa.

7. (a) Kodi munthu akakhala pa mavuto amafuna kutonthozedwa chifukwa chiyani? (b) Kodi Yehova amachiritsa bwanji “mtima wosweka ndi wophwanyika”?

7 Tikakumana ndi mavuto timafuna kutonthozedwa chifukwa chakuti timavutika mumtima ndi m’maganizo. Timafookanso mwakuthupi ndiponso mwauzimu. Mwachitsanzo, taganizirani za kuvutika mu mtima. Mawu a Mulungu amatiuza kuti munthu amatha kukhala ndi “mtima wosweka ndi wophwanyika.” (Sal. 51:17) Yehova amatha kuthandiza munthu wotere chifukwa iye “amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.” (Sal. 147:3) Ngakhale zinthu zitafika povuta kwambiri, Mulungu amatha kutonthoza mtima wosweka ngati tipemphera kwa iye ndi chikhulupiriro chonse ndiponso ngati tisunga malamulo ake.​—Werengani 1 Yohane 3:19-22; 5:14, 15.

8. Kodi Yehova angatithandize bwanji tikamavutika maganizo?

8 Chifukwa choti timakumana ndi mavuto ambiri, timafuna kuti titonthozedwe tikamavutika maganizo. Komabe, ndi mphamvu yathu yokha sitingathe kupirira zinthu zoyesa chikhulupiriro chathu. Wamasalimo anaimba kuti: “Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.” (Sal. 94:19) Nayenso Paulo analemba kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Choncho kuwerenga ndi kusinkhasinkha Malemba n’kothandiza kwambiri ngati tikuvutika maganizo.​—2 Tim. 3:15-17.

9. Kodi tingachite chiyani ngati tikudzikayikira kapena kuchita mantha?

9 Nthawi zina tingakhumudwe kwambiri chifukwa cha mmene timadzionera. Mwina tingamakayikire zoti tingakwanitse bwinobwino udindo wa m’Malemba kapena utumiki winawake. Apanso Yehova akhoza kutithandiza komanso kutitonthoza. Mwachitsanzo, pamene Yoswa anapatsidwa udindo wotsogolera Aisiraeli pokamenyana ndi mitundu yamphamvu, Mose anauza anthu kuti: “Limbani mtima ndipo chitani zinthu mwamphamvu. Musawaope kapena kuchita nawo mantha, chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono.” (Deut. 31:6) Mothandizidwa ndi Yehova, Yoswa anatsogolera anthu a Mulungu kulowa m’Dziko Lolonjezedwa ndipo anagonjetsa adani onse. Izi zisanachitike, Mose anaona Mulungu akuwathandiza pa Nyanja Yofiira.​—Eks. 14:13, 14, 29-31.

10. Kodi n’chiyani chingatithandize ngati tafooka mwakuthupi chifukwa cha mavuto?

10 Mavuto ena akhoza kutifoola mwakuthupi. Kudya chakudya chopatsa thanzi, kupuma mokwanira, kuchita masewera olimbitsa thupi komanso kukhala aukhondo zimathandiza kuti munthu akhale ndi thanzi labwino. Kuganizira zinthu zimene Baibulo limatilonjeza, kumathandizanso  kuti tikhale athanzi. Choncho tikakumana ndi mavuto tingachite bwino kukumbukira zimene Paulo anakumana nazo komanso mawu ake olimbikitsa. Iye anati: “Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse, koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira. Timazunzidwa, koma osati mochita kusowa kolowera. Timagwetsedwa pansi, koma sitiwonongedwa.”​—2 Akor. 4:8, 9.

11. Kodi munthu angatani ngati akudwala mwauzimu?

11 Mavuto ena akhoza kutifoola mwauzimu. Pamenepanso, Yehova akhoza kutipulumutsa. Mawu ake amatitsimikizira kuti: “Yehova amachirikiza amene ali pafupi kugwa, ndipo amaweramutsa onse amene awerama chifukwa cha masautso.” (Sal. 145:14) Ngati tikuona kuti tayamba kufooka mwauzimu, ndi bwino kuuza akulu achikhristu kuti atithandize. (Yak. 5:14, 15) Kuganizira nthawi zonse chiyembekezo cha m’Malemba cha moyo wosatha kukhoza kutithandiza kupirira mavuto amene amayesa chikhulupiriro chathu.​—Yoh. 17:3.

Zitsanzo za Anthu Omwe Anatonthozedwa ndi Mulungu

12. Kodi Yehova analimbikitsa bwanji Abulahamu?

12 Wamasalimo anauziridwa kulemba kuti: “Kumbukirani mawu amene [inu Yehova] munandiuza ine mtumiki wanu, mawu amene ndikuwayembekezera malinga ndi lonjezo lanu. Chimenechi ndi chilimbikitso changa mu nsautso yanga, pakuti mawu anu andisungabe wamoyo.” (Sal. 119:49, 50) Masiku ano tili ndi mawu a Yehova olembedwa ndipo m’mawu amenewa muli zitsanzo za anthu omwe anatonthozedwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, Abulahamu anada nkhawa kwambiri atamva kuti Yehova akufuna kuwononga Sodomu ndi Gomora. Munthu wokhulupirikayu anafunsa Mulungu kuti: “Kodi zoona mungawononge olungama pamodzi ndi oipa?” Yehova analimbikitsa Abulahamu pomuuza kuti ngati kutapezeka anthu olungama 50 okha sadzawononga Sodomu. Kenako Abulahamu anafunsanso Yehova maulendo ena asanu kuti: Nanga bwanji atapezeka anthu olungama 45? 40? 30? 20? kapena 10 okha? Pa nthawi yonseyi Yehova ankaleza mtima ndipo mokoma mtima anatsimikizira Abulahamu kuti sadzawononga Sodomu. Ngakhale kuti anthu olungama sanakwane 10, powononga mizindayi Yehova anapulumutsa Loti ndi ana ake aakazi.​—Gen. 18:22-32; 19:15, 16, 26.

13. Kodi Hana anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Yehova?

13 Hana, yemwe anali mkazi wa Elikana ankafunitsitsa kukhala ndi mwana. Koma iye sankabereka ndipo izi zinkamupweteka kwambiri mu mtima. Iye anapemphera kwa Yehova n’kumuuza nkhawa zake ndipo Eli, yemwe anali mkulu wa ansembe, anamuuza kuti: “Mulungu wa Isiraeli  akupatse zimene wam’pempha.” Izi zinalimbikitsa kwambiri Hana moti “sanakhalenso ndi nkhawa.” (1 Sam. 1:8, 17, 18) Hana ankakhulupirira kwambiri Yehova ndipo nkhaniyi anaisiya m’manja mwake. Ngakhale kuti sankadziwa kuti nkhaniyo itha bwanji, iye anapeza mtendere wamumtima. Patapita nthawi, Yehova anayankha pemphero lake. Iye anadzakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna n’kumupatsa dzina lakuti Samueli.​—1 Sam. 1:20.

14. Kodi n’chifukwa chiyani Davide ankafuna kutonthozedwa ndipo anapempha ndani kuti amutonthoze?

14 Munthu wina amene analimbikitsidwa ndi Mulungu ndi Mfumu Davide ya Isiraeli. Yehova “amaona mmene mtima ulili” ndipo pamene ankasankha Davide kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli, ankadziwa kuti anali wodzipereka ndi mtima wonse pa kulambira koona. (1 Sam. 16:7; 2 Sam. 5:10) Koma pa nthawi ina, Davide anachita chigololo ndi Bateseba. Pofuna kuti tchimo lakelo lisadziwike anakonza zoti mwamuna wa Bateseba aphedwe. Davide atazindikira kukula kwa tchimo lake anapemphera kwa Yehova kuti: “Malinga ndi kuchuluka kwa chifundo chanu, fafanizani zolakwa zanga. Mundisambitse bwinobwino ndi kuchotsa cholakwa changa, ndiyeretseni ku tchimo langa. Pakuti zolakwa zanga ndikuzidziwa bwino, ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.” (Sal. 51:1-3) Davide analapa kuchokera pansi pa mtima ndipo Yehova anamukhululukira. Komabe Davide anakumana ndi zotsatira za tchimo lake. (2 Sam. 12:9-12) Ngakhale zinali choncho, mtumiki wa Yehova wodzichepetsayu anatonthozedwa chifukwa cha chifundo cha Yehova.

15. Kodi Yehova analimbikitsa bwanji Yesu atatsala pang’ono kuphedwa?

15 Yesu ali padziko lapansi anakumana ndi mavuto ambirimbiri. Mulungu analola kuti iye akumane ndi mayesero oterewa, ndipo Yesu anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Yesu ankadalira kwambiri Yehova ndipo anasonyeza kuti Iye ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Atatsala pang’ono kuperekedwa ndiponso kuphedwa, Yesu anapemphera kwa Yehova kuti: “Chifuniro chanu chichitike osati changa.” Ndiyeno mngelo anaonekera kwa Yesu n’kumulimbikitsa. (Luka 22:42, 43) Choncho tingati Yehova analimbikitsa, kutonthoza ndiponso kuthandiza Yesu pa nthawi yoyenera.

16. Kodi Mulungu angatithandize bwanji pamene moyo wathu uli pangozi chifukwa cha chikhulupiriro chathu?

16 Ngati moyo wathu uli pa ngozi chifukwa cha chikhulupiriro chathu, Yehova adzatithandiza kuti tikhalebe ndi mtima wosagawanika. Kuwonjezera pamenepo, timatonthozedwa ndi chiyembekezo chakuti akufa adzauka. Ndipotu timayembekezera mwachidwi nthawi imene imfa nayonso, monga mdani womalizira, “idzawonongedwa.” (1 Akor. 15:26) N’zosatheka kuti Yehova aiwale atumiki ake okhulupirika amene anamwalira. Iye adzawaukitsa limodzi ndi anthu enanso. (Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15) Kukhulupirira kuti Yehova adzaukitsa anthu akufa kumatitonthoza komanso kutipatsa chiyembekezo pamene tikuzunzidwa.

17. Kodi Yehova angatitonthoze bwanji munthu amene timamukonda akamwalira?

17 N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti anthu amene timawakonda, omwe panopa ali m’manda a anthu onse adzauka m’dziko latsopano lopanda mavuto amene alipowa. Ndipo zidzakhala zosangalatsa pamene “khamu lalikulu” la atumiki a Yehova amene adzapulumuke mapeto a dongosolo lino azidzalandira anthu oukitsidwawa padziko lapansi.​—Chiv. 7:9, 10.

Tili M’manja mwa Mulungu Amene Adzakhalapo Mpaka Kalekale

18, 19. Kodi Mulungu amathandiza bwanji atumiki ake akamazunzidwa?

18 M’nyimbo ina yolimbikitsa ndiponso yogwira  mtima, Mose anatsimikizira Aisiraeli kuti: “Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo, ndipo iwe uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale.” (Deut. 33:27, 28) Pa nthawi ina, mneneri Samueli anauzanso Aisiraeli kuti: “Musapatuke n’kusiya kutsatira Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse. . . . Chifukwa cha dzina lake lalikulu, Yehova sadzasiya anthu ake.” (1 Sam. 12:20-22) Ngati timamatira Yehova ndiponso kulambira koona, iye sadzatisiya. Iye adzatilimbikitsa pa nthawi imene tikufunika thandizo.

19 Kunena zoona, Mulungu akuthandiza ndiponso kulimbikitsa anthu ake m’masiku otsiriza ovuta ano. Kwa zaka zoposa 100, abale ndi alongo athu ambirimbiri padziko lonse lapansi akhala akuzunzidwa ndiponso kutsekeredwa m’ndende chifukwa chotumikira Yehova. Zimene akumana nazo zimasonyeza kuti Yehova amalimbikitsadi atumiki ake. Mwachitsanzo, m’bale wina analamulidwa kuti akhale m’ndende zaka 23 kudziko limene linkatchedwa Soviet Union. Ngakhale zinali choncho, njira inkapezeka yoti alandire chakudya chauzimu moti ankalimbikitsidwa ndiponso kutonthozedwa. Iye anati: “Pa zaka zonsezi, ndinaphunzira kudalira Yehova ndipo iye ankandilimbikitsa kwambiri.”​—Werengani 1 Petulo 5:6, 7.

20. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti Yehova sadzatisiya?

20 Kaya tikumane ndi zotani, tingachite bwino kukumbukira mawu olimbikitsa a wamasalimo akuti: “Yehova sadzataya anthu ake.” (Sal. 94:14) Ngakhale kuti aliyense amafuna kutonthozedwa, tonsefe tili ndi mwayi wotonthoza ena. M’nkhani yotsatira tiona kuti tili ndi mwayi wotonthoza anthu amene akulira m’dziko loipali.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingachititse kuti tifune kutonthozedwa?

• Kodi Yehova amatonthoza bwanji atumiki ake?

• Ngati moyo wathu uli pa ngozi chifukwa cha chikhulupiriro chathu, kodi n’chiyani chingatilimbikitse?

[Mafunso]

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 25]

MALEMBA AMENE ANGATITHANDIZE . . .

tikamavutika mu mtima Sal. 147:3; 1 Yoh. 3:19-22; 5:14, 15

tikamavutika maganizo Sal. 94:19; Afil. 4:6, 7

tikamachita mantha chifukwa cha mmene timadzionera Eks. 14:13, 14; Deut. 31:6

tikafooka mwakuthupi 2 Akor. 4:8, 9

tikafooka mwauzimu Sal. 145:14; Yak. 5:14, 15