Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mukuitanidwa!

Mukuitanidwa!

 Mukuitanidwa!

KODI mukuitanidwa kupita kuti? Kuti mukaone maofesi a nthambi a Mboni za Yehova omwe amatchedwa Beteli. Pali maofesi a nthambi okwana 118 m’mayiko osiyanasiyana. Anthu amene amafika ku Beteli amayamikira kwambiri zimene amaona pa malo amenewa.

Mnyamata wina amene ankaphunzira Baibulo anachita chidwi kuona anthu akutumikira Yehova mwakhama koma mosangalala pa ofesi ya nthambi ku Mexico ndipo anafunsa kuti: “Kodi ndingatani kuti ndidzabwere kudzakhala ndiponso kudzagwira ntchito kuno?” Iye anauzidwa kuti: “Choyamba uyenera kubatizidwa. Kenako ungachite bwino kuyamba kuchita upainiya kapena kuti utumiki wa nthawi zonse wolengeza Ufumu.” Mnyamatayu anachitadi zimene anauzidwazi ndipo pambuyo pa zaka ziwiri anaitanidwa kuti akatumikire ku Beteli ya ku Mexico ndipo wakhala akutumikira kumeneku kwa zaka 20.

Kodi Beteli N’chiyani?

M’chiheberi, mawu akuti Beteli amatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” (Gen. 28:17, 19) Maofesi a nthambi amagwiritsidwa ntchito posindikiza ndi kufalitsa mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo ndiponso kuthandiza mwauzimu mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 100,000 padziko lonse. Amuna ndi akazi pafupifupi 20,000 ochokera m’madera osiyanasiyana ndiponso a chikhalidwe chosiyanasiyana, nthawi zonse amatumikira Yehova ndi abale ndi alongo awo auzimu modzipereka. Akhristu amene akhala akutumikira pa Beteli kwa zaka zambiri amagwira ntchito limodzi ndi achinyamata amphamvu. Madzulo ndiponso kumapeto kwa mlungu, anthu a m’banja la Beteli amachita misonkhano ndi mipingo ya Mboni za Yehova ya pafupi ndi Beteli komanso kugwira nawo ntchito yolalikira. Iwo amagwiritsa ntchito nthawi yawo ina kuphunzira Baibulo ndiponso kuchita zinthu zawo zina.

Anthu a m’banja la Beteli amalandira kandalama kochepa mwezi uliwonse. Iwo amapatsidwa chakudya chabwino ndipo amakhala m’nyumba zaukhondo komanso zabwino. Nyumba za pabeteli sizikonzedwa kuti zizikhala zapamwamba kwambiri. Koma zimakhala zoyenerera. Alendo amachita chidwi ndi nyumba zosamalidwa bwino, malo okongola, kugwira ntchito mwadongosolo ndiponso kukoma mtima ndi mgwirizano wa pa Beteli. Aliyense amagwira ntchito mwakhama koma sikuti amatanganidwa kwambiri moti sangapeze nthawi yocheza ndi anthu. Anthu pa Beteli sasankhana kapena kudziona ngati apamwamba chifukwa cha ntchito imene amagwira. Ntchito iliyonse ya pa Beteli ndi yofunika kwambiri, kaya ikhale yoyeretsa, yokongoletsa malo, yophika, yosindikiza mabuku kapena ya mu ofesi. Atumiki a pa Beteli amagwira  ntchito mogwirizana popititsa patsogolo utumiki wa Mboni za Yehova.​—Akol. 3:23.

Tiyeni Tidziwe Ena Amene Akutumikira pa Beteli

Tiyeni tidziwe anthu ena amene ali m’banja la Beteli la padziko lonse limeneli. Kodi n’chiyani chinawalimbikitsa kuti ayambe utumiki wa pa Beteli? Poyamba tiyeni tione za Mario. Pa nthawi imene anakhala wa Mboni za Yehova Mario ankagwira ntchito yapamwamba kwambiri ku kampani ya magalimoto ya ku Germany ndipo akanatha kulemera kwambiri. Koma atangobatizidwa kumene anadzipereka kuti akagwire ntchito pa Beteli kwa mlungu umodzi m’dziko lawo. Pa nthawi imeneyi anauzidwa kuti agwire nawo ntchito kosindikizira mabuku. Mario anaona kusiyana kwakukulu pakati pa anthu a pa Beteli ndi amene ankagwira nawo ntchito kunja. Choncho anafunsira kuti azitumikira pa Beteli nthawi zonse. Ngakhale kuti achibale ake komanso anzake a kuntchito sanamvetse zimene anasankhazi, Mario akusangalala kwambiri ndi utumiki wa pa Beteli ku Germany.

Anthu ambiri amayamba utumiki wa pa Beteli alibe maphunziro a padera kapena luso la ntchito ina iliyonse. Umu ndi mmene zinalili ndi Abel amene wakhala akutumikira pa Beteli ku Mexico kwa zaka 15. Iye anati: “Ndaphunzira zinthu zambiri pa Beteli. Ndaphunzira kugwiritsa ntchito makina ovuta kwambiri osindikizira mabuku. Ndikudziwa kuti luso limene ndapeza pa ntchitoyi likanatha kundipezetsa ndalama zambiri ndikanakhala kuti sindikugwira ntchito pa Beteli. Koma sindikanasangalala ngati mmene ndikusangalalira panopa. Ndimakhala moyo wosatekeseka, wopanda nkhawa ndiponso wopanda mpikisano ngati mmene zimakhalira m’makampani ambiri. Ndikuona kuti zimene ndaphunzira ndi zabwino kwambiri chifukwa zandithandiza kukhala ndi luso komanso kupita patsogolo mwauzimu. Sindikanapeza madalitso auzimu amenewa ngakhale ndikanapita ku yunivesite ya pamwamba kwambiri.”

Mukadzabwera Kudzaona Nthambi Mudzalimbikitsidwa

Kungopita kukaona ku Beteli kungakulimbikitseni mwauzimu. Izi n’zimene zinachitikira Omar ku Mexico. Mayi ake ndi amene anam’phunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Koma atakwanitsa zaka 17, Omar anasiya kusonkhana ndiponso kulalikira. Iye anayamba khalidwe loipa  komanso kukonda chuma. Iye akugwira ntchito pa kampani ya matelefoni, anali pa gulu la anthu amene anatumizidwa ku Beteli ya ku Mexico kuti akafotokoze mmene makina ena amagwirira ntchito. Omar anati: “Titawauza mmene makinawo amagwirira ntchito, abale anatiyendetsa kuti tione malowo. Zimene ndinaona ndiponso mmene anandisamalirira zinandichititsa kuganiziranso za moyo wotalikirana ndi Yehova umene ndinali kukhala. Nthawi yomweyo ndinayambanso kupezeka pa misonkhano ndiponso kuphunzira Baibulo. Patangopita miyezi 6 kuchokera pamene ndinapita ku Beteli, ndinabatizidwa. Ndikuthokoza Yehova chifukwa ndinalimbikitsidwa nditakaona ku Beteli.”

Masahiko wa ku Japan anakuliranso m’banja la Mboni. Koma kenako anayamba kuona ngati moyo wachikhristu ukumumanitsa zinthu zambiri. Anayamba kutanganidwa kwambiri ndi zochitika za pa sukulu ndipo anasiya kupezeka pa misonkhano ndi kugwira nawo ntchito yolalikira. Masahiko anati: “Tsiku lina banja lathu linaganiza zokaona ku Beteli limodzi ndi anzathu ena achikhristu. Anthu a m’banja langa atandikakamiza kwambiri ndinapita nawo. Nditakaona ku Beteli ndinalimbikitsidwa kwambiri. Ndinasangalala kwambiri kuyenda ndi Akhristu anzanga pa ulendo umenewu ndipo ndinasiyanitsa kwambiri ndi mmene ndinkamvera ndikakhala ndi anzanga ena omwe si Mboni. Ndinayamba kulakalaka moyo wachikhristu ndipo ndinapempha kuti wina azindiphunzitsa Baibulo.” Panopa Masahiko akuchita utumiki wa nthawi zonse mu mpingo wa kwawo.

Mlongo wina anasamuka ku France n’kupita kukagwira ntchito ku Moscow. Atafika kumeneku sanakumane ndi anthu a Yehova ndipo anafooka mwauzimu. Anayamba khalidwe loipa ndipo kenako anakwatiwa ndi munthu wina yemwe sanali Mboni. Kenako mlongo wina wochokera ku France anabwera kudzamuona ndipo anapitira limodzi kukaona Beteli mumzinda wa St. Petersburg ku Russia. Iye analemba kuti: “Anthu ku Beteli anandilandira bwino ndipo izi zinandikhudza kwambiri. Anali malo a bata. Ndinkaoneratu kuti pamalowo pali mzimu wa Yehova. Ndinaona kuti ndinalakwitsa kwambiri posiyana pang’onopang’ono ndi gulu la Yehova. Nditabwerera ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Ndinayambanso kuphunzitsa Baibulo ana anga aakazi awiri ndipo ndinkachita izi ndi mtima wonse.” Kuwonjezera pa thandizo lauzimu limene mlongo wofookayu anapatsidwa, ulendo wake wokaona ku Beteli unamulimbikitsa kwambiri ndipo izi zinathandiza kuti apite patsogolo.

Kodi anthu omwe sadziwa kwambiri Mboni za Yehova amamva bwanji akapita kukaona ku Beteli? M’chaka cha 1988, Alberto yemwe ankakonda kwambiri ndale anapita kukaona Beteli ya ku Brazil. Iye anachita chidwi kwambiri kuona kuti malowa anali aukhondo, zinthu zinkachitika mwadongosolo ndiponso anaona kuti palibe ntchito zachinsinsi zimene zinkachitika pa Beteli. Pa nthawi imene anapita kukaona malo ku Beteli, Alberto anali atangopita kumene kuseminale komwe mulamu wake ankagwira ntchito ngati wansembe. Alberto anaona kusiyana kwakukulu. Alberto anati: “Chilichonse ku seminale chinkachitika mwachinsinsi.” Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anakaona Beteli, iye anavomera kuphunzira Baibulo, anasiya ndale ndipo tsopano akutumikira mu mpingo ngati mkulu.

Bwerani Mudzaone ku Beteli

Anthu ambiri amayesetsa kuti akaone maofesi a nthambi m’dziko lawo. Mwachitsanzo, ku Brazil, Paulo ndi Eugenia anasunga ndalama kwa zaka zinayi kuti ayende kwa masiku awiri ulendo wa pabasi wa makilomita 3,000 kupita kukaona Beteli m’dziko lawo. Iwo anati: “Tinachita bwino kupita pa ulendo umenewu. Panopa tikulidziwa bwino gulu la Yehova. Tikamauza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo ntchito zimene zimachitika ku Beteli, amatifunsa kuti, ‘Kodi inuyo munapitako?’ Masiku ano timayankha kuti inde.”

Kodi pali maofesi a nthambi kapena Beteli m’dziko lanu kapena malo ena a pafupi? Tikukuitanani kuti mukaone malo amenewa. Mudzalandiridwa ndi manja awiri ndipo mudzalimbikitsidwa kupitiriza kutumikira Yehova.

[Chithunzi patsamba 18]

Mario

[Chithunzi patsamba 18]

Abel

[Chithunzi patsamba 18]

Germany

[Chithunzi patsamba 18]

Japan

[Chithunzi patsamba 18]

Brazil