Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akazi, N’chifukwa Chiyani Muyenera Kugonjera Amuna Monga Mutu?

Akazi, N’chifukwa Chiyani Muyenera Kugonjera Amuna Monga Mutu?

 Akazi, N’chifukwa Chiyani Muyenera Kugonjera Amuna Monga Mutu?

“Mutu wa mkazi ndi mwamuna.”​—1 AKOR. 11:3.

1, 2. (a) Kodi mtumwi Paulo analemba zotani pa nkhani yokhudza dongosolo la Yehova la umutu ndiponso kugonjera? (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhani ino?

YEHOVA anakhazikitsa dongosolo labwino limene mtumwi Paulo anatchula pamene analemba kuti: “Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna” ndipo “mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akor. 11:3) Nkhani yapitayi inanena kuti Yesu ankaona kuti ndi mwayi kugonjera Mutu wake, Yehova Mulungu, ndipo ankasangalala kuchita zimenezi. Inanenanso kuti mutu wa amuna achikhristu ndi Khristu. Khristu anali wokoma mtima, wodekha, wachifundo ndiponso wopanda dyera pochita zinthu ndi anthu. Amuna mumpingo ayeneranso kusonyeza makhalidwe amenewa pochita zinthu ndi anthu ena makamaka akazi awo.

2 Nanga bwanji akazi? Kodi mutu wawo ndi ndani? Paulo analemba kuti: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna.” Kodi akazi ayenera kuona bwanji mawu ouziridwa amenewa? Kodi mfundo imeneyi imagwiranso ntchito ngati mwamuna ali wosakhulupirira? Kodi kugonjera mwamuna monga mutu kumatanthauza kuti mkazi azingokhala chete osanena maganizo ake pamene zosankha zikupangidwa m’banja?  Nanga mkazi angatani kuti azitamandidwa?

“Ndidzam’pangira Wom’thangatira”

3, 4. N’chifukwa chiyani dongosolo la umutu n’lothandiza m’banja?

3 Mulungu ndi amene anakhazikitsa dongosolo la umutu. Adamu atalengedwa, Yehova Mulungu anati: “Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzam’pangira wom’thangatira iye.” Hava atalengedwa, Adamu anasangalala kwambiri kuona kuti ali ndi mnzake woti azimuthandiza moti ananena kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga.” (Gen. 2:18-24) Adamu ndi Hava anali ndi mwayi wapadera wokhala atate ndi amayi a anthu angwiro omwe akanakhala mosangalala m’paradaiso kosatha padziko lonse.

4 Chifukwa cha kupanduka kwa makolo athu oyambirira, anthu sanalinso angwiro ngati mmene zinalili poyamba m’munda wa Edene. (Werengani Aroma 5:12.) Koma dongosolo la umutu silinasinthe. Mwamuna ndi mkazi akamatsatira dongosolo limeneli amapindula kwambiri ndipo banja lawo limakhala losangalala. Zotsatira zake zimakhala zofanana ndi mmene Yesu ankamvera pa nkhani yogonjera Yehova monga mutu wake. Asanakhale munthu, Yesu ‘ankakondwera pamaso pa Yehova nthawi zonse.’ (Miy. 8:30) Chifukwa cha kupanda ungwiro amuna amavutika kukhala mutu wabwino ndipo akazi zimawavutanso kugonjera bwinobwino. Koma amuna ndi akazi akamayesetsa kuchita zonse zimene angathe, dongosolo la umutu limeneli limathandiza kuti akhale ndi banja losangalatsa.

5. N’chifukwa chiyani anthu okwatirana ayenera kutsatira malangizo opezeka pa Aroma 12:10?

5 Chofunika kwambiri kuti banja likhale losangalala ndi kutsatira malangizo a m’Malemba opita kwa Akhristu onse akuti: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Mwamuna ndi mkazi ayeneranso kuyesetsa ‘kukhala okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.’​—Aef. 4:32.

Ngati Mwamuna Wanu Ali Wosakhulupirira

6, 7. Kodi chingachitike n’chiyani ngati mkazi wachikhristu akhalabe wogonjera mwamuna wake wosakhulupirira?

6 Bwanji ngati mwamuna kapena mkazi wanu satumikira Yehova? Nthawi zambiri amuna ndi amene amakhala osakhulupirira. Zikatere, kodi mkazi ayenera kuona bwanji mwamuna wake? Baibulo limayankha kuti “Inu akazi, muzigonjera amuna anu, kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.”​—1 Pet. 3:1, 2.

7 Mawu a Mulungu amalimbikitsa akazi kukhalabe ogonjera amuna awo osakhulupirira. Khalidwe labwino la mkazi lingachititse mwamuna kuti aganizire za zimene zimapangitsa mkazi kukhala ndi khalidwe labwinolo. Zotsatira zake n’zakuti mwamunayo angayambe kukhala ndi chidwi ndi zimene mkazi wake yemwe ndi Mkhristu amakhulupirira, ndipo m’kupita kwanthawi angaphunzire choonadi.

8, 9. Kodi mkazi wachikhristu angatani ngati mwamuna wake wosakhulupirira sakulabadira khalidwe lake labwino?

 8 Bwanji ngati mwamuna wosakhulupirirayo salabadira zimene mkazi wake amachita? Malemba amalimbikitsa mkazi wokhulupirirayo kusonyeza makhalidwe achikhristu nthawi zonse ngakhale kuti zimenezi zingakhale zovuta. Mwachitsanzo, lemba la 1 Akorinto 13:4 limati: “Chikondi n’choleza mtima.” Choncho mkazi wachikhristu ayenera kupitirizabe kuchita zinthu “modzichepetsa kotheratu ndi mofatsa, moleza mtima” ndipo azilolera mwachikondi zimene zikumuchitikira. (Aef. 4:2) Mzimu woyera, womwe ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito, ungakuthandizeni kukhalabe ndi makhalidwe abwino ngakhale pamene zinthu zili zovuta.

9 Paulo analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Mzimu wa Mulungu umathandiza mwamuna kapena mkazi wachikhristu kuchita zinthu zambiri zomwe sakanazikwanitsa payekha. Mwachitsanzo, munthu akamachitiridwa nkhanza ndi mwamuna kapena mkazi wake angakhale ndi maganizo ofuna kubwezera. Koma Baibulo limalangiza Akhristu onse kuti: “Musabwezere choipa pa choipa; . . . pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’” (Aroma 12:17-19) Nalonso lemba la 1 Atesalonika 5:15 limatilangiza kuti: “Onetsetsani kuti wina asabwezere choipa pa choipa kwa wina aliyense, koma nthawi zonse yesetsani kuchita chabwino kwa wina ndi mnzake ndi kwa ena onse.” Mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Yehova tingakwanitse kuchita zinthu zimene sizingatheke mwa mphamvu yathu. Choncho ndi bwino kupempha mzimu woyera wa Mulungu kuti utithandize pa zimene tikulephera kuchita.

10. Kodi Yesu ankatani anthu ena akamunenera kapena kumuchitira zinthu zoipa?

10 Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa zimene tiyenera kuchita anthu akamatinenera kapena kutichitira zinthu zoipa. Lemba la 1 Petulo 2:23 limati: “Pamene anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” Tikulimbikitsidwa kutengera chitsanzo chake chabwino. Musamakhumudwe chifukwa cha khalidwe loipa la anthu ena. Monga mmene Akhristu onse akulangizidwira, muzikhala “a chifundo chachikulu, a maganizo odzichepetsa. Osabwezera choipa pa choipa kapena chipongwe pa chipongwe.”​—1 Pet. 3:8, 9.

Kodi Akazi Ayenera Kungokhala Chete?

11. Kodi ndi mwayi wapadera uti umene akazi ena achikhristu apatsidwa?

11 Kodi kugonjera amuna monga mutu kumatanthauza kuti akazi safunika kulankhula chilichonse pa nkhani za m’banja kapena nkhani zina? Ayi si choncho. Yehova wapatsa akazi ndi amuna zinthu zambiri zoti achite. Tangoganizani za mwayi wapadera umene anthu a 144,000 ali nawo wokhala mafumu ndi ansembe kumwamba motsogoleredwa ndi Khristu pamene azidzalamulira dziko lapansi. M’gulu limeneli mulinso akazi. (Agal. 3:26-29) Apatu n’zoonekeratu kuti Yehova wapatsa akazi ntchito yaikulu m’gulu lake.

12, 13. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti akazi ankanenera.

12 Mwachitsanzo, m’nthawi za Baibulo akazi ena ankanenera. Pa lemba la Yoweli 2:28, 29 pali ulosi wakuti: “Ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, . . . ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.”

13 Ophunzira a Yesu okwana 120 amene anasonkhana m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E. anali akazi ndi amuna. Mzimu wa Mulungu unatsanulidwa pa anthu onsewo. Choncho Petulo anagwira mawu a ulosi wa mneneri Yoweli ndipo anasonyeza kuti zimene ankachita amuna ndi akazi amenewa, kunali kukwaniritsidwa kwa ulosiwo. Iye anati: “Izi ndi zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yoweli kuti:  ‘Ndipo m’masiku otsiriza,’ akutero Mulungu, ‘ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyanasiyana. Pamenepo ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera. . . .  Ndidzatsanuliranso mbali ya mzimu wanga ngakhale pa akapolo ndi adzakazi anga m’masiku amenewo, ndipo iwo adzanenera.’”​—Mac. 2:16-18.

14. Kodi akazi anachita zotani pothandiza kuti Chikhristu choyambirira chifalikire?

14 M’nthawi ya atumwi akazi anathandiza kwambiri kufalitsa Chikhristu. Iwo ankalalikira za Ufumu wa Mulungu ndipo anachita zinthu zina zothandiza pa ntchito yolalikira. (Luka 8:1-3) Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anatchula za Febe ‘amene ankatumikira mumpingo wa ku Kenkereya.’ Popereka moni kwa antchito anzake, Paulo anatchula akazi okhulupirika angapo kuphatikizapo “Turufena ndi Turufosa, akazi ogwira ntchito mwakhama potumikira Ambuye.” Iye ananenanso kuti, ‘Peresida, wokondedwa wathu anachita ntchito zambiri potumikira Ambuye.’​—Aroma 16:1, 12.

15. Masiku ano, kodi akazi amachita zotani pothandiza kuti Chikhristu chifalikire?

15 Masiku ano, ambiri mwa anthu oposa 7 miliyoni amene akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse, ndi akazi a misinkhu yonse. (Mat. 24:14) Ambiri mwa akazi amenewa akuchita utumiki wanthawi zonse. Ena ndi amishonale pomwe ena akutumikira pa Beteli. Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Ambuye anapatsa mawu: Akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.” (Sal. 68:11) Mawu amenewa akukwaniritsidwa masiku ano. Yehova amayamikira kwambiri ntchito imene akazi amagwira polengeza uthenga wabwino ndiponso pokwaniritsa zolinga zake. Choncho mfundo yakuti akazi achikhristu azigonjera siitanthauza kuti azingokhala chete.

Akazi Awiri Amene Sanangokhala Chete

16, 17. Kodi chitsanzo cha Sara chikusonyeza bwanji kuti akazi sayenera kungokhala chete m’banja?

16 Ngati Yehova wapatsa akazi zinthu zambiri zoti achite, ndiye kuti amuna ayenera kufunsira maganizo kwa akazi awo asanapange zosankha zikuluzikulu. Akamachita zimenezi ndiye kuti akusonyeza nzeru. Malemba amatchula zochitika zingapo pamene akazi analankhula kapena kuchita zinthu ngakhale kuti amuna awo sanalabadire zonena kapena zochita zawo. Taganizirani zitsanzo ziwiri izi.

17 Sara ankauza mobwerezabwereza mwamuna wake Abulahamu kuti achotse mkazi wake wachiwiri limodzi ndi mwana wake chifukwa chakuti sanali kusonyeza ulemu. “Mawuwo anaipira Abulahamu,” koma osati Mulungu. Ndipo Yehova anauza Abulahamu kuti: “Usaipidwe nawo, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mawu ake.” (Gen. 21:8-12) Abulahamu anamvera Yehova ndipo anachita zimene Sara ananena.

18. Kodi Abigayeli anachita chiyani?

18 Taganiziraninso za Abigayeli, mkazi wa Nabala. Pamene Davide ankathawa mfumu ya nsanje, Sauli, anakakhala pafupi ndi ziweto za Nabala. Davide ndi anyamata ake sanatenge chilichonse pa katundu wochuluka wa Nabala yemwe anali wolemera koma m’malo mwake  iwo ankateteza katundu wakeyu. Koma Nabala “anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake,” ndipo ‘anakalipira’ anyamata a Davide. Nabala anali ‘munthu woipa’ ndiponso ‘wopusa.’ Pamene anyamata a Davide mwaulemu anam’pempha Nabala kuti awapatseko zinthu, iye anakana. Kodi Abigayeli anatani atamva zimene zinachitikazi? Popanda kuuza Nabala iye “anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zowotchawotcha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri,” ndipo anazipereka kwa Davide ndi anyamata ake. Kodi pamenepa, Abigayeli anachita zolondola? Inde, chifukwa chakuti Baibulo limati: “Yehova anam’kantha Nabala, nafa.” Ndipo kenako Davide anakwatira Abigayeli.​—1 Sam. 25:3, 14-19, 23-25, 38-42.

‘Mkazi Amene Amatamandidwa’

19, 20. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti mkazi azitamandidwa?

19 Malemba amayamikira akazi okwatiwa amene amachita zinthu mmene Yehova amafunira. Buku la Miyambo limatamanda “mkazi wangwiro,” ndipo limati: “Mtengo wake uposa ngale. Mtima wa mwamuna wake um’khulupirira, sadzasowa phindu. Mkaziyo am’chitira zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake.” Limatinso, “Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake. Ayang’anira mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi. Ana ake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake nam’tama.”​—Miy. 31:10-12, 26-28.

20 Kodi n’chiyani chimachititsa kuti mkazi azitamandidwa? Lemba la Miyambo 31:30 limati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” Kuopa Yehova kumaphatikizapo kugonjera mofunitsitsa dongosolo la umutu limene Mulungu anakhazikitsa. Baibulo limati: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna,” monga zililinso kuti “mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu” ndipo “mutu wa Khristu ndiye Mulungu.”​—1 Akor. 11:3.

Yamikirani Mulungu Chifukwa cha Mphatso Imene Wakupatsani

21, 22. (a) Kodi Akhristu okwatirana ali ndi zifukwa zotani zoyamikira Mulungu chifukwa cha mphatso ya ukwati? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza dongosolo la Yehova la ulamuliro ndiponso umutu? (Onani bokosi pa tsamba 17.)

21 Akhristu okwatirana ali ndi zifukwa zambiri zoyamikira Mulungu. Iwo angamayende mosangalala atagwirana manja. Iwo makamaka ayenera kuthokoza Mulungu chifukwa cha mphatso ya ukwati. Ndipo ukwati umawapatsa mwayi wochitira limodzi zinthu ndiponso kuyenda ndi Yehova. (Rute 1:9; Mika 6:8) Popeza Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati, amadziwa bwino zimene zimafunika kuti okwatirana akhale osangalala. Nthawi zonse, chitani zinthu mogwirizana ndi zimene amafuna, ndipo ngakhale kuti tili m’dziko la mavuto ‘chimwemwe cha Yehova chidzakhala mphamvu yanu.’​—Neh. 8:10.

22 Mwamuna wachikhristu amene amakonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera, amachita umutu wake mwachikondi ndiponso mwachifundo. Amakonda kwambiri mkazi wake woopa Mulungu popeza mkaziyo amam’thandiza ndiponso amam’lemekeza kwambiri. Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti, ukwati wawo wachitsanzo chabwino umalemekeza Yehova Mulungu wathu yemwe ndi woyenera kutamandidwa.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi dongosolo la Yehova ndi lotani pa nkhani ya umutu ndi kugonjera?

• N’chifukwa chiyani anthu okwatirana ayenera kulemekezana?

• Kodi mkazi yemwe ndi Mkhristu ayenera kuchita zinthu motani ndi mwamuna wake wosakhulupirira?

• N’chifukwa chiyani amuna ayenera kufunsa akazi awo asanapange zosankha pa nkhani zikuluzikulu?

[Mafunso]

 [Chithunzi patsamba 17]

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kugonjera Ulamuliro?

Yehova wakhazikitsa dongosolo la ulamuliro ndiponso umutu pakati pa angelo ake komanso anthu. Wachita zimenezi n’cholinga chakuti zinthu ziziyenda bwino pakati pa zolengedwa zake zauzimu ndiponso anthu. Dongosolo limeneli limathandiza angelo ake ndiponso anthu kuti azigwiritsa ntchito ufulu wawo wosankha polemekeza Mulungu komanso kum’tumikira mogwirizana.​—Sal. 133:1.

Mpingo wa Akhristu odzozedwa umazindikira ulamuliro umene Yesu Khristu ali nawo ndiponso kuti iye ndi mutu. (Aef. 1:22,23) Popeza amazindikira ulamuliro wa Yehova, “Mwanayonso adzadziika pansi pa Uyo amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.” (1 Akor. 15:27, 28) Ndiyetu, mpake kuti atumiki a Mulungu odzipereka ayenera kugonjera dongosolo la umutu mumpingo ndiponso m’banja. (1 Akor. 11:3; Aheb. 13:17) Tikamachita zimenezi timapindula chifukwa Yehova amatiyanja ndiponso amatidalitsa.​—Yes. 48:17.

[Chithunzi patsamba 13]

Pemphero lingathandize mkazi wachikhristu wokwatiwa kusonyeza makhalidwe abwino

[Zithunzi patsamba 15]

Yehova amayamikira ntchito imene akazi amagwira popititsa patsogolo zinthu za Ufumu