Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amafuna Kuti Mukhale Otetezeka

Yehova Amafuna Kuti Mukhale Otetezeka

 Yehova Amafuna Kuti Mukhale Otetezeka

NKHONDO yoopsa kwambiri ikadzayamba mwadzidzidzi, Mulungu Wamphamvuyonse adzaonetsetsa kuti anthu onse amene amamumvera, ndi otetezeka. (Yow. 2:32) Koma kunena zoona, Yehova nthawi zonse wakhala akuteteza anthu. Popeza “chitsime cha moyo chili ndi [Iye],” amaona kuti anthu onse ndi amtengo wapatali ndipo ndi ofunika kutetezedwa.​—Sal. 36:9.

Atumiki okhulupirika a Mulungu akale ankaona moyo mmene iye amauonera. Malinga ndi lemba la Genesis 33:18, Yakobo ndi banja lake anayenda ulendo woopsa koma anakafika bwinobwino kumene ankapita. Yakobo anadalira Yehova kuti amuteteze iye ndi banja lake koma anachitanso zimene akanatha kuti ateteze anthu onse amene anayenda naye. (Gen. 32:7, 8; 33:14, 15) Mukamatsatira mfundo za m’Baibulo, inuyo ndiponso anthu ena mungakhale otetezeka. Tiyeni tione mmene kuchita zimenezi kungathandizire anthu ogwira ntchito zomanga Nyumba za Ufumu, ogwira ntchito zofanana ndi zimenezi ndiponso opereka thandizo pakagwa masoka a chilengedwe.

Chilamulo cha Mose Chinkalimbikitsa Anthu Kupewa Ngozi

M’Chilamulo cha Mose, anthu a Mulungu ankafunika kutsatira mfundo zowathandiza kupewa ngozi. Mwachitsanzo, Mwisiraeli aliyense akamanga nyumba, ankafunika kumanga kampanda kakafupi kozungulira denga la nyumba yakeyo. Popeza anthu ankakonda kukhala padenga la nyumba zawo lomwe linkakhala la fulati, kampandako kankathandiza kuti asagwe. (1 Sam. 9:26; Mat. 24:17) Ngati pachitika ngozi chifukwa chakuti mwiniwake wa nyumba sanatsatire lamulo lomanga kampanda, ankakhala ndi mlandu ndi Yehova.​—Deut. 22:8.

Mfundo za Chilamulo zinkagwiranso ntchito ziweto zikavulaza munthu. Ngati ng’ombe yagunda munthu mpaka kumupha, mwiniwake wa ng’ombeyo ankayenera kuipha kuti anthu ena atetezeke. Popeza mwini wa ng’ombeyo sankadya nyama yotereyi kapena kuigulitsa, iye ankaluza kwambiri. Nanga ng’ombe ikavulaza munthu, koma mwiniwake osachita chilichonse pofuna kupewa ngozi ina, kodi chinkachitika n’chiyani? Ngati ng’ombe yomweyo yapha munthu, ng’ombeyo inkaphedwa ndipo mwiniwake ankaphedwanso. Lamulo limeneli linkachititsa kuti aliyense amene anali ndi chizolowezi chosasamalira ziweto zake, asinthe.​—Eks. 21:28, 29.

Chilamulo chinkalimbikitsanso kugwiritsa ntchito bwino zipangizo. Aisiraeli ambiri ankagwiritsa ntchito nkhwangwa kudulira nkhuni. Ngati nkhwangwa yaguluka mwangozi n’kupha munthu amene ali pafupi, wodula nkhuniyo ankathawira kumudzi wopulumukirako. Zikatero ankafunika kukhalabe konko mpaka mkulu wa ansembe adzafe. Choncho munthu wopha munthu mwangoziyo ankasiyana ndi banja lake kwa zaka zambiri. Dongosolo limeneli linkaphunzitsa  Aisiraeli kuti Yehova amaona kuti moyo ndi wopatulika. Munthu amene ankaona moyo mmene Mulungu amauonera, ankaonetsetsa kuti zipangizo zake zili bwino ndiponso ankazigwiritsa ntchito moyenera.​—Num. 35:25; Deut. 19:4-6.

Kudzera m’malamulo amenewa, Yehova anasonyeza bwino kuti ankafuna anthu ake azisamala pochita zinthu akakhala kunyumba ndiponso kwina kulikonse. Munthu akapha kapena kuvulaza mnzake ngakhale mwangozi, ankakhala ndi mlandu ndi Yehova. Maganizo a Yehova pankhani yopewa ngozi sanasinthe. (Mal. 3:6) Amafunabe kuti anthu azipewa zinthu zimene zingawavulaze iwowo ndiponso anthu ena. Izi ndi zofunika kwambiri tikamamanga kapena kukonza malo olambirira Yehova.

 Kupewa Ngozi Pantchito ya Zomangamanga

Kugwira nawo ntchito yomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu, Nyumba za Msonkhano ndiponso maofesi a nthambi, ndi mwayi waukulu. N’chimodzimodzinso ndi kugwira nawo ntchito yopereka thandizo pakagwa masoka. Koma nthawi zonse tikamagwira ntchito ngakhale zing’onozing’ono tiyenera kukhala osamala, chifukwa kupanda kutero tingavulale ndiponso tingavulaze anthu ena. (Mlal. 10:9) Ndithudi tikakhala ndi chizolowezi chogwira ntchito mosamala, tidzapewa ngozi.

Baibulo limati: “Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yawo; kukongola kwa nkhalamba ndi imvi.” (Miy. 20:29) Achinyamata ndi ofunika pa ntchito yofuna mphamvu zambiri. Koma anthu achikulire omwe amadziwa zambiri pa ntchito ya zomangamanga, amagwiritsa ntchito bwino zipangizo pomalizitsa ntchito zina ndi zina zofunika luso. Ndipo anthu ena amene panopa ndi achikulire, pa nthawi imene anali anyamata ankagwira ntchito zofuna mphamvu zambiri. Ngati mwangoyamba kumene kugwira ntchito yodzipereka, muyenera kuona mmene anthu amene anayamba kale akugwirira ntchitoyo, ndipo muzitsatira malangizo awo. Ngati mukufuna kuphunzira, abale amene akudziwa zambiri pa ntchito ya zomangamanga angakuphunzitseni zambiri. Angakuphunzitseni mmene mungagwiritsire ntchito zinthu zoopsa ndiponso mmene  mungamanyamulire zinthu zolemera. Zimenezi zingathandize kuti muzigwira bwino ntchito ndiponso mosangalala.

Nthawi zonse anthu ogwira ntchito ya zomangamanga ayenera kukhala osamala chifukwa chakuti pamalopo zinthu zimasinthasintha. Malo amene nthawi ina anali abwinobwino, pangakhale dzenje. Anzathu ena nthawi zina angaike zinthu monga makwerero, thabwa kapena chitini cha penti pamalo ena. Ngati zimenezi zitachitika, zinthu zimenezi zingakupingeni ndipo mwina mungavulale. Nthawi zambiri malangizo opewera ngozi amati ogwira ntchito pamalo a zomangamanga ayenera kugwiritsa ntchito zinthu zodzitetezera. Zinthu monga magalasi oteteza maso, chipewa choteteza mutu ndiponso nsapato zoyenera, zingakuthandizeni kuti mupewe ngozi pamalo a ntchito. Koma zinthu zimenezi zingakutetezeni ngati mumazisunga bwino ndiponso mumazivala pogwira ntchito.

Zipangizo zambiri zingaoneke ngati zosavuta kugwiritsira ntchito. Koma kuti muzizigwiritsa ntchito mosamala ndiponso mwaluso, mufunika kuphunzitsidwa. Ngati simudziwa kugwiritsa ntchito chipangizo china, mufunika kuuza m’bale yemwe akuyang’anira ntchitoyo. Iye angakonze zoti muphunzitsidwe. Kudzichepetsa ndiponso kudziwa zimene simungathe kuchita, n’kofunika. Ndipotu makhalidwe amenewa ndi ofunika kuti tipewe kudzivulaza ndiponso kuvulaza ena pamalo a ntchito.​—Miy. 11:2.

Pa ntchito ya zomangamanga anthu ambiri amavulala chifukwa cha kugwa. Musanakwere pa makwerero kapena pa katawala, onetsetsani kuti ali bwino ndipo sangachititse ngozi. Ngati muzigwirira ntchito pa katawala kapena pa denga, mungafunike kuvala malamba okutetezani kuti musagwe komanso kutchinga m’mbali kuti musagwe. Ngati mungakhale ndi mafunso okhudza mmene mungagwirire ntchito pamwamba, funsani amene akukuyang’anirani. *

Pamene anthu amene akutumikira Yehova akuwonjezereka padziko lonse, pakufunikanso kumanga Nyumba za Ufumu zambiri komanso zinthu zina zimene zimagwiritsidwa ntchito polambira Yehova. Onse amene amayang’anira ntchito zosiyanasiyana pomanga Nyumba za Ufumu ndi zinthu zina, ali ndi udindo woteteza anthu amene akugwira nawo ntchito omwe ndi nkhosa za mtengo wapatali za Yehova. (Yes. 32:1, 2) Ngati mwapatsidwa mwayi wotsogolera abale ndi alongo pa ntchito yomanga, musaiwale kufunika kopewa ngozi. Onetsetsani kuti malowo akuoneka bwino ndiponso zinthu sizili balalabalala. Ngati ena sakutsatira malangizo opewera ngozi, akumbutseni mosapita m’mbali koma mokoma mtima. Muzionetsetsa kuti ana ndiponso anthu omwe sanaphunzitsidwe, sakufika m’malo amene kumachitika ngozi kawirikawiri. Muzioneratu zinthu zimene zingachititse ngozi, ndipo muzilangiza anthu mmene angagwirire ntchito mosamala. Musaiwale kuti cholinga chathu chimakhala kumaliza ntchito popanda wina kuvulala.

Chikondi N’chofunika

N’zosavuta kuchita ngozi pomanga Nyumba za Ufumu ndiponso zinthu zina zimene zimagwiritsidwa ntchito polambira Yehova. Choncho anthu amene amagwira nawo ntchito zimenezi ayenera kusamala. Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo, kumvera malangizo onse okhudza ntchito yathuyo ndiponso kuganiza bwino, tidzapewa ngozi ndipo ifeyo komanso anthu amene tikugwira nawo ntchito tidzakhala otetezeka.

Kodi n’chiyani chimatipangitsa kuti tiziyesetsa kupewa ngozi? Ndi chikondi. Kukonda Yehova kumatichititsa kuona kuti moyo ndi wamtengo wapatali ngati mmene iye amauonera. Komanso kukonda anthu kumatithandiza kuti tisachite zinthu zimene zingavulaze ena. (Mat. 22:37-39) Choncho, tiyeni tizichita zonse zimene tingathe n’cholinga chakuti anthu amene tikugwira nawo ntchito yomanga akhale otetezeka.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Onani bokosi lakuti “Mmene Mungapewere Ngozi Mukamagwiritsa Ntchito Makwerero” patsamba 30.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 30]

Mmene Mungapewere Ngozi Mukamagwiritsa Ntchito Makwerero

M’chaka cha posachedwapa ku America ogwira ntchito oposa 160,000 anavulala atagwa pa makwerero. Ndipo anthu pafupifupi 150 anafa pa ngozi zoterezi. Kaya mumakhala kapena kugwira ntchito kuti, mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti musagwe mukamagwiritsa ntchito makwerero.

◇ Musamagwiritse ntchito makwerero agwedegwede kapena owonongeka ndipo musamakonze makwerero oterewa, muzingowataya.

◇ Kulemera kwa inuyo ndiponso katundu amene mwatenga kuzikhala kogwirizana ndi makwerero amene mukugwiritsa ntchito.

◇ Ikani makwerero anu pamalo afulati ndiponso olimba. Musamawaike pa zinthu zogwedera monga pa katawala, pa zidebe kapena makatoni.

◇ Nthawi zonse pokwera kapena kutsika, makwerero azikhala kutsogolo kwanu.

◇ Musamaime kapena kukhala pa masitepe awiri apamwamba pa makwerero.

◇ Mukafuna kugwiritsa ntchito makwerero pokwera ndiponso kutsika padenga kapena pamalo ena, makwererowo ayenera kukhala aatali kupitirira dengalo kapena malowo ndi 1 mita. Kuti makwerero asaterereke, muziwamangirira kapena kuika thabwa kutsogolo kwake. Ngati zimenezi sizingatheke, muzipempha munthu wina kuti agwirizire makwererowo pamene inuyo mwakwerapo. Muziwamangirira makwererowo pamalo amene atsamira kuti asamayendeyende.

◇ Musamagwiritse ntchito masitepe a makwerero kupanga katawala.

◇ Kunyanyamphira zinthu muli pa makwerero kungachititse kuti makwererowo azigwedera, choncho musamachite zimenezi. M’malo mwake muzisuntha makwerero kuti akhale pafupi ndi malo amene mukugwirapo ntchito.

◇ Mukamagwira ntchito pa makwerero omwe ali pafupi ndi chitseko chotseka, muziika chizindikiro pa chitsekocho ndiponso muzichikhoma. Ngati simungathe kukhoma chitsekocho, uzani munthu wina kuti aime pafupi ndi chitsekocho kuti azichenjeza anthu ofuna kudutsa.

◇ Munthu mmodzi ndi amene amayenera kukwera pa makwerero pokhapokha ngati makwererowo anapangidwa moti anthu awiri angakwerepo pa nthawi imodzi. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 33 Mfundo zina zokhudza mmene mungagwiritsire ntchito makwerero mungazipeze mu Galamukani! ya Chingelezi ya August 8, 1999 masamba 22 mpaka 24.

[Chithunzi patsamba 29]

M’Chilamulo cha Mose, anthu ankafunika kumanga kampanda padenga la fulati