Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Misonkhano Yachigawo Itatu Inasinthira Moyo Wanga

Mmene Misonkhano Yachigawo Itatu Inasinthira Moyo Wanga

 Mmene Misonkhano Yachigawo Itatu Inasinthira Moyo Wanga

Yosimbidwa ndi George Warienchuck

KODI zinayamba zakuchitikiranipo kuti mfundo inayake imene munamva pamsonkhano wachigawo wina, inakukhudzani kwambiri moti inakuchititsani kusintha kwambiri moyo wanu? Zimenezo zinandichitikira ineyo. Ndikayang’ana m’mbuyo, ndimaona kuti misonkhano yachigawo itatu inasintha kwambiri moyo wanga. Woyamba unandithandiza kuti ndikhale wolimba mtima, wachiwiri unandithandiza kuti ndikhale wokhutira ndi zimene ndili nazo, ndipo wachitatu unandithandiza kuti ndikhale wodzipereka. Koma ndisanakuuzeni za mmene ndinasinthira, ndikuuzani kaye zinthu zimene zinachitika kale kwambiri misonkhano yachigawo imeneyi isanachitike. Zinthu zimenezi zinachitika pa ubwana wanga.

Ndinabadwa m’chaka cha 1928, ndipo ndinali mwana womaliza m’banja la ana atatu. Ineyo limodzi ndi alongo anga awiri, Margie ndi Olga, tinakulira m’tauni ya South Bound Brook, ku New Jersey, m’dziko la United States. Pa nthawiyi, m’tauniyi mwina munali anthu pafupifupi 2,000. Banja lathu linali losauka, koma amayi anali owolowa manja. Akapeza ndalama, ankagula chakudya chabwino, ndipo anali kupatsako anthu oyandikana nawo nyumba. Pamene ndinali ndi zaka 9, tsiku lina kunyumba kwathu kunabwera Mboni imene inalankhula ndi amayi m’chinenero chawo cha Chihangare. Zimenezi zinawachititsa kuti amvetsere uthenga wa m’Baibulo. Kenako Bertha, mlongo amene anali ndi zaka za m’ma 20, anapitiriza kuphunzira Baibulo ndi amayi ndipo anawathandiza kukhala mtumiki wa Yehova.

Mosiyana ndi amayi, ine ndinali wamanyazi mwachibadwa, ndipo sindinali kudzidalira. Kuwonjezera apo, amayi ankakonda kundinena. Tsiku lina ndinawafunsa misozi ili m’maso kuti, “N’chifukwa chiyani mumangokhalira kundinena?” Iwo anandiyankha kuti amandikonda koma sakufuna kundisasatitsa. Amayiwo anali kundifunira zabwino, koma chifukwa choti sanali kundiyamikira ndinakhala munthu wodziderera.

Tsiku lina, amayi ena oyandikana nawo nyumba amene nthawi zonse anali kulankhula nane mwachifundo, anandipempha kuti ndipite limodzi ndi ana awo aamuna ku Sande sukulu ya kutchalitchi kwawo. Ndinadziwa kuti Yehova sasangalala ndikapita, koma sindinafune kuwakhumudwitsa amayiwo. Choncho, kwa miyezi ingapo, ndinali kupita kutchalitchi, ngakhale kuti ndinkadziimba mlandu ndi zimene ndinali kuchitazo. Kusukulu nakonso, ndinkachita zinthu zosemphana ndi chikumbumtima changa chifukwa choopa anthu. Mphunzitsi wamkulu pasukulupo, amene anali wopondereza kwambiri, anauza aphunzitsi onse kuti azionetsetsa kuti ana onse akuchitira sawatcha mbendera. Inenso ndinali kuchita nawo sawatchayo. Zimenezi zinachitika mwina kwa chaka chimodzi, kenako zinthu zinasintha.

Ndinaphunzira Kulimba Mtima

Mu 1939, tinayamba kuchitira phunziro la buku kunyumba kwathu. Ben Mieszkalski, amene anali mpainiya wachinyamata, ndiye anali wochititsa. Tinkamutcha Ben Wamkulu, ndipo dzina limeneli linali lomukhaladi. Kwa ine, anali kuoneka wamtali ndiponso wamkulu ngati chitseko cha kumaso kwa nyumba yathu. Koma ngakhale anali wamkulu ngati chimphona, anali ndi mtima wabwino kwambiri. Ankakonda kundimwetulira nthawi zonse, choncho ndinayamba kumasuka naye pasanapite  nthawi yaitali. Chotero pamene Ben anandipempha kuti ndipite naye mu utumiki, ndinavomera mosangalala. Kenako anakhala mnzanga. Ndikakhumudwa, anali kundilankhula ngati mmene munthu angalankhulire kwa mng’ono wake wokondedwa. Zimenezi zinandikhudza mtima kwambiri, ndipo ndinayamba kumukonda kwambiri.

Mu 1941, Ben anauza banja lathu kuti lipite naye limodzi kumsonkhano wachigawo ku St. Louis, ku Missouri, pagalimoto yake. Ndinali wosangalala kwambiri. Ndinali ndisanayendepo mtunda woposa makilomita 80 kuchokera kwathu, koma tsopano tinayenda mtunda woposa makilomita 1,500. Koma titafika ku St. Louis, tinakumana ndi zovuta. Akuluakulu a chipembedzo anauza anthu a m’matchalitchi mwawo kuti asalole Mboni kukhala m’makomo mwawo monga momwe anakonzera poyamba. Choncho anthu ambiri amene poyamba ananena kuti Mboni zikhoza kukhala m’makomo mwawo anasintha maganizo. Banja limene linakonza zoti ifeyo tikhale kwawo linaopsezedwanso kuti lisinthe. Koma iwo anatilandirabe. Anati sangaphwanye lonjezo lawo loti atipatsa malo ogona. Kulimba mtima kwawo kunandigometsa.

Achemwali anga awiri anabatizidwa pamsonkhano umenewo. Tsiku limene anabatizidwalo, M’bale Rutherford, wochokera ku Beteli ku Brooklyn anakamba nkhani yokhudza mtima kwambiri. Munkhaniyo anapempha ana onse amene anali kufuna kuchita chifuniro cha Mulungu kuti aimirire. Ana pafupifupi 15,000 anaimirira. Inenso ndinaimirira. Kenako ananena kuti aliyense wa ife amene akufuna kuchita zonse zimene angathe mu ntchito yolalikira anene kuti “Inde.” Ineyo limodzi ndi ana enawo tinakuwa kuti, “Inde!” Kenako anthu anatiwombera m’manja mwamphamvu kwambiri. Ndinatenthedwa maganizo kwambiri ndi zimenezi.

Msonkhanowo utatha, tinapita kunyumba kwa m’bale wina ku West Virginia. M’baleyo anatiuza kuti tsiku linalake akulalikira, gulu lokwiya la anthu linamumenya ndi kumupakapaka phula ndiponso kumumatamata nthenga. Ndinamvetsera mokhudzidwa mtima kwambiri. Ndiyeno m’baleyo anati: “Koma sindisiya kulalikira.” Pamene tinali kusiyana ndi m’baleyo, ndinamva ngati kuti ndine Davide. Ndinali wokonzeka kuthana ndi mphunzitsi wamkulu wakusukulu kwathu uja, amene anali ngati Goliati kwa ine.

Nditabwerera kusukulu, ndinapita kwa mphunzitsi wamkulu uja. Iye anandiyang’anitsitsa mokwiya. Ndinapemphera mwakachetechete kwa Yehova. Kenako ndinanena mofulumira kuti: “Ndinapita kumsonkhano wa Mboni za Yehova. Kuyambira lero, sindidzachitiranso sawatcha mbendera!” Mphunzitsi wamkuluyo sanayankhe kalikonse. Kenako anaimirira pang’onopang’ono kuchokera pampando pamene anakhala pafupi ndi desiki, n’kuyamba kubwera pamene ineyo ndinali. Nkhope yake inali itafiira ndi mkwiyo. Kenako analankhula mokuwa kuti: “Chitira sawatcha mbendera, apo ayi uchotsedwa sukulu!” Ulendo uno sindinagonje, ndipo mumtima mwanga ndinamva chimwemwe chimene ndinali ndisanachimvepo.

Ndinkangoona kuchedwa kuti ndikamuuze Ben zimene zinachitika. Nditamuona ku Nyumba ya Ufumu, ndinamuuza mofuula kuti: “Andichotsa sukulu! Sindinachitire sawatcha mbendera!” Ben anandikoleka dzanja lake m’khosi akumwetulira, ndipo anati: “Yehova amakukonda kwabasi.” (Deut. 31:6) Mawu amenewo anandilimbikitsa kwambiri. Pa 15 June 1942, ndinabatizidwa.

Ndinaphunzira Chinsinsi Chokhutira ndi Zimene Ndili Nazo

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, dziko lathu linatukuka mofulumira. Kenako mzimu wokonda chuma unafala kwambiri. Ndinali pa ntchito yabwino ndipo tsopano ndikanatha kugula zinthu zimene kale ndinkaona ngati sindingazikwanitse. Anzanga ena anagula njinga zamoto, ndipo ena anakongoletsa nyumba zawo. Ine ndinagula galimoto yatsopano. Posakhalitsa, ndinayamba kukankhira pambali zinthu za Ufumu chifukwa chofuna kukhala ndi moyo wawofuwofu. Ndinadziwa kuti ndikulowerera. Mwamwayi, msonkhano umene unachitikira ku New York City mu 1950 unandithandiza kusintha.

 Pamsonkhano umenewo, okamba nkhani osiyanasiyana analimbikitsa omvera kuti alimbikire kugwira ntchito yolalikira. Wokamba nkhani wina anati: “Mungotsala ndi katundu wochepa yekha, kuti muzithamanga bwino pampikisanowu.” Ndinamva ngati akulankhula kwa ineyo. Ndinaonereranso mwambo wa omaliza maphunziro a Gileadi. Zimenezi zinandichititsa kuganiza kuti, ‘Ngati Mboni za msinkhu wangazi zili zokonzeka kudzimana moyo wawofuwofu kuti zikatumikire kunja, inenso ndiyenera kuchita zomwezo kumudzi kuno.’ Pofika pamapeto pa msonkhanowo, ndinali nditatsimikiza mtima kuti ndikhala mpainiya.

Pa nthawi imeneyi, ndinayamba chibwenzi ndi Evelyn Mondak, mlongo wachangu wa mumpingo mwathu. Amayi ake a Evelyn, amene analera ana 6, anali opanda mantha. Ankakonda kuchita ulaliki wa mumsewu kutsogolo kwa tchalitchi chachikulu cha Roma Katolika. Wansembe wa tchalitchicho anali kuwauza mokwiya kambirimbiri kuti achoke, koma iwo sanali kuchoka. Mofanana ndi amayi akewo, Evelyn nayenso sanali kuopa munthu.​—Miy. 29:25.

Mu 1951, ine ndi Evelyn tinakwatirana, tinasiya ntchito, ndipo tinayamba upainiya. Woyang’anira dera wina anatilimbikitsa kuti tisamukire kumudzi winawake wotchedwa Amagansett. Mudziwu unali m’mphepete mwa nyanja ya Atlantic, pamtunda wa makilomita 160 kuchokera ku New York City. Mpingo wakumeneko utatiuza kuti unalibe malo oti tingamakhaleko, tinafunafuna kalavani yoti tingamakhalemo, koma onse amene tinali kuwapeza anali odula. Kenako tinaona kalavani inayake yakutha. Mwiniwake anatiuza kuti tikhoza kuigula pa mtengo wa madola 900. Zimenezi zinali ndendende ndalama zimene tinapatsidwa monga mphatso paukwati wathu. Tinaigula ndi kuikonzakonza. Kenako tinaikoka kupita nayo kugawo lathu latsopano. Koma tinafika kumeneko tilibe ndalama iliyonse, ndipo sitinali kudziwa kuti tikhala bwanji monga apainiya.

Evelyn anayamba kugwira ntchito yoyeretsa m’nyumba za anthu, ndipo ine ndinapeza ntchito ya usiku yoyeretsa mulesitilanti ya Mtaliyana. Mwiniwake wa lesitilantiyo anandiuza kuti: “Pakakhala zakudya zilizonse zotsala, ukhoza kumatenga kuti uzikapatsa mkazi wako kunyumba.” Choncho ndikafika kunyumba 2 koloko ya m’mawa, m’kalavani mwathu munkadzaza kafungo kabwino ka zakudya zachitaliyana monga pizza ndi pasta. Tinali kutenthetsa zakudyazi ndipo tinkazikonda kwambiri. Zinali kutithandiza kwambiri makamaka nthawi yozizira, pamene tinali kunjenjemera chifukwa choti m’kalavanimo munkazizira koopsa. Komanso, nthawi zina abale a mumpingomo anali kusiya nsomba yaikulu pamasitepe a kalavaniyo kuti tidye. Zaka zimene tinatumikira limodzi ndi abale athu okondedwa a ku Amagansett, tinaphunzira kuti kukhutira ndi zochepa kumabweretsa chimwemwe pa moyo. Pa zaka zimenezo tinali osangalala kwambiri.

Tinalimbikitsidwa Kukhala Odzipereka

Mu July chaka cha 1953, tinakumana ndi amishonale ambirimbiri amene anabwera kuchokera kumagawo awo akunja kudzachita msonkhano wa mayiko ku New York City. Amishonalewo anafotokoza mosangalala zinthu zambiri zochititsa chidwi zimene anali kukumana nazo. Nawonso omvera anasangalala. Ndipo pamene wokamba nkhani wina pamsonkhanopo anagogomezera kuti m’mayiko ambiri uthenga wa Ufumu unali usanafikemo, ine ndi mkazi wanga tinadziwa kuti tiyenera kudzipereka kwambiri pa utumiki wathu. Pamsonkhano pomwepo, tinapempha kuti akatiphunzitse umishonale. Chaka chomwecho, tinaitanidwa kuti tikaphunzire nawo kalasi ya nambala 23 ya Sukulu ya Gileadi, yomwe inayamba mu February 1954. Umenewo unalidi mwayi wapadera.

Tinasangalala koopsa titauzidwa kuti tikatumikire ku Brazil. Tisanayambe ulendo wathu wa masiku 14 wapasitima yapanyanja, m’bale wina wokhala ndi udindo ku Beteli anandiuza kuti: “Palinso alongo ena 9 osakwatiwa amene ayendere nanu limodzi popita ku Brazil. Uwasamalire bwino!” Tangoganizirani  mmene ogwira ntchito m’sitimamo anachitira chidwi kundiona ndikukwera sitimayo ndi akazi 10 pambuyo panga. Koma alongowo anadziwa mochitira ndi vutoli. Komabe, mtima wanga sunali m’malo mpaka pamene tinafika bwino ku Brazil.

Nditaphunzira Chipwitikizi, ndinauzidwa kuti ndikhala woyang’anira dera m’boma la Rio Grande do Sul, limene lili kum’mwera kwa Brazil. Woyang’anira dera amene ndinali kukalowa m’malo mwake, amene anali wosakwatira, anandiuza ine ndi mkazi wanga kuti: “Ndikudabwa kuti kunoko atumizako anthu apabanja chifukwa n’kutchire ndiponso kumapiri.” Mipingo yake inali yapatalipatali m’dera lalikulu lakumidzi. Panalibe njira yokafikira kumipingo ina kupatulapo kukwera lole. Mukamugulira dalaivala wa loleyo chakudya, anali kukulolani kuti mukwere kumbuyo. Tikakwera pamwamba pa loleyo, tinali kukhala chotang’adza pamwamba pa katundu, ngati kuti takwera hatchi, kwinaku titagwiritsa zingwe zomangira katunduyo. Loleyo ikamakhota pamakona, tinkagwiritsa ndi mphamvu zathu zonse uku katunduyo akupendekekera mbali imodzi. Zikatero tinkapendekekera kuphedi, kuzigwa zimene zinali kumunsi kwa msewuwo. Tinali kuyenda tsiku lonse pa maulendo oterowo. Koma tikaona abale athu amene anali kutidikirira akumwetulira potiona, tinkaiwala zoti tinayenda ulendo woopsa.

Tinkakhala m’nyumba za abale. Anali osauka kwambiri, koma anali opatsa. M’gawo lina lakutali, abale onse anali kugwira ntchito m’fakitale yolongedza nyama. Malipiro amene anali kulandira anali ochepa, choncho ankadya kamodzi kokha pa tsiku. Akapanda kugwira ntchito tsiku limenelo, sanali kulipidwa. Komabe, ife tikafika kudzawachezera, ankatenga tchuthi cha masiku awiri kuntchito kuti achite nawo ntchito zampingo. Iwo anali kudalira Yehova. Abale osauka amenewo anatiphunzitsa zinthu zimene sitidzaiwala. Anatiphunzitsa kukhala odzimana chifukwa cha Ufumu wa Mulungu. Chifukwa chokhala nawo, tinaphunzira maphunziro amene sapezeka kusukulu ina iliyonse. Mpaka lero, ndikakhala n’kumaganizira za abale amenewo, misozi imalengeza m’maso mwanga.

Mu 1976 tinabwerera ku United States kuti tikasamalire amayi anga amene anali kudwala. Ku Brazil sitinafune kuchokako, komabe ndife oyamikira kuti tinaona ofalitsa a Ufumu akuwonjezeka kwambiri m’dzikolo. Tikalandira makalata ochokera ku Brazil, timakumbukira zinthu zambiri zosangalatsa zimene zinatichitikira pa nthawi imene tinali kumeneko.

Kukumananso ndi Anthu Okondedwa

Pa nthawi imene tinali kusamalira amayi anga, tinali kuchita upainiya ndipo tinkagwira ntchito zosiyanasiyana zoyeretsa malo. Amayi anamwalira mu 1980 ali okhulupirika kwa Yehova. Kenako ndinapemphedwa kukhala woyang’anira dera m’dziko la United States. Mu 1990, ine ndi mkazi wanga tinakayendera mpingo ku Connecticut, ndipo kumeneko tinakumana ndi munthu wokondedwa kwambiri. Mmodzi wa akulu mumpingomo anali Ben. Inde, Ben wake anali yemwe uja amene anandithandiza kuti ndiime zolimba kumbali ya Yehova zaka pafupifupi 50 m’mbuyomo. Tangoganizani chimwemwe chimene tinali nacho pamene tinakumbatirana!

Kuyambira mu 1996, ine ndi Evelyn takhala tikutumikira monga apainiya apadera odwala mumpingo wachipwitikizi ku Elizabeth, ku New Jersey. Ndine wodwaladwala, koma ndi thandizo la mkazi wanga wokondedwa, ndimachita nawo utumiki mmene ndingathere. Evelyn amathandizanso mayi wina wokalamba wodwaladwala amene amakhala pafupi ndi nyumba yathu. Kodi mukudziwa dzina lake? Ndi Bertha, inde, Bertha yemwe uja amene anathandiza amayi anga kuti akhale mtumiki wa Yehova zaka zoposa 70 zapitazo! Ndife okondwa kukhala ndi mwayi womusonyeza kuti timayamikira kwambiri zonse zimene anachita pothandiza banja lathu kuphunzira choonadi.

Ndikuthokoza kwambiri kuti misonkhano yachigawo yakalekale ija inandithandiza kuima nji pa kulambira koona, kukhala ndi moyo wosalira zambiri, ndiponso kuchita zambiri mu utumiki wanga. Zoonadi, misonkhano yachigawo imeneyo, inasintha moyo wanga.

[Chithunzi patsamba 23]

Amayi ake a Evelyn (kumanzere) ndi amayi anga

[Chithunzi patsamba 23]

Mnzanga Ben

[Chithunzi patsamba 24]

Tili ku Brazil

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi Evelyn masiku ano