Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ogwirizana Chifukwa cha Chikondi Lipoti la Msonkhano Wapachaka

Ogwirizana Chifukwa cha Chikondi Lipoti la Msonkhano Wapachaka

Ogwirizana Chifukwa cha Chikondi Lipoti la Msonkhano Wapachaka

M’MAWA wa pa October 3, 2009, anthu anasangalala kwambiri m’Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova mumzinda wa Jersey ku New Jersey m’dziko la United States. Anthu oposa 5,000 anasonkhana pa msonkhano wapachaka wa nambala 125 wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Anthu enanso ambirimbiri anamvetsera ndi kuonera pulogalamu ya msonkhanowu m’nyumba zitatu za Beteli ku United States ndiponso ku Canada. Anthu okwana 13,235 omwe ndi ogwirizana chifukwa chokonda Yehova, anasangalala ndi msonkhanowu womwe unatenga maola atatu.

Tcheyamani wa msonkhanowu anali Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira. Iye anatsegulira pulogalamu ya msonkhanowu mwa kuitana gulu la kwaya la anthu otumikira pa Beteli omwe anayimba nyimbo za m’buku latsopano. M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene ankatsogolera nyimbo ndipo anafotokoza mwachidule kufunika kwa nyimbo pa kulambira koona. Kenako anthu onse pa msonkhanowu anapemphedwa kuti aimbe nawo nyimbo zitatu zatsopano. Kwaya ija ndi imene inkayamba kuyimba ndipo kenako ankaimbira limodzi ndi anthu onse. Dongosolo loti pakhale kwayali, linali la pamsonkhano wapaderawu basi, siliyenera kutengedwa ngati chitsanzo pochita misonkhano ya mpingo, yadera kapena yachigawo.

Malipoti Ochokera M’maofesi a Nthambi

Abale a m’Makomiti a Nthambi anapereka malipoti ochokera ku nthambi zisanu zosiyanasiyana. M’bale Kenneth Little ananena kuti nthambi ya Canada posachedwapa iyamba kusindikiza pafupifupi magazini onse a dziko la United States ndi Canada. Iye anati zimenezi zichititsa kuti chiwerengero cha magazini amene nthambiyi imasindikiza chiwonjezeke kwambiri. Kuti zimenezi zitheke, makina atsopano osindikizira azigwiritsidwa ntchito kwa maola 16 patsiku.

M’bale Reiner Thompson anapereka lipoti lonena za ntchito ya Ufumu ku Dominican Republic, ndipo m’bale Albert Olih anafotokoza mmene ntchito yathu ikuyendera ku Nigeria. M’bale Emile Kritzinger wochokera ku Mozambique anafotokoza kuti Mboni za Yehova zinaloledwa kukhala chipembedzo chovomerezeka m’dzikoli mu 1992 patatha zaka zambiri zikuzunzidwa. Chiwerengero cha ofalitsa m’mayiko atatuwa chawonjezeka kwambiri. Nthambi ya Australia imayang’aniranso ntchito ya Ufumu ku East Timor ndipo m’bale Viv Mouritz wochokera ku nthambiyi anafotokoza mmene ntchito yathu ikuyendera ku East Timor.

Makomiti a Bungwe Lolamulira

Kuyambira mu 1976 ntchito zonse za Mboni za Yehova zinayamba kuyang’aniridwa ndi makomiti 6 a Bungwe Lolamulira. Kenako anthu a m’gulu la nkhosa zina anasankhidwa kuti azithandiza Bungwe Lolamulira. Panopa anthu amenewa alipo 23. Anthu 6 mwa anthu amenewa anafunsidwa mafunso pamsonkhanowu. Tikaphatikiza zaka zimene anthu 6 amenewa akhala mu utumiki wanthawi zonse, zikukwana 341 ndipo paavereji aliyense wakhala zaka 57 mu utumiki wanthawi zonse.

M’bale Don Adams amene anayamba kutumikira pa Beteli mu 1943 anafotokoza kuti ogwirizanitsa a m’makomiti asanu ndi amene amakhala mu Komiti ya Ogwirizanitsa. Zimenezi zimathandiza kuti makomiti asanu amenewa azigwira ntchito mogwirizana. Komiti imeneyi imathandiza pakachitika mavuto akuluakulu a mwadzidzidzi, chizunzo, milandu imene ili ku khoti, masoka a chilengedwe ndiponso zinthu zina zofunika kusamaliridwa mwamsanga zokhudza Mboni za Yehova padziko lonse.

M’bale Dan Molchan anafotokoza ntchito ya Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli. Komiti imeneyi imaonetsetsa kuti abale ndi alongo amene akutumikira pa Beteli okwana 19,851 akusamaliridwa mwauzimu ndiponso mwakuthupi. M’bale David Sinclair anafotokoza mmene Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku imagwirira ntchito poonetsetsa kuti nthambi iliyonse ili ndi zinthu zokwanira. Kenako M’bale Robert Wallen yemwe watumikira pa Beteli kwa zaka pafupifupi 60 anafotokoza ntchito ya Komiti ya Utumiki. Komitiyi imayang’anira ntchito yolalikira ya anthu a Yehova ndipo imayang’aniranso mipingo. M’bale William Malenfant anafotokoza ntchito yotamandika imene Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa imachita pokonza mapulogalamu a misonkhano ikuluikulu. Pomaliza, m’bale John Wischuk anafotokoza ntchito ya Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku. Komitiyi imaonetsetsa kuti mabuku ndi magazini athu akonzedwa ndiponso kulembedwa bwino. *

Lemba la Chaka cha 2010 Likunena za Chikondi

Nkhani zitatu zotsatira zinakambidwa ndi abale a m’Bungwe Lolamulira. M’bale Gerrit Lösch anayamba nkhani yake ndi funso lakuti: “Kodi mukufuna kuti anthu ena azikukondani?” Iye anafotokoza kuti munthu aliyense amafuna kukondedwa ndipo timasangalala tikamakondedwa. Timadziwa kuti tili ndi moyo chifukwa cha chikondi. Tikutero chifukwa chakuti chikondi chopanda dyera n’chimene chinachititsa Yehova kutilenga. Timalalikira ndi kuphunzitsa anthu, chifukwa chokonda Yehova.

Timasonyeza chikondi chenicheni osati kwa anansi athu okha, komanso kwa adani athu. (Mat. 5:43-45) Omvera analimbikitsidwa kuganizira zimene Yesu anakumana nazo pofuna kuti ifeyo tipindule. Iye anakwapulidwa, kunyozedwa, kulavuliridwa ndiponso kulasidwa. Ngakhale kuti anakumana ndi zonsezi, iye anapempherera asilikali achiroma amene anamupachika. Kodi zimenezi sizingatichititse kumukonda kwambiri? Kenako m’bale Lösch analengeza lemba la chaka cha 2010 lochokera pa 1 Akorinto 13:7, 8. Lembali ndi lakuti, ‘Chikondi chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha konse.’ Akhristufe tili ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo, kukonda ena ndiponso kukondedwa mpaka kalekale.

Kodi Muli Ngati Galimoto Yotha Mafuta?

M’bale Samuel Herd anayamba nkhani yake ndi fanizo. Tiyerekeze kuti mnzanu wakuuzani kuti muyende naye ulendo wa pagalimoto wa makilomita 50. Mutangokwera galimotolo mukuzindikira kuti lilibe mafuta okwanira. Ndiyeno mukumuuza mnzanuyo za vutolo koma iye akukuuzani kuti musadandaule chifukwa mu thanki muli mafuta okwana malita anayi. Ndiyeno musanapite patali galimotolo likutha mafuta. Kodi ndi nzeru kuyamba ulendo wautali mukudziwa kuti mafuta akutherani panjira ndipo muvutika? Kodi sizingakhale bwino kuonetsetsa kuti muli ndi mafuta okwanira musananyamuke? Mophiphiritsira ifenso tifunika kukhala ndi mafuta okwanira nthawi zonse ndipo mafuta amenewa, ndi kudziwa Yehova.

Choncho, tifunika kuyesetsa kuti nthawi zonse tizikhala ndi mafuta ophiphiritsawa okwanira. Tingachite zimenezi m’njira zinayi. Njira yoyamba ndi kulidziwa bwino Baibulo mwa kuliphunzira tsiku lililonse. Tisamangowerenga ngati nyuzipepala koma tizimvetsa zimene tikuwerengazo. Njira yachiwiri, ndi kuyesetsa kuti tizipindula ndi pulogalamu ya Kulambira kwa Pabanja. Kodi mlungu uliwonse timathira mafuta okwanira mu thanki yathu kapena timangothiramo pang’ono chabe? Njira yachitatu ndiyo kupezeka pa misonkhano nthawi zonse ndiponso kuyesetsa kuti tiphunzirepo kanthu. Njira yachinayi, tiyenera kupeza malo abata kuti tizisinkhasinkha njira za Yehova. Lemba la Salmo 143:5 limati: “Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo.”

“Olungama Adzawala Ngwee”

M’bale John Barr anakamba nkhani yachitatu yomwenso inali yomaliza. M’nkhaniyi, iye anafotokoza fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole. (Mat. 13:24-30, 38, 43) Fanizo limeneli limanena za nthawi “yokolola” pamene “ana a ufumu” akusonkhanitsidwa ndipo namsongole akulekanitsidwa kuti awotchedwe.

M’bale Barr anamveketsa bwino mfundo yakuti ntchito yokololayi siidzachitika mpaka kalekale. Iye anatchula mfundo ya pa lemba la Mateyu 24:34 lomwe limati: “M’badwo uwu sudzatha wonse kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zitachitika.” Iye anawerenga kawiri mawu akuti: “Yesu ayenera ankatanthauza kuti Akhristu odzozedwa amene anali ndi moyo nthawi imene chizindikiro chinayamba kuoneka mu 1914, adzakhala alipo pamene Akhristu odzozedwa ena amene adzaone chiyambi cha chisautso chachikulu azidzabadwa.” Sitikudziwa kuti “m’badwowu” ukhalapo kwa nthawi yaitali bwanji, koma wapangidwa ndi Akhristu odzozedwa a m’magulu awiri amenewa. Ngakhale kuti odzozedwa ndi amisinkhu yosiyanasiyana, magulu awiri onsewa amene apanga m’badwo umenewu akhalapo m’masiku otsiriza. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Akhristu odzozedwa amene akhala ndi moyo limodzi ndi odzozedwa achikulire amene anaona chizindikiro kuyambira mu 1914, sadzafa onse chisautso chachikulu chisanayambe.

“Ana a ufumu” akuyembekezera mphoto yawo kumwamba koma ena tonsefe tiyenera kukhalabe okhulupirika ndiponso kupitiriza kuwala mpaka mapeto. Kunena zoona, tili ndi mwayi waukulu woona “tirigu” akusonkhanitsidwa.

Nyimbo yomaliza itatha, m’bale Theodore Jaracz wa m’Bungwe Lolamulira anapereka pemphero lomaliza. Pulogalamu ya msonkhano wapachaka imeneyi inali yolimbikitsa kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Kuti mumvetse bwinobwino za makomiti 6 a Bungwe Lolamulira, onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 2008, tsamba 29.

[Bokosi patsamba 5]

SUKULU YA AKULU

Pa msonkhano umenewu m’bale Anthony Morris yemwenso ndi wa m’Bungwe Lolamulira analengeza kuti payambika sukulu yophunzitsa akulu. Ku United States sukulu ya akulu imeneyi inayamba mu 2008 ku likulu la maphunziro ku Patterson mumzinda wa New York. Anthu a kalasi la nambala 72 anamaliza maphunziro awo ndipo panopa akulu pafupifupi 6,720 aphunzitsidwa. Koma ntchito idakalipobe. Ku United States kokha kuli akulu oposa 86,000. Choncho, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti sukulu ina itsegulidwe pa December 7, 2009 ku Brooklyn mumzinda wa New York.

Panakonzedwa pulogalamu yakuti oyang’anira madera anayi aziphunzitsidwa kwa miyezi iwiri ku Patterson kuti akhale alangizi. Akamaliza maphunziro awo, azipita ku Brooklyn kukaphunzitsa, ndipo oyang’anira madera ena azibweranso kudzaphunzitsidwa. Amenewanso azipita kukaphunzitsa ku Brooklyn ndipo anayi oyambirira aja azipita kukaphunzitsa ku sukulu imene izichitikira ku Nyumba za Misonkhano ndiponso ku Nyumba za Ufumu. Izi zikhala zikuchitika mpaka pakhale alangizi 12 ophunzitsa masukulu 6 mlungu uliwonse m’Chingelezi ku United States. Kenako alangizi anayi adzaphunzitsidwa kuti aziphunzitsa m’Chisipanishi. Sukuluyi sikulowa m’malo mwa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yomwe ilipo panopa. Cholinga cha sukuluyi n’kuthandiza akulu kuti akule mwauzimu. Nthambi zonse padziko lapansi zidzayamba kukhala ndi sukulu imeneyi pa Nyumba za Misonkhano ndiponso Nyumba za Ufumu m’chaka cha utumiki cha 2011.

[Zithunzi patsamba 4]

Msonkhano wapachaka unayamba ndi nyimbo zochokera m’buku la nyimbo latsopano lakuti “Imbirani Yehova”