Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi

Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi

 Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi

NDI MWAYI waukulu kutumikira mu mpingo monga mkulu. Ngakhale zili choncho Mawu a Mulungu amanena kuti akulu amakumana ndi mavuto. Nthawi zina amafunika kusamalira milandu ndipo amayenera ‘kuweruzira Yehova.’ (2 Mbiri 19:6) Komanso, nthawi zina woyang’anira amapatsidwa ntchito imene akuona kuti sangakwanitse kuchita, monga mmene zinalili ndi Mose yemwe anadandaulira Yehova modzichepetsa kuti, “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao?”​—Eks. 3:11.

Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera pouzira Malemba. Mzimu woyera womwewo ndi umene umatsogolera poika akulu mu mpingo. M’Malemba ouziridwawo muli zitsanzo za oyang’anira amene anakumana ndi mavuto n’kuthana nawo bwinobwino. Pinihasi anali mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni. Iye anali mu mzera wodzakhala mkulu wa ansembe. Zinthu zitatu zimene zinachitika pa moyo wake zimasonyeza kuti akulu masiku ano ayenera kukhala olimba mtima, omvetsa zinthu ndiponso odalira Yehova pakabuka mavuto.

“Nthawi Yomweyo Ananyamuka”

Pinihasi anali wachinyamata pamene Aisiraeli anamanga misasa kuchigwa cha Mowabu. Baibulo limati: “Iwo anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu. . . . Kumeneko, Aisiraeliwo ankadya ndi kugwadira milungu ya Amowabuwo.” (Num. 25:1, 2) Yehova analanga anthu ochimwawo ndi mliri wakupha. Kodi mukuganiza kuti Pinihasi anamva bwanji atamva za machimowo ndiponso mliri womwe unawagwera?

Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Kenako anthuwo anangoona mwamuna wina wachiisiraeli akubwera ndi mkazi wachimidiyani. Anali kubwera naye kufupi ndi abale ake, pamaso pa Mose ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Isiraeli. Pa nthawiyi n’kuti Aisiraeliwo akulira pakhomo la chihema chokumanako.” (Num. 25:6) Pamene izi zinkachitika, n’kuti Pinihasi ali wachinyamata. Komanso, Mwisiraeli amene amachita zonyansazi ankatsogolera kulambira koona pakati pa anthu a Mulungu. (Num. 25:14) Kodi Pinihasi anachita chiyani?

Pinihasi ankaopa Yehova osati anthu. Atangoona anthu awiriwo, nthawi yomweyo anatenga mkondo n’kuwatsatira m’hema n’kuwabaya onsewo pamodzi. Kodi Yehova anamva bwanji Pinihasi atachita zinthu molimba mtima ndiponso mosazengereza? Nthawi yomweyo Yehova analetsa mliriwo komanso anachita naye pangano lakuti iye ndi mbadwa zake adzakhala ansembe “mpaka kalekale.”​—Num. 25:7-13.

Masiku ano akulu sachita chiwawa. Koma mofanana ndi Pinihasi iwo ayenera kukhala okonzeka kuchita zinthu mosazengereza ndiponso molimba mtima. Mwachitsanzo, Guilherme atangotumikira monga mkulu kwa miyezi yowerengeka, anauzidwa kuti akhale nawo m’komiti yachiweruzo. Nkhani yake inali yokhudza mkulu amene anamuthandiza ali mwana. Guilherme ananena kuti: “Ndinkaona kuti sindiyenera kuweruza nawo nkhani imeneyi. Nkhani imeneyi inkandisowetsa tulo. Nthawi zonse ndinkangoganizira mmene  ndingasamalirire nkhaniyi mosakondera n’kumaiona mmene Yehova akuionera. Ndinapemphera kwa Yehova kwa masiku angapo ndiponso kufufuza m’mabuku ofotokoza Baibulo.” Zimenezi zinamuthandiza kuti akhale wolimba mtima n’kusamalira bwinobwino nkhani yovuta kwambiri imeneyi ndiponso kuthandiza m’bale wake amene anachimwa.​—1 Tim. 4:11, 12.

Akulu akamachita zinthu molimba mtima ndiponso mosazengereza pakabuka mavuto mu mpingo, amakhala chitsanzo chosonyeza chikhulupiriro ndiponso kukhulupirika. Komanso, Mkhristu aliyense ayenera kukhala wolimba mtima kuulula machimo akuluakulu amene angawadziwe. Pamafunikanso kukhulupirika kuti munthu asiye kucheza ndi mnzake kapena wachibale wake amene wachotsedwa mu mpingo.​—1 Akor. 5:11-13.

Kumvetsa Zinthu Kunathandiza Kupewa Mavuto

Sikuti Pinihasi anangochita zinthuzo mwachibwanabwana asanaganize bwinobwino. Taganizani mmene anasonyezera kuti ndi womvetsa zinthu. Atamva za nkhani inayake, iye anachita zinthu mosamala ndiponso mwanzeru. Mafuko a Rubeni ndi Gadi ndiponso hafu ya fuko la Manase anamanga guwa pafupi ndi mtsinje wa Yorodano. Aisiraeli ena atamva zimenezi anaganiza kuti guwalo ndi la milungu yonyenga ndipo anakonza zokamenyana nawo.​—Yos. 22:11, 12.

Kodi Pinihasi anatani? Iye ndi atsogoleri ena achiisiraeli anakambirana bwinobwino nkhaniyo ndi anthu amene anamanga guwalo. Mafuko amene ankaimbidwa mlanduwo anafotokoza chifukwa chimene anamangira guwalo kuti chinali ‘kutumikira Yehova.’ Chifukwa cha zimenezi anapewa mavuto.​—Yos. 22:13-34.

Ngati Mkhristu atamva Mkhristu mnzake akunenezedwa, angachite bwino kutsanzira Pinihasi. Kumvetsa zinthu kungatithandize kuti tisakwiyire mnzathuyo kapena kuthirirapo ndemanga pa zinthu zimene tilibe nazo umboni.​—Miy. 19:11.

Kodi kumvetsa zinthu kungathandize bwanji akulu kuti achite zinthu ngati Pinihasi? Jaime amene watumikira monga mkulu kwa zaka zoposa 10 ananena kuti: “Wofalitsa akayamba kulankhula mavuto amene ali nawo ndi munthu wina, nthawi yomweyo ndimapemphera kuti Yehova andithandize kuti ndisaikire kumbuyo aliyense koma ndithandize wodandaulayo pogwiritsa ntchito Malemba. Nthawi ina mlongo wina anandiuza za vuto limene anali nalo ndi m’bale yemwe anali mkulu mu mpingo wina. Popeza m’baleyo anali mnzanga, zinali zosavuta kuti ndikangolankhula naye. M’malomwake ndinakambirana ndi mlongoyo mfundo zingapo za m’Baibulo. Iye anavomereza kuti choyamba akakambirane yekha ndi m’baleyo. (Mat. 5:23, 24) Koma ulendo woyamba sanagwirizane. Choncho ndinamulimbikitsa kuganizira mfundo zina za m’Malemba. Mlongoyo anaganiza zopemphera kuti aiwale nkhaniyo komanso kukhululukira m’baleyo.”

Kodi zotsatira zake zinali zotani? Jaime anati:  “Patapita miyezi ingapo, mlongoyo anabweranso. Anafotokoza kuti patapita nthawi m’bale uja anamva chisoni ndi zimene analankhula. Anakonza zoti alowere limodzi mu utumiki ndipo anamuthokoza kwambiri chifukwa cha makhalidwe ake abwino. Vutolo linathera pomwepo. Kodi ndikanakhala kuti ndailowerera nkhani imeneyi n’kuikira kumbuyo wina, ikanatha bwino chonchi?” Baibulo limatilangiza kuti: “Usamapite kukazenga mlandu mofulumira.” (Miy. 25:8) Akulu omvetsa zinthu amalimbikitsa Akhristu amene asemphana maganizo kuti azigwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba n’cholinga choti ayambirenso kukhala mwa mtendere.

Anapemphera Kaye kwa Yehova

Pinihasi anali ndi mwayi wotumikira monga wansembe wa anthu osankhidwa a Mulungu. Monga taonera, iye anali wolimba mtima kwambiri komanso womvetsa zinthu kuyambira ali wachinyamata. Komabe iye anathana bwinobwino ndi mavuto amenewo chifukwa choti ankadalira Yehova.

Amuna a ku Gibeya, a fuko la Benjamini atagwirira ndi kupha mdzakazi wa Mlevi wina, mafuko ena ananyamuka kukamenyana ndi Abenjamini. (Ower. 20:1-11) Iwo anapemphera kwa Yehova asanakamenye nkhondo imeneyi koma anagonjetsedwa maulendo awiri. (Ower. 20:14-25) Kodi umenewu unali umboni woti Mulungu sanamve mapemphero awo? Kodi Yehova anasangalala kuona anthu amenewa akupita kukabwezera chiwembucho?

Mosazengereza, Pinihasi yemwe pa nthawiyi anali mkulu wa ansembe, anafunsa Yehova kuti: “Kodi ndipitenso kukamenyana ndi ana a m’bale wanga Benjamini kapena ndisapite?” Poyankha pempheroli Yehova anapereka Abenjamini m’manja mwawo moti mzinda wonse wa Gibeya unatenthedwa.​—Ower. 20:27-48.

Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Mavuto ena mu mpingo amapitirirabe ngakhale kuti akulu mu mpingo akuchitapo kanthu komanso kupemphera kwa Mulungu kuti awathandize. Zimenezi zikachitika, akulu angachite bwino kukumbukira mawu a Yesu akuti: “Pitirizani kufunafuna [kapena kupemphera], ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.” (Luka 11:9) Ngakhale kuti nthawi zina yankho la pemphero lingachedwe, oyang’anira ayenera kudziwa kuti Yehova adzawayankha pa nthawi yake.

Mwachitsanzo, mpingo wina ku dziko la Ireland unkafuna kumanga Nyumba ya Ufumu koma bwana woyang’anira ntchito ya zomangamanga m’deralo ankakaniza. Iye ankangokaniza malo alionse amene abale ankafuna kumanga. Abalewo anaona kuti mwina amene angawathandize ndi bwana wamkulu amene amayang’anira ntchito ya zomangamanga m’dziko lonselo. Kodi pemphero likanawathandiza ngati mmene zinalili m’masiku a Pinihasi?

M’bale wina yemwe ndi mkulu anati: “Titapemphera komanso kupembedzera kwa Mulungu, tinanyamuka kupita ku likulu la zomangamanga. Ndinauzidwa kuti padutsa masabata angapo kuti ndionane ndi bwana wamkulu wa kumeneko. Koma mwamwayi ndinaonana naye kwa mphindi zisanu. Ataona pulani yathu anatiloleza ndipo bwana yemwe ankakana uja anayamba kutithandiza. Zimenezi zinatithandiza kudziwa mphamvu ya pemphero.” Izi zikusonyezeratu kuti Yehova adzayankha mapemphero ochokera pansi pa mtima omwe akulu amene amamudalira amapereka.

Pinihasi anali ndi udindo waukulu mu Isiraeli wakale koma anathana ndi mavuto bwinobwino chifukwa cha kulimba mtima, kumvetsa zinthu ndiponso kudalira Mulungu. Komanso zimene Pinihasi anachita posamalira mpingo wa Mulungu zinasangalatsa kwambiri Yehova. Patapita zaka 1,000, Ezara anauziridwa kulemba kuti: “Pinihasi mwana wa Eleazara ndiye anali mtsogoleri wawo kalekale, ndipo Yehova anali naye.” (1 Mbiri 9:20) Mawu amenewa ayeneranso kugwira ntchito kwa amene amatsogolera anthu a Mulungu masiku ano komanso Akhristu onse amene amatumikira Mulungu mokhulupirika.