Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

• N’chifukwa chiyani Mesiya anafunika kufa?

Imfa ya Yesu inasonyeza kuti munthu wangwiro angakhalebe wodzipereka kwa Mulungu ngakhale atayesedwa kwambiri. Ndiponso, iye analipirira chilango cha uchimo chimene mbadwa za Adamu zinatengera kwa makolo awo, ndipo zimenezi zinatsegula njira ya ku moyo wosatha.​—12/15, masamba 22-23.

• Kodi n’chiyani chingathandize munthu kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya kumwa mowa?

Kupemphera ndiponso kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni. Kudziletsa, kusasintha zimene mwatsimikiza kuchita, ndiponso kucheza ndi anthu akhalidwe labwino n’kofunika kwambiri. Munthu amene wasankha kumwa mowa ayenera kudziikira malire ndiponso kuzindikira nthawi imene ayenera kukana.​—1/1, masamba 7 mpaka 9.

• Kodi mungachite chiyani kuti muzilankhula ndi ana momasuka?

Kuti muzilankhula momasuka ndi ana pamafunika zambiri. Pamafunika kuwafunsa mafunso ndi kumvetsera mayankho awo moleza mtima. Makolo ambiri amaona kuti nthawi yakudya, ndi nthawi yabwino kulankhulana.​—1/15, masamba 18 ndi 19.

• Popeza Yehova ndi wangwiro, kodi amamva chisoni m’njira yotani?

Nthawi zina, Mulungu amasintha mmene amaonera anthu. Mwachitsanzo, kangapo konse Aisiraeli anasiya Yehova n’kuyamba kutsatira milungu ina. Chifukwa cha zimenezi, Yehova anasiya kuwateteza. Komabe, anthuwa atazindikira kulakwa kwawo, n’kupempha Mulungu kuti awathandize, Yehova anasintha mmene ankawaonera, kapena kuti ‘anamva chisoni.’ (Ower. 2:18)​—2/1, tsamba 21.

• Kodi munthu angasankhe kubatizidwanso pa zifukwa zotani?

Angatero ngati panthawi imene ankabatizidwa, ankachita mwamseri zinazake zoipa moti akanakhala kuti ndi wobatizidwa kale, akanayenera kuchotsedwa.​—2/15, tsamba 22.

• Kodi ndi zifukwa zitatu zolakwika ziti zimene anthu ena amanena kuti zimawachititsa kusaona mtima?

Anthu ena amaganiza kuti kuba chifukwa cha umphawi sikulakwa. Ndipo ena amanena kuti kuba sikulakwa chifukwa chakuti “aliyense amaba.” Ena sabweza zinthu zimene atola poganiza kuti Mulungu “sapatsa pamanja.” Koma Baibulo silivomereza zifukwa zonsezi.​—3/1, masamba  12 mpaka 14.

• M’fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole, kodi kufesa, kapena kuti kubzala mbewu zabwino kumaimira chiyani?

Yesu yemwe ndi “Mwana wa munthu” ankalima munda panthawi ya utumiki wake padziko lapansi. Ndiyeno kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., mbewu zabwino zinayamba kufesedwa pamene Akhristu ankadzozedwa kukhala ana a Mulungu, omwe ndi ana a Ufumu.​—3/15, tsamba 20.

• Kodi tirigu wophiphiritsa wa m’fanizo la Yesu, akusonkhanitsidwa bwanji munkhokwe ya Yehova? (Mat. 13:30)

Zimenezi zikuchitika kwa nthawi yaitali m’nthawi ya mapeto a dongosolo la zinthu. Ana a Ufumu odzozedwa, omwe ndi tirigu wophiphiritsa, akusonkhanitsidwa munkhokwe ya Yehova pamene akusonkhanitsidwa mumpingo wachikhristu kapena pamene akulandira mphoto yawo kumwamba.​—3/15, tsamba 22.

• Kodi ndani anasankha mabuku ovomerezeka a Malemba Achigiriki Achikhristu?

Silinali bungwe la tchalitchi kapena mtsogoleri wa chipembedzo. Koma Akhristu oona amene mzimu woyera wa Mulungu unawatsogolera ndi omwe anazindikira malemba amene analidi ouziridwa. Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yakuti imodzi mwa mphatso za mzimu zimene ankalandira mpingo wachikhristu utangoyamba kumene, inali “kuzindikira mawu ouziridwa.” (1 Akor. 12:4, 10)​—4/1, tsamba 28.