Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kabuku Kamene Kamandithandiza Kuwafika Anthu pa Mtima”

“Kabuku Kamene Kamandithandiza Kuwafika Anthu pa Mtima”

 “Kabuku Kamene Kamandithandiza Kuwafika Anthu pa Mtima”

M’MBUYOMU, mumzinda wa Porto Alegre umene uli kum’mwera m’dziko la Brazil, kunali msonkhano wa mayiko osiyanasiyana wokhudza chikhalidwe cha anthu. Ku msonkhanowu kunabwera anthu ambirimbiri ochokera m’mayiko 135. Tsiku lililonse pa nthawi yopuma gulu la Mboni lochokera kumpingo wina wa ku Porto Alegre linkawafikira anthuwa kuti awalalikire uthenga wa Ufumu wa m’Baibulo. Kodi ankalankhula nawo bwanji?

Mpainiya wina dzina lake Elizabete ananena kuti: “Tinkagwiritsa ntchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse.” Iye ananenanso kuti: “Ambiri mwa anthu amene anabwera ku msonkhanowu anali asanamvepo uthenga wabwino wa Ufumu koma ankamvetsera mwachidwi uthenga wathu. Tinalankhula ndi anthu ochokera ku Bolivia, China, France, India, Israel, ndiponso Nigeria. Tinali ndi mabuku ofotokoza Baibulo achinenero cha ena mwa anthuwa ndipo analandira mabukuwo mosangalala.”

Mpainiya wina wa ku Mexico dzina lake Raúl anagwiritsiranso ntchito kabukuka ndipo zotsatira zake zinali zabwino. Tsiku lina anakumana ndi bambo wina wa zaka 80 wachiarabu amene mkazi wake anali atangomwalira kumene. Bamboyu atawerenga uthenga wabwino wa Ufumu m’kabukuka mu Chiarabu anayamba kulira. Kodi n’chifukwa chiyani iye analira? Atawerenga m’chinenero chake lonjezo la Mulungu lopezeka pa Chivumbulutso 21:3, 4 lakuti sikudzakhalanso imfa, anakhudzidwa kwambiri. Pa nthawi ina Raúl akulalikira mwamwayi, anakumana ndi bambo wina yemwe amalankhula Chipwitikizi. Mwana wa mwamuna wa bamboyo analinso atamwalira. Raúl anamupempha kuti awerenge uthenga wabwino m’kabukuka m’Chipwitikizi. Bamboyu atawerenga, anasonyeza kuti akufuna kudziwa zambiri za Baibulo ndipo anavomera kuti aziphunzira Baibulo.

Raúl wagwiritsapo ntchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu Amitundu Yonse kuti alalikire kwa anthu amene amalankhula Chiameniya, Chifalansa, Chihindi, Chijeremani, Chikoleya, Chimikise, Chingelezi, Chiperisiya, Chirasha, Chitchaina ndi Chizapoteki. Iye ananena kuti: “Ndaona kufunikira kogwiritsa ntchito kabuku kameneka mu utumiki. Kamandithandiza kuwafika anthu pamtima ngakhale kuti sindilankhula chinenero chawo.”

Tili ndi mwayi wokumana ndi anthu amene amalankhula zinenero zina chifukwa masiku ano anthu ambiri akuyenda ndiponso kusamukira m’mayiko ena. Choncho tikhoza kulalikira uthenga wa Ufumu kwa anthu amenewa pogwiritsa ntchito kabuku kakuti, Uthenga Wabwino wa Anthu Amitundu Yonse. Kodi inu mumayenda nako kabuku kameneka?

[Chithunzi patsamba 32]

Raúl watenga kabuku kamene kamamuthandiza kuwafika anthu pamtima