Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe ndi Chimwemwe Mukamakumana ndi Mavuto

Khalanibe ndi Chimwemwe Mukamakumana ndi Mavuto

 Khalanibe ndi Chimwemwe Mukamakumana ndi Mavuto

“Akondwere onse amene athawira kwa [Yehova], afuule mokondwera kosaleka.”​—SAL. 5:11.

1, 2. (a) Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimavutitsa kwambiri anthu masiku ano? (b) Kuwonjezera pa mavuto amene anthu onse amakumana nawo, kodi Akhristu oona amafunikanso kupirira chiyani?

MBONI ZA YEHOVA zimakumana ndi mavuto amene anthu onse amakumana nawo. Ndipo anthu a Mulungu ambiri amakhudzidwa ndi chiwawa, nkhondo ndiponso zinthu zina zoipa. Mwachitsanzo, zinthu monga masoka achilengedwe, umphawi, matenda ndi imfa zimavutitsa kwambiri anthu. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zopweteka mpaka pano.” (Aroma 8:22) Timavutikanso chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu. Mofanana ndi Mfumu Davide, tinganene kuti: “Mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga: Ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.”​—Sal. 38:4.

2 Kuwonjezera pa mavuto amene anthu onse amakumana nawo, Akhristu oona amanyamulanso mtengo wozunzikirapo wophiphiritsa. (Luka 14:27) Ophunzira a Yesu amadedwa ndiponso amazunzidwa ngati mmene zinalili ndi Yesu. (Mat. 10:22, 23; Yoh. 15:20; 16:2) Motero, kuti titsatire Khristu tifunika kuyesetsa kwambiri ndiponso kupirira pamene tikuyembekeza madalitso m’dziko latsopano.​—Mat. 7:13, 14; Luka 13:24.

3. Kodi timadziwa bwanji kuti Akhristu safunika kuvutika nthawi zonse kuti akondweretse Mulungu?

3 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti nthawi zonse Akhristu oona amakhala osasangalala? Kodi moyo wathu uyenera kukhala wamavuto okhaokha mpaka mapeto? Zoona zake n’zakuti Yehova amafuna kuti tikhale osangalala pamene tikudikira kuti adzakwaniritse malonjezo ake. Nthawi zambiri Baibulo limafotokoza  kuti olambira oona amakhala anthu osangalala. (Werengani Yesaya 65:13, 14.) Lemba la Salmo 5:11 limati: “Akondwere onse amene athawira kwa [Yehova], afuule mokondwera kosaleka.” N’zotheka ndithu kukhala osangalala, ndiponso kukhala ndi mtendere wa mumtima pamene tikukumana ndi mavuto. Tiyeni tione mmene Baibulo lingatithandizire kukhalabe osangalala pamene tikukumana ndi mavuto.

Yehova Ndi “Mulungu wa Chisangalalo”

4. Kodi Mulungu amamva bwanji anthu akamakana chifuniro wake?

4 Taganizirani chitsanzo cha Yehova. Popeza ndi Mulungu Wamphamvuyonse, amayang’anira chilengedwe chonse. Iye sasowa kalikonse ndipo atha kuchita zinthu pa iye yekha. Koma ngakhale kuti Yehova ali ndi mphamvu kuposa wina aliyense, iye ayenera kuti anakhumudwa kwambiri pamene mngelo wina anapanduka n’kukhala Satana. Ndipo Mulungu ayenera kuti anakhudzidwa kwambiri pamene angelo ena anagwirizana ndi Satana. Taganiziraninso mmene Mulungu zinamupwetekera pamene Adamu ndi Hava, omwe anali zolengedwa zake zapadera padzikoli, anam’kana. Kuchokera nthawi imeneyo, mbadwa zawo zambirimbiri zakana ulamuliro wa Yehova.​—Aroma 3:23.

5. Kodi ndi zinthu ziti makamaka zimene zakhala zikumupweteka mtima kwambiri Yehova?

5 Kupanduka kumene Satana anayambitsa kukupitirirabe. Kwa zaka pafupifupi 6,000 Yehova wakhala akuona anthu akuchita zoipa zosiyanasiyana monga kulambira mafano, chiwawa, kuphana ndiponso chiwerewere. (Gen. 6:5, 6, 11, 12) Kuwonjezera pamenepo, wakhala akumva anthu akunena mabodza amkunkhuniza ndiponso akumunyoza. Ngakhale atumiki ake nthawi zina amamukhumudwitsa. Baibulo limafotokoza nkhani ina yokhudza atumiki ake, ndipo limati: “Kawirikawiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako, namumvetsa chisoni m’chipululu. Pakuti anabwerera m’mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israyeli.” (Sal. 78:40, 41) Yehova amapwetekedwa mtima kwambiri anthu ake akamukana. (Yer. 3:1-10) N’zoonekeratu kuti zoipa zikamachitika, Yehova zimamupweteka kwambiri mumtima.​—Werengani Yesaya 63:9, 10.

6. Kodi Mulungu amatani pakachitika zinthu zokhumudwitsa?

6 Koma Yehova sasiya kuchita zinthu chifukwa choti wakwiya ndiponso wakhumudwa. Pakakhala zovuta zina, Yehova mwamsanga amachitapo kanthu kuti zinthu zisaipiretu. Iye  wakonzanso dongosolo lomwe lidzathandize kuti cholinga chake chikwaniritsidwe mtsogolo. Chifukwa cha zimenezi Yehova mosangalala amalakalaka kusonyeza kuti iye ndiye woyenera kulamulira ndipo amalakalakanso kuti atumiki ake okhulupirika adzadalitsidwe. (Sal. 104:31) Ngakhale kuti Yehova wanyozedwa kwambiri, iye amakhalabe “Mulungu wa chisangalalo.”​—1 Tim. 1:11; Sal. 16:11.

7, 8. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pamene zinthu sizikuyenda bwino?

7 N’zoona kuti sitingadziyerekeze ndi Yehova pa nkhani yothetsa mavuto. Koma tingamutsanzire pokumana ndi mavuto. Mwachibadwa, ngati zinthu sizili bwino timakhumudwa koma sitiyenera kupitirizabe kukhala okhumudwa. Popeza tinalengedwa m’chifanizo cha Yehova, timatha kuganiza ndiponso tili ndi nzeru. Zimenezi zingatithandize kuganizira bwino mavuto athu n’kuona zoyenera kuchita.

8 Chinthu china chofunika kwambiri chimene chingatithandize kupirira mavuto ndi kuzindikira kuti nthawi zina palibe zimene tingachite kuti tithetse mavutowo. Kudera nkhawa kwambiri zinthu zimenezi kumangowonjezera kukhumudwa ndipo kungachititse kuti tisamasangalale ndi zinthu zambiri zokhudza kulambira koona. Ngati tachita zonse zimene tikanatha polimbana ndi mavuto ena ake, ndi bwino kusiya kuganizira mavutowo n’kuyamba kuganizira zinthu zabwino. Zitsanzo za m’Baibulo zotsatirazi zikufotokoza bwino mfundo imeneyi.

Kuganiza Bwino N’kofunika

9. Kodi Hana anasonyeza bwanji kuganiza bwino?

9 Taganizirani chitsanzo cha Hana amene anadzakhala mayi a mneneri Samueli. Iye ankakhumudwa kwambiri chifukwa choti anali wosabereka. Ankasekedwa ndiponso kunyozedwa chifukwa cha vuto lakeli. Nthawi zina Hana ankakhumudwa kwambiri moti ankalira ndiponso ankakana kudya. (1 Sam. 1:2-7) Nthawi ina atapita kukachisi wa Yehova, Hana “anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi.” (1 Sam. 1:10) Hana atapemphera kwa Yehova za vuto lakeli, mkulu wa ansembe Eli anabwera n’kumuuza kuti: “Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israyeli akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.” (1 Sam. 1:17) Pamenepa Hana anadziwa kuti wachita zonse zimene akanatha. Iye anadziwanso kuti palibe chilichonse chimene akanachita kuti athetse vuto lake la kusaberekalo. Apatu Hana anasonyeza kuganiza bwino. Iye kenako “anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni.”​—1 Sam. 1:18.

10. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuganiza bwino atakumana ndi vuto limene sakanatha kulithetsa?

10 Mtumwi Paulo atakumana ndi vuto linalake, nayenso anasonyeza kuganiza bwino. Iye anali ndi vuto limene linkamudetsa nkhawa kwambiri ndipo analitcha “munga m’thupi.” (2 Akor. 12:7) Kaya vutolo linali lotani, Paulo anachita zonse zimene akanatha kuti alithetse ndipo anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Kodi Paulo anapemphera kangati kwa Yehova za vutoli? Katatu. Atapemphera kachitatuko, Mulungu anamuuza kuti ‘munga wake wa m’thupiwo’ suchoka mozizwitsa. Paulo anavomereza mfundoyi ndipo anaika maganizo ake onse pa kutumikira Yehova mokwanira.​—Werengani 2 Akorinto 12:8-10.

11. Kodi mapemphero ndi mapembedzero angatithandize bwanji kupirira mavuto?

11 Zitsanzo zimenezi sizikutanthauza kuti tizisiya kupemphera kwa Yehova za mavuto amene akutidetsa nkhawa. (Sal. 86:7) M’malomwake, Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” Kodi Yehova amayankha bwanji mapembedzero ndi mapemphero oterewa? Baibulo limapitiriza kuti: “Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) N’zoona kuti Yehova sangachotse vuto lathu, koma angayankhe mapemphero athuwo mwa kuteteza maganizo athu. Tikapemphera za vuto  linalake, tingazindikire kuopsa kwa kuda nkhawa kwambiri.

Khalani Osangalala Pochita Chifuniro cha Mulungu

12. N’chifukwa chiyani kukhala wokhumudwa nthawi yaitali kuli kovulaza?

12 Lemba la Miyambo 24:10 limanena kuti: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” Mwambi winanso umati: “Moyo umasweka ndi zowawa za m’mtima.” (Miy. 15:13) Akhristu ena amakhumudwa kwambiri mpaka kusiya kuwerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu. Mapemphero awo amangokhala amwambo ndipo amasiya kucheza ndi olambira anzawo. N’zoonekeratu kuti kukhala wokhumudwa kwanthawi yaitali kungativulaze.​—Miy. 18:1, 14.

13. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kusiya kukhumudwa n’kuyamba kukhala osangalala?

13 Komabe kukhala ndi maganizo abwino kungatithandize kuika maganizo athu pa zinthu zimene zingatichititse kukhala osangalala pa moyo wathu. Davide analemba kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga.” (Sal. 40:8) Tikamakumana ndi mavuto, tisamayerekeze n’komwe kusiya kuchita zinthu zauzimu. Ndipotu njira yabwino yothetsera kukhumudwa ndiyo kuchita zinthu zimene zingatithandize kukhala osangalala. Yehova amatiuza kuti tingakhale osangalala mwa kuwerenga Mawu ake ndi kuwasinkhasinkha nthawi zonse. (Sal. 1:1, 2; Yak. 1:25) M’Baibulo ndiponso pamisonkhano yachikhristu timalandira “mawu okoma” amene angatilimbikitse komanso kutithandiza kukhala osangalala.​—Miy. 12:25; 16:24.

14. Kodi ndi lonjezo la Yehova liti limene limatipangitsa kukhala osangalala panopa?

14 Mulungu amatipatsa zifukwa zambiri zokhalira osangalala. Lonjezo lake lakuti adzatipulumutsa, ndi chifukwa chachikulu chokhalira osangalala. (Sal. 13:5) Tikudziwa kuti ngakhale tikumane ndi zotani panopa, pomaliza Mulungu adzapereka mphoto kwa amene amamufunafuna ndi mtima wonse. (Werengani Mlaliki 8:12.) Mneneri Habakuku ankakhulupirira kwambiri mfundo imeneyi ndipo anaifotokoza bwino kuti: “Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m’minda m’mosapatsa  chakudya; ndi zoweta zachotsedwa kukhola, palibenso ng’ombe m’makola mwawo; koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.”​—Hab. 3:17, 18.

“Odala Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova”

15, 16. Tchulani mphatso zina za Mulungu zimene tingasangalale nazo pamene tikuyembekezera madalitso am’tsogolo.

15 Pamene tikuyembekezera zimene Yehova adzatichitire m’tsogolo, iye amafuna kuti tizisangalala ndi zinthu zabwino zimene amatipatsa. Baibulo limati: “Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.” (Mlal. 3:12, 13) “Kuchita zabwino” kumaphatikizapo kuthandiza ena. Yesu ananena kuti kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira. Kukomera mtima mwamuna kapena mkazi wathu, ana athu, makolo ndiponso achibale athu n’kosangalatsa kwambiri. (Miy. 3:27) Kukhala achikondi, ochereza ndi okhululukira abale ndi alongo athu auzimu, kumatipatsanso chimwemwe ndipo kumasangalatsa Yehova. (Agal. 6:10; Akol. 3:12-14; 1 Pet. 4:8, 9) Timapezanso madalitso ambiri tikamachita utumiki wathu ndi mtima wodzimana.

16 Mawu a pa lemba la Mlaliki amene ali pamwambawa amatchula zinthu zimene timasangalala nazo nthawi zonse monga kudya ndi kumwa. Ndithudi, ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto, tingasangalale ndi zinthu zimene Yehova watipatsa pa nthawiyo. Ndiponso kuonerera zinthu monga kulowa kwa dzuwa kokongola, malo okongola, kusewera kwa tiana ta nyama ndiponso zinthu zina zodabwitsa zam’chilengedwe, sikufuna ndalama iliyonse koma kungatichititse kulemekeza Mulungu ndi kukhala osangalala. Tikamaganizira zinthu zimenezi timakonda kwambiri Yehova chifukwa mphatso zonse zabwino zimachokera kwa iye.

17. Kodi n’chiyani chingatithandize kudzakhala ndi moyo wopanda mavuto, nanga panopa n’chiyani chimene chimatilimbikitsa?

17 Choncho, ngati timakonda Mulungu, kumvera malamulo ake ndiponso kukhulupirira nsembe ya dipo, m’tsogolo tidzakhala ndi moyo wopanda mavuto amene amabwera chifukwa chopanda ungwiro ndipo tidzakhala osangalala kwamuyaya. (1 Yoh. 5:3) Panopa timalimbikitsidwa chifukwa chodziwa kuti Yehova amadziwa zinthu zonse zimene zimativutitsa. Davide analemba kuti: “Ndidzakondwera ndi kusangalala m’chifundo chanu: Pakuti mudapenya zunzo langa; ndipo mudzadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga.” (Sal. 31:7) Chifukwa chotikonda, Yehova adzatipulumutsa ku mavuto amene tikukumana nawo.​—Sal. 34:19.

18. N’chifukwa chiyani anthu a Mulungu ayenera kukhala osangalala nthawi zonse?

18 Pamene tikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova, tiyeni tizimutsanzira Mulungu wa chisangalalo ameneyu. Tisalole kuti kukhumudwa kutilepheretse kuchita zinthu zauzimu. Tikakumana ndi mavuto tizigwiritsa ntchito luso lathu la kulingalira ndiponso nzeru zathu. Yehova adzatithandiza kulamulira maganizo athu ndiponso kuchita zonse zimene tingathe kuti zinthu zisaipiretu chifukwa cha mavutowo. Tiyeni tizisangalala ndi zinthu zabwino zimene Yehova amatipatsa zakuthupi ndi zauzimu. Tikakhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu tidzakhala osangalala chifukwa Baibulo limati: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”​—Sal. 144:15.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Pamene tikukumana ndi mavuto kodi tingamutsanzire bwanji Yehova?

• Kodi kuganiza bwino kungatithandize bwanji kuti tipirire mavuto?

• Kodi kuchita chifuniro cha Mulungu kungatithandize bwanji kukhala achimwemwe tikamakumana ndi mavuto?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 16]

Yehova akamaona zoipa zimene zikuchitikira anthu zimamupweteka kwambiri mumtima

[Mawu a Chithunzi]

© G.M.B. Akash/​Panos Pictures

[Zithunzi patsamba 18]

Yehova watipatsa zinthu zotithandiza kukhalabe achimwemwe