Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumadziwika Ndi Yehova?

Kodi Mumadziwika Ndi Yehova?

 Kodi Mumadziwika Ndi Yehova?

“Yehova amadziwa anthu ake.”​—2 TIM. 2:19.

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chinali chinthu chofunika kwambiri kwa Yesu? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

TSIKU lina, Mfarisi wina anapita kwa Yesu ndi kum’funsa kuti: “Kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?” Yesu anamuyankha kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mat. 22:35-37) Yesu ankakonda kwambiri Atate wake wakumwamba ndipo ankachitadi zimene ananenazi. Zimene iye ankachita pa moyo wake zinkasonyeza kuti ankafunitsitsa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. N’chifukwa chake Yesu atatsala pang’ono kufa ananena kuti anali wokhulupirika kwa Mulungu. Iye anati: “Ndasunga malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.”​—Yoh. 15:10.

2 Anthu ambiri masiku ano amanena kuti amakonda Mulungu. Ifenso timanena zimenezi. Koma ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amandidziwa? Kodi Yehova amandiona bwanji? Kodi amaona kuti ndine wakedi?’ (2 Tim. 2:19) Zingakhale zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti tikhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mfumu ya chilengedwe chonse.

3. N’chifukwa chiyani anthu ena amakayikira zoti amadziwika ndi Yehova, ndipo angachite chiyani kuti asamaganize choncho?

3 Komabe anthu ena amene amakonda Yehova zimawavuta kukhulupirira kuti Iye amawaona kuti ndi anthu amtengo wapatali. Anthu ambiri amadziona kuti ndi achabechabe choncho amakayikira zoti angakhale anthu a Yehova. N’zosangalatsa kudziwa kuti Mulungu sationa choncho. (1 Sam. 16:7) Mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Ngati munthu akukonda Mulungu, ameneyo amadziwika kwa Mulungu.” (1 Akor. 8:3) Kuti munthu adziwike ndi Mulungu, choyamba ayenera kukonda Mulunguyo. Taganizirani izi: N’chifukwa chiyani mukuwerenga magaziniyi? N’chifukwa chiyani mukuyesetsa kutumikira Yehova ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, nzeru zanu zonse ndi mphamvu zanu zonse? Ngati munadzipereka kwa Mulungu ndi kubatizidwa, kodi n’chiyani chinakuchititsani zimenezi? Baibulo limanena kuti Yehova amene amaona mu mtima ndi amene amakoka anthu amene amawakonda. (Werengani Hagai 2:7; Yohane 6:44.) Choncho dziwani kuti mukutumikira Yehova chifukwa choti anakukokani. Iye sadzasiya anthu amene anawakoka ngati anthuwo angapitirizebe kukhala okhulupirika. Mulungu amawaona kuti ndi anthu amtengo wapatali komanso amawakonda kwambiri.​—Sal. 94:14.

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kukhala anthu odziwika ndi Mulungu?

4 Popeza Yehova watikoka, tiyenera kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingachititse kuti Mulungu apitirize kutikonda. (Werengani Yuda 20, 21.) Pajatu Baibulo limanena kuti n’zotheka kutengeka pang’onopang’ono kapena kuchoka kwa Mulungu. (Aheb. 2:1; 3:12, 13) Mwachitsanzo, Paulo asananene mfundo ya pa 2 Timoteyo 2:19, ananena za Hemenayo ndi Fileto. Anthu awiri amenewa ayenera kuti anali anthu a Yehova koma kenako anasiya choonadi. (2 Tim. 2:16-18) Kumbukirani kuti panali anthu ena m’mipingo ya ku Galatiya amene ankadziwika ndi Mulungu koma kenako anadzachoka m’kuwala. (Agal. 4:9) Tiyeni nthawi zonse tizikumbukira kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri ndipo sitiyenera kuuona mopepuka.

5. (a) Kodi ndi makhalidwe ati amene Mulungu amafuna kuti tikhale nawo? (b) Kodi tikambirana zitsanzo ziti?

5 Pali makhalidwe ena amene Yehova amawaona kuti ndi ofunika kwambiri. (Sal. 15:1-5;  1 Pet. 3:4) M’mbuyomu, anthu amene ankadziwika ndi Mulungu ankakhala ndi chikhulupiriro ndiponso anali odzichepetsa. Tiyeni tikambirane zitsanzo za anthu awiri kuti tione mmene makhalidwe amenewa anawathandizira kukhala amtengo wapatali pamaso pa Yehova. Tikambirananso za munthu wina amene ankaganiza kuti akudziwidwa ndi Mulungu koma Yehova anamukana chifukwa cha kudzikuza. Tiphunzira zinthu zofunika kwambiri pa zitsanzo zimenezi.

Tate wa Onse Okhala ndi Chikhulupiriro

6. (a) Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira malonjezo a Yehova? (b) Kodi Abulahamu anali wodziwika bwanji ndi Yehova?

6 Abulahamu “anakhulupirira mwa Yehova.” Ndipotu iye amatchedwa “tate wa onse osadulidwa okhala ndi chikhulupiriro.” (Gen. 15:6; Aroma 4:11) Mwa chikhulupiriro, Abulahamu anasiya nyumba yake, mabwenzi ake ndiponso chuma chake n’kupita kudziko lina la kutali. (Gen. 12:1-4; Aheb. 11:8-10) Abulahamu anapitirizabe kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Umboni wake ndi wakuti patapita zaka zambiri, iye anamvera mawu a Yehova oti apereke nsembe mwana wake. Kumvera kokhako kunali “ngati wapereka kale Isaki nsembe.” (Aheb. 11:17-19) Abulahamu anasonyeza kuti ankakhulupirira malonjezo a Yehova ndipo Mulunguyo ankaona kuti iye ndi munthu wamtengo wapatali. Izi zikusonyeza kuti Abulahamu ankadziwidwadi ndi Mulungu. (Werengani Genesis 18:19.) Sikuti Yehova ankangodziwa kuti Abulahamu aliko, koma ankadziwa kuti iye ndi bwenzi lake.​—Yak. 2:22, 23.

7. Kodi Abulahamu ankadziwa zotani zokhudza malonjezo a Yehova ndipo anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro?

7 N’zochititsa chidwi kuti Abulahamu sanalandire cholowa cha dziko limene Mulungu anamulonjeza pa nthawi imene anali moyo. Iye sanaonenso kukwaniritsidwa kwa mawu oti ‘mbewu yake idzakhala ngati nyenyezi zakumwamba, monganso mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.’ (Gen. 22:17, 18) Ngakhale kuti malonjezo amenewa sanakwaniritsidwe pa nthawi imene anali moyo, Abulahamu ankakhulupirirabe kwambiri Yehova. Iye ankadziwa kuti Mulungu akalankhula zimakhala ngati wachita kale. Zoonadi, Abulahamu anakhala ndi moyo mogwirizana ndi chikhulupiriro chake. (Werengani Aheberi 11:13.) Kodi Yehova amationa kuti tili ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Abulahamu?

Kuyembekezera Yehova Ndi Chizindikiro Chakuti Tili ndi Chikhulupiriro

8. Kodi ndi zinthu ziti zimene ambiri mwachibadwa amalakalaka?

8 Pali zinthu zina zimene timalakalaka pa moyo wathu. Timafuna titakwatira kapena kukwatiwa, kukhala ndi ana kapena kukhala ndi thanzi labwino. Ndipo palibe vuto kulakalaka zinthu ngati zimenezi. Komabe kwa anthu  ambiri zinthu zina zimene amalakalaka sizichitika. Zimene timachita ngati zolakalaka zathu sizikuchitika n’zimene zimasonyeza kuti chikhulupiriro chathu ndi cholimba kapena ayi.

9, 10. (a) Kodi anthu ena achita chiyani kuti apeze zimene akufuna pa moyo wawo? (b) Kodi mumamva bwanji mukaganizira za mmene Mulungu adzakwaniritsire malonjezo ake?

9 Kungakhale kupanda nzeru ngati Mkhristu atanyalanyaza malangizo a Mulungu pofuna kukwaniritsa zimene akulakalaka. Izi zikhoza kuwononga moyo wake wauzimu. Mwachitsanzo, anthu ena amafuna chithandizo cha mankhwala chosemphana ndi malangizo a Yehova. Ena amayamba ntchito imene imawachititsa kuti asiye banja lawo n’kupita kutali kapena ntchito imene imawalepheretsa kusonkhana. Ena amayamba chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira. Kodi tinganene kuti Mkhristu amene wachita zimenezi amafunadi kudziwidwa ndi Yehova? Kodi Yehova akanamva bwanji Abulahamu akanayamba kuona kuti zimene Mulungu anamulonjeza zikuchedwa? Chikanachitika n’chiyani ngati Abulahamu akanangochita za m’mutu mwake mwina n’kuyamba moyo wofuna kukhazikikanso ndiponso kuchita zinthu zoti atchuke m’malo moyembekezera Yehova? (Yerekezerani ndi Genesis 11:4.) Kodi akanadziwikabe ndi Yehova?

10 Kodi inuyo mumalakalaka zinthu ziti? Kodi chikhulupiriro chanu n’cholimba moti mungayembekeze Yehova amene amalonjeza kukwaniritsa zokhumba zanu? (Sal. 145:16) Mofanana ndi Abulahamu, zinthu zina zimene Mulungu watilonjeza sizingachitike pa nthawi imene tikuganizira. Komabe Yehova amasangalala akaona kuti tili ndi chikhulupiriro ngati cha Abulahamu ndipo tikuchita zinthu mogwirizana ndi chikhulupirirocho. Kuchita zimenezi kungatithandize kwambiri.​—Aheb. 11:6.

Chitsanzo cha Kudzichepetsa Ndiponso cha Kudzikuza

11. Kodi Kora anali ndi mwayi wochita zinthu ziti potumikira Mulungu ndipo zimenezi zikusonyeza kuti ankamuona bwanji Mulungu?

11 Tikambirana zitsanzo za anthu awiri omwe anachita zinthu mosiyana kwambiri pa nkhani ya kulemekeza zimene Yehova anasankha kuchita. Anthu amenewa ndi Mose ndi Kora. Zimene anachita zikusonyeza mmene Yehova amationera tikamalemekeza kapena kupeputsa zimene wasankha. Kora anali wa m’banja la Kohati m’fuko la Levi ndipo anali ndi maudindo ambirimbiri. Iye anaona Aisiraeli akupulumutsidwa pa Nyanja Yofiira, ndipo anathandiza pamene Yehova ankapereka chiweruzo kwa Aisiraeli osamvera paphiri la Sinai. Iye anagwiranso ntchito yonyamula likasa la pangano. (Eks. 32:26-29; Num. 3:30, 31) Zikuoneka kuti kwa zaka zambiri, Kora anali munthu wokhulupirika kwa Yehova ndiponso Aisiraeli ambiri mumsasa anali kumulemekeza.

12. Malinga ndi chithunzi cha patsamba 28, kodi kudzikuza kwa Kora kunawononga bwanji ubwenzi wake ndi Mulungu?

12 Koma ali pa ulendo wopita ku Dziko Lolonjezedwa, Kora anayamba kuona kuti njira imene Yehova ankagwiritsa ntchito potsogolera Aisiraeli inali yolakwika. Ndiyeno amuna 250 anagwirizana naye poganiza kuti akhoza kusintha zinthu. Kora ndi anzakewo ayenera kuti ankaganiza kuti ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Iwo anauza Mose kuti: “Tatopa nanu tsopano! Khamu lonseli ndi loyera, ndipo Yehova ali pakati pawo.” (Num. 16:1-3) Apa n’zoonekeratu kuti anthuwa anali odzidalira kwambiri ndiponso odzikuza kwabasi. Mose anawauza kuti: “Yehova aonetsa amene ali wake.” (Werengani Numeri 16:5.) Madzulo a tsiku lotsatira, Kora ndi anzake amene anapanduka nawo anaphedwa.​—Num. 16:31-35.

13, 14. Kodi Mose anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa?

13 Mosiyana ndi Kora, Mose anali “munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” (Num. 12:3) Iye anaonetsa kuti anali wofatsa ndiponso wodzichepetsa potsatira malangizo a Yehova nthawi zonse. (Eks. 7:6; 40:16) M’Baibulo, palibe paliponse pamene timawerenga posonyeza kuti Mose ankakayikira mmene Yehova amayendetsera zinthu, kapena kunyansidwa ndi kutsatira malangizo  a Yehova. Mwachitsanzo, Yehova analamula Mose kuti apange chihema chopatulika. Anamufotokozera china chilichonse kuphatikizapo zinthu zing’onozing’ono monga mtundu wa ulusi ndiponso chiwerengero cha zingwe zopota zokolekamo ngowe zogwiritsa ntchito polumikiza nsalu za chihema. (Eks. 26:1-6) Ngati woyang’anira m’gulu la Mulungu amapereka malangizo ambirimbiri zikhoza kukutopetsani. Yehova ndi woyang’ayanira wabwino kwambiri amene amagawira ena zochita ndiponso kukhulupirira atumiki ake. Ngati akupereka malangizo ambirimbiri amachita zimenezo pa zifukwa zomveka. Mutha kuona kuti Mose sanakhumudwe chifukwa chakuti Yehova anapereka malangizo ambirimbiri. Iye sanaganize kuti Yehova akumupeputsa kapena kumuphera ufulu woonetsa luso lake. M’malomwake Mose anaonetsetsa kuti ogwira ntchitowo “anachita zonse” potsatira malangizo amene Mulungu anapereka. (Eks. 39:32) Apatu anasonyeza kudzichepetsa kwambiri. Mose ankadziwa kuti ntchitoyo ndi ya Yehova ndipo iye ankangogwiritsidwa ntchito kuti ntchitoyo itheke.

14 Kudzichepetsa kwa Mose kunaonekeranso patachitika vuto lina limene linakhudza iyeyo. Pa nthawi ina, Mose sanathe kudziletsa ndipo analephera kulemekeza Mulungu pamaso pa anthu ong’ung’udza. Zotsatira zake zinali zakuti Yehova anauza Mose kuti sadzalowetsa anthu m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 20:2-12) Mose ndi m’bale wake Aroni anali atapirira kwa zaka zambiri chifukwa cha kung’ung’udza kwa Aisiraeli. Kulakwa kwa Mose pa nthawiyi, kunachititsa kuti asaone zinthu zimene anakhala akuziyembekezera kwa nthawi yaitali. Kodi zitatero Mose anatani? M’pomveka kuti Mose anakhumudwa koma anavomereza modzichepetsa zimene Yehova anasankha kuchita. Iye ankadziwa kuti Yehova ndi Mulungu wokhulupirika amene sachita chosalungama. (Deut. 3:25-27; 32:4) Masiku ano tikaganizira za Mose timadziwa kuti anali munthu wodziwika ndi Yehova.​—Werengani Ekisodo 33:12, 13.

Kumvera Yehova Kumafuna Kudzichepetsa

15. Kodi tikuphunzira chiyani pa kudzikuza kwa Kora?

15 Ngati timalolera pamene zinthu zasintha mu mpingo wachikhristu, tikhoza kukhala anthu odziwika kwa Yehova. Tingadziwikenso ndi Mulungu ngati timalemekeza kwambiri  anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito kutsogolera mpingo. Kora ndi anzake anawononga ubwenzi wawo ndi Mulungu chifukwa chodzidalira kwambiri, kudzikuza ndiponso kusowa chikhulupiriro. Ngakhale kuti Kora ankaona Mose akusankha zochita tsiku ndi tsiku, zoona zake n’zakuti Yehova ndi amene ankatsogolera mtundu wa Isiraeli. Kora anaiwala zimenezi ndipo sanakhale wokhulupirika kwa anthu amene Mulungu ankawagwiritsa ntchito. Iye akanakhala wanzeru, akanadikira Yehova kuti amuthandize kumvetsa zinthu kapena kuti asinthe zinthu ngati panafunika kutero. Ngakhale kuti Kora anali mtumiki wokhulupirika, iye anawononga mbiri yake chifukwa cha kudzikuza.

16. Kodi kutsanzira kudzichepetsa kwa Mose kungatithandize bwanji kuti tidziwike kwa Yehova?

16 Nkhani imeneyi ndi chenjezo kwa akulu ndi anthu ena onse mu mpingo masiku ano. Kudzichepetsa n’kofunika kwambiri kuti munthu ayembekezere Yehova ndiponso kuti atsatire malangizo amene oyang’anira amapereka. Kodi timasonyeza kuti ndife odzichepetsa ndiponso ofatsa ngati Mose? Kodi timalemekeza anthu amene akutsogolera ndiponso kugonjera malangizo amene timalandira? Kodi timaugwira mtima tikakhumudwitsidwa? Ngati timatero tidzakhala anthu odziwika ndiponso ovomerezeka pamaso pa Yehova. Iye adzatikonda kwambiri chifukwa cha kudzichepetsa ndiponso kugonjera kwathu.

Yehova Amadziwa Anthu Ake

17, 18. N’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe anthu odziwika ndi Yehova?

17 Kuganizira za anthu amene anakokedwa ndiponso kudziwidwa ndi Yehova n’kothandiza kwambiri. Abulahamu ndi Mose anali anthu opanda ungwiro ndipo ankalakwitsa zina ndi zina ngati mmene timachitira ifeyo. Koma anali anthu odziwidwa ndi Yehova ndipo iye ankawaona kuti ndi anthu ake. Koma chitsanzo cha Kora chikusonyeza kuti n’zotheka kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova amandiona bwanji? Kodi ndikuphunzira chiyani pa zitsanzo za m’Baibulo zimenezi?’

18 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amaona atumiki ake okhulupirika amene wawakoka kukhala anthu ake. Pitirizani kukhala ndi makhalidwe monga chikhulupiriro ndi kudzichepetsa. Mukatero mudzakhala anthu amtengo wapatali kwa Mulungu wathu yemwe ndi wabwino kwambiri. Ndi mwayi wosaneneka kukhala anthu odziwidwa ndi Yehova. Anthu amene ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova amasangalala masiku ano ndipo adzadalitsidwa kwambiri m’tsogolo.​—Sal. 37:18.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi kudziwidwa ndi Yehova kumatanthauza chiyani?

• Kodi mungatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Abulahamu?

• Kodi tikuphunzira chiyani kwa Kora ndi Mose?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi timakhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake onse ngati mmene Abulahamu anachitira?

[Chithunzi patsamba 28]

Kora sanali wodzichepetsa ndipo sankafuna kumvera malangizo

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi Yehova amakudziwani kuti mumatsatira malangizo modzichepetsa?