Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi pa lemba la Miyambo 24:27 tikuphunzirapo chiyani?

Popereka malangizo kwa mnyamata, wolemba Miyambo anati: “Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.” Kodi ndi mfundo yotani imene ili m’mwambi wouziridwawu? Ndi mfundo yakuti munthu ayenera kukonzekera bwinobwino asanakwatire n’kukhala ndi banja lakelake. Ayenera kuchita zimenezi pozindikira kuti kusamalira banja ndi udindo waukulu zedi.

M’mbuyomu pofotokozera lembali, tatchulapo kuti mwamuna ndiponso bambo ayenera kusamalira ntchito imene amagwira komanso ayenera kumanga, kapena kuti kulimbikitsa banja lake, mwachitsanzo poliphunzitsa zinthu zauzimu. Mfundo imeneyi ndi yoona ndipo ndi yogwirizana ndi Malemba, kungoti si mfundo imene lembali limafotokoza. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani zifukwa ziwiri.

Choyamba n’chakuti ponena za kumanga, lembali silikutanthauza kulimbikitsa banja limene lilipo kale. Kwenikweni mawu a m’lembali amatanthauza kumanga nyumba yeniyeni. Koma mawuwo angatanthauzenso kumanga banja n’kukhazikika, kapena kuti kukwatira n’kukhala ndi ana.

Chachiwiri n’chakuti lembali limanena za dongosolo loyenera lochitira zinthu. Tingati limanena kuti, “Choyamba uyenera kuchita zakutizakuti; kenako n’kuchita zakutizakuti.” Ndiyeno kodi tingati mwambi umenewu ukutanthauza kuti tiyenera kukwaniritsa maudindo ena amene tili nawo, tisanakwaniritse maudindo auzimu? Ayi ndithu si zimene ukutanthauza.

M’nthawi za m’Baibulo, ngati munthu akufuna “kumanga nyumba” yake kapena kuti kukhazikika pokwatira n’kukhala ndi ana, anayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wokonzeka kusamalira ndi kuthandiza mkazi ndiponso ana amene tingakhale nawo?’ Asanakhale ndi banja, anayenera kugwira kaye ntchito kumunda. N’chifukwa chake Baibulo la Today’s English Version linamasulira vesili motere: “Usamange nyumba yako n’kukhala ndi banja pamene sunakonzeke kumunda kwako, ndipo sunatsimikize kuti uzidzapeza zofunika pa moyo.” Kodi mfundo imeneyi imagwiranso ntchito masiku ano?

Inde. Mwamuna amene akufuna kukwatira ayenera kukonzekera bwino udindo umenewo. Ngati angathe, ayenera kugwira ntchito. N’zoona kuti ntchito imene mwamuna ayenera kuchita posamalira banja lake, siyenera kukhala yongodyetsa kapena kuveka banjalo basi. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti mwamuna amene sakonda banja lake ndiponso salisamalira mwakuthupi ndi mwauzimu, amaipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro. (1 Tim. 5:8) Motero, pokonzekera ukwati ndiponso moyo wabanja, mwamuna ayenera kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi ndine wokonzeka kupezera banja langa zinthu zofunikira mwakuthupi? Kodi ndine wokonzeka kukhala mutu wa banja pa nkhani zauzimu? Kodi ndidzakwanitsa udindo wochita phunziro la Baibulo mokhazikika ndi mkazi komanso ana anga?’ Mawu a Mulungu amagogomezera kwambiri maudindo amenewa.​—Deut. 6:6-8; Aef. 6:4.

Motero mnyamata amene akufuna kukwatira ayenera kuganizira bwino mfundo ya pa Miyambo 24:27. Mtsikananso ayenera kudzifunsa ngati ali wokonzeka kukwaniritsa udindo wokhala mkazi ndiponso mayi. Komanso achinyamata amene angokwatirana kumene ayenera kudzifunsa mafunso omwewa ngati akuganiza zokhala ndi ana. (Luka 14:28) Anthu a Mulungu akatsatira malangizo amenewa, amapewa mavuto ambiri ndipo amasangalala ndi moyo wabanja.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Kodi mnyamata amene akufuna kukwatira ayenera kudzifunsa mafunso otani?