Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Abale, Feserani Mzimu Ndipo Yesetsani Kuti Muyenerere Udindo

Abale, Feserani Mzimu Ndipo Yesetsani Kuti Muyenerere Udindo

 Abale, Feserani Mzimu Ndipo Yesetsani Kuti Muyenerere Udindo

“Iye amene akufesera mzimu adzakolola moyo wosatha.”​—AGAL. 6:8.

1, 2. Kodi lemba la Mateyo 9:37, 38 likukwaniritsidwa bwanji, ndipo zimenezi zachititsa kuti pafunike chiyani m’mipingo?

PANOPA mukuona zinthu zimene sizidzaiwalika. Ntchito imene Yesu Khristu analosera ikugwirika mokwanira. Yesu anati: “Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” (Mat. 9:37, 38) Yehova Mulungu akuyankha mapemphero okhudza ntchitoyi kuposa ndi kale lonse. M’chaka cha utumiki cha 2009, mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse inawonjezeka ndi 2,031 ndipo inakwana 105,298. Pa avereji anthu okwana 757 ankabatizidwa tsiku lililonse.

2 Chifukwa cha kuwonjezeka kumeneku, pakufunika abale oti azitsogolera ntchito yophunzitsa ndiponso yoweta nkhosa mumpingo. (Aef. 4:11) Kwa zaka zambiri, Yehova waonetsetsa kuti pakhale amuna oyenerera kuti azisamalira nkhosa zake ndipo tikukhulupirira kuti apitirizabe kuchita zimenezi. Ulosi wa pa Mika 5:5 umatitsimikizira kuti m’masiku otsiriza anthu a Yehova adzakhala ndi “abusa asanu ndi awiri” ndiponso “akalonga asanu ndi atatu.” Abusa ndi akalongawa akuimira amuna amene amatsogolera anthu a Yehova.

3. Kodi ‘kufesera mzimu’ kumatanthauza chiyani?

3 Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mukhale ndi mtima wofuna kuyenerera udindo? Chofunika kwambiri ndi ‘kufesera mzimu.’ (Agal. 6:8) Kuchita zimenezi kumafuna kuti tizichita zinthu zimene zingathandize kuti mzimu woyera wa Mulungu uzigwira ntchito bwinobwino pa moyo wathu. Yesetsani kuti ‘musafesere thupi.’ Musalole kuti zinthu ngati kufuna moyo wabwino ndiponso zosangalatsa zikulepheretseni kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Mulungu. Akhristu onse ayenera ‘kufesera mzimu,’ ndipo m’kupita kwa nthawi amuna amene akuchita zimenezi angayenerere udindo mumpingo. Popeza masiku ano pakufunika atumiki othandiza ndi akulu ambiri, nkhani iyi yalembedwera makamaka amuna achikhristu. Choncho, abale tikukulimbikitsani kuganizira mfundo za m’nkhaniyi ndipo pochita zimenezi muzipemphera.

Yesetsani Kuti Mugwire Ntchito Yabwino

4, 5. (a) Kodi amuna obatizidwa akulimbikitsidwa kuti ayesetse kukhala pa maudindo ati mumpingo? (b) Kodi munthu angatani kuti ayenerere udindo?

4 M’bale sangakhale woyang’anira popanda kuchita khama. Iye ayenera kuyesetsa kuti agwire “ntchito yabwino” imeneyi. (1 Tim. 3:1) Ntchito imeneyi imaphatikizapo kutumikira Akhristu anzathu ndiponso kuwathandiza akakhala pa mavuto. (Werengani Yesaya 32:1, 2.) Ngati m’bale akuyesetsa kuti akhale pa udindo ndi zolinga zabwino, sikuti akungofuna kukhala patsogolo pa ena. Koma akufuna kuthandiza ena mwachikondi.

5 Munthu angayenerere kukhala mtumiki wothandiza ndipo kenako woyang’anira, ngati akuyesetsa kukwaniritsa zimene Malemba amanena pa nkhaniyi. (1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9) Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimalalikira mokwanira ndiponso kuthandiza ena kuti azilalikiranso? Kodi ndimalimbikitsa Akhristu anzanga mwa kuwathandiza kuchokera pansi pa mtima? Kodi ndimadziwika  kuti ndine wokonda kuphunzira Mawu a Mulungu? Kodi ndimayesetsa kupereka ndemanga zogwira mtima? Kodi ndimagwira bwino ntchito zimene akulu andipatsa?’ (2 Tim. 4:5) Ndi bwino kuganizira mofatsa mafunso amenewa.

6. Kodi chofunika kwambiri n’chiyani kuti munthu ayenerere maudindo mumpingo?

6 Njira ina imene ingathandize kuti muyenerere udindo mumpingo ndiyo ‘kulola kuti munthu wanu wa mkati akhale wamphamvu, mwa mphamvu ya mzimu wa Mulungu.’ (Aef. 3:16) Kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu mumpingo wachikhristu si nkhani yoti munthu amangosankhidwa. Izi zimachitika ngati munthuyo akuyesetsa kukula mwauzimu. Kodi mungatani kuti mukule mwauzimu? Njira imodzi ndi yakuti muyenera “kupitiriza kuyenda mwa mzimu” ndiponso kusonyeza zipatso zake. (Agal. 5:16, 22, 23) Mukamasonyeza makhalidwe abwino amene angakuthandizeni kusamalira maudindo ena ndiponso mukamagwiritsa ntchito malangizo amene mukupatsidwa, ‘kupita kwanu patsogolo kudzaonekera kwa anthu onse.’​—1 Tim. 4:15.

M’pofunika Kukhala ndi Mtima Wodzimana

7. Kodi kutumikira ena kumafuna chiyani?

7 Kutumikira ena kumafuna khama ndiponso mtima wodzimana. Popeza oyang’anira achikhristu ndi abusa auzimu, amakhudzidwa kwambiri ndi mavuto amene nkhosa zikukumana nawo. Taonani mmene udindo wake wochita ubusa unakhudzira mtumwi Paulo. Iye anauza Akhristu anzake a ku Korinto kuti: “Ndinakulemberani kalata ija ndikusautsidwa ndi kuzunzika kwambiri mu mtima, pamodzi ndi misozi yambiri, osati kuti muchite chisoni, koma kuti mudziwe chikondi chimene ndili nacho makamaka pa inu.” (2 Akor. 2:4) Apa n’zoonekeratu kuti Paulo ankagwira ntchito yake ndi mtima wonse.

8, 9. Perekani zitsanzo za m’Baibulo za amuna amene anasamalira anthu ena.

8 Nthawi zonse mzimu wodzimana wakhala chizindikiro cha amuna amene amagwira ntchito molimbika potumikira anthu a Yehova. Mwachitsanzo, Nowa sanauze anthu am’banja lake kuti: ‘Mukatha kumanga chingalawa, mundiuze  kuti inenso ndilowemo.’ Mose sanauze Aisiraeli ku Iguputo kuti: ‘Aliyense anyamuke, tikakumana pa Nyanja Yofiira.’ Yoswa sananene kuti: ‘Makoma a Yeriko akagwa mundiuze.’ Ndipo Yesaya sanaloze munthu wina n’kunena kuti: ‘Uyo ali apoyo! M’tumizeni ameneyo.’​—Yes. 6:8.

9 Yesu Khristu ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu amene analola mzimu wa Mulungu kumutsogolera. Iye analandira ndi mtima wonse udindo wotumikira anthu monga Mpulumutsi. (Yoh. 3:16) Kodi chikondi cha Yesu chodzimana sichingatilimbikitsenso kukhala odzimana? Pofotokoza mmene amaonera nkhosa, mkulu wina yemwe watumikira nthawi yaitali anati: “Mawu amene Yesu anauza Petulo akuti weta tiana tankhosa tanga, amandikhudza mtima kwambiri. Kwa zaka zambiri, ndaona kuti kuchitira munthu zinthu zinazake ngakhale zazing’ono kumalimbikitsa munthuyo. N’chimodzimodzinso ndi kulankhula mawu achikondi ngakhale atakhala ochepa. Ubusa ndi ntchito imene ndimaikonda kwambiri.”​—Yoh. 21:16.

10. Kodi n’chiyani chingalimbikitse amuna achikhristu kutsanzira Yesu potumikira ena?

10 Pa nkhani ya kusamalira nkhosa za Mulungu, amuna obatizidwa mumpingo amafunitsitsa kusonyeza mzimu umene Yesu anali nawo. Iye anati: “Ndidzakutsitsimutsani.” (Mat. 11:28) Kukhulupirira Mulungu ndiponso kukonda anthu mumpingo kumalimbikitsa amuna achikhristu kuyesetsa kuti agwire ntchito yabwinoyi popanda kuganiza kuti kuchita zimenezi ndi kudzimana mopambanitsa kapena kuti kumafuna zambiri. Bwanji ngati m’bale alibe mtima wofuna kutumikira pa udindo uliwonse? Kodi zingatheke kuti m’bale wotereyu angakhale ndi mtima wofuna kutumikira mumpingo?

Khalani ndi Mtima Wofuna Kutumikira

11. Kodi m’bale angatani kuti akhale ndi mtima wofuna kutumikira ena?

11 Ngati mukukayikira zoti mungakwanitse kutumikira pa udindo winawake, ndi bwino kupempha mzimu woyera. (Luka 11:13) Mzimu wa Yehova ungakuthandizeni kuthetsa nkhawa zilizonse zimene mungakhale nazo pa nkhani imeneyi. Mulungu ndi amene amapereka mtima wofuna kutumikira. Tikutero chifukwa chakuti mzimu wa Yehova ndi umene umalimbikitsa m’bale kuyesetsa kuti akhale pa udindo ndipo umam’patsa mphamvu kuti athe kuchita utumiki umenewu. (Afil. 2:13; 4:13) Choncho, ndi bwino kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi mtima wofuna kulandira udindo wotumikira ena.​—Werengani Salmo 25:4, 5.

12. Kodi munthu angapeze bwanji nzeru zomuthandiza kusamalira udindo umene wapatsidwa?

12 Mwina m’bale sangafune kutumikira chifukwa choganiza kuti kusamalira nkhosa mumpingo n’kovuta kwambiri. Apo ayi angamaganize kuti sadziwa zinthu zambiri zomuthandiza kusamalira bwino maudindo amenewa. Ngati ndi choncho, m’baleyo ayenera kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu ndi mabuku ofotokoza Baibulo kuti apeze nzeru. Angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapatula nthawi yophunzira Mawu a Mulungu ndiponso kupempha Mulungu kuti andipatse nzeru?’ Wophunzira Yakobe analemba kuti: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzam’patsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndi mosatonza.” (Yak. 1:5) Kodi mumakhulupirira mawu ouziridwa amenewa? Poyankha pemphero la Solomo, Mulungu anamupatsa “mtima wanzeru ndi wakuzindikira” umene unamuthandiza kuzindikira pakati pa zabwino ndi zoipa poweruza. (1 Maf. 3:7-14) N’zoona kuti Mulungu sangatichitire zinthu ngati mmene anachitira ndi Solomo poyankha pemphero lake. Komabe, tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu amapatsa nzeru amuna amene apatsidwa udindo mumpingo kuti asamalire bwino nkhosa zake.​—Miy. 2:6.

13, 14. (a) Fotokozani mmene “chikondi chimene Khristu ali nacho” chinakhudzira Paulo. (b) Kodi “chikondi chimene Khristu ali nacho” chiyenera kutikhudza bwanji?

13 Chinthu china chimene chingatithandize kukhala ndi mtima wofuna kutumikira, ndicho kuganizira kwambiri zimene Yehova ndi Mwana wake watichitira. Mwachitsanzo, taonani zimene lemba la 2 Akorinto 5:14, 15 limanena. (Werengani.) Kodi ‘chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza’ bwanji? Chikondi chimene Khristu anasonyeza potifera malinga ndi chifuniro cha Mulungu n’chapadera kwambiri. Pamene tizindikira ndiponso kuyamikira kwambiri chikondi chimenechi, timalimbikitsidwa  kuchitapo kanthu. Chikondi cha Khristu n’chimene chinkatsogolera Paulo. Chinamuthandiza kuti asamachite zinthu modzikonda ndiponso kuti cholinga chake chachikulu chikhale kutumikira Mulungu ndi anthu anzake mumpingo komanso kunja kwa mpingo.

14 Kusinkhasinkha mmene Yesu amakondera anthu kumatithandiza kukhala oyamikira. Tikamatero, timazindikira kuti si bwino kuti tipitirizebe ‘kufesera thupi’ mwa kukhala ndi zolinga zongotipindulitsa ifeyo ndiponso kukhala moyo wongofuna kudzisangalatsa. Koma timasintha zochita pa moyo wathu kuti tiike patsogolo ntchito imene Mulungu watipatsa. Timafuna ‘kutumikira’ abale athu chifukwa chowakonda. (Werengani Agalatiya 5:13.) Tikamaona kuti ndife akapolo n’kumagwira ntchito modzichepetsa pothandiza anthu odzipereka a Yehova, tidzawalemekeza pochita nawo zinthu. Mosakayikira tidzapewa mzimu woipa ndiponso wokonda kuweruza ena umene Satana amalimbikitsa.​—Chiv. 12:10.

Banja Lonse Lifunika Kuyesetsa

15, 16. Kodi anthu a m’banja angathandize bwanji kuti mwamuna ayenerere kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza?

15 Ngati m’bale ali wokwatira ndipo ali ndi ana, akulu akamaona ngati akuyenerera kutumikira monga mtumiki wothandiza kapena mkulu, amaonanso mmene zinthu zilili m’banja lake. Ndithudi, moyo wauzimu wa banja lake ndiponso mbiri imene banjalo lili nayo, zingachititse kuti m’baleyo ayenerere kapena ayi. Zimenezi zikusonyeza udindo umene banja lili nawo pothandiza mwamuna ndiponso tate amene akufuna kutumikira mumpingo monga mtumiki wothandiza kapena mkulu.​—Werengani 1 Timoteyo 3:4, 5, 12.

16 Yehova amasangalala kwambiri mabanja achikhristu akamakhala ogwirizana. (Aef. 3:14, 15) Pamafunika kulinganiza bwino zinthu kuti mutu wa banja uzisamalira bwino udindo wa mumpingo komanso kuyang’anira “bwino” banja lake. Motero akulu ndi atumiki othandiza afunika kuphunzira Baibulo ndi akazi ndiponso ana awo mlungu uliwonse pa Kulambira kwa Pabanja. Iwo ayeneranso kumapeza nthawi yoyenda ndi banja lawo mu utumiki. Nawonso akazi ndi ana afunika kugwirizana ndi zimene mutu wa banja wakonza.

Kodi Mungatumikirenso?

17, 18. (a) Ngati m’bale sakuyenereranso kutumikira paudindo winawake, kodi ayenera kuchita chiyani? (b) Kodi m’bale amene nakhalapo mkulu kapena mtumiki wothandiza ayenera kukhala ndi maganizo otani?

17 Mwina nthawi ina munali mtumiki wothandiza kapena mkulu koma tsopano simukutumikiranso pa udindo umenewo. Mumakonda Yehova ndipo dziwani kuti iye amasamala za inu. (1 Pet. 5:6, 7) Kodi munauzidwa kuti muyenera kusintha zinthu zina? Vomerezani zimene munalakwitsa ndipo yesetsani kusintha mothandizidwa ndi Mulungu. Pewani kumangokhala wokwiya nthawi zonse. Muzichita zinthu mwanzeru ndipo khalani ndi maganizo oyenera. Mbale wina amene anatumikira kwa nthawi yaitali monga mkulu koma pa nthawi ina anasiyitsidwa, ananena kuti: “Ndinaganiza kuti ndisasinthe zimene ndinkachita ndili mkulu monga kupezeka pamisonkhano, kulowa mu utumiki wakumunda ndiponso kuwerenga Baibulo. Ndipo ndinathadi kuchita zimenezi. Ndinaphunzira kukhala woleza mtima, chifukwa poyamba ndinkaganiza kuti pakangotha chaka chimodzi kapena ziwiri ndikhalanso mkulu. Koma panapita zaka pafupifupi 7 kuti ndiyambirenso kutumikira monga mkulu. Pa nthawi imeneyi, malangizo oti ndisafooke koma ndipitirizebe kuyesetsa kuti ndiyenererenso kutumikira, anandithandiza kwambiri.”

18 Ngati umu ndi mmene zinthu zilili ndi inu, musataye mtima. Ganizirani mmene Yehova akudalitsira utumiki wanu ndiponso banja lanu.  Muzilimbikitsa banja lanu mwauzimu, kuchezera amene akudwala ndiponso kulimbikitsa ofooka. Koposa zonse, muziona kuti muli ndi mwayi waukulu chifukwa ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo mukutamanda Mulungu komanso kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu. *​—Sal. 145:1, 2; Yes. 43:10-12.

Onaninso Mmene Zinthu Zilili pa Moyo Wanu

19, 20. (a) Kodi abale obatizidwa onse akulimbikitsidwa kutani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 Masiku ano, pakufunika akulu ndiponso atumiki othandiza ambiri kuposa ndi kale lonse. Choncho, tikulimbikitsa abale onse kuti aonenso mmene zinthu zilili pa moyo wawo n’kudzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani sindikutumikira ngati mkulu kapena mtumiki wothandiza?’ Lolani kuti mzimu wa Mulungu ukuthandizeni kuona nkhani yofunika imeneyi moyenera.

20 Anthu onse mumpingo amapindula ndi mtima wodzimana ndiponso khama limene Akhristu anzawo amasonyeza. Tikamachita zinthu mokoma mtima ndiponso mwachikondi, tidzapeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chotumikira ena ndiponso kufesera mzimu. Koma tiyenera kupewa kumvetsa chisoni mzimu woyera wa Mulungu ndipo m’nkhani yotsatira tidzakambirana mmene tingachitire zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ulosi umene uli pa lemba la Mika 5:5 umatitsimikizira za chiyani?

• Kodi mzimu wodzimana umaphatikizapo chiyani?

• Kodi munthu angatani kuti akhale ndi mtima wofuna kutumikira ena?

• Kodi kugwirizana m’banja n’kofunika bwanji kuti m’bale ayenerere kutumikira monga mtumiki wothandiza kapena mkulu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 25]

Kodi mungatani kuti muyenerere udindo mumpingo?