Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi lemba la Ezekieli 18:20 limene limati “mwana sadzasenza mphulupulu za atate wake,” limatsutsana ndi la Eksodo 20:5 limene limati Yehova amalanga “ana chifukwa cha atate awo”?

Malembawa satsutsana. Lemba linali limasonyeza kuti munthu aliyense adzayankha mlandu wa zochita zake, ndipo linalo likusonyeza mfundo yoti zoipa zimene munthu angachite zingakhudze ana ake.

Tikaganizira nkhani yonse ya Ezekieli chaputala 18 timaona kuti mfundo yake yaikulu ndi yakuti, munthu aliyense adzadziyankhira yekha mlandu wa zochita zake. vesi 4 limati: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” Nanga bwanji munthu “akakhala wolungama, nakachita chiweruzo ndi chilungamo”? Iye “adzakhala ndi moyo ndithu.” (Ezek. 18:5, 9) Choncho, munthu akafika msinkhu woti angathe kusankha yekha zochita, amaweruzidwa “monga mwa njira zake.”​—Ezek. 18:30.

Chitsanzo cha mfundo imeneyi ndi zimene zinachitikira Mlevi wina dzina lake Kora. Pamene Aisiraeli anali m’chipululu, Kora anayamba kusakhutira ndi utumiki wake. Iye ndi anthu ena anapandukira Mose ndi Aroni, anthu amene ankaimira Yehova, chifukwa iwo ankafuna kuti azigwiranso ntchito za ansembe. Chifukwa chakuti Kora ndi anthu amene anapanduka naye anali odzikuza n’kumafuna udindo umene sanayenerere, Yehova anawawononga.  (Num. 16:8-11, 31-33) Koma ana a Kora sanapanduke nawo. Choncho, Mulungu sanawalange chifukwa cha tchimo la bambo awo. Chifukwa chakuti anali okhulupirika kwa Yehova, iwo sanawonongedwe.​—Num. 26:10, 11.

Nanga bwanji chenjezo limene likupezeka pa Eksodo 20:5, lomwenso ndi mbali ya Malamulo Khumi? Apanso tiyeni tiganizire nkhani yonse. Yehova anayambitsa pangano la Chilamulo ndi mtundu wa Isiraeli. Atamva mfundo zonse zokhudza panganolo, Aisiraeli anayankhira pamodzi kuti: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.” (Eks. 19:5-8) Motero mtundu wonsewo unakhala paubwenzi wapadera ndi Yehova. Choncho mawu a pa Eksodo 20:5 ankakhudza kwenikweni mtundu wonsewu.

Pa nthawi imene Aisiraeli anali okhulupirika kwa Yehova, mtundu wonsewo unkapindula ndipo unkadalitsidwa kwambiri. (Lev. 26:3-8) Koma mtundu wa Isiraeli ukasiya Yehova n’kumalambira milungu yonyenga, iye ankasiya kuudalitsa ndi kuuteteza ndipo unkavutika koopsa. (Ower. 2:11-18) N’zoona kuti panali anthu ena amene anali ndi mtima wosagawanika ndipo ankatsatira malamulo a Mulungu ngakhale kuti mtunduwo unkalambira mafano. (1 Maf. 19:14, 18) N’zachidziwikire kuti anthu okhulupirikawa ankapeza mavuto chifukwa cha machimo a mtunduwu, komabe Yehova ankawakomera mtima.

Aisiraeli atasiya kutsatira mfundo za Yehova, moti anthu amitundu ina n’kuyamba kunyoza dzina lake, Yehova anawalanga mwa kulola kuti atengedwe ukapolo ku Babulo. Chilangochi chinakhudza munthu aliyense payekha ndiponso mtundu wonse. (Yer. 52:3-11, 27) Baibulo limasonyeza kuti kuchimwa kwa mtundu wa Isiraeli kunali kwakukulu moti machimo a makolo awo anakhudza mibadwo yoposa itatu. Ndipo zimenezi n’zogwirizana ndi zimene lemba la Eksodo 20:5 limanena.

Mawu a Mulungu amafotokozanso nkhani zokhudza mabanja ena amene anakhudzidwa chifukwa cha khalidwe loipa la makolo. Eli, yemwe anali mkulu wa ansembe, anachimwira Yehova mwa kulola ana ake omwe anali “oipa” kuti akhalebe ansembe. (1 Sam. 2:12-16, 22-25) Eli ankalemekeza kwambiri ana ake kuposa Yehova. Chifukwa cha zimenezi, Mulungu ananena kuti anthu a m’banja la Eli sazikhalanso akulu a ansembe ndipo izi zinayambira pa Abyatara yemwe anali mdzukulu wa mdzukulu wake. (1 Sam. 2:29-36; 1 Maf. 2:27) Mfundo ya lemba la Eksodo 20:5 ikusonyezedwanso ndi chitsanzo cha Gehazi. Namani yemwe anali mkulu wa asilikali a Aaramu atachiritsidwa, Gehazi anagwiritsa ntchito molakwa udindo wake wotumikira Elisa n’cholinga chakuti apeze chuma. Yehova anapereka chiweruzo kudzera mwa Elisa pamene ananena kuti: “Khate la Namani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire.” (2 Maf. 5:20-27) Choncho, tchimo la Gehazi linachititsa kuti mbadwa zake zivutike.

Popeza kuti Yehova ndi Mlengi ndiponso Wopatsa moyo, iye ali ndi ufulu wopereka chilango chimene akuchiona kuti n’choyenera ndiponso cholungama. Zitsanzo tatchulazi, zikusonyeza kuti ana kapena mbadwa za munthu zingavutike chifukwa cha tchimo la kholo lawo. Komabe Yehova ‘amamva kufuula kwa ozunzika’ ndipo anthu amene moona mtima amapemphera kwa iye, amawayanja ndiponso amawathandiza.​—Yobu 34:28.

[Chithunzi patsamba 29]

Kora ndiponso anthu amene anapanduka naye analangidwa chifukwa cha zochita zawo