Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumayamikiradi Madalitso Amene Mwalandira?

Kodi Mumayamikiradi Madalitso Amene Mwalandira?

 Kodi Mumayamikiradi Madalitso Amene Mwalandira?

ANA a Isiraeli atangopulumutsidwa mozizwitsa ku ukapolo ku Iguputo, anasangalala kwambiri kukhala ndi ufulu wolambira Yehova. (Eks. 14:29–15:1, 20, 21) Koma pasanapite nthawi yaitali, zinthu zinasintha. Iwo anayamba kudandaula. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa chakuti anayamba kuganizira kwambiri za mavuto amene anali kukumana nawo m’chipululu osati zimene Yehova anali atawachitira. Iwo anauza Mose kuti: “Munatitulutsiranji m’dziko la Iguputo? Kodi mumafuna kuti tidzafere m’chipululu? Kuno chakudya kulibe, madzinso kulibe. Chakudya chonyansachi [mana] chafika potikola.”​—Num. 21:5.

Patapita zaka zambiri, Mfumu Davide ya ku Isiraeli inaimba kuti: “Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha. Mtima wanga ukondwere chifukwa cha chipulumutso chanu. Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandifupa ndi zinthu zabwino.” (Sal. 13:5, 6) Davide sanaiwale kukoma mtima kosatha kumene Yehova anali atamusonyeza. Koma iye ankakonda kuganizira zimene Mulungu anali atamuchitira. (Sal. 103:2) Ifenso Yehova watifupa ndi zinthu zabwino zambiri, ndipo tingachite bwino kuyamikira zimene watichitira. Tsopano, tiyeni tikambirane madalitso ena ochokera kwa Mulungu amene tili nawo masiku ano.

“Ubwenzi Wolimba ndi Yehova”

Wamasalimo anaimba kuti: “Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa.” (Sal. 25:14) Kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndi mwayitu waukulu kwambiri kwa anthu opanda ungwirofe. Koma bwanji ngati tayamba kutanganidwa kwambiri ndi zochita zathu za tsiku ndi tsiku moti n’kumalephera kupemphera? Taganizirani zimene zingachitikire ubwenzi wathu wabwino ndi Yehova. Popeza kuti Yehova ndi bwenzi lathu, amafuna kuti timukhulupirire ndi kumuuza m’pemphero zakukhosi kwathu. Amafuna kuti tizimuuza zimene timaopa, timafuna ndiponso zimene zimatidetsa nkhawa. (Miy. 3:5, 6; Afil.  4:6, 7) Choncho m’pofunika kuganizira mofatsa zimene timanena m’mapemphero athu.

Pamene m’bale wina wachinyamata dzina lake Paul anaganiziranso za mapemphero ake, anaona kuti ayenera kusintha zimene amanena akamapemphera. * Iye ananena kuti: “Ndinali ndi chizolowezi chongonena mawu ofanana nthawi zonse ndikamapemphera kwa Yehova.” Pamene Paul anafufuza nkhani ya pemphero mu mlozera nkhani wa Watch Tower Publications Index, anaona kuti m’Baibulo munalembedwa mapemphero pafupifupi 180. M’mapemphero amenewa atumiki a Yehova akale anatchula za pansi pa mtima pawo. Paul ananena kuti: “Nditaganizira mofatsa mapemphero olembedwa m’Baibulo amenewa, ndinaona kuti ndiyenera kutchula zinthu mwachindunji ndikamapemphera. Zimenezi zandithandiza kuuzadi Yehova zimene zili mumtima mwanga. Tsopano ndimamasuka kwambiri ndikamalankhula ndi Mulungu m’pemphero.”

“Chakudya pa Nthawi Yoyenera”

Mfundo zambiri zoona zimene taphunzira m’Malemba ndi madalitso ena amene Yehova watipatsa. Popeza kuti tili ndi chakudya chauzimu cha mwanaalirenji tikhoza ‘kufuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.’ (Yes. 65:13, 14) Komabe, tiyenera kusamala kuti zinthu zina zisatilepheretse kukonda choonadi. Mwachitsanzo, tikamachita chidwi ndi nkhani zabodza za ampatuko tikhoza kusokonezeka maganizo. Nkhani zimenezi zingatichititse kuti tisaone kufunika kwa “chakudya [chauzimu cha] pa nthawi yoyenera” chimene Yehova amapereka kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”​—Mat. 24:45-47.

M’bale wina dzina lake André, amene anali atatumikira Yehova kwa zaka zambiri, anasocheretsedwa ndi ampatuko. Iye ankaganiza kuti kungoonako pang’ono nkhani za ampatuko pa Intaneti si koopsa. Iye anati: “Poyamba, ndinakopeka ndi mfundo zimene zinkaoneka ngati zoona, zimene ampatukowo ankanena. Ndikaganizira kwambiri zimene ankanena, ndinkaona kuti ndingachite bwino kuchoka m’gulu la Yehova. Koma kenako nditafufuza mfundo zimene ampatukowo amagwiritsa ntchito potsutsa Mboni za Yehova, ndinazindikira kuti aphunzitsi abodzawo ndi ochenjera kwambiri. Zimene iwowo ankanena kuti ndi umboni wawo wosatsutsika zinali zinthu zimene anali kungozipotoza. Choncho ndinaona kuti ndi bwino kuyambiranso kuwerenga mabuku athu ndiponso kupita ku misonkhano. Nditayamba kuchita zimenezi, ndinazindikira kuti pa nthawi imene ndinachoka m’gulu, ndinkadzimana zinthu zambiri.” N’zosangalatsa kwambiri kuti André anabwereranso mumpingo.

“Gulu Lonse la Abale”

Gulu lathu logwirizana la abale achikondi ndi dalitso linanso lochokera kwa Yehova. (Sal. 133:1) N’chifukwa chake mtumwi Petulo analemba kuti: “Kondani gulu lonse la abale.” (1 Pet. 2:17) Popeza kuti tili m’gulu la abale achikhristu, tili ndi abambo, amayi, abale ndiponso alongo auzimu amene amatithandiza mwachikondi.​—Maliko 10:29, 30.

 Ngakhale zili choncho, nthawi zina timavutika kugwirizana ndi abale ndi alongo athu chifukwa cha zinthu zina zimene zimachitika. Mwachitsanzo, n’zosavuta kukwiya chifukwa cha zolakwa za munthu wina kenako n’kumangoona zimene munthuyo amalakwitsa basi. Zimenezi zikachitika, tizikumbukira kuti Yehova amakonda atumiki ake ngakhale kuti amalakwitsa zinthu. Komabe, “tikanena kuti: ‘Tilibe uchimo,’ ndiye kuti tikudzinamiza ndipo mwa ife mulibe choonadi.” (1 Yoh. 1:8) Choncho, tiyeni tiziyesetsa ‘kupitiriza kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.’​—Akol. 3:13.

Mtsikana wina dzina lake Ann anaona kufunika kwa ubwenzi wake ndi abale ndi alongo achikhristu zinthu zitamuvuta. Iye anachita zofanana ndi mwana wolowerera amene Yesu anamutchula mu fanizo lake ndipo anachoka mu mpingo. Koma kenako nzeru zinamubwerera ndipo anayambanso kusonkhana ndi mpingo. (Luka 15:11-24) Kodi Ann anaphunzirapo chiyani pa zimene zinamuchitikirazi? Iye anati: “Pamene ndabwerera m’gulu la Yehova, ndimaona kuti abale ndi alongo onse ndi ofunika kwambiri ngakhale kuti amalakwitsa zina ndi zina. M’mbuyomu ndinkafulumira kuona zolakwa zawo. Koma tsopano sindifuna ngakhale pang’ono kulola chilichonse kusokoneza madalitso amene ndili nawo chifukwa chokhala limodzi ndi Akhristu anzanga. M’dzikoli mulibe chilichonse chimene chingapose paradaiso wathu wauzimu.”

Nthawi Zonse Muziyamikira Madalitso Anu

Chiyembekezo chathu chakuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onse a anthu ndi chamtengo wapatali kwambiri. Titangophunzira kumene za chiyembekezo chimenechi tinkachiyamikira ndi mtima wonse. Tinamva ngati wamalonda amene Yesu anamutchula m’fanizo lake yemwe ‘anakagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo’ kuti akagule “ngale imodzi yamtengo wapatali.” (Mat. 13:45, 46) Yesu sananene kuti patapita nthawi wamalondayo anasiya kuyamikira ngaleyo. Ifenso tiyeni tisasiye kuyamikira chiyembekezo chathu chabwino kwambiri chimene tili nacho.​—1 Ates. 5:8; Aheb. 6:19.

Taganizirani za Jean amene wakhala akutumikira Yehova kwa zaka zoposa 60. Iye anati: “Chimene chandithandiza kuti nthawi zonse ndiziganizira za Ufumu wa Mulungu ndi kuuzako ena za Ufumuwo. Ndikamaona anthu akusangalala kwambiri chifukwa chomvetsa mfundo zokhudza Ufumuwo, inenso ndimalimbikitsidwa. Ndikaona wophunzira Baibulo wanga akusintha chifukwa chophunzira choonadi chokhudza Ufumu, mumtima ndimanena kuti, ‘Ichitu ndi choonadi chamtengo wapatali ndipo ndili ndi mwayi wouzako ena choonadi chimenechi.’”

Tili ndi zifukwa zabwino zoyamikirira madalitso auzimu ambiri amene tili nawo. Ngakhale kuti mwina tikukumana ndi mavuto monga kutsutsidwa, matenda, ukalamba, kuvutika maganizo, imfa ya munthu amene timamukonda ndi mavuto a zachuma, timadziwa kuti mavutowa sadzakhalapo mpaka kalekale. Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dziko lonse lapansi, sitidzangokhala ndi madalitso auzimu okha koma tidzalandiranso madalitso akuthupi. Mavuto onse amene tikupirira masiku ano adzatha mu dongosolo latsopano.​—Chiv. 21:4.

Padakali pano, tiyeni tiziyamikira kwambiri madalitso athu auzimu ndipo tikhalebe ndi mtima ngati umene wamasalimo anali nawo. Iye anaimba kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa, ndipo mumatiganizira. Palibe angafanane ndi inu. Ndikafuna kulankhula ndi kunena za zodabwitsazo, zimachuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.”​—Sal. 40:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mayinawa asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 18]

Akhristu anzathu amatilimbikitsa tikakumana ndi mavuto