Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata, Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?

Achinyamata, Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?

 Achinyamata, Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?

“Mmene ndikuponyera nkhonya zanga, sikuti ndikungomenya mphepo ayi.”​—1 AKOR. 9:26.

1, 2. Kuti zinthu zikuyendereni bwino pa moyo wanu, kodi muyenera kukhala ndi chiyani?

TIYEREKEZERE kuti mukupita pa ulendo wautali kudera limene simunapiteko ndipo muyenda usiku. Kuti muyende bwino muyenera kukhala ndi mapu abwino ndiponso nyali. Mapuwo angakuthandizeni kudziwa malo amene muli ndiponso kumene muyenera kulowera. Nyali ingakuthandizeni kuti musapunthwe komanso kuti musaphonye njira. Koma mapu ndi nyaliyo sizingakuthandizeni ngati palibe malo enieni amene mukupita. Choncho kuti musamangozungulira malo amodzi muyenera kukhala ndi malo enieni amene mukupita.

2 Pamene mukukula mumakhala ngati munthu amene akuyenda pa ulendo ngati umenewu. Baibulo lili ngati mapu amene angakuthandizeni kudziwa njira imene muyenera kulowera. (Miy. 3:5, 6) Ngati mutaphunzitsa bwino chikumbumtima chanu, chingakuthandizeni kuti musaphonye njirayo. (Aroma 2:15) Pamenepa chikumbumtima chikhoza kukhala ngati nyali yokuunikirani. Choncho kuti zinthu zikuyendereni bwino pa moyo wanu muyenera kukhala ndi malo enieni amene mukupita kapena kuti kukhala ndi zolinga zodziwika bwino.

3. Pa 1 Akorinto 9:26, kodi Paulo anafotokoza bwanji ubwino wokhala ndi zolinga?

3 Mtumwi Paulo anafotokoza ubwino wokhala ndi zolinga komanso kuyesetsa kuzikwaniritsa. Iye analemba kuti: “Sikuti ndikungothamanga osadziwa kumene ndikulowera. Mmene ndikuponyera nkhonya zanga, sikuti ndikungomenya mphepo ayi.” (1 Akor. 9:26) Mukakhala ndi zolinga zimakhala ngati mukudziwa kumene mukulowera pothamanga. Posachedwapa, muyenera kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu monga kulambira, ntchito, kukwatira kapena kukwatiwa, kukhala ndi ana ndi zina zotero. Nthawi zina mungavutike kusankha zochita. Koma mukakhala ndi zolinga zogwirizana ndi choonadi komanso mfundo za m’Mawu a Mulungu, simudzasocheretsedwa kapena kusankha zolakwika.​—2 Tim. 4:4, 5.

4, 5. (a) Kodi chingachitike n’chiyani ngati mulibe zolinga pa moyo wanu? (b) N’chifukwa chiyani zinthu zimene mumasankha pa moyo wanu ziyenera kukhala zosangalatsa Mulungu?

4 Ngati mulibe zolinga, ndiye kuti mukhoza kulolera kuti anzanu ndi aphunzitsi anu akusankhireni zinthu zimene akuganiza kuti ndi zoyenera. Koma ngakhale mutakhala ndi zolinga zooneka bwino, ena adzaperekabe maganizo awo. Mukamamvetsera maganizo awo muzidzifunsa kuti, ‘Kodi zolinga zimene akutchulazi zingandithandize kukumbukira Mlengi wanga pamene ndili wachinyamata kapena zingandilepheretse kuchita zimenezi?’​—Werengani Mlaliki 12:1.

5 N’chifukwa chiyani zinthu zimene mumasankha pa moyo wanu ziyenera kukhala zogwirizana ndi cholinga chofuna kusangalatsa Mulungu? Chifukwa chimodzi n’chakuti Yehova ndi amene anatipatsa chinthu chilichonse chabwino chimene tili nacho. (Yak. 1:17) Kunena zoona, aliyense ayenera kuthokoza Yehova. (Chiv. 4:11) Palibenso njira ina imene mungathokozere Yehova kuposa kumukumbukira posankha zochita pa moyo wanu. Tsopano tiyeni tikambirane zolinga zimene muyenera kukhala nazo ndiponso zimene mungachite kuti muzikwaniritse.

 Kodi Mungakhale ndi Zolinga Ziti?

6. Kodi cholinga chofunika kwambiri chimene muyenera kukhala nacho ndi chiti, ndipo n’chifukwa chiyani?

6 Monga tafotokozera m’nkhani yapitayi, cholinga chachikulu chimene mungakhale nacho ndi kutsimikizira kuti zimene Baibulo limanena ndi zoona. (Aroma 12:2; 2 Akor. 13:5) Mwina anzanu ena amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina kapena amakhulupirira ziphunzitso za zipembedzo zonyenga. Amachita zimenezi chifukwa chakuti anthu ena anawauza kuti azikhulupirira zimenezo. Komabe simuyenera kungokhulupirira zimene anthu ena akufuna kuti muzikhulupirira. Musaiwale kuti Yehova akufuna kuti mum’tumikire ndi maganizo anu onse. (Werengani Mateyu 22:36, 37.) Atate wathu wakumwamba akufuna kuti muzikhala ndi umboni wa zimene mumakhulupirira.​—Aheb. 11:1.

7, 8. (a) Kodi mungalimbitse chikhulupiriro chanu mwa kukhala ndi zolinga zing’onozing’ono ziti? (b) Kodi chingachitike n’chiyani ngati mutakwaniritsa zolinga zanu zing’onozing’ono?

7 Kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu mungachite bwino kukhala ndi zolinga zing’onozing’ono zimene mungazikwaniritse pa nthawi yochepa. Cholinga chimodzi chingakhale kupemphera tsiku ndi tsiku. Mapemphero anu asamangokhala achizolowezi koma muzitchula zinthu zenizeni zimene zili mumtima mwanu. Kuti zimenezi zitheke, muyenera kuganizira kapena kulemba zinthu zimene zakuchitikirani n’cholinga choti muzitchule m’mapemphero anu. Onetsetsani kuti mwatchula mavuto amene mwakumana nawo komanso zinthu zimene mwasangalala nazo. (Afil. 4:6) Cholinga china ndi kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. Kodi mukudziwa kuti ngati mutamawerenga pafupifupi masamba anayi pa tsiku mukhoza kumaliza Baibulo lonse pa chaka chimodzi? * Lemba la Salimo 1:1, 2 limati: “Wodala ndi munthu amene . . . amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.”

8 Cholinga chinanso chimene mungakhale nacho ndi kukonzekera kuyankha pa misonkhano yonse ya mpingo. Poyamba, mukhoza  kungowerenga yankholo kapena lemba. Kenako, mukhoza kumayankha m’mawu anuanu. Dziwani kuti nthawi iliyonse imene mumayankha mumakhala mukupereka mphatso kwa Yehova. (Aheb. 13:15) Mukakwaniritsa zina mwa zolinga zing’onozing’ono zimenezi, mumasiya kudzikayikira ndipo mumayamikira kwambiri Yehova. Mumakhalanso okonzeka kukhala ndi zolinga zikuluzikulu.

9. Ngati panopo sindinu wofalitsa Ufumu, kodi cholinga chanu chachikulu chingakhale chiyani?

9 Kodi ndi zolinga zikuluzikulu ziti zimene mungakhale nazo? Ngati panopo simunayambe kulalikira uthenga wabwino, muyenera kukhala ndi cholinga chokhala wofalitsa Ufumu. Mutakwaniritsa cholinga chabwino chimenechi, muziphunzira kulalikira mogwira mtima ndiponso kulowa mu utumiki nthawi zonse, osaphonya ngakhale mwezi umodzi. Muyenera kuphunziranso kugwiritsa ntchito bwino Baibulo mu utumiki. Mukamachita zimenezi mungayambe kukonda kwambiri ntchito yolalikira. Kenako mungawonjezere nthawi imene mumagwira ntchito yolalikira ku nyumba ndi nyumba ndiponso kuyesetsa kuti muzichititsa phunziro la Baibulo. Ngati ndinu wofalitsa wosabatizidwa cholinga chabwino kwambiri chimene muyenera kukhala nacho ndi kudzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa kuti mukhale wa Mboni za Yehova.

10, 11. Kodi achinyamata obatizidwa angakhale ndi zolinga zikuluzikulu ziti?

10 Ngati ndinu mtumiki wa Yehova wobatizidwa, palinso zolinga zikuluzikulu zimene mungakhale nazo. Nthawi zina mukhoza kuthandiza mipingo kulalikira m’madera amene safikidwa kawirikawiri. Mungasankhenso kugwiritsa ntchito mphamvu zanu kuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Anthu ambiri amene akusangalala ndi upainiya akhoza kukuuzani kuti utumiki wa nthawi zonse ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti mukukumbukira Mlengi wanu pa nthawi ya unyamata. Zimenezi ndi zolinga zimene mungakwaniritse muli kunyumba kwanu. Mpingo wanu ukhoza kupindulanso mukamakwaniritsa zolinga zimenezi.

11 Pali zolinga zina zikuluzikulu zimene mungakwaniritse ngati mutasamukira kudera lina. Mwachitsanzo, mukhoza kukonza zokatumikira kudera lina kapena kudziko lina kumene kukufunika olalikira ambiri. Mwina mungafune kukathandiza kumanga Nyumba za Ufumu kapena maofesi a nthambi m’mayiko ena. Mwinanso mukhoza kuyamba utumiki wa pa Beteli kapena kukhala mmishonale. Komabe chinthu chofunika kwambiri n’chakuti muyenera kubatizidwa kaye musanayambe kukhala ndi zina mwa zolinga zikuluzikulu zimene tatchulazi. Ngati simunabatizidwe, ganizirani zimene mungachite kuti mukwaniritse cholinga chofunika kwambiri chimenechi.

Zimene Mungachite Kuti Mubatizidwe

12. Kodi anthu ena amabatizidwa pa zifukwa ziti, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi si zifukwa zabwino?

12 Kodi inu mumaona kuti cholinga cha ubatizo n’chiyani? Ena amaganiza kuti ubatizo umawateteza kuti asachite tchimo. Ena amaganiza kuti ayenera kubatizidwa chifukwa anzawo anabatizidwa. Achinyamata ena amabatizidwa pofuna kusangalatsa makolo awo. Komatu, kubatizidwa sikukuletsani kuchita zinthu zimene mumafuna mumtima mwanu. Ndiponso simuyenera kubatizidwa chifukwa chokakamizidwa ndi anthu ena. Muyenera kubatizidwa mutazindikira zimene kukhala wa Mboni za Yehova kumafuna ndiponso mutatsimikiza kuti ndinu wokonzeka komanso wofunitsitsa kukwaniritsa udindo umenewu.​—Mlal. 5:4, 5.

13. Kodi muyenera kubatizidwa pa zifukwa ziti?

13 Chifukwa china chokuchititsani kubatizidwa n’chakuti Yesu anauza otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu “kuti akhale ophunzira . . . ndi kuwabatiza.” Iye anaperekanso chitsanzo mwa kubatizidwa. (Werengani Mateyu 28:19, 20; Maliko 1:9.) Ndipotu ubatizo ndi wofunika kwambiri kwa anthu amene akufuna kupulumutsidwa. Mtumwi Petulo atanena zoti Nowa anapanga chingalawa chimene chinathandiza kuti iye ndi banja lake apulumuke Chigumula, ananenanso kuti: “Chofanana ndi chingalawacho chikupulumutsanso inuyo tsopano. Chimenechi ndicho ubatizo, . . . mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.” (1 Pet. 3:20, 21) Komabe, izi sizikutanthauza kuti munthu akabatizidwa ndiye kuti basi, adzapulumuka. M’malomwake muyenera kubatizidwa chifukwa  chakuti mumakonda Yehova ndiponso mukufuna kumutumikira ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndi mphamvu zanu zonse.​—Maliko 12:29, 30.

14. N’chifukwa chiyani anthu ena amaopa kubatizidwa, koma n’chiyani chingawathandize kuthetsa maganizo amenewo?

14 Ena safuna kubatizidwa poopa kuti angadzachotsedwe. Kodi inunso mumaganiza choncho? Ngati mumatero, dziwani kuti maganizo amenewa pa okha si olakwika. Mwina ungakhale umboni wakuti mukudziwa udindo umene munthu angakhale nawo akakhala wa Mboni za Yehova. Kodi pangakhale chifukwa chinanso? Mwina simunatsimikizire zoti kutsatira mfundo za Mulungu n’kwabwino kwambiri. Ngati ndi choncho, kuganizira zimene zimachitikira anthu amene amanyalanyaza mfundo za m’Baibulo kungakuthandizeni kusankha bwino zochita pa nkhani imeneyi. Apo ayi, mwina mumakonda mfundo za Mulungu koma mumakayikira zoti mungazitsatire bwinobwino. Maganizo amenewatu angakhale abwino chifukwa akusonyeza kuti ndinu wodzichepetsa. Pajatu Baibulo limanena kuti mitima ya anthu onse opanda ungwiro ndi yonyenga. (Yer. 17:9) Koma zinthu zikhoza kukuyenderani bwino ngati nthawi zonse ‘mukudziyang’anira ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu a Mulungu.’ (Werengani Salimo 119:9.) Kaya mukukayikira kubatizidwa pa zifukwa ziti, muyenera kuyesetsa kuti muthetse maganizo amenewo. *

15, 16. Kodi mungadziwe bwanji ngati ndinu woyenera kubatizidwa?

15 Kodi mungadziwe bwanji ngati ndinu woyenera kubatizidwa? Chinthu china chimene mungachite ndi kudzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi ndikhoza kufotokoza ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo kwa ena? Kodi ndimalalikira nawo ngakhale pamene makolo anga sakulalikira? Kodi ndimachita khama kupezeka pa misonkhano yonse yachikhristu? Kodi ndikukumbukira nthawi imene ndinakana kutengera zofuna za anzanga? Kodi ndingapitirize kutumikira Yehova ngakhale makolo anga ndi anzanga atasiya? Kodi ndapemphererapo za ubwenzi wanga ndi Mulungu? Nanga kodi ndadzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse mwa kumuuza m’pemphero kuti ndikufuna kumutumikira?’

16 Ubatizo umasintha kwambiri moyo wa munthu ndipo sitiyenera kuuona mopepuka. Kodi ndinu wokonzekadi kubatizidwa? Kukamba bwino nkhani papulatifomu ndi kupereka mayankho abwino pa misonkhano pa zokha si umboni wakuti ndinu wokhwima mwauzimu. Munthu wokhwima mwauzimu amatha kusankha zinthu mogwirizana ndi mfundo zimene waphunzira m’Baibulo. (Werengani Aheberi 5:14.) Ngati ndinu wokonzeka kubatizidwa, muli ndi mwayi wamtengo wapatali. Mwayiwu ndi wotumikira Yehova ndi mtima wonse ndiponso kukhala ndi moyo wosonyeza kuti ndinudi wodzipereka kwa Mulungu.

17. N’chiyani chingakuthandizeni kuthana ndi mayesero amene mungakumane nawo mutabatizidwa?

 17 Mukangobatizidwa mukhoza kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Mulungu kwambiri. Koma kenako, chikhulupiriro ndi kupirira kwanu zikhoza kuyesedwa. (2 Tim. 3:12) Musaganize kuti muyenera kuthana ndi mayesero amenewa panokha. Muzipempha malangizo kwa makolo anu. Mukhozanso kupempha thandizo kwa anthu olimba mwauzimu mu mpingo. Muzigwirizana ndi anthu amene angakuthandizeni. Musaiwale kuti Yehova amakuderani nkhawa ndipo adzakupatsani mphamvu zokuthandizani kuthana ndi vuto lililonse limene mungakumane nalo.​—1 Pet. 5:6, 7.

Kodi Mungatani Kuti Mukwaniritse Zolinga Zanu?

18, 19. Kodi kuonanso bwino zimene mumaika patsogolo pa moyo wanu kuli ndi phindu lotani?

18 Kodi mumaona kuti mulibe nthawi yokwanira yochita zinthu zimene mumafuna ndiponso zimene muyenera kuchita ngakhale kuti muli ndi zolinga zabwino? Ngati ndi choncho, muyenera kuonanso bwino zimene mumaika patsogolo pa moyo wanu. Kuti mumvetse zimenezi, tayesani kuchita izi: Tengani chitini n’kuikamo miyala ikuluikulu. Kenako muthiremo mchenga mpaka kudzaza chitinicho. Tsopano khuthulani zonsezo koma musataye kapena kuziwonjezera. Ndiyeno yambani kuthira mchengawo m’chitinicho, pambuyo pake muikemo miyala yomwe ija. Mutha kuona kuti sizingakwanemo. Zili choncho chifukwa chakuti munayamba ndi mchenga.

19 Ndi mmenenso zimakhalira ndi nthawi imene mumakhala nayo. Mukamaika patsogolo zinthu monga zosangalatsa, mudzapeza kuti mulibe nthawi yochita zinthu zofunika kwambiri zimene ndi zinthu zauzimu. Koma mukatsatira malangizo a m’Baibulo akuti “muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti” mudzapeza kuti muli ndi nthawi yochita zinthu za Ufumu ndiponso yochita zosangalatsa.​—Afil. 1:10.

20. Kodi mungatani ngati mumada nkhawa kapena kukayikakayika pamene mukuyesetsa kukwaniritsa zolinga zanu?

20 Mukamayesetsa kukwaniritsa zolinga zanu, kuphatikizapo cholinga chofuna kubatizidwa, nthawi zina muzikhala ndi nkhawa kapena muzikayikakayika. Zikatero, ‘muzitulira Yehova nkhawa zanu, ndipo iye adzakuchirikizani.’ (Sal. 55:22) Panopa muli ndi mwayi wogwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu padziko lonse. Ntchito imeneyi ndi yosangalatsa ndiponso yofunika kwambiri kuposa ntchito ina iliyonse m’mbiri ya anthu. (Mac. 1:8) Mungasankhe kumangoonerera pamene anzanu akugwira ntchitoyi kapena inunso mungagwire nawo. Musalephere kugwiritsa ntchito luso lanu pogwira nawo ntchito yopititsa patsogolo Ufumuyi. Simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono chifukwa chotumikira ‘Mlengi wanu wamkulu masiku a unyamata wanu.’​—Mlal. 12:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Kuti mupeze mfundo zothandiza pa nkhani imeneyi, onani buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, mutu 34.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani muyenera kukhala ndi zolinga?

• Tchulani zolinga zimene mungachite bwino kuzikwaniritsa.

• Kodi chofunika n’chiyani kuti mukwaniritse cholinga chofuna kubatizidwa?

• Kodi kuonanso bwino zimene mumaika patsogolo pa moyo wanu kungakuthandizeni bwanji kukwaniritsa zolinga zanu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi muli ndi cholinga chowerenga Baibulo tsiku lililonse?

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukwaniritsa cholinga chanu chofuna kubatizidwa?

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi mukuphunzira chiyani pa chitsanzo ichi?