Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Khalani Mwamtendere ndi Anthu Onse’

‘Khalani Mwamtendere ndi Anthu Onse’

 ‘Khalani Mwamtendere ndi Anthu Onse’

“Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”​—AROMA 12:18.

1, 2. (a) Kodi Yesu anachenjeza otsatira ake za chiyani? (b) N’kuti kumene tingapezeko malangizo a zimene tingachite potsutsidwa?

YESU anachenjeza otsatira ake kuti adzatsutsidwa ndi anthu a mitundu yonse ndipo usiku woti aphedwa mawa lake, anafotokoza chifukwa chimene ananenera zimenezi. Anauza atumwi ake kuti: “Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake. Koma popeza simuli mbali ya dzikoli, koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko limadana nanu.”​—Yoh. 15:19.

2 Chifukwa cha zimene zinamuchitikira mtumwi Paulo, iye anazindikira kuti mawu a Yesuwa ndi oona. M’kalata yake yachiwiri kwa mnzake wachinyamata Timoteyo, Paulo analemba kuti: “Iwe wayesetsa kutsatira chiphunzitso changa, moyo wanga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, masautso anga.” Kenako Paulo anapitiriza kuti: “Paja onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Tim. 3:10-12) M’chaputala 12 cha kalata  imene Paulo analembera Akhristu a ku Roma, anapereka malangizo anzeru okhudza zimene Akhristuwo anayenera kuchita akamatsutsidwa. Mawu akewo angatithandizenso mu nthawi ya mapeto ino.

‘Chitani Zabwino’

3, 4. Kodi malangizo amene ali pa Aroma 12:17 angagwiritsidwe ntchito bwanji (a) m’banja limene muli anthu osiyana zipembedzo? (b) pochita zinthu ndi anthu anzathu?

3 Werengani Aroma 12:17. Paulo anafotokoza kuti anthu akamatichitira zinthu zoipa, tisamawabwezere pochitanso zoipa. Kumvera malangizo amenewa n’kothandiza kwambiri makamaka m’mabanja amene mwamuna ndi mkazi ndi osiyana zipembedzo. Mwamuna kapena mkazi amene ali Mkhristu m’banja lotereli, sayenera kubwezera mawu oipa kapena kuchitanso zinthu zoipa pofuna kubwezera. Sitipindula m’njira iliyonse ‘pobwezera choipa ndi choipa.’ Kuchita zimenezi kungangochititsa kuti zinthu ziipireipire.

4 Paulo anafotokoza njira yabwinopo yochitira zinthu. Anati: “Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino.” Ngati mwamuna wanena zinthu zoipa zokhudza zimene mkazi wake amakhulupirira, koma mkaziyo n’kumamuchitirabe mwamuna wakeyo zinthu mokomadi mtima, zingathandize kuti pasabuke mkangano woopsa. (Miy. 31:12) Carlos, amene tsopano ali m’banja la Beteli, anafotokoza mmene mayi ake anapiririra pamene bambo ake anali kuwatsutsa kwambiri. Anati mayi akewo anapitirizabe kukhala okoma mtima kwa bambo akewo ndiponso anali kusamalira bwino pakhomo. Iye anapitiriza kuti: “Amayi anatilimbikitsa anafe kuti tiziwachitira ulemu bambo. Anandiumiriza kuti ndizisewera nawo masewera enaake, ngakhale kuti masewerawo sanali kundisangalatsa. Koma masewerawa anathandiza kuti bambo azikhala osangalala.” Patapita nthawi, bambowo anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa. Pofuna ‘kuchita zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino,’ nthawi zambiri Mboni za Yehova zimathandiza anthu anzawo pakagwa tsoka linalake. Zimenezi zathandiza kuti anthu amene anali kudana nazo asinthe maganizo awo.

Kuunjika “Makala a Moto” Pamutu pa Otitsutsa

5, 6. (a) Kodi timaunjika bwanji “makala a moto” pamutu pa mdani wathu? (b) Fotokozani zimene zinachitikapo kwanuko zosonyeza kuti kutsatira malangizo a pa Aroma 12:20 kumathandizadi.

5 Werengani Aroma 12:20. Polemba mawu amene ali pavesili, mosakayikira Paulo anali kuganizira mawu amene timawerenga pa Miyambo 25:21, 22, akuti: “Mdani wako akamva njala um’dyetse, akamva ludzu um’mwetse madzi, pakuti udzaunjika makala amoto pamtu pake; ndipo Yehova adzakupatsa mphoto.” Tikaganizira malangizo onse amene ali m’chaputala 12 cha buku la Aroma, tingathe kuona kuti palembali Paulo sanali kutanthauza kuti makala a moto ophiphiritsawo cholinga chake chinali kulanga kapena kuchititsa manyazi anthu otitsutsa. M’malomwake, zikuoneka kuti mawu amene ali m’buku la Miyambo, ndiponso mawu a Paulowa kwa Aroma, akunena za njira imene anali kugwiritsa ntchito kale poyenga zitsulo. Katswiri wina  wa ku England amene anakhalapo m’zaka za m’ma 1800, Charles Bridges, anafotokoza kuti: “Ikani pamoto chitsulo cholimbacho. Musangochiika pamotopo, koma muunjikenso makala a moto pamwamba pake kuti motowo ukhale pansi ndi pamwamba pomwe. Pali mitima yochepa chabe imene ingalephere kusungunuka ndi mphamvu ya chikondi choleza mtima, chodzimana, ndi choyaka moto.”

6 Mofanana ndi “makala a moto,” kukomera anthu mtima kungakhudze mitima ya otsutsa, mwina mpaka kusungunula chidani chawo ndi kuchithetsa. Kungachititse anthuwo kuyamba kuganiza zabwino za anthu a Yehova ndi uthenga wa m’Baibulo umene amalalikira. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Sungani khalidwe labwino pakati pa anthu amitundu, kuti pamene akukunenerani monga ochita zoipa, pa mapeto pake iwo pokhala mboni zimene zikuona ndi maso zochita zanu zabwino, adzatamande Mulungu m’tsiku lake la kuyendera.”​—1 Pet. 2:12.

‘Khalani Mwamtendere ndi Anthu Onse’

7. Kodi mtendere umene Khristu amasiyira ophunzira ake n’chiyani, ndipo uyenera kutithandiza kuchita chiyani?

7 Werengani Aroma 12:18. Usiku womaliza umene Yesu anali ndi atumwi ake, anawauza kuti: “Ndikusiyirani mtendere, ndikupatsani mtendere wanga.” (Yoh. 14:27) Mtendere umene Khristu amasiyira ophunzira ake ndiwo mtendere wa mumtima umene iwo amakhala nawo chifukwa chodziwa kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake wokondedwa, amawakonda ndiponso amakondwera ndi zimene iwowo akuchita. Mtendere wa mumtima umenewu uyenera kutithandiza kukhala mwamtendere ndi ena. Akhristu enieni amakonda mtendere ndipo amachita zinthu zolimbikitsa mtendere.​—Mat. 5:9.

8. Kodi tingatani kuti tikhale anthu olimbikitsa mtendere kunyumba ndi kumpingo?

8 Njira imodzi yochitira zinthu zolimbikitsa mtendere pabanja, ndiyo kuthetsa mwamsanga kusemphana maganizo m’malo molekerera kuti zinthu zifike poipa. (Miy. 15:18; Aef. 4:26) N’chimodzimodzinso mumpingo wachikhristu. Mtumwi Petulo anasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kuyesetsa kufunafuna mtendere ndi kulamulira lilime lathu. (1 Pet. 3:10, 11) Nayenso Yakobe, pambuyo popereka malangizo amphamvu okhudza kugwiritsa ntchito lilime moyenera ndi kupewa nsanje ndiponso mtima wandewu, analemba kuti: “Nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yopanda chinyengo. Komanso, chilungamo ndicho chipatso cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.”​—Yak. 3:17, 18.

9. Poyesetsa kukhala “mwa mtendere ndi anthu onse,” kodi tiyenera kukumbukira chiyani?

9 Mawu amene Paulo ananena pa Aroma 12:18 sanali kungonena za kukhala mwamtendere pabanja ndi mumpingo mokha. Ananena kuti tikhale “mwa mtendere ndi anthu onse.” Zimenezi zikutanthauza anthu akunja, akuntchito, akusukulu, ndi amene timakumana nawo polalikira. Koma mtumwiyu anawonjezera mawu ena pa  malangizo akewa, ponena kuti: “Ngati ndi kotheka, . . . monga mmene mungathere.” Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tikhale “mwa mtendere ndi anthu onse,” koma osachita kufika pophwanya mfundo zolungama za Mulungu.

Kubwezera Ndi kwa Yehova

10, 11. Kodi ‘timasiyira malo mkwiyo wa Mulungu’ m’njira yotani, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zoyenera?

10 Werengani Aroma 12:19. Ngakhale pochita zinthu ndi “anthu otsutsa” ntchito yathu ndiponso uthenga wathu, kuphatikizapo amene amatitsutsa mochita kuonetseratu, tiyenera kukhala ‘ougwira mtima pokumana ndi zoipa’ ndiponso tiyenera kumachita zinthu “mofatsa.” (2 Tim. 2:23-25) Paulo analangiza Akhristu kuti sayenera kubwezera koma ayenera ‘kusiyira malo mkwiyo wa Mulungu.’ Monga Akhristu, tikudziwa kuti siife oyenera kubwezera. Wolemba masalmo wina anati: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: Usavutike mtima ungachite choipa.” (Sal. 37:8) Ndipo Solomo anatilangiza kuti: “Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.”​—Miy. 20:22.

11 Anthu otitsutsa akatichitira zinthu zoipa, chinthu chanzeru kuchita ndicho kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova kuti adzawalange ngati akuona kuti n’zoyenera kutero, ndiponso pa nthawi yoyenera kutero. N’zachidziwikire kuti Paulo anali kuganiza zimenezi, chifukwa anapitiriza kuti: “Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’” (Yerekezerani ndi Deuteronomo 32:35.) Kufuna kubwezera tokha kungakhale kudzikuza chifukwa zingakhale ngati tikufuna kuchita zimene Yehova wanena kuti ndi iye yekha amene ali woyenera kuchita. Komanso, tingasonyeze kuti sitikukhulupirira lonjezo la Yehova lakuti: “Ndidzawabwezera ndine.”

12. Kodi mkwiyo wa Yehova udzasonyezedwa liti ndiponso motani?

12 Kumayambiriro kwa kalata yake yopita kwa Aroma, Paulo anati: “Mkwiyo wa Mulungu ukusonyezedwa kuchokera kumwamba pa anthu onse osaopa Mulungu ndi ochita zosalungama amene akupondereza choonadi m’njira yosalungama.” (Aroma 1:18) Mkwiyo wa Yehova udzasonyezedwa kuchokera kumwamba kudzera mwa Mwana wake pa nthawi ya “chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:14) Umenewo udzakhala “umboni wa chiweruzo cholungama cha Mulungu,” monga momwe Paulo anafotokozera m’kalata yake ina youziridwa, kuti: “Izi zili choncho pakuti n’kolungama kwa Mulungu kubwezera masautso kwa okusautsani. Koma kwa inu amene mukukumana ndi masautso, adzakubwezerani mpumulo limodzi ndi ife pa vumbulutso la Ambuye Yesu, kuchokera kumwamba ndi angelo ake amphamvu m’moto wa lawilawi. Adzabwezera chilango kwa osadziwa Mulungu ndi kwa osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.”​—2 Ates. 1:5-8.

Kugonjetsa Choipa mwa Kuchita Chabwino

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani sitidabwa anthu akamatitsutsa? (b) Kodi tingadalitse bwanji anthu amene amatizunza?

13 Werengani Aroma 12:14, 21. Popeza tili ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova adzakwaniritsa zolinga zake, tingathe kuika maganizo athu onse pa ntchito imene watipatsa kuti tichite, yolalikira ‘uthenga wabwino uwu wa ufumu padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.’ (Mat. 24:14) Tikudziwa kuti ntchito yathuyi monga Akhristu imautsa mkwiyo wa adani athu. Tikudziwa zimenezi chifukwa Yesu anatichenjeza kuti: “Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa.” (Mat. 24:9) Chotero sitidabwa kapena kufooka tikamatsutsidwa. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Okondedwa, musadabwe ndi moto umene ukuyaka pakati panu, ngati kuti mukukumana ndi chinthu chachilendo. Motowo ukuyaka pofuna kukuyesani. Koma muzikondwera pamene mukugawana nawo masautso a Khristu.”​—1 Pet. 4:12, 13.

14 M’malo modana ndi anthu amene akutizunza, timayesetsa kuwaphunzitsa kuti atseguke maganizo, chifukwa tikudziwa kuti ena mwa iwo amachita zimenezo chifukwa cha kusadziwa. (2 Akor. 4:4) Timayesetsa kutsatira malangizo a Paulo akuti: “Pitirizani kudalitsa anthu amene amakuzunzani; muzidalitsa, osatemberera.” (Aroma 12:14) Njira imodzi yodalitsira anthu amene amatitsutsa ndiyo kuwapempherera.  Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anati: “Pitirizani kukonda adani anu, kuchita zabwino kwa amene akudana nanu, kudalitsa okutembererani, kupempherera amene akukunyozani.” (Luka 6:27, 28) Chifukwa cha zimene zinamuchitikira mtumwi Paulo, iye anali kudziwa kuti munthu wozunza ena akhoza kukhala wophunzira wokhulupirika wa Khristu ndiponso mtumiki wa Yehova wachangu. (Agal. 1:13-16, 23) M’kalata ina, Paulo anati: “Pamene akutinenera zachipongwe, timadalitsa; pozunzidwa, timapirira; ponyozedwa, timayankha mofatsa.”​—1 Akor. 4:12, 13.

15. Kodi njira yabwino kwambiri yogonjetsera choipa mwa kuchita chabwino ndi iti?

15 Chifukwa cha zimenezi, Mkhristu weniweni amatsatira zimene vesi lomaliza la Aroma chaputala 12 limanena, kuti: “Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” Gwero la zoipa zonse ndi Satana Mdyerekezi. (Yoh. 8:44; 1 Yoh. 5:19) Mu chivumbulutso chimene mtumwi Yohane anaonetsedwa, Yesu anasonyeza kuti abale ake odzozedwa “anam’gonjetsa [Satana] chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mawu a umboni wawo.” (Chiv. 12:11) Zimenezi zikusonyeza kuti njira yabwino kwambiri yogonjetsera Satana ndiponso zinthu zoipa zimene iye akuchititsa m’dongosolo la zinthu lino, ndiyo kuchitira ena zabwino mwa kugwira nawo ntchito yathu yochitira umboni. Ntchito imeneyi ndi yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu.

Kukondwera ndi Chiyembekezo

16, 17. Kodi chaputala 12 cha Aroma chatiphunzitsa chiyani pa nkhani ya (a) mmene tiyenera kukhalira pa moyo wathu? (b) mmene tiyenera kuchitira zinthu mumpingo? (c) mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu amene amatsutsa chikhulupiriro chathu?

16 Pokambirana mwachidule chaputala 12 cha kalata ya Paulo kwa Akhristu a ku Roma, takumbutsidwa zinthu zambiri. Taphunzira kuti monga atumiki a Yehova odzipereka, tiyenera kukhala ofunitsitsa kudzimana. Motsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, timakhala odzimana mwakufuna kwathu chifukwa pogwiritsa ntchito luntha lathu la kulingalira, tatsimikiza kuti chimenecho ndicho chifuniro cha Mulungu. Timayaka ndi mzimu ndipo timagwiritsa ntchito mwachangu mphatso zathu zosiyanasiyana. Timatumikira modzichepetsa ndiponso timadziwa malire athu, ndipo timayesetsa kuti tisunge mgwirizano wathu wachikhristu. Timakhala ochereza ndipo timaganiziradi ena.

17 Chaputala 12 cha Aroma chilinso ndi malangizo ochuluka a zimene tiyenera kuchita tikamatsutsidwa. Sitiyenera kubwezera choipa. Tiyenera kugonjetsa otsutsa poyesetsa kuwachitira zinthu mokoma mtima. Popanda kuphwanya mfundo za m’Baibulo, tiyenera kuyesetsa mmene tingathere kukhala mwamtendere ndi anthu onse. Tiyenera kuchita zimenezi kunyumba, kumpingo, kwa anthu akunja, kuntchito, kusukulu, ndiponso mu utumiki. Ngakhale anthu akachita kuonetseratu kuti amadana nafe, tiyenera kuyesetsa kugonjetsa choipa pochita chabwino, pozindikira kuti kubwezera ndi kwa Yehova.

18. Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene tikulangizidwa pa Aroma 12:12?

18 Werengani Aroma 12:12. Kuwonjezera pa malangizo anzeru ndiponso opindulitsa onsewa, Paulo anaperekanso malangizo ena atatu. Popeza sitingakwanitse kuchita zinthu zonsezi ngati Yehova atapanda kutithandiza, mtumwiyu anatilangiza kuti ‘tilimbikirebe kupemphera.’ Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tithe kutsatira malangizo ake ena akuti ‘tipirire chisautso.’ Pomaliza, tiyenera kuganiza kwambiri za tsogolo limene Yehova watilonjeza ndipo tiyenera ‘kukondwera ndi chiyembekezo’ chokhala ndi moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padziko lapansi pano.

Tibwereze

• Kodi tiyenera kutani tikamatsutsidwa?

• Kodi tiyenera kuyesetsa kulimbikitsa mtendere kuti, ndipo tingachite motani zimenezi?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kubwezera?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

Kuchitira anthu anzathu zabwino kungathandize kuti iwo asiye kudana nafe

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi mumayesetsa kulimbikitsa mtendere mumpingo?