Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto Amene Takumana Nawo Atithandiza Kudalira Yehova

Mavuto Amene Takumana Nawo Atithandiza Kudalira Yehova

 Mavuto Amene Takumana Nawo Atithandiza Kudalira Yehova

Yosimbidwa ndi Ada Dello Stritto

Ndangomaliza kumene kukopera lemba la tsiku m’kope langa. Ndili ndi zaka 36, koma kuchita zimenezi kwanditengera maola awiri. N’chifukwa chiyani zanditengera nthawi yaitali choncho? Amayi anga afotokoza chifukwa chake.​—Joel

INE ndi mwamuna wanga tinabatizidwa n’kukhala Mboni za Yehova mu 1968. Ndinabereka ana aamuna awiri athanzi, David ndi Marc, ndipo kenako ndinabereka wachitatu, Joel. Iye anabadwa mu 1973 pa chipatala china chomwe chili pafupi ndi tauni ya Binche, yomwe ili pamtunda wa makilomita 60 kumwera kwa mzinda wa Brussels, m’dziko la Belgium. Iye anabadwa masiku ake asanakwane ndipo ankalemera makilogalamu 1.7 okha. Pamene ndinkatuluka m’chipatala, Joel anatsala kuti anenepeko.

Patapita milungu ingapo, mwana wathu sankasintha ndipo ine ndi mwamuna wanga Luigi, tinapita naye kwa dokotala wa ana. Dokotala atamaliza kumuyeza Joel, ananena kuti: “Pepani kwambiri. Mwana wanuyu akuoneka kuti ali ndi mavuto ambiri amene azichimwene ake alibe.” Tonse tinakhala chete kwa nthawi yaitali. Pa nthawi imeneyi ndinazindikira kuti mwana wathu ali ndi matenda aakulu. Kenako dokotalayu anatengera mwamuna wanga pambali n’kumuuza kuti: “Mwana wanu ali ndi matenda oopsa kwambiri (trisomy 21).” Matenda amenewa munthu amabadwa nawo ndipo amachititsa kuti azichedwa kuphunzira zinthu.

Titakhumudwa ndi zimene dokotalayu anapeza, tinaganiza zokaonananso ndi dokotala wina. Dokotala ameneyu anamuyeza bwinobwino Joel kwa nthawi yokwana pafupifupi ola lathunthu, koma pa nthawi yonseyi sananene kanthu. Kwa ine ndi Luigi, nthawi imeneyi inali yaitali kwambiri. Kenako, dokotalayu anatiyang’ana n’kunena kuti: “Mwana wanuyu azidalira kwambiri inuyo.” Ndiyeno, mokoma mtima anati: “Koma Joel adzakhala wosangalala chifukwa makolo akenu mumamukonda kwambiri.” Nditakhudzidwa kwambiri, ndinamunyamula bwinobwino ndipo tinapita naye kunyumba. Pa nthawi imeneyi n’kuti ali ndi miyezi iwiri.

Misonkhano ya Mpingo Ndiponso Utumiki wa Kumunda Zinatilimbikitsa Kwambiri

Joel atamuyezanso anapeza kuti alinso ndi vuto la mtima ndiponso matewe. Chifukwa choti mtima wake unali waukulu kwambiri, unkagunda mapapo ndipo izi zinkachititsa  kuti azidwaladwala. Pasanapite nthawi yaitali, ali ndi miyezi inayi, anayamba kudwala chibayo ndipo tinabwereranso kuchipatala komwe anakamugoneka m’chipinda chayekha. Zinali zopweteka kwambiri kuona mmene ankavutikira. Tinkalakalaka kumunyamula ndi kumusisita, koma kwa milungu 10, sitinkaloledwa n’kumugwira komwe. Nthawi imeneyi inali yosautsa kwambiri. Ine ndi Luigi tinkangoyang’ana zimene zinkachitika, kukumbatirana ndiponso kupemphera.

Pa nthawi yovuta imeneyi, tinapitirizabe kupezeka pamisonkhano limodzi ndi David ndi Marc. Pa nthawiyi n’kuti David ali ndi zaka 6 ndipo Marc ali ndi zaka zitatu. Tikakhala pa Nyumba ya Ufumu tinkaona ngati Yehova watinyamula m’manja mwake. Tikakhala ndi abale ndi alongo athu, tinkaona kuti taika nkhawa zathu kwa Yehova ndipo tinkakhala ndi mtendere wa mumtima. (Sal. 55:22) Ngakhale manesi amene ankasamalira Joel ananena kuti ankaona kuti kupezeka pamisonkhano kunkatithandiza kuti tiziona zinthu moyenera.

Pa nthawi imeneyi, ndinapemphanso Yehova kuti andilimbikitse kuti ndizitha kupita mu utumiki wa kumunda. M’malo mongokhala panyumba n’kumalira, ndinkafuna kukambirana ndi anthu kuwauza mmene kukhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti m’dziko latsopano simudzakhala matenda, kumandithandizira. Nthawi iliyonse ndikapita mu utumiki, ndinkaona kuti Yehova wayankha mapemphero anga.

“Zimenezi N’zodabwitsa Kwambiri”

Tinasangalala kwambiri tsiku limene tinatuluka m’chipatala ndi Joel n’kupita naye kunyumba. Koma chisangalalochi sichinapitirire chifukwa tsiku lotsatira, Joel anadwala kwambiri ndipo tinathamangira naye kuchipatala. Madokotala atamuyeza, ananena kuti: “Joel amwalira pakangotha miyezi 6.” Patapita miyezi iwiri, Joel ali ndi miyezi pafupifupi 8, anadwala kwambiri ndipo zimenezi zinatichititsa kuganiza kuti zimene ananena madokotala zija, ndi zoona. Dokotala wina anakhala pafupi nafe ndipo anati: “Pepani kwambiri. Palibenso chomwe tingachite.” Ndipo anapitiriza kuti: “Zafikapa, ndi Yehova yekha amene angamuthandize.”

Ndinabwerera kuchipinda kumene Joel anagonekedwa. Ngakhale kuti ndinali ndi nkhawa ndiponso ndinali wotopa kwambiri, sindinafune kuchoka pafupi ndi bedi lake. Alongo angapo ankasinthana kukhala nane popeza Luigi ankasamalira ana athu awiri aja. Patapita mlungu umodzi, Joel mwadzidzidzi anadwala mtima. Manesi anathamangira m’chipindachi, koma palibe chimene akanachita kuti am’thandize. Patapita mphindi zingapo, nesi wina mokoma mtima anati, “Basi wamwalira . . . ” Mawu amenewa anandifoola kwambiri, ndiyamba kulira mokweza ndipo ndinatuluka m’chipindacho. Ndinayesetsa kupemphera kwa Yehova, koma ndinkalephera kufotokoza mmene mtima wanga umapwetekera. Patapita mphindi 15, nesi wina anafuula kuti, “Joel akutsitsimuka.” Anandigwira pa mkono n’kundiuza kuti, “Bwera udzamuone.” Nditabwerera kumene Joel anali, ndinapeza kuti mtima wake wayambanso kugunda. Pasanapite nthawi, uthenga woti sanamwalire unafalikira mwamsanga. Manesi ndi madokotala ambiri anabwera kudzamuona, ndipo ambiri ankanena kuti, “Zimenezi n’zodabwitsa kwambiri.”

Ali ndi Zaka Zinayi, Anayamba Kuyenda

Pa zaka zoyambirira za moyo wa Joel, dokotala ankatiuza mobwerezabwereza kuti: “M’pofunika kuti Joel muzimukonda  kwambiri.” Kuyambira pamene Joel anabadwa, Yehova wakhala akutisamalira mwachikondi, choncho ine ndi Luigi tinkafuna kuti mwana wathu tizimukondanso kwambiri. Tinali ndi mipata yambiri yochita zimenezi chifukwa tinkafunika kumuthandiza pa chilichonse.

Pa zaka 7 zoyambirira, Joel ankadwala matenda enaake chaka chilichonse. Miyezi ya pakati pa October ndi March, ankadwaladwala ndipo tinkangokhalira kupita naye kuchipatala. Pa nthawi imeneyinso, ndinkayesetsa kupeza nthawi yosamalira David ndi Marc. Iwonso ankatithandiza kwambiri kusamalira Joel ndipo zimenezi zinathandiza kwambiri. Mwachitsanzo, madokotala angapo anatiuza kuti Joel sadzatha kuyenda. Koma tsiku lina, Joel ali ndi zaka zinayi, Marc anamuuza kuti, “Yenda Joel, asonyeze amayi kuti nawenso ungathe kuyenda.” Ndinadabwa kwambiri kuona Joel atayamba kuyenda. Tinasangalala kwambiri ndipo tinapemphera kwa Yehova kumuyamikira kuchokera mumtima. Nthawi zonse, Joel akachita chinthu chilichonse chosonyeza kuti akuchita bwino, tinkamuyamikira kwambiri.

Kuphunzitsa Joel Kuyambira Ali Wakhanda Kunakhala ndi Zotsatira Zabwino

Nthawi zambiri tinkayesetsa kupita ndi Joel ku Nyumba ya Ufumu. Pofuna kum’teteza ku tizilombo toyambitsa matenda, tinkamuika m’chikuku chapadera chomwe chinali chokutidwa ndi pepala loonekera m’kati. Koma ngakhale kuti ankakhala m’chikuku chimenechi, iye ankasangalala kupezeka pamisonkhano.

Abale ndi alongo athu ankatilimbikitsa, kutikonda ndiponso ankatithandiza kwambiri. Nthawi zambiri, m’bale wina ankatikumbutsa mawu opezeka pa Yesaya 59:1, akuti: “Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake silili logontha, kuti silingamve.” Mawu olimbikitsa amenewa anatithandiza kukhulupirira Yehova.

Pamene Joel ankakula, tinkayesetsa kumuphunzitsa kuti azikonda kwambiri kutumikira Yehova. Nthawi zonse tikamalankhula naye za Yehova, tinkalankhula mwa njira yoti timuthandize kukhala paubwenzi wolimba ndi Atate wake wa kumwamba. Tinapempha Yehova kuti adalitse khama lathu kuti zimene tinkamuphunzitsa zikhale ndi zotsatira zabwino.

Pamene Joel ankakwanitsa zaka 13, tinasangalala kwambiri kuona kuti ankakonda kuuza anthu amene ankakumana nawo choonadi cha m’Baibulo. Ali ndi zaka 14, anapangidwa opaleshoni ndipo pamene ankachira ndinasangalala kwambiri atandifunsa kuti, “Amayi, kodi adokotala ndingawapatse buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo?” Patangopita zaka zochepa, Joel ankafunika kuchitidwa opaleshoni ina. Tinkaganiza kuti mwina sakhala moyo akachitidwa opaleshoniyi. Asanayambe kumupanga opaleshoni, iye anapatsa adokotala kalata imene tinalemba naye limodzi. Kalatayi inkafotokoza zimene Joel amakhulupirira pa nkhani ya magazi. Adokotala anam’funsa kuti, “Kodi ukugwirizana ndi zimenezi?” Joel anayankha molimba mtima kuti, “Inde ndikugwirizana nazo.” Tinasangalala kwambiri poona kuti mwana wathu amakhulupirira Mlengi ndiponso ali ndi mtima wofuna kum’sangalatsa. Ogwira ntchito pachipatalachi anatithandiza kwambiri ndipo tinayamikira kwambiri zimenezi.

 Mmene Joel Anapitira Patsogolo Mwauzimu

Ali ndi zaka 17, Joel anasonyeza kudzipereka kwa Mulungu mwa kubatizidwa m’madzi. Sitidzaiwala tsiku limeneli. Timasangalala kwambiri tikamaona mmene akupitira patsogolo mwauzimu. Kuyambira nthawi imeneyo, sanabwerere m’mbuyo pa nkhani yokonda Yehova ndiponso choonadi. Ndipotu, Joel amakonda kunena kuti, “Choonadi ndiye moyo wanga.”

Atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 19, Joel anaphunzira kuwerenga ndi kulemba. Koma panafunika khama kwambiri kuti achite zimenezi. Akakwanitsa kulemba mawu alionse tinkaona kuti akupita patsogolo. Kuyambira nthawi imeneyo, m’mawa uliwonse amachita lemba la tsiku pogwiritsa ntchito kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Akatero, amakopera lemba la tsikulo m’kope lake lomwe panopo lili ndi malemba ambiri ochititsa chidwi.

Pa masiku a misonkhano, Joel amaonetsetsa kuti tifike mofulumira pa Nyumba ya Ufumu chifukwa amafuna azipereka moni kwa onse amene akulowa m’Nyumba ya Ufumu. Amasangalala kuyankha pamisonkhano komanso kuchita zitsanzo. Iye amathandizanso kuyendetsa maikolofoni ndipo amagwiranso ntchito zina. Mlungu uliwonse, akakhala kuti akupezako bwino, amapita nafe mu utumiki wa kumunda. M’chaka cha 2007, Joel analengezedwa pampingo kuti waikidwa kukhala mtumiki wothandiza. Tinasangalala kwambiri moti tinagwetsa misozi. Limenelitu linali dalitso lochokera kwa Yehova.

Timaona Kuti Yehova Akutithandiza

M’chaka cha 1999 tinakumananso ndi vuto lina. Galimoto yathu inaombedwa ndi galimoto ina yomwe dalaivala wake ankayendetsa mosasamala, ndipo Luigi anavulala kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti mwendo wake umodzi udulidwe, ndipo anamuchita maopaleshoni angapo pa fupa lamsana. Apanso tinadalira Yehova, ndipo tinkaona kuti iye amathandizadi atumiki ake. (Afil. 4:13) Ngakhale kuti Luigi ndi wolumala, timayesetsa kuona zabwino zimene angathe kuchita. Popeza sali pantchito yolembedwa, amakhala ndi nthawi yambiri yosamalira Joel. Zimenezi zimandithandiza kukhala ndi nthawi yochuluka yochita zinthu zauzimu. Zathandizanso kuti Luigi azikhala ndi nthawi yambiri yosamalira banja lathu mwauzimu ndiponso mpingo. Iye akupitirizabe kutumikira monga wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu.

Chifukwa cha mavuto amene takumana nawo, taphunzira kuchitira zinthu pamodzi monga banja. Taphunziranso kukhala ololera ndi kupewa mzimu wofuna zambiri. Tikakhumudwa timapemphera kwa Yehova ndipo timam’fotokozera mmene tikumvera. Koma n’zomvetsa chisoni kuti pamene ana athu David ndi Marc anakula n’kuchoka panyumba, kenako anasiya kutumikira Yehova. Timayembekezera kuti nthawi ina adzabwereranso kwa Yehova.​—Luka 15:17-24.

Pa zaka zonsezi, taona kuti Yehova amatithandiza ndipo taphunzira kum’dalira pa vuto lililonse limene tingakumane nalo. Mawu opezeka pa Yesaya 41:13 ndi ofunika kwambiri kwa ife. Lembali limati: “Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, usaope ndidzakuthandiza iwe.” Timalimbikitsidwa kwambiri kudziwa kuti Yehova wagwira molimba dzanja lathu. Ndithudi, mavuto amene takumana nawo atithandiza kudalira Atate wathu wa kumwamba, Yehova.

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Joel ali ndi amayi ake, a Ada

[Chithunzi patsamba 18]

Ada, Joel ndi Luigi

[Chithunzi patsamba 19]

Joel amasangalala kupereka moni kwa abale ndi alongo pa Nyumba ya Ufumu