Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngati Munatumikirapo pa Udindo Wina Mumpingo, Kodi Mungatumikirenso?

Ngati Munatumikirapo pa Udindo Wina Mumpingo, Kodi Mungatumikirenso?

 Ngati Munatumikirapo pa Udindo Wina Mumpingo, Kodi Mungatumikirenso?

KODI munayamba mwatumikirapo pa udindo winawake mumpingo? Mwina munali mtumiki wothandiza kapena mkulu. Mwinanso munachitapo utumiki wa nthawi zonse. N’zosakayikitsa kuti munkasangalala kwambiri ndi utumikiwo, koma mwina pa zifukwa zina panopa simukuchitanso utumikiwo.

N’kutheka kuti munatula pansi udindowo n’cholinga choti muzisamalira banja lanu. Mwinanso chinali chifukwa cha ukalamba kapena matenda. Ngati munasiya pa zifukwa zimenezi, sizikutanthauza kuti ndinu wolephera. (1 Tim. 5:8) M’nthawi ya atumwi, Filipo anali mmishonale koma kenako anasiya n’kukakhala ku Kaisareya kumene ankasamalira banja lake. (Mac. 21:8, 9) Nayenso Mfumu Davide atakalamba, anakonza zoti mwana wake Solomo alowe ufumu wake. (1 Maf. 1:1, 32-35) Ngakhale zinali choncho, Yehova ankakondabe Filipo ndi Davide ndipo ankayamikira zimene anachita. Mpaka pano timawakumbukira kuti iwo anali anthu abwino.

N’kuthekanso kuti munachita kuimitsidwa pa udindo wanuwo. Kodi pali zimene munalakwitsa? Kapena kodi mavuto ena m’banja lanu ndi amene anachititsa? (1 Tim. 3:2, 4, 10, 12) Mwina pa nthawiyo munaona kuti nkhani yanuyo sinaweruzidwe mwachilungamo ndipo mpaka pano zimakupwetekani kwambiri.

Yesetsani Kuti Mutumikirenso

Kodi munthu amene anasiya kutumikira pa udindo winawake sangatumikirenso? Ayi, akhoza kutumikiranso. Koma ayenera kuyesetsa kuti ayenerere kutumikiranso. (1 Tim. 3:1) N’chifukwa chiyani muyenera kufuna kuyambanso kutumikira? Chifukwa chake n’chofanana ndi chimene chinakuchititsani kudzipereka kwa Mulungu, chomwe ndi kukonda Yehova ndiponso anthu amene amam’tumikira. Ngati mukufuna kusonyeza chikondi chimenechi mwa kutumikiranso, Yehova angakugwiritseni ntchito. Ndipo zinthu zimene munaphunzira pa nthawi imene munkatumikira komanso imene munasiya kutumikira, zingathandize kwambiri.

Taganizirani mawu olimbikitsa amene Yehova anauza Aisiraeli pambuyo poti mtunduwo wataya mwayi wom’tumikira chifukwa chosamvera. Mawu ake amati: “Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwa.” (Mal. 3:6) Yehova ankakonda Aisiraeli ndipo ankafunabe kuwagwiritsa ntchito. Iye akufunabe kukugwiritsani ntchito m’tsogolo. Ndiyeno, kodi muyenera kuchita chiyani panopa? Chimene chimathandiza kwambiri kuti munthu azitumikira bwino Mulungu, ndi moyo wake wauzimu osati luso lachibadwa limene ali nalo. Motero, nthawi imene mwasiya kutumikira mumpingo, muyenera kuchita khama kuti moyo wanu wauzimu ulimbe.

Kuti ‘mukhale amphamvu’ m’chikhulupiriro, muyenera ‘kufuna Yehova, ndi mphamvu yake.’ (1 Akor. 16:13; Sal. 105:4) Njira ina imene mungachitire zimenezi ndiyo kupemphera mochokera pansi pa mtima. Mukamamufotokozera Yehova vuto lanu, muzimuuza zakukhosi kwanu ndiponso muzipempha mzimu wake woyera. Mukatero mudzayandikira kwambiri Yehova ndipo izi zidzakuthandizani kukhala olimba. (Sal. 62:8; Afil. 4:6, 13) Njira ina imene ingakuthandizeni kulimbitsa moyo wanu wauzimu, ndiyo kuphunzira Mawu a Mulungu mozamirapo. Popeza panopa  mulibe zochita zambiri, mukhoza kuyambanso kutsatira pulogalamu imene inkakuvutani kuitsatira, monga kuphunzira kwambiri Baibulo panokha ndiponso kuchita phunziro labanja nthawi zonse.

Panopa mukutumikirabe Yehova chifukwa ndinu wa Mboni. (Yes. 43:10-12) Mwayi wamtengo wapatali kwambiri umene tonsefe tili nawo ndi kukhala “antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Kuchita zambiri pa ntchito yolalikira ndi njira inanso yolimbitsira moyo wanu wauzimu ndiponso wa anthu ena amene mumalalikira nawo.

Kulimbana ndi Nkhawa

Kuimitsidwa pa udindo kungakuchititseni manyazi ndiponso kungakudandaulitseni. Mwina mungayambe kupeza zifukwa zodzikhululukira. Kodi chingachitike n’chiyani ngati abale anamvetsera maganizo anu komabe n’kuona kuti simuyenera kupitiriza udindo wanu? Mungayambe kudana ndi abalewo ndipo izi zingapangitse kuti musafunenso kuyesetsa kuti muyambenso kutumikira. Zingakulepheretseninso kuphunzirapo kanthu pa zimene zinachitikazo. Tiyeni tione zimene zinachitikira Yobu, Manase ndi Yosefe, ndiponso mmene zingakuthandizireni kuti mulimbane ndi maganizo amenewa.

Yobu ankaimira anthu ena kwa Yehova. Iye analinso mkulu ndiponso woweruza wa m’mudzi. (Yobu 1:5; 29:7-17, 21-25) Kenako, pa nthawi yovuta kwambiri ya moyo wake, chuma chake chinawonongeka, ana ake anafa ndipo iye anayamba kudwala. Izi zinachititsa kuti anthu asiye kumulemekeza. N’chifukwa chake Yobu anati: “Iwo osafikana msinkhu wanga andiseka.”​—Yobu 30:1.

Yobu ankaona kuti sanalakwe chilichonse ndipo anafuna kudzitchinjiriza pamaso pa Mulungu. (Yobu 13:15) Komabe Yobu anayembekeza Yehova ndipo zotsatira zake zinali zabwino. Yobu anaphunzira kuti anafunika kuthandizidwa kuti asinthe maganizo ake makamaka chifukwa cha zimene anachita pamene ankayesedwa. (Yobu 40:6-8; 42:3, 6) Kudzichepetsa kwa Yobu kunachititsa kuti adalitsidwe kwambiri ndi Mulungu.​—Yobu 42:10-13.

Ngati munaimitsidwa pa udindo chifukwa choti munachita zinazake zosayenera, mwina mungamakayikire ngati Yehova ndiponso Akhristu anzanu angakukhululukireni n’kuiwala zimene munachitazo. Koma taganizirani za Mfumu Manase ya Yuda. Iye “anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.” (2 Maf. 21:6) Koma pa nthawi imene ankamwalira anali wokhulupirika ndiponso anali mfumu. Kodi zimenezi zinatheka bwanji?

Manase anasintha pambuyo polangidwa. Poyamba, iye sanamvere machenjezo ndipo Yehova analola kuti Asuri am’mange n’kupita naye ku ukapolo kudziko lakutali ku Babulo. Ali kumeneko, “anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.” Manase analapa kuchokera pansi pa mtima n’kuyamba kuchita zinthu zabwino ndipo Yehova anamukhululukira.​—2 Mbiri 33:12, 13.

Sikuti munthu amangofikira kupatsidwanso maudindo onse amene anali nawo poyamba. Komabe pang’ono ndi pang’ono mungayambe kupatsidwa maudindo ena ang’onoang’ono. Kulandira maudindo amenewa n’kumawachita ndi mtima wonse kungathandize kuti mupatsidwe maudindo ena. Koma izi sizichitika kamodzi n’kamodzi ndipo si zophweka. Nthawi zina pangachitike zinthu zokubwezerani m’mbuyo. Ngakhale  zili choncho, zinthu zidzayenda bwino ngati muli ndi mtima wofunitsitsa ndiponso wopirira.

Taganizirani chitsanzo cha Yosefe mwana wa Yakobo. Iye ali ndi zaka 17, abale ake anamuchitira zinthu zopanda chilungamo. Iwo anamugulitsa kukhala kapolo. (Gen. 37:2, 26-28) Iye sanayembekezere kuti abale ake enieni angamuchitire zinthu zoterezi. Komabe, iye anapirira zonsezi ndipo Yehova anamudalitsa moti anakhala woyang’anira “nyumba ya mbuyake.” (Gen. 39:2) Kenako Yosefe anatsekeredwa m’ndende. Ngakhale zinali choncho, iye anakhalabe wokhulupirika ndipo Yehova anali naye moti anaikidwa kukhala woyang’anira akaidi anzake.​—Gen. 39:21-23.

Yosefe sanadziwe kuti zimenezi zidzathandiza m’tsogolo. Iye ankangochita zimene akanatha. Motero, Yehova anamugwiritsa ntchito kuti apulumutse mzera wa makolo amene anadzatulutsa Mbewu yolonjezedwa. (Gen. 3:15; 45:5-8) Ngakhale kuti panopa palibe amene angakhale ndi udindo waukulu ngati umene Yosefe anali nawo, nkhani yakeyi imasonyeza kuti Yehova ndi amene amathandiza kuti atumiki ake alandire maudindo osiyanasiyana. Inunso khalani okonzeka kutumikira mwa kutsanzira Yosefe.

Phunzirani pa Zimene Zinachitika

Yobu, Manase ndi Yosefe anakumana ndi zinthu zovuta kwambiri. Koma anthu atatu onsewa anavomereza zimene Yehova analola kuti ziwachitikire, ndipo anaphunzirapo kanthu. Kodi inuyo mungaphunzirepo chiyani pa zimene zakuchitikirani?

Ganizirani zimene Yehova akufuna kukuphunzitsani. Yobu atapanikizika ndi mavuto, anayamba kuganizira kwambiri za iye mwini n’kulephera kuona bwino nkhani yonseyo. Yehova atamuthandiza mwachikondi, iye anasintha maganizo ake n’kumaona zinthu bwinobwino ndipo anati: “Ndinafotokozera zimene sindinazizindikira.” (Yobu 42:3) Ngati mumawawidwa mtima chifukwa chakuti munaimitsidwa pa udindo, ‘musamadziganizire koposa mmene muyenera kudziganizira; koma muziganiza m’njira yakuti mukhale munthu woganiza bwino.’ (Aroma 12:3) Yehova angakhale akukuphunzitsani m’njira imene mwina simungaimvetse.

Vomerezani chilango. Mwina poyamba, Manase ankaganiza kuti sanayenere kupatsidwa chilango chowawa kwambiri choncho. Koma iye anavomereza chilangocho, analapa ndipo anasiya zoipa zake. Kaya panopa mumamva bwanji ndi chilango chimene munapatsidwa, “dzichepetseni pamaso pa Yehova, ndipo iye adzakukwezani.”​—1 Pet. 5:6; Yak. 4:10.

Khalani oleza mtima ndiponso ololera. Zimene Yosefe anakumana nazo zikanatha kumuchititsa kusunga mkwiyo n’kukhala ndi maganizo obwezera. Koma m’malomwake iye anaphunzira kuchita zinthu mwanzeru ndiponso mwachifundo. (Gen. 50:15-21) Ngati inunso munakhumudwa, lezani mtima. Lolani kuti Yehova akuphunzitseni.

Kodi munatumikirapo pa udindo winawake mumpingo wachikhristu? Lolani kuti Yehova adzakugwiritseni ntchito m’tsogolo. Chitani zimene mungathe kuti mulimbitse moyo wanu wauzimu. Khalani woleza mtima ndiponso wodzichepetsa pamene mukulimbana ndi nkhawa zanu. Landirani ndi mtima wonse utumiki uliwonse umene mungapatsidwe. Dziwani kuti ‘Yehova sadzakaniza chokoma iwo akuyenda mwangwiro.’​—Sal. 84:11.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

Khalani amphamvu m’chikhulupiriro mwa kupemphera kuchokera pansi pa mtima

[Chithunzi patsamba 31]

Kuchita zambiri mu utumiki ndi njira yabwino kwambiri yolimbitsira moyo wanu wauzimu

[Chithunzi patsamba 32]

Lolani kuti Yehova adzakugwiritseni ntchito m’tsogolo