Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaona Kuti Yehova Ndi Atate Wanu?

Kodi Mumaona Kuti Yehova Ndi Atate Wanu?

 Kodi Mumaona Kuti Yehova Ndi Atate Wanu?

WOPHUNZIRA wina wa Yesu atapempha kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera,” Yesuyo anayankha kuti: “Mukamapemphera muziti, ‘Atate, dzina lanu liyeretsedwe.’” (Luka 11:1, 2) Yesu akanafuna akanatchula Yehova ndi maina apamwamba monga “Wamphamvuyonse,” ‘Mlangizi Wamkulu,’ “Mlengi,” “Nkhalamba ya kale lomwe” kapena “Mfumu yamuyaya.” (Gen. 49:25; Yes. 30:20; 40:28; Dan. 7:9; 1 Tim. 1:17) Komano n’chifukwa chiyani Yesu anasankha kugwiritsa ntchito mawu akuti “Atate”? Mwina n’chifukwa chakuti ankafuna kuti tikamapemphera kwa Yehova yemwe ndi wamkulu m’chilengedwe chonse, tizikhala ngati mmene mwana amachitira akamalankhula ndi bambo ake omwe amamukonda kwambiri.

Koma anthu ena zimawavuta kwambiri kuona kuti Mulungu ndi Atate wawo. Mkhristu wina dzina lake Atsuko * anati: “Ngakhale kuti panali patatha zaka zambiri nditabatizidwa, zinkandivutabe kuti ndikhale paubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso kuti ndizipemphera kwa iye monga Atate wanga.” Pofotokoza chifukwa chake anali ndi maganizo amenewa, iye anati: “Sindikukumbukira nthawi imene bambo anga anandisonyezapo chikondi.”

Masiku otsiriza ano omwe ndi ovuta, “chikondi chachibadwa” chimene munthu amafuna kwa bambo wake chikusowa kwambiri. (2 Tim. 3:1, 3) Motero n’zosadabwitsa kuti anthu ena amakhala ndi maganizo ngati a Atsuko. Komabe n’zolimbikitsa kudziwa kuti pali zifukwa zomveka zoti tiziona kuti Yehova ndi Atate wathu wachikondi.

Yehova Amatipatsa Zinthu Mwachikondi

Kuti tiziona kuti Yehova ndi Atate wathu, tiyenera kumudziwa bwino kwambiri. Yesu anati: ‘Palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate yekha, komanso palibe amene akum’dziwa bwino Atate koma Mwana yekha ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atateyo.’ (Mat. 11:27) Njira yabwino kwambiri imene ingatithandize kudziwa kuti Yehova ndi Atate wotani, ndiyo kuganizira zimene Yesu ananena zokhudza Mulungu woona. Ndiye, kodi Yesu anaphunzitsa zotani zokhudza Atate?

Yesu ankadziwa kuti Yehova ndiye anam’patsa moyo, n’chifukwa chake anati: “Ndili ndi moyo chifukwa cha Atate.” (Yoh. 6:57) Nafenso timadziwa kuti tili ndi moyo chifukwa cha Atate. (Sal. 36:9; Mac. 17:28) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anapatsa ena moyo? Ndithudi, n’chifukwa cha chikondi. Ifenso tiyenera kukonda Atate wathu wakumwamba chifukwa cha mphatso imene watipatsayi.

Njira yaikulu imene Mulungu anasonyezera chikondi kwa anthu, ndi mwa kupereka Yesu monga nsembe ya dipo. Dipo limeneli limachititsa kuti anthu ochimwa akhale paubwenzi wolimba ndi Yehova kudzera mwa Mwana wake wokondedwa. (Aroma 5:12; 1 Yoh. 4:9, 10) Ndipo chifukwa chakuti Atate wathu amakwaniritsa malonjezo ake, tingakhale otsimikiza kuti anthu onse omwe amamumvera, adzasangalala ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”​—Aroma 8:21.

Ndiponso Atate wathu wakumwamba ‘amatiwalitsira dzuwa lake’ tsiku ndi tsiku. (Mat. 5:45) Nthawi zambiri sitiganiza kuti n’zofunika kupempha Mulungu kuti atiwalitsire dzuwa. Komatu anthufe timafunikira dzuwa ndipo timasangalala likamawala. Palibe amene angafanane ndi Atate wathu pa nkhani yopatsa. Iye amadziwa zosowa zathu zakuthupi tisanamupemphe n’komwe. Motero tiyenera kupeza nthawi yoganizira ndiponso kuyamikira mmene Atate  wathu wakumwamba amasamalilira zolengedwa zake.​—Mat. 6:8, 26.

Atate Wathu ‘Amateteza Mwachikondi’

Ulosi wa Yesaya unatsimikizira anthu akale a Mulungu kuti: “Mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma ubwenzi wanga ndi iwe sudzatha kapena chipangano changa cha mtendere sichidzasunthika, ati Yehova amene amakuteteza mwachikondi.” (Yes. 54:10, The Bible in Living English) Potsindika mfundo imeneyi, Yesu m’pemphero lake limene anapemphera usiku wake womaliza padziko lapansi, anasonyeza kuti Yehova ‘amatetezadi mwachikondi.’ Popempherera ophunzira ake iye anati: “Ine sindikhalanso m’dzikoli pakuti ndikubwera kwa inu, koma iwo akali m’dzikoli. Atate Woyera, ayang’anireni chifukwa cha dzina lanu.” (Yoh. 17:11, 14) Ndipo kuyambira nthawi imeneyi, Yehova wakhala akuyang’aniradi ndiponso kuteteza otsatira a Yesu.

Njira ina imene Mulungu amatitetezera ku misampha ya Satana, ndiyo kutipatsa chakudya chauzimu panthawi yake kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Kuti ‘tivale zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu,’ tifunika kulandira chakudya chotilimbitsa chimenechi. Mwachitsanzo, taganizirani za “chishango chachikulu cha chikhulupiriro” chimene timatha “kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipitsitsayo.” (Aef. 6:11, 16) Chikhulupiriro chimateteza moyo wathu wauzimu ndipo umenewu ndi umboni wakuti Atate wathu amatiteteza.

Tingaphunzirenso zambiri ponena za chikondi cha Atate wathu wakumwamba mwakuona mmene Mwana wake ankachitira zinthu ali padziko lapansi. Mwachitsanzo, taonani nkhani imene ili pa Maliko 10:13-16. Pa lembali, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Alekeni ana aang’onowo abwere kwa ine.” Anawo atamuzungulira, Yesu anawakumbatira mwachikondi ndipo anawadalitsa. Ana amenewa ayenera kuti anasangalala kwambiri. Ndiye popeza Yesu ananena kuti, “amene waona ine waonanso Atate,” timadziwa kuti Mulungu woona amafuna kuti timuyandikire.​—Yoh. 14:9.

Yehova Mulungu ndiye chimake cha chikondi. Palibe amene angafanane naye pa nkhani ya kupatsa ndiponso kuteteza. Ndipo iye amafuna kuti timuyandikire. ( Yak. 4:8) Motero, n’zosakayikitsa kuti Yehova ndiye Atate wabwino kwambiri kuposa wina aliyense.

Timapindula Kwambiri

Timapindula kwambiri tikamakhulupirira Yehova monga Atate wathu wachikondi ndiponso wachifundo. (Miy. 3:5, 6) Yesu anapindula chifukwa chokhulupirira kwambiri Atate wake. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Sindili ndekha, Atate amene anandituma ali nane.” (Yoh. 8:16) Nthawi zonse Yesu sankakayikira kuti Yehova amuthandiza. Mwachitsanzo, paubatizo wake Atate anamulimbikitsa mwachikondi ponena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mat. 3:15-17) Komanso Yesu atatsala pang’ono kufa anafuula kuti: “Atate, ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.” (Luka 23:46) Pa nthawiyi Yesu anali akukhulupirirabe Atate wake.

Ifenso tingachite chimodzimodzi. Palibe chimene tingaope chifukwa Yehova ali ku mbali yathu. (Sal. 118:6) Atsuko yemwe tamutchula poyamba uja anali ndi chizolowezi chodzidalira akakumana ndi mavuto. Koma kenako anaphunzira za moyo ndiponso utumiki wa Yesu, makamaka ubwenzi wolimba ndi Atate wake wakumwamba. Kodi atachita zimenezi zotsatira zake zinali zotani? Iye anati: “Ndinadziwa ubwino wokhala ndi Atate ndiponso kuwadalira.” Iye anatinso: “Ndinayamba kukhala pa mtendere weniweni ndiponso ndinkakhala wosangalala. Kunena zoona, palibe chifukwa chokhalira ndi nkhawa iliyonse.”

Kodi timapindulanso bwanji tikamaona Yehova kuti ndi Atate wathu? Mwachibadwa, ana amakonda makolo awo ndipo amafuna kuwasangalatsa. Chifukwa chokonda Atate wake, Mwana wa Mulungu ‘ankachita zinthu zokondweretsa Atate wakewo nthawi zonse.’ (Yoh. 8:29) Ifenso kukonda Atate wathu wakumwamba kungatithandize kuchita zinthu mwanzeru ndiponso ‘kuwatamanda pamaso pa onse.’​—Mat. 11:25; Yoh. 5:19.

 Atate Wathu Wagwira Dzanja Lathu Lamanja

Atate wathu wakumwamba watipatsanso mzimu woyera kuti uzitithandiza. Yesu anati mzimu umenewu ‘udzakutsogolerani m’choonadi chonse.’ (Yoh. 14:15-17; 16:12, 13) Mzimu woyera wa Mulungu ungatithandize kudziwa bwino Atate wathu. Ungatithandizenso kugwetsa “zinthu zozikika molimba,” zomwe ndi mfundo zongoganizira, mfundo zabodza kapena maganizo olakwika. Tikamachita zimenezi, ‘lingaliro lililonse timalitenga ukapolo kuti likhale lomvera Khristu.’ (2 Akor. 10:4, 5) Choncho, tizipemphera kwa Yehova kuti atipatse “mthandizi” yemwe analonjeza. Tizichita zimenezi, tili ndi chikhulupiriro chakuti “Atate wakumwamba . . . adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Ndi bwinonso kupempha kuti mzimu woyera uzitithandiza kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova.

Mwana wamng’ono akamayenda ndi bambo ake saopa ndipo amaona kuti ndi wotetezeka. Mukamaonadi kuti Yehova ndi Atate wanu, mungalimbikitsidwe ndi mawu akuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.” (Yes. 41:13) Mungakhale ndi mwayi wapadera ‘woyenda’ ndi Mulungu kosatha. (Mika 6:8) Pitirizani kuchita chifuniro chake, ndipo mudzazindikira kuti Yehova amakukondani, mudzakhala osangalala ndiponso mudzaona kuti ndinu wotetezeka chifukwa choona kuti Yehova ndi Atate wanu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Si dzina lake lenileni.