Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kamtsikana Kowolowa Manja

Kamtsikana Kowolowa Manja

 Kamtsikana Kowolowa Manja

POSACHEDWAPA, kamtsikana kazaka 9 ku Brazil kanaganiza zogawa pawiri ndalama zimene kanasunga. Kanatenga madola 18 kukaponya m’bokosi la zopereka za mpingo ku Nyumba ya Ufumu. Ndipo kanatumiza madola 25 ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, limodzi ndi kalata yachidule. M’kalatayo, kamtsikanaka kanalemba kuti: “Ndikupereka ndalama izi kuti zithandize pa ntchito yapadziko lonse. Ndikufuna kuthandiza abale ndi alongo ambiri padziko lonse lapansi kulalikira uthenga wabwino. Ndapereka ndalamazi ndi mtima wanga wonse ndiponso chifukwa chokonda kwambiri Yehova.”

Makolo a kamtsikanaka anakaphunzitsa kufunika kochita zonse zimene kangathe pa ntchito yolalikira Ufumu. Komanso anakathandiza kumvetsa kufunika ‘kolemekeza Yehova ndi chuma’ chimene kali nacho. (Miy. 3:9) Mofanana ndi kamtsikana kameneka, tiyeni tonse tikhale achangu popititsa patsogolo zinthu za Ufumu, m’dera lakwathu komanso padziko lonse.