Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mzimu Woyera Umatipatsa Mphamvu Yolimbana ndi Vuto Lililonse

Mzimu Woyera Umatipatsa Mphamvu Yolimbana ndi Vuto Lililonse

 Mzimu Woyera Umatipatsa Mphamvu Yolimbana ndi Vuto Lililonse

“Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”​—AFIL. 4:13.

1. N’chifukwa chiyani anthu a Yehova amakumana ndi mavuto ambiri?

ANTHU a Yehova amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mavuto ena amayamba chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu koma ena amayamba chifukwa cha dongosolo limene tikukhalamoli. Ena amabwera chifukwa cha chidani cha pakati pa anthu amene amatumikira Mulungu ndi amene samutumikira. (Gen. 3:15) Kuyambira kalekale, Mulungu wakhala akuthandiza atumiki ake okhulupirika kupirira pozunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Wawathandizanso kupewa kumangotengera zofuna za anzawo komanso kupirira mavuto osiyanasiyana. Mzimu wake woyera ungatipatse mphamvu kuti nafenso tichite zimenezi.

Umatithandiza Tikamazunzidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chathu

2. Kodi cholinga cha anthu amene amazunza anzawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo chimakhala chiyani ndipo kodi amachita motani zimenezi?

2 Anthu ena amazunza anzawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Amachita zimenezi ndi cholinga choti awasiyitse zimene amakhulupirira, zikhulupiriro zawo zisafalikire, kapena kuti  chipembedzo chawo chithe. Nthawi zina anthuwo amachita zimenezi moonetsera koma nthawi zina mwakabisira. Baibulo limayerekezera zochita za Satana ndi za mkango wamphamvu ndiponso njoka ya mamba.​—Werengani Salimo 91:13.

3. Mungafotokoze bwanji chizunzo chobwera ngati mkango wamphamvu ndi chobwera ngati njoka ya mamba?

3 Mofanana ndi mkango wolusa, Satana amaukira mwachindunji olambira oona pogwiritsa ntchito anthu achiwawa, kuwatsekera m’ndende kapena kuletsa chipembedzo chawo. (Sal. 94:20) Nkhani za m’buku la Yearbook, zimafotokoza za kuzunzidwa kwa Mboni za Yehova masiku ano m’njira zosiyanasiyana. M’madera ambiri, atumiki a Mulungu amazunzidwa ndi anthu achiwawa amene nthawi zina amatsogoleredwa ndi akuluakulu achipembedzo kapena andale. Njira zimenezi zili ngati za mkango wamphamvu ndipo zachititsa anthu ena ochepa kusiya kulambira koona. Mofanana ndi njoka ya mamba, Mdyerekezi amachita zinthu mwakabisira pofuna kusokoneza maganizo a anthu n’kuwanyenga kuti azichita zofuna zake. Cholinga chake n’kutifooketsa kapena kutisokoneza mwauzimu. Koma tikhoza kulimbana ndi njira zonsezi ndi mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu.

4, 5. Kodi njira yabwino yokonzekerera chizunzo ndi iti? Perekani chifukwa ndiponso chitsanzo.

4 Kuyesa kuganizira chizunzo chimene tingakumane nacho n’kosathandiza kwenikweni. Tikutero chifukwa chakuti sitingadziwe chizunzo chimene tingakumane nacho m’tsogolo ndipo tikhoza kungodzivutitsa podera nkhawa zinthu zimene mwina sizidzachitika. Komabe pali zinthu zimene tingachite kuti tikonzekere chizunzo. Anthu ambiri amene anatha kupirira pozunzidwa anatero chifukwa chakuti ankaganizira moyo wa anthu otchulidwa m’Malemba amene anakhala okhulupirika. Ankaganiziranso zimene Yesu anaphunzitsa ndiponso chitsanzo chake. Izi zinawathandiza kuti azikonda kwambiri Yehova. Chikondi chimenechi n’chimene chinawathandiza kulimbana ndi mavuto alionse amene anakumana nawo.

5 Taganizirani za alongo athu awiri a ku Malawi. Pofuna kuwakakamiza kuti agule makadi achipani, gulu la anthu olusa linawamenya, kuwavula zovala ndiponso kuwaopseza kuti liwagwiririra. Kenako anthuwo anawanamiza kuti abale ena a ku Beteli agula makadi achipani. Kodi alongowo anatani? Iwo anayankha kuti: “Ife timatumikira Yehova Mulungu yekha. Ndiye ngati abale a ku ofesi ya nthambi agula makadi ife sizikutikhudza. Sitilola ngakhale mutiphe.” Atasonyeza kulimba mtima chonchi, alongowo anamasulidwa.

6, 7. Kodi Yehova amapereka bwanji mphamvu kwa atumiki ake akamazunzidwa?

6 Mtumwi Paulo ananena kuti Akhristu a ku Tesalonika analandira uthenga wa choonadi “ndi chimwemwe cha mzimu woyera,” ngakhale kuti anali “m’masautso ambiri.” (1 Ates. 1:6) Akhristu akale ndiponso a masiku ano amene apirira pozunzidwa amanena kuti pamene chizunzo chinafika poipa kwambiri, iwo anali ndi mtendere wa mumtima womwe ndi chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu. (Agal. 5:22) Mtendere umenewu ndi umene unateteza mitima ndi maganizo awo. Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu yake yogwira ntchito pothandiza atumiki ake kuti apirire mavuto alionse komanso kuti azichita zinthu mwanzeru akakumana ndi mavuto. *

7 Anthu amadabwa kwambiri kuona anthu a Mulungu akukhalabe okhulupirika ngakhale pamene akuzunzidwa mwankhanza. Zimaoneka kuti Mbonizi zili ndi mphamvu yoposa yachibadwa ndipo umu ndi mmene zimakhaliradi. Mtumwi Petulo akutitsimikizira kuti: “Ngati anthu akukunyozani chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala chifukwa zikusonyeza kuti mzimu waulemerero, umene ndi mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.” (1 Pet. 4:14) Kuzunzidwa chifukwa chotsatira mfundo zolungama ndi umboni wakuti Mulungu akusangalala nafe. (Mat. 5:10-12; Yoh. 15:20) N’zolimbikitsa kwambiri kuona kuti Yehova akusangalala nafe.

 Umatithandiza Kuti Tisamangotengera Zofuna za Anzathu

8. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza Yoswa ndi Kalebe kuti asangotengera maganizo a anzawo? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yoswa ndi Kalebe?

8 Pali njira inanso yovuta kuizindikira imene Satana amagwiritsa ntchito potsutsa Akhristu. Njira yake ndi kuwakakamiza kuti azingotengera zofuna za anzawo. Komabe, mzimu wa Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa mzimu wa dzikoli, choncho tikhoza kupirira pamene anthu akutinyoza, kufalitsa mabodza okhudza ifeyo kapena akamayesa kutikakamiza kuti tizitsatira mfundo zimene iwo amayendera. Mwachitsanzo, kodi n’chiyani chinathandiza Yoswa ndi Kalebe kuti asagwirizane ndi maganizo a anthu ena 10 amene anatumidwa kukazonda dziko la Kanani? Mzimu woyera unawathandiza kukhala ndi “mzimu” kapena kuti maganizo osiyana ndi anzawowo.​—Werengani Numeri 13:30; 14:6-10, 24.

9. N’chifukwa chiyani Akhristu sayenera kumangotengera maganizo a anthu ena?

9 Mzimu woyera unathandizanso atumwi a Yesu kuti amvere Mulungu osati anthu amene ankaonedwa ngati aphunzitsi a chipembedzo choona. (Mac. 4:21, 31; 5:29, 32) Anthu ambiri amangotsatira zimene anthu ena akuchita poopa kutsutsidwa kapena kukangana. Koma nthawi zambiri Akhristu oona amayenera kuchita zinthu zosiyana ndi anzawo pofuna kutsatira zimene akudziwa kuti n’zolondola. Iwo saopa kuchita zimenezi chifukwa chakuti amathandizidwa ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. (2 Tim. 1:7) Tiyeni tione nkhani ina imene sitiyenera kungotengera maganizo a ena.

10. Kodi Akhristu ena amakumana ndi vuto lotani?

10 Achinyamata ena amasowa chochita akaona kuti mnzawo wachita zinazake zosemphana ndi Malemba. Iwo amaganiza kuti akauza akulu kuti amuthandize adzakhala osakhulupirika kwa mnzawoyo, choncho amangoona kuti ndi bwino osanenapo kalikonse. Nthawi zina munthu amene wachita zoipayo akhoza kukakamiza anzake kuti asaulule tchimo lakelo. Koma sikuti izi zingachitikire achinyamata okha. Achikulire ena amaopanso kuuza akulu za tchimo limene mnzawo kapena munthu wina wa m’banja lawo wachita. Koma kodi Akhristu oona ayenera kutani izi zikachitika?

11, 12. Kodi tiyenera kutani ngati m’bale kapena mlongo wina akutiuza kuti tisaulule tchimo lake? Perekani chifukwa.

11 Taganizirani izi. Tiyerekeze kuti m’bale wina wachinyamata dzina lake Alex wadziwa zoti mnzake wina mu mpingo dzina lake Steve amakonda kuonera zolaula. Ndiyeno Alex akuuza Steve kuti sakusangalala ndi zimene iye amachita koma Steve sakumvera. Kenako Alex atauza mnzakeyo kuti akauze akulu, Steve akumuuza kuti ngati ali mnzakedi sayenera kuulula za nkhaniyo. Kodi Alex ayenera kuchita mantha poganiza kuti adana ndi mnzakeyo? Mwina akhoza kuganiza kuti akulu sangamukhulupirire ngati Steve atakana tchimo lakelo. Komatu zinthu sizingayendenso bwino ngati Alex angalekerere nkhaniyo. Izi zingachititse kuti Steve asakhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. Alex ayenera kukumbukira kuti “kuopa anthu n’kumene kumatchera msampha,  koma wokhulupirira Yehova adzatetezedwa.” (Miy. 29:25) Ndiyeno kodi Alex angachite chiyani? Iye angapitenso kwa Steve n’kukamufotokozera mokoma mtima za cholakwacho. Koma kuti achite zimenezi angafunike kulimba mtima. N’kutheka kuti akapitanso, Steve akhoza kuvomereza kukambirana za vuto lakeli. Alex ayenera kulimbikitsanso Steve kuti akauze akulu n’kumuuzanso kuti ngati sachita zimenezi pofika nthawi inayake, iyeyo akawauza.​—Lev. 5:1.

12 Ngati mutatsatira zimenezi, mwina mnzanuyo poyamba sangamvetse zimene inu mukuchita pofuna kumuthandiza. Koma pakapita nthawi akhoza kuzindikira kuti mukuchita zimenezi chifukwa chakuti mumamufunira zabwino. Ngati munthu wochimwayo angalandire thandizolo adzakuyamikirani kwambiri chifukwa chakuti munalimba mtima n’kuchita zinthu mokhulupirika. Koma ngati sangamvere zimene inu mukumuuza, kodi munganene kuti ndi munthu woyeneradi kukhala mnzanu? Kuchita zinthu zosangalatsa Yehova, yemwe ndi Mnzathu weniweni, n’kofunika kwambiri. Tikamamuika pa malo oyamba pa moyo wathu, anthu amene amam’konda adzatilemekeza chifukwa cha kukhulupirika kwathu ndipo adzakhala mabwenzi athu enieni. Choncho tisam’patse malo Mdyerekezi mumpingo wachikhristu chifukwa tikatero tidzamvetsa chisoni mzimu woyera wa Yehova. Timachita zinthu mogwirizana ndi mzimu woyera mwa kuyesetsa kuthandiza kuti mpingo wachikhristu ukhalebe woyera.​—Aef. 4:27, 30.

Mzimu Woyera Umatipatsa Mphamvu Yopirira Mavuto a Mtundu Uliwonse

13. Kodi anthu a Yehova amakumana ndi mavuto ati, nanga n’chifukwa chiyani mavuto amenewa akufala kwambiri?

13 Anthufe tikhoza kukumana ndi mavuto osiyanasiyana monga mavuto azachuma, kuchotsedwa ntchito, masoka achilengedwe, imfa ya munthu amene timam’konda ndiponso matenda. Popeza kuti tikukhala mu ‘nthawi yovuta,’ aliyense ayenera kudziwa kuti pa nthawi ina adzakumana ndi vuto linalake. (2 Tim. 3:1) Izi zikachitika sitiyenera kuda nkhawa kwambiri. Mzimu woyera udzatipatsa mphamvu kuti tipirire vuto lililonse.

14. Kodi Yobu anapeza kuti mphamvu yomuthandiza kupirira mavuto amene anakumana nawo?

14 Yobu anakumana ndi mavuto motsatizanatsatizana. Chuma chake chinawonongedwa, ana ake anaphedwa, anzake anasiya kucheza naye, anadwala ndiponso mkazi wake anasiya kukhulupirira Yehova. (Yobu 1:13-19; 2:7-9) Komabe Elihu anamutonthoza. Iye anamuuza kuti: “Imani chilili ndi kuganizira mozama ntchito zodabwitsa za Mulungu.” (Yobu 37:14) Yehova analimbikitsanso Yobu kuchita zimene Elihu ananenazi. Kodi n’chiyani chinathandiza Yobu kupirira mavuto amene anakumana nawo? Nanga n’chiyani chingatithandize kupirira mavuto athu? Kukumbukira komanso kuganizira mmene Yehova amagwiritsira ntchito mzimu woyera ndiponso mphamvu yake kungatithandize. (Yobu 38:1-41; 42:1, 2) Mwina pa nthawi ina tinaona umboni wakuti Mulungu amatikonda ifeyo patokha. Iye amatikondabe ndipo sanasinthe.

15. Kodi n’chiyani chinapatsa mphamvu mtumwi Paulo kuti apirire mavuto?

15 Mtumwi Paulo anapirira mavuto oopsa kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chake. (2 Akor. 11:23-28) N’chiyani chinamuthandiza kuti aziona mavutowo m’njira yoyenera komanso kuti asasokonezeke maganizo? Iye ankapemphera  ndiponso kudalira Yehova. Pa nthawi imene Paulo ankavutika kwambiri ndiponso atatsala pang’ono kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake, analemba kuti: “Ambuye anaima pafupi ndi ine ndi kundipatsa mphamvu, kuti kudzera mwa ine, ntchito yolalikira ichitidwe mokwanira, ndi kuti mitundu yonse ya anthu imve uthengawo. Ndiponso ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.” (2 Tim. 4:17) Chifukwa cha zimene anakumana nazozi, Paulo anatsimikizira okhulupirira anzake kuti ‘asamade nkhawa ndi kanthu kalikonse.’​—Werengani Afilipi 4:6, 7, 13.

16, 17. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova amapatsa anthu ake mphamvu yolimbana ndi mavuto masiku ano.

16 Mpainiya wina dzina lake Roxana anaonanso kuti Yehova amathandiza kwambiri anthu ake. Iye atapempha bwana wake kuti akhale pa tchuthi n’cholinga choti akapezeke pa msonkhano wachigawo, bwanayo analusa n’kumuuza kuti ngati atapita adzamuchotsa ntchito. Roxana anapitabe ku msonkhanoko koma anapemphera ndi mtima wonse kuti asachotsedwe ntchito. Atatero, mtima wake unakhala m’malo. Msonkhanowu utatha, tsiku Lolemba bwana wake uja anamuchotsadi ndipo Roxana anadandaula kwambiri. Iye ankafunabe kugwira ntchitoyi kuti azipeza ndalama zothandizira banja lake ngakhale kuti ankamulipira ndalama zochepa. Iye anapempheranso n’kumaganizira mfundo yakuti popeza Mulungu anamuthandiza mwauzimu pa msonkhano ndiye kuti amuthandizanso kuti apeze zofunika pa moyo. Akubwerera kwawo, Roxana anapeza chikwangwani cholembedwa kuti “Tikufuna Antchito.” Chikwangwanichi chinali chofuna anthu odziwa kugwiritsa ntchito makina osokera ndipo iye anafunsira ntchitoyi. Bwana wa pakampaniyi anazindikira zoti iye sadziwa kusoka pa makina koma anamulembabe ntchito ndipo malipiro ake anali owirikiza pafupifupi kawiri malipiro amene ankamupatsa ku ntchito yoyamba ija. Apa Roxana anaona kuti mapemphero ake ayankhidwa. Koma anaona kuti wadalitsidwa kwambiri atatha kulalikira uthenga wabwino kwa anthu angapo amene ankagwira nawo ntchito. Pa anthu amene anawalalikirawa, anthu asanu kuphatikizapo bwana wa pakampaniyi anaphunzira choonadi n’kubatizidwa.

17 Nthawi zina tingaone ngati mapemphero athu sakuyankhidwa kapena tingaone kuti sanayankhidwe m’njira imene tinkafuna. Ngati zili choncho, tiyenera kudziwa kuti pali chifukwa chabwino. Yehova akudziwa chifukwacho ndipo mwina tidzachidziwanso m’tsogolo. Mfundo imodzi imene sitiyenera kuiwala ndi yakuti Mulungu sataya anthu ake okhulupirika.​—Aheb. 6:10.

Umatithandiza Kulimbana ndi Mavuto Ndiponso Mayesero

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera kukumana ndi mavuto komanso mayesero? (b) Kodi mungatani kuti mulimbane ndi mavuto?

18 Anthu a Yehova sadabwa akakumana ndi mayesero, zinthu zofooketsa, chizunzo kapena kukakamizidwa kuti azingotengera zochita za anzawo. Zoona zake n’zakuti dzikoli limadana nafe. (Yoh. 15:17-19) Koma mzimu woyera ungatithandize kulimbana ndi vuto lililonse limene tingakumane nalo potumikira Mulungu. Yehova sadzalola kuti tiyesedwe kufika pamene sitingapirire. (1 Akor. 10:13) Iye sadzatisiya kapena kutitaya. (Aheb. 13:5) Kumvera Mawu ake ouziridwa kumatiteteza ndi kutipatsa mphamvu. Ndipotu mzimu wa Mulungu ukhoza kuchititsa okhulupirira anzathu kuti atipatse thandizo pa nthawi imene tikulifuna kwambiri.

19 Tiyeni tonse tiziyesetsa kuti tilandire mzimu woyera mwa kupemphera komanso kuphunzira Malemba. Tiyeni tiziyesetsabe ‘kulandira mphamvu zazikulu chifukwa cha mphamvu za Mulungu zaulemerero, kuti tithe kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.’​—Akol. 1:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mwachitsanzo, onani Nsanja ya Olonda ya May 1, 2001, tsamba 16 ndi ya May 1, 1997 tsamba 24 mpaka 29.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi mungakonzekere bwanji chizunzo?

• Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mnzanu akukuuzani kuti musaulule tchimo lake?

• Kodi simuyenera kukayikira za chiyani mukakumana ndi vuto lililonse?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yoswa ndi Kalebe?

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi mungathandize bwanji mnzanu amene wachita tchimo?