Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Imbirani Yehova

Imbirani Yehova

 Imbirani Yehova

“Ndidzaimbira Mulungu wanga nyimbo zomutamanda kwa moyo wanga wonse.”​—SAL. 146:2.

1. N’chiyani chinachititsa Davide kukonza zina mwa nyimbo zake?

DAVIDE ali mnyamata, ankakhala maola ambiri kutchire pafupi ndi Betelehemu kumene ankaweta nkhosa za bambo ake. Pamene ankaweta nkhosazi, Davide ankaona zinthu zochititsa chidwi zimene Yehova analenga monga nyenyezi zakumwamba, “zilombo zakutchire” ndi “mbalame zam’mlengalenga.” Zimene ankaonazi zinamukhudza kwambiri moti zinachititsa kuti akonze nyimbo zabwino zotamanda Mlengi wa zinthu zogometsazi. Nyimbo zambiri zimene Davide anakonza zimapezeka m’buku la Masalimo. *​—Werengani Masalimo 8:3, 4, 7-9.

2. (a) Kodi nyimbo n’zothandiza bwanji kwa anthu? Perekani chitsanzo. (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya ubwenzi wa pakati pa Davide ndi Yehova pa Masalimo 34:7, 8 ndi Masalimo 139:2-8?

2 N’kutheka kuti pa nthawi imeneyi, Davide  anakulitsa luso lake loimba. Iye anakhala waluso kwambiri poimba moti anapemphedwa kuti azikaimbira nyimbo Mfumu Sauli. (Miy. 22:29) Nyimbo zokhazika mtima pansi zimene Davide ankaimba zinathandiza kwambiri mfumu imene inasokonezeka maganizo. Ngakhale masiku ano, nyimbo zabwino zimathandiza anthu. Davide akatenga chipangizo chake n’kumaimba nyimbo, “Sauli anali kupeza bwino.” (1 Sam. 16:23) Nyimbo zimene munthu woopa Mulunguyu anapeka ndiponso kuimba n’zothandizabe ngakhale kuti papita nthawi yaitali kuchokera pamene zinakonzedwa. Tangoganizani, panopa papita zaka zoposa 3,000 kuchokera pamene Davide anabadwa. Koma anthu mamiliyoni ambiri ochokera m’mitundu ndiponso m’mayiko osiyanasiyana amakonda kuwerenga masalimo a Davide pofuna kuti atonthozedwe kapena kuti akhale ndi chiyembekezo.​—2 Mbiri 7:6; werengani Masalimo 34:7, 8; 139:2-8; Amosi 6:5.

Nyimbo N’zofunika Kwambiri pa Kulambira Koona

3, 4. Kodi ndi dongosolo liti lokhudza kuimbira Mulungu limene linalipo nthawi ya Davide?

3 Davide anali ndi luso loimba ndipo analigwiritsa ntchito ndi mtima wonse polemekeza Yehova. Atakhala mfumu ya Isiraeli, Davide anakonza zoti anthu akamalambira Mulungu pa chihema chopatulika aziimba nyimbo zabwino. Alevi okwana 4,000 anasankhidwa n’kuphunzitsidwa kuti ‘aziimbira Yehova zitamando.’ ‘Ndipo akatswiri onse ophunzitsidwa kuimbira Yehova, anakwana 288.’​—1 Mbiri 23:3, 5; 25:7.

4 Davide ndi amene anakonza nyimbo zambiri zimene Alevi ankaimba. Mwisiraeli aliyense amene anali ndi mwayi womvetsera anthu akuimba masalimo a Davide ayenera kuti ankakhudzidwa kwambiri. Kenako likasa la chipangano atalibweretsa ku Yerusalemu, “Davide anauza atsogoleri a Alevi kuti aike m’malo awo abale awo oimba okhala ndi zipangizo zoimbira. Zipangizozo zinali zoimbira za zingwe, azeze, ndi zinganga. Anawauza kuti aimbe mokweza kuti nyimbo zachisangalalo zimveke.”​—1 Mbiri 15:16.

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani anthu ankachita khama pa nkhani yoimba mu ulamuliro wa Davide? (b) Tikudziwa bwanji kuti kuimba kunali kofunika kwambiri pa kulambira kwa Aisiraeli akale?

5 N’chifukwa chiyani anthu ankachita khama chonchi pa nkhani yoimba m’masiku a Davide? Kodi n’chifukwa chakuti mfumu inali yoimba? Ayi, pali chifukwa china ndipo chinadziwika zaka zingapo pambuyo pake, pa nthawi imene Mfumu Hezekiya yomwe inali yolungama inayambitsanso utumiki wa pakachisi. Pa 2 Mbiri 29:25 timawerenga kuti: “Hezekiya anaika Alevi panyumba ya Yehova atanyamula zinganga, zoimbira za zingwe, ndi azeze. Iwo anali kutsatira ndondomeko yoimbira imene anaikhazikitsa Davide, Gadi yemwe anali wamasomphenya wa mfumu, ndi mneneri Natani, popeza ndondomekoyo inachokera kwa Yehova kudzera mwa aneneri ake.”

6 Kudzera mwa aneneri ake, Yehova analamula kuti anthu amene amamulambira azimutamanda ndi nyimbo. Anthu oimba nyimbo ochokera m’fuko la ansembe sankaloledwa kugwira ntchito zina zimene Alevi ena ankagwira n’cholinga choti akhale ndi nthawi yokwanira yokonza nyimbo n’kuyesa kuziimba.​—1 Mbiri 9:33.

7, 8. Pa nkhani yoimba nyimbo za Ufumu, kodi chofunika kwambiri kuposa luso n’chiyani?

7 Mwina munganene kuti, “Ine nkhani yoimbayi ndi kumanzere kwanga ndipo ndikanakhalapo pa nthawiyo sindikanasankhidwa kukhala m’gulu la akatswiri oimba pa chihema chopatulika.” Koma dziwani kuti Alevi ena amene ankaimba sanali akatswiri. Malinga ndi 1 Mbiri 25:8, panalinso anthu amene ‘anali ongophunzira kumene.’ Dziwaninso kuti Yehova anangosankha fuko la Levi lokha kuti liziimba ngakhale kuti mwina panali akatswiri ena a zoimbaimba m’mafuko ena. Choncho kaya munthu anali “katswiri” kapena “wophunzira kumene,” Alevi onse okhulupirika amene anasankhidwa kuti  akhale m’gulu loimba ankayesetsa kuimba ndi mtima wonse.

8 Davide ankakonda kwambiri nyimbo ndipo analidi katswiri poimba. Koma kodi Mulungu amasangalala ndi luso lokha? Pa Masalimo 33:3, Davide analemba kuti: “Muimbireni choimbira cha zingwe ndi mtima wonse ndi kufuula mosangalala.” Apa n’zodziwikiratu kuti chimene Yehova amafuna ndi kuimba “ndi mtima wonse” pomutamanda.

Kufunika kwa Nyimbo Davide Atamwalira

9. Fotokozani zimene mukanaona ndiponso kumva potsegulira kachisi mu ulamuliro wa Solomo.

9 Mu ulamuliro wa Solomo, nyimbo zinali zofunika kwambiri pa kulambira koona. Pa nthawi yotsegulira kachisi, panali gulu la anthu oimba pogwiritsa ntchito zipangizo zoimbira ndipo panali anthu 120 oimba malipenga. (Werengani 2 Mbiri 5:12.) Baibulo limatiuza kuti, “anthu oimba malipenga [amene onse anali ansembe] ndi oimba pakamwa anayamba kuimba mogwirizana n’kumamveka ngati mawu amodzi otamanda ndi kuthokoza Yehova . . . ‘chifukwa iye ndi wabwino, pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.’” Anthu atayamba kuimba bwino chonchi “mtambo unadzaza nyumbayo” ndipo ichi chinali chizindikiro chakuti Yehova akusangalala nazo. Zinalitu zosangalatsa kwambiri ndiponso zodabwitsa kumva anthu akuimba malipenga mogwirizana ndi oimba ndi pakamwa moti zinkamveka ngati mawu amodzi.​—2 Mbiri 5:13.

10, 11. Tikudziwa bwanji kuti Akhristu oyambirira ankaimba polambira?

10 Akhristu oyambirira ankaimbanso polambira Mulungu. N’zoona kuti Akhristu oyambirira sankakumana m’mahema opatulika kapena muakachisi, koma m’nyumba za anthu. Chifukwa cha chizunzo ndiponso zinthu zina sankatha kuimba pamalo amene ankasonkhana. Komabe Akhristu amenewa ankatamanda Mulungu ndi nyimbo.

11 Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake ku Kolose kuti: “Pitirizani . . . kulangizana mwa masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu zogwira mtima.” (Akol. 3:16) Paulo ndi Sila atatsekeredwa m’ndende anayamba “kupemphera ndi kutamanda Mulungu poimba nyimbo” ngakhale kuti analibe mabuku a nyimbo. (Mac. 16:25) Kodi inu mukanatsekeredwa m’ndende mukanatha kuimba nyimbo za Ufumu zingati popanda kuona m’buku?

12. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nyimbo za Ufumu?

12 Popeza nyimbo ndi zofunika kwambiri pa kulambira kwathu tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimasonyeza kuti ndimayamikira nyimbo? Kodi ndimayesetsa kufika msanga pa misonkhano ya mpingo, yadera ndi yachigawo kuti ndikaimbe limodzi ndi abale ndi alongo nyimbo yotsegulira? Nanga kodi ndimaimba ndi mtima wonse? Kodi ndimauza ana anga kuti tikamaimba nyimbo pakati pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki kapena pakati pa nkhani ya onse ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda si nthawi yopuma kapena yoti azingoyendayenda pofuna kuwongola miyendo?’ Kuimba ndi mbali ya kulambira kwathu. Kaya ndife ‘akatswiri’ kapena ‘ophunzira kumene,’ tonsefe tiyenera kuimba limodzi nyimbo zotamanda Yehova.​—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 8:12.

Zinthu Zimasintha Pakapita Nthawi

13, 14. Kodi kuimba ndi mtima wonse pa misonkhano ya mpingo n’kofunika bwanji? Perekani chitsanzo.

13 Zaka zoposa 100 zapitazo, magazini ya Nsanja ya Olonda, yomwe pa nthawiyo inkatchedwa Zion’s Watch Tower, inafotokoza kufunika kwa nyimbo zathu za Ufumu. Inati: “Kuimba ndi njira yabwino kwambiri yothandiza kuti choonadi chikhazikike m’maganizo ndi m’mitima ya anthu a Mulungu.” Mawu ambiri a m’nyimbo zathu ndi ochokera m’Malemba, choncho kuphunzira zina mwa nyimbozi ndi njira yabwino kwambiri yothandiza kuti choonadi chikhazikike m’mitima yathu. Nthawi zambiri,  anthu akafika koyamba pa misonkhano yathu amakhudzidwa kwambiri mpingo ukamaimba nyimbo ndi mtima wonse.

14 Tsiku lina madzulo mu 1869, C. T. Russell akuweruka kuntchito anamva anthu akuimba mu holo inayake. Pa nthawi imeneyi, iye anaona kuti n’zovuta kupeza choonadi pa nkhani ya Mulungu. Choncho anaganiza zongoyesetsa kugwira ntchito mwakhama n’cholinga choti apeze ndalama zoti azithandizira anthu ovutika pozindikira kuti sangakwanitse kuwathandiza mwauzimu. M’bale Russell atalowa m’holo yosasamaliridwayo anapeza anthu akuchita mwambo wa mapemphero. Iye anakhala pansi n’kumamvetsera. Kenako pofotokoza zimene anamva tsiku limenelo analemba kuti: “Zinali zokwanira ndipo ndinathandizidwa ndi Mulungu kuti chikhulupiriro changa chakuti Baibulo ndi louziridwa ndi Mulungu chilimbe.” Onani kuti zimene zinakopa M’bale Russell kuti apite ku msonkhanowu zinali nyimbo.

15. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinasintha m’kamvedwe kathu zomwe zachititsa kuti buku la nyimbo lisinthidwe?

15 Nthawi ikamadutsa pamakhala kusintha pa kamvedwe kathu ka Malemba? Lemba la Miyambo 4:18 limanena kuti: “Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” Kuwala kumeneku kukamawonjezereka, kumachititsa kuti pakhale kusintha pa mawu a choonadi amene timayimba. Pa zaka 25 zapitazi, Mboni za Yehova zakhala zikuimba nyimbo m’buku lakuti Imbirani Yehova Zitamando. * Koma kuchokera pa nthawi imene bukuli linakonzedwa kuwala kwakhala kukuwonjezereka pa nkhani zosiyanasiyana ndipo mawu ena amene analembedwa m’buku limeneli tinasiya kuwagwiritsa ntchito. Mwachitsanzo timanena kuti dzina la Yehova “lidzayeretsedwa” osati “kutsimikiziridwa.” Choncho pa nkhani ya ziphunzitso m’pofunika kusintha nyimbo zina kuti zigwirizane ndi kamvedwe katsopano.

16. Kodi buku la nyimbo latsopano litithandiza bwanji kutsatira malangizo a Paulo a pa Aefeso 5:19?

16 Pa chifukwa chimenechi ndiponso zifukwa zina, Bungwe Lolamulira linavomereza zoti pakonzedwe buku la nyimbo latsopano la mutu wakuti Imbirani Yehova. M’buku latsopanoli muli nyimbo 135 zokha. Popeza nyimbozi n’zochepa n’zosavuta kuloweza mawu a nyimbo zina. Izi n’zogwirizana ndi mawu a Paulo a pa Aefeso 5:19.​—Werengani.

Sonyezani Kuyamikira

17. Kodi ndi mfundo iti imene ingatithandize kuti tisamachite mantha kapena manyazi poimba nyimbo mu mpingo?

17 Kodi ndi bwino kusaimba pa misonkhano yachikhristu chifukwa cha mantha kapena manyazi? Taganizirani izi. Pa nkhani ya zolankhula “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yak. 3:2) Koma sitisiya kutamanda Yehova mwa kulalikira nyumba ndi nyumba poopa kuti tilakwitsa polankhula chifukwa chakuti  ndife opanda ungwiro. Choncho palibe chifukwa chosatamandira Mulungu poimba chifukwa choti sititha kuimba mwanthetemya. Yehova amene “anapatsa munthu pakamwa” amasangalala akamaona tikugwiritsa ntchito mawu athu pomutamanda kudzera mu nyimbo.​—Eks. 4:11.

18. N’chiyani chikuthandiza abale ndi alongo ambiri kuphunzira nyimbo zatsopano?

18 Ma CD a nyimbo zatsopano (Sing to Jehovah​—Piano Accompaniment) akuthandiza abale ndi alongo ambiri kuphunzira nyimbozi. Nyimbozi ndi zosangalatsa kwambiri kumvetsera. Mukakhala ndi chizolowezi chomvetsera nyimbozi kunyumba kwanu n’kumatsatira m’buku lanu la nyimbo, muzidzatha kuimba bwino ku Nyumba ya Ufumu.

19. Fotokozani zimene zimachitika pokonza nyimbo za Ufumu.

19 Nthawi zina sitiganizira n’komwe nyimbo zimene timamvera pa misonkhano yadera, yachigawo ndi pa tsiku la msonkhano wapadera. Koma pamakhala ntchito yaikulu kwambiri kuti nyimbo zimenezi zikonzedwe. Nyimbozi zikasankhidwa, zimakonzedwanso mwaluso kwambiri kuti abale 64 amene amadziwa kugwiritsa ntchito zipangizo zoimbira aimbe nyimbozi. Ndiyeno oimbawa amayesetsa kwa maola ambiri kukonza nyimbozo kenako n’kumayesera kuziimba. Akamaliza amakaziimba ku situdiyo ya ku Patterson, New York. Pa gulu la oimbali, pali abale ndi alongo 10 omwe si a ku United States koma amachokera kumayiko ena. Onsewa amaona kuti ndi mwayi kuthandiza nawo pokonza nyimbo zoimba pa misonkhano yolambira Mulungu. Choncho, tiyenera kuyamikira kwambiri khama limene abale ndi alongowa amachita. Ngati tcheyamani pa misonkhano yadera ndi yachigawo atiuza kuti tikhale pansi n’kumamvetsera nyimbo zamalimba tiyenera kuchita zimenezo posonyeza kuyamikira.

20. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

20 Yehova amaona tikamamutamanda mwa kuimba nyimbo. Iye amaona kuti nyimbo ndi zofunika kwambiri. Choncho tingakondweretse mtima wake mwa kuimba ndi mtima wonse tikamamulambira pa misonkhano yathu. Kaya ndife akatswiri kapena ongophunzira kumene, tiyeni ‘tiziimbira Yehova.’​—Sal. 104:33.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Chochititsa chidwi n’chakuti, patapita zaka 1,000 kuchokera pamene Davide anamwalira, gulu la angelo linaonekera kwa abusa n’kuwauza za kubadwa kwa Mesiya. Pa nthawiyi, abusawa ankayang’anira nkhosa kutchire pafupi ndi Betelehemu.​—Luka 2:4, 8, 13, 14.

^ ndime 15 Nyimbo zonse 225 zinalipo m’zinenero zoposa 100.

Kodi Mukuganiza Bwanji?

• Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zimene zikusonyeza kuti nyimbo ndi zofunika kwambiri pa kulambira kwathu?

• Kodi mukuona kuti pali kugwirizana kotani pakati pa lamulo la Yesu lopezeka pa Mateyu 22:37 ndi kuimba nyimbo za Ufumu mochokera pansi pa mtima?

• Fotokozani njira zimene tingasonyezere kuyamikira nyimbo zathu za Ufumu.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi mumauza ana anu kuti asamangotulukatuluka nthawi ya nyimbo?

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi mukuphunzira mawu a nyimbo zathu zatsopano kunyumba kwanu?