Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pewani Zosokoneza ‘M’tsiku la Uthenga Wabwino’

Pewani Zosokoneza ‘M’tsiku la Uthenga Wabwino’

 Pewani Zosokoneza ‘M’tsiku la Uthenga Wabwino’

AKHATE anayi sanadziwe kuti atani. Pachipata cha mzinda pamene analipo, palibe amene anawapatsa mphatso zachifundo. Aaramu amene anazinga mzinda wa Samariya, sanalole kuti chakudya chilowe mumzindawo ndipo munali njala. Kulowa mumzindawo, sikukanawathandiza chifukwa chakudya chinali chodula kwambiri. Pa nthawi imeneyi kunali kutamveka kale kuti ena adya munthu.​—2 Maf. 6:24-29.

Akhate aja anaganiza kuti: ‘Bwanji tipite kumsasa wa Aaramu. Chifukwatu mulimonse mmene zingakhalire, tifa basi.’ Ndiyeno kachisisira katayamba, anauyamba ulendo wa kumsasako. Atafika kumeneko, anapeza kuli zii. Kunalibe mlonda aliyense. Mahatchi ndi abulu anali omanga koma panalibe asilikali. Akhate aja atayang’ana muhema, anaona kuti munalibe munthu aliyense koma munali zakudya ndi zakumwa zambiri. Iwo anadya ndi kumwa mmene anafunira. Akhatewo anaonanso golide, siliva, zovala ndi zinthu zina zamtengo wapatali. Iwo anatenga zinthu zimenezi kukazibisa, n’kubwereranso kuti adzatenge zina. Anthu onse anali atathawa pamsasawo. Izi zinachitika chifukwa chakuti mozizwitsa Yehova anachititsa Aaramuwo kumva phokoso la gulu la asilikali ankhondo. Poganiza kuti aukiridwa, Aaramu anathawa wapansi. Iwo analolera kusiya zinthu zawo zonse kuti kaya wina atenga, atenge.

Akhate aja anali kututa zinthu zamtengo wapatali n’kumakazibisa. Koma kenako chikumbumtima chinayamba kuwavutitsa, poganizira kuti anzawo ku Samariya anali kuvutika ndi njala. Ndiyeno anayamba kuuzana kuti: “Sitili kuchita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino.” Motero akhatewa anathamangira ku Samariya kukauza anthu uthenga wabwino wa zimene anapezazi.​—2 Maf. 7:1-11.

Ifenso tikukhala mu nthawi imene tingati ndi “tsiku la uthenga wabwino.” Ponena za mbali yofunika kwambiri ya “chizindikiro cha . . . mapeto a dongosolo lino la zinthu,” Yesu anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:3, 14) Kodi zimenezi ziyenera kutikhudza bwanji?

Tingalemedwe ndi Nkhawa Zathu

Chifukwa chosangalala ndi zinthu zimene anapeza, akhate aja poyamba anaiwala anzawo ku Samariya. Iwo ankangoganizira kwambiri zimene akanatenga. Kodi zoterezi zingatichitikirenso ifeyo? “Njala” ndi mbali ya chizindikiro cha nthawi ya mapeto a dongosolo lino la zinthu. (Luka 21:7, 11) Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) Akhristufe, tiyenera kusamala. Tisalole nkhawa za moyo wathu wa tsiku ndi tsiku kutiiwalitsa kuti nthawi imene tikukhala ndi “tsiku la uthenga wabwino.”

Mlongo wina dzina lake Blessing, sanalole kulemedwa ndi nkhawa za moyo. Iye ankachita upainiya pa nthawi imene ankaphunzira ntchito, kenako anakwatiwa ndi m’bale wina wa pa Beteli ndipo anaitanidwa kukatumikira pa Beteli ya ku Benin. Iye anati: “Ntchito yanga pa Beteli ndi yoyeretsa zipinda, ndipo ndimasangalala nayo kwambiri.” Panopa Blessing amasangalala akaganizira zaka 12 zimene wakhala ali mu utumiki  wa nthawi zonse. Amasangalalanso kuti nthawi zonse wakhala akukumbukira kuti nthawi imene tikukhalayi ndi “tsiku la uthenga wabwino.”

Samalani ndi Zinthu Zimene Zingakuwonongereni Nthawi

Potumiza ophunzira 70, Yesu anawauza kuti: “Zokolola n’zochulukadi, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokololazo kuti atumize antchito okam’kololera.” (Luka 10:2) Kulephera kukolola zinthu pa nthawi yake, kungachititse kuti zinthuzo ziwonongeke. Mofanana ndi zimenezi, kuchita ulesi pa ntchito yolalikira, kungachititse kuti anthu ena adzawonongedwe. Motero Yesu anawauzanso kuti: “Musamachedwe mukamapereka moni panjira.” (Luka 10:4) Mawu amene anawamasulira kuti ‘kupereka moni’ samangotanthauza kunena kuti “moni” kapena kuti “muli bwanji.” Koma amatanthauzanso kukumbatirana popatsana moni ndi kulankhula mawu ena ambirimbiri amene munthu amanena akakumana ndi mnzake. Choncho Yesu analangiza otsatira ake kugwiritsa ntchito bwino nthawi, ndi kupewa zinthu zosafunika zimene zingawasokoneze. Uthenga umene ankafunika kulalikira unali wamwamsanga.

Taganizirani za nthawi imene anthu amathera pa zinthu zina. Kwa zaka zambiri, anthu akhala akuthera nthawi yawo yambiri pa kuonera TV. Nanga bwanji za mafoni ndi makompyuta? Atafunsa anthu 1,000 a ku Britain, anapeza kuti “pa avereji, tsiku lililonse munthu mmodzi amalankhula pafoni ya galaundi kwa maminitsi 88, pafoni ya m’manja kwa maminitsi 62, amatumiza ma Imelo kwa maminitsi 53 ndipo amatumiza mauthenga ena kwa maminitsi 22.” Tikaphatikiza nthawi yonseyi, kuchuluka kwake kumaposa nthawi yonse imene mpainiya wothandiza amathera mu utumiki pa tsiku. Kodi ndi nthawi yochuluka bwanji imene inuyo mumathera pa zinthu zimenezi?

Erns Seliger ndi mkazi wake Hildegard, ankagwiritsa ntchito nthawi yawo mwanzeru. Tikaphatikiza zaka zimene iwo anakhala m’ndende za Nazi ndi za Chikomyunizimu, zimakwana 40. Atatulutsidwa kundendeko, ankachita upainiya mpaka pamene anamaliza utumiki wawo wapadziko lapansi.

Anthu ambiri ankafuna kulemberana makalata ndi banja la Seliger. Izi zikanachititsa kuti banjali lizithera nthawi yawo yonse, likulemba ndi kuwerenga makalata. Koma iwo ankaika patsogolo zinthu zauzimu pa moyo wawo.

N’zoona kuti tonsefe timasangalala kulankhulana pafoni kapena kulemberana makalata ndi anthu amene timawakonda, ndipo palibe cholakwika ndi zimenezo. Ndi bwino tsiku lililonse kupeza nthawi yoyenera yochitira zinthu ngati zimenezi. Komabe, tisalole zinthu ngati zimenezi kutidyera nthawi chifukwa nthawi imene tikukhalayi ndi tsiku lolalikira uthenga wabwino.

Lalikirani Uthenga Wabwino Mokwanira

Ndi mwayi kukhala ‘m’tsiku la uthenga wabwino.’ Tisalole maganizo athu kutisokoneza ngati mmene anachitira akhate aja poyamba. Iwo kenako anati: “Sitili kuchita bwino ife.” Nafenso sitiyenera kulola kuti zofuna zathu kapena zinthu zotayitsa nthawi zitilepheretse kulalikira mokwanira.

Tili ndi chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Pambuyo poganizira zimene anachita mu utumiki kwa zaka 20, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu.” (Aroma 15:19) Paulo sanalole kuti changu chake chizirale. Nafenso tiyeni tikhale achangu ngati mmene iye analili polalikira uthenga wa Ufumu ‘m’tsiku la uthenga wabwino.’

[Chithunzi patsamba 28]

Blessing sanalole kuti zofuna zake zimulepheretse kuchita utumiki wa nthawi zonse

[Chithunzi patsamba 29]

Banja la a Seliger linkagwiritsa ntchito nthawi yawo mwanzeru