Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Anayambiranso Kukhala ndi Chiyembekezo cha Moyo Wosatha Padziko Lapansi

Anthu Anayambiranso Kukhala ndi Chiyembekezo cha Moyo Wosatha Padziko Lapansi

 Anthu Anayambiranso Kukhala ndi Chiyembekezo cha Moyo Wosatha Padziko Lapansi

“Iwe Danieli, tsekera mawu awa . . . mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.”​—DAN. 12:4.

1, 2. Kodi m’nkhani ino tikambirana mafunso ati?

ANTHU mamiliyoni ambiri masiku ano amamvetsa bwino mfundo za m’Malemba zotsimikizira kuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Chiv. 7:9, 17) Mulungu atalenga anthu, anasonyeza kuti anapanga munthu osati n’cholinga choti akhale ndi moyo kwa zaka zowerengeka kenako n’kufa, koma kuti akhale ndi moyo kosatha.​—Gen. 1:26-28.

2 Aisiraeli anali ndi chiyembekezo choti anthu adzakhalanso angwiro ngati mmene Adamu analili poyamba. Malemba Achigiriki Achikhristu amafotokoza njira imene Mulungu adzagwiritsa ntchito kuti anthu apeze moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Ndiyeno n’chifukwa chiyani anthu anafunika kuyambiranso kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi? Kodi zinatheka bwanji kuti chidziwike kwa anthu mamiliyoni ambiri?

Chiyembekezo Chisokonezedwa

3. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti chiyembekezo cha anthu cha moyo wosatha padziko lapansi chinasokonezeka?

3 Yesu analosera kuti aneneri onyenga adzasokoneza ziphunzitso zake ndipo anthu ambiri adzasocheretsedwa. (Mat. 24:11) Mtumwi Petulo anachenjeza Akhristu kuti: “Padzakhala aphunzitsi onyenga pakati panu.” (2 Pet. 2:1) Mtumwi Paulo ananena za “nthawi imene anthu sadzafunanso chiphunzitso chopindulitsa, koma mogwirizana ndi zilakolako za iwo eni, adzadzipezera okha aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu.” (2 Tim. 4:3, 4) Satana ndi amene akusocheretsa anthu ndipo amagwiritsa ntchito Chikhristu champatuko pobisa choonadi chogwira mtima chokhudza cholinga cha Mulungu polenga anthu ndi dziko lapansi.​—Werengani 2 Akorinto 4:3, 4.

4. Kodi atsogoleri achipembedzo ampatuko amatsutsa chiyembekezo chiti?

4 Malemba amanena kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba limene lidzaphwanya ndi kutha maulamuliro onse a anthu. (Dan. 2:44) Mu Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000, Satana adzatsekeredwa m’phompho, akufa adzaukitsidwa ndiponso anthu padziko lapansi adzakhalanso angwiro. (Chiv. 20:1-3, 6, 12; 21:1-4) Koma atsogoleri ampatuko a Matchalitchi Achikhristu amaphunzitsa zosiyana ndi zimenezi. Mwachitsanzo, cha m’ma 200 C.E., Bambo wa Tchalitchi wa ku Alexandria, dzina lake Origen, ankatsutsa anthu amene ankakhulupirira kuti madalitso amene adzakhalapo mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, ndi apadziko lapansi. Katswiri wa maphunziro a zaumulungu wachikatolika wa ku Hippo, dzina lake Augustine (amene anakhalapo mu 354 mpaka 430 C.E.), “ankakhulupirira ndi kulimbikitsa mfundo yakuti sikudzakhala Ulamuliro wa Zaka 1,000.”​—The Catholic Encyclopedia. *

5, 6. N’chifukwa chiyani Origen ndi Augustine ankanena kuti sikudzakhala Ulamuliro wa Zaka 1,000 padziko lapansi?

5 N’chifukwa chiyani Origen ndi Augustine ankanena kuti sikudzakhala Ulamuliro wa Zaka 1,000 padziko lapansi? Origen anaphunzitsidwa ndi Clement wa ku Alexandria, yemwe anatengera chiphunzitso cha Agiriki chakuti mzimu suufa. Katswiri wina wa maphunziro a zaumulungu, dzina lake Werner  Jaeger, ananena kuti chifukwa chotengera kwambiri ziphunzitso za Plato zokhudza mzimu, Origen “anasakaniza ziphunzitso zachikhristu ndi ziphunzitso za Plato.” Motero Origen ankaphunzitsa kuti madalitso a Ulamuliro wa Zaka 1,000 si apadziko lapansi koma akumwamba.

6 Augustine analowa Chikhristu champatuko ali ndi zaka 33 koma izi zisanachitike, iye ankakhulupirira chiphunzitso cha Plato chimene Plotinus anayambitsa m’zaka za m’ma 200 C.E. Maganizo a Augustine sanasinthe ngakhale pamene analowa Chikhristucho. Buku lina linanena kuti: “Iye anasakaniza mfundo za chipembedzo za m’Chipangano Chatsopano ndi ziphunzitso za Plato zomwe zinachokera ku zikhulupiriro za Agiriki.” (The New Encyclopædia Britannica) Pofotokoza za Ulamuliro wa Zaka 1,000, wotchulidwa m’buku la Chivumbulutso chaputala 20, Augustine “ankaphunzitsa zoti nkhaniyi ndi yophiphiritsa.” (The Catholic Encyclopedia) Bukuli linanenanso kuti: “Nkhani imeneyi . . . pambuyo pake inayambanso kuphunzitsidwa ndi akatswiri a zaumulungu a ku Girisi ndi a ku Roma, moti panalibenso munthu amene akanaphunzitsa za chiyembekezo chimene anthu anali nacho poyamba cha Ulamuliro wa Zaka 1,000.”

7. Kodi ndi chiphunzitso chonyenga chiti chimene chinasokoneza chiyembekezo cha anthu cha moyo wosatha padziko lapansi, ndipo zimenezi zinachitika motani?

7 Motero, chiyembekezo cha anthu chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, chinasokonezedwa ndi chiphunzitso chakuti munthu ali ndi mzimu umene umakhala m’thupi lake, chimene chinayambira ku Babulo wakale n’kufalikira padziko lonse. Matchalitchi Achikhristu atatengera chiphunzitsochi, akatswiri amaphunziro a zaumulungu anapotoza Malemba kuti mavesi ofotokoza za chiyembekezo cha kumwamba, azioneka ngati amaphunzitsa zoti anthu onse abwino amapita kumwamba. Ngati tingayendere mfundo imeneyi, ndiye kuti moyo wa munthu padziko lapansi ungangokhala wakanthawi ndipo cholinga chake ndi kungoona ngati munthuyo ali woyenera kupita kumwamba. Ziphunzitso ngati zimenezi zinasokonezanso chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi chimene Ayuda anali nacho poyamba. Ayudawa atayamba kutengera pang’onopang’ono chiphunzitso cha Agiriki chakuti mzimu suufa, chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi chomwe anali nacho poyamba chinazimiririka. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi mmene Baibulo limafotokozera munthu. Munthu ndi munthu si mzimu. Yehova anamuuza munthu woyamba kulengedwa kuti: “Ndiwe fumbi.” (Gen. 3:19) Kwawo kwa munthu si kumwamba koma padziko lapansi ndipo adzakhalapo kosatha.​—Werengani Salmo 104:5; 115:16.

Choonadi Chiyamba Kuwala Mumdima

8. Kodi akatswiri a zaka za m’ma 1600 ananena zotani pa nkhani ya chiyembekezo cha anthu?

8 Ngakhale kuti zipembedzo zambiri zimene zimati n’zachikhristu zimatsutsa chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi, Satana sanathe kusokonezeratu choonadi cha nkhani ya chiyembekezo cha anthu chimenechi. Kuyambira kale, anthu ena ochepa amene ankawerenga Baibulo mosamalitsa, anayamba kuzindikira choonadi atayamba kumvetsa mmene Mulungu adzabwezeretsere anthu ku ungwiro. (Sal. 97:11; Mat. 7:13, 14; 13:37-39) Cha m’ma 1600, Baibulo linali litamasuliridwa ndi kusindikizidwa m’zinenero zambiri ndipo anthu ambiri anali ndi Malemba Oyera. M’chaka cha 1651, katswiri wina analemba kuti popeza kudzera mwa Adamu, anthu “anataya Paradaiso ndi Moyo Wosatha wapadziko lapansi,” kudzera mwa Khristu “anthu onse adzakhalanso ndi moyo Padziko Lapansi, chifukwa  kupanda kutero ndiye kuti palibe kufanana pa zimene lembali limanena.” (Werengani 1 Akorinto 15:21, 22.) Mmodzi wa akatswiri a ndakatulo otchuka pakati pa anthu olankhula Chingelezi, dzina lake John Milton (anabadwa mu 1608 n’kumwalira mu 1674), analemba buku lakuti Paradise Lost (Paradaiso Wotayika) ndi linzake lakuti Paradise Regained (Paradaiso Wobwezeretsedwa). M’mabuku akewa, Milton anatchula za mphoto imene anthu okhulupirika adzalandire m’paradaiso padziko lapansi. Ngakhale kuti Milton anadzipereka kwambiri pamoyo wake kuphunzira Baibulo, iye anazindikira kuti anthu sangamvetse choonadi cha m’Malemba mpaka nthawi ya kukhalapo kwa Khristu.

9, 10. (a) Kodi Isaac Newton analemba zotani zokhudza chiyembekezo cha anthu? (b) N’chifukwa chiyani Newton ankaona kuti kukhalapo kwa Khristu kunali m’tsogolo kwambiri?

9 Katswiri wina wa masamu wotchuka, dzina lake Isaac Newton (anabadwa mu 1642 n’kumwalira mu 1727), ankachitanso chidwi kwambiri ndi Baibulo. Iye anamvetsa mfundo yakuti anthu oyera mtima adzaukitsidwa n’kukakhala ndi moyo kumwamba ndipo adzalamulira ndi Khristu. (Chiv. 5:9, 10) Ndiyeno ponena za nzika za Ufumuwo, iye analemba kuti: “Anthu adzapitiriza kukhala padziko lapansi pambuyo pa tsiku la chiweruzo, osati kwa zaka 1000 zokha, koma kosatha.”

10 Newton ankakhulupirira kuti kukhalapo kwa Khristu kudzachitika m’tsogolo pambuyo pa zaka zambirimbiri. Wolemba mbiri wina dzina lake Stephen Snobelen, ananena kuti: “Chifukwa china chimene chinachititsa Newton kuona kuti Ufumu wa Mulungu uli kutsogolo choncho, n’chakuti anakhumudwa kwambiri ndi chiphunzitso champatuko cha Utatu chimene chinali ponseponse.” Uthenga wabwino unali udakali wophimbika. Ndipo Newton sanaone gulu lililonse la Akhristu lomwe likanalalikira uthengawu. Iye analemba kuti: “Sitingamvetse ulosi wa Danieli ndiponso wa Yohane [womwe unalembedwa m’buku la Chivumbulutso] mpaka nthawi ya chimaliziro itafika.” Iye analembanso kuti: “Danieli anati, ‘ambiri adzathamanga chauko ndi chauko ndi chidziwitso chidzachuluka.’ Uthenga Wabwino uyenera kulalikidwa ku mitundu yonse chisautso chachikulu chisanafike ndiponso dzikoli lisanathe. Khamu lalikulu lonyamula nthambi za kanjedza limene lidzatuluka m’chisautso chachikulu, silingakhale losawerengeka ndiponso lochokera m’mitundu yonse pokhapokha Uthenga Wabwino utalalikidwa chisautsocho chisanafike.”​—Dan. 12:4; Mat. 24:14; Chiv. 7:9, 10.

11. N’chifukwa chiyani chiyembekezo cha anthu chinali chobisika kwa anthu ambiri m’masiku a Milton ndi Newton?

11 M’masiku a Milton ndi Newton, kufotokoza maganizo otsutsana ndi ziphunzitso za tchalitchi kunali koopsa. Motero, zinthu zambiri zimene Milton ndi Newton analemba pambuyo pophunzira Baibulo, sizinafalitsidwe mpaka iwo atamwalira. Anthu amene anachoka m’tchalitchi cha Katolika m’zaka za m’ma 1500, analephera kusintha chiphunzitso chakuti mzimu suufa, ndipo matchalitchi akuluakulu achipolotesitanti anapitiriza kuphunzitsa zimene Augustine ankaphunzitsa zoti Ulamuliro wa Zaka 1,000 suli kutsogolo koma unachitika kale. Ndiyeno kodi chidziwitso chachuluka pa nthawi ya mapeto ino?

“Chidziwitso Chidzachuluka”

12. Kodi chidziwitso chinayenera kuchuluka pa nthawi iti?

12 Danieli analosera kuti “nthaŵi ya chimaliziro” kudzachitika zinthu zosangalatsa. (Werengani Danieli 12:3, 4, 9, 10.) Yesu anati: “Panthawi imeneyo olungama adzawala ngwee ngati dzuwa.” (Mat. 13:43) Kodi chidziwitso chinachuluka motani nthawi ya chimaliziro? Taganizirani zinthu zina zimene zinachitika chaka cha 1914 chisanafike. Chaka chimenechi ndi chimene nthawi ya chimaliziro inayamba.

13. Kodi Charles Taze Russell analemba zotani atafufuza nkhani yonena za kubwezeretsedwa kwa anthu ku ungwiro?

13 Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kagulu ka anthu ofuna kudziwa choonadi kanayamba kufufuza Malemba kuti kamvetse “chitsanzo cha mawu opindulitsa.” (2 Tim. 1:13) Mmodzi wa anthu amenewa, anali Charles Taze Russell. M’chaka cha 1870, iye ndi anthu ena ochepa ofuna kudziwa choonadi anayambitsa kagulu kophunzira Baibulo. Mu 1872, iwo anafufuza nkhani yonena za kubwezeretsedwa kwa anthu ku ungwiro. Kenako Russell analemba kuti: “Poyamba sitinkadziwa bwinobwino kusiyana pakati pa mphoto imene tchalitchi (mpingo wa Akhristu odzozedwa) chimene chikuyesedwa panopa chidzalandire, ndi mphoto imene anthu onse okhulupirika adzalandire.” Mphoto imene anthu onse okhulupirika adzalandire ndi yakuti iwo “adzakhalanso anthu angwiro ngati mmene kholo lawo Adamu analili mu Edene.” Russell ananena kuti anthu ena anachita kumuthandiza kufufuza mfundo za m’Baibulo. Kodi anthu amenewa anali ndani?

14. (a) Kodi Henry Dunn analimva bwanji lemba la Machitidwe 3:21? (b) Kodi Dunn anati ndani adzakhale padziko lapansi kosatha?

 14 Mmodzi mwa anthu amenewa anali Henry Dunn. Iye anali atalemba za “kubwezeretsa zinthu zonse, kumene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri ake oyera akale.” (Mac. 3:21) Dunn anadziwa kuti kubwezeretsa zinthu kumeneku kukuphatikizapo kuthandiza anthu kuti akhalenso angwiro padziko lapansi, ndipo izi zidzachitika mu Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000. Iye anafufuzanso yankho la funso limene anthu ambiri ankathedwa nalo nzeru. Funsoli linali lakuti, Kodi ndani adzakhale padziko lapansi kosatha? Iye anafotokoza kuti anthu mamiliyoni ambiri adzaukitsidwa, kuphunzitsidwa choonadi ndiponso adzapatsidwa mpata wosonyeza chikhulupiriro mwa Khristu.

15. Kodi George Storrs anazindikira mfundo iti pa nkhani ya kuuka kwa akufa?

15 Mu 1870, nayenso George Storrs anazindikira kuti anthu osalungama adzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi wokhala ndi moyo kosatha. Iye anazindikiranso mfundo ya m’Malemba yakuti munthu amene waukitsidwa, n’kulephera kugwiritsa ntchito mwayi umenewu, “adzawonongedwa, ngakhale ‘wochimwayo atakhala wa zaka zana limodzi.’” (Yes. 65:20) Storrs ankakhala ku Brooklyn, mumzinda wa New York ndipo anali mkonzi wa magazini yotchedwa Bible Examiner.

16. Kodi n’chiyani chinasiyanitsa Ophunzira Baibulo ndi Matchalitchi Achikhristu?

16 Russsell anazindikira kuchokera m’Baibulo kuti nthawi inali itakwana yoti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse. Choncho, mu 1879 anayamba kufalitsa magazini yotchedwa Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence imene panopa imatchedwa Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Poyamba, anthu ochepa kwambiri ndi amene ankadziwa chiyembekezo cha anthu chodzakhala ndi moyo wosatha, koma pa nthawiyi magulu a Ophunzira Baibulo m’mayiko ambiri anayamba kulandira ndiponso kuphunzira Nsanja ya Olonda. Chikhulupiriro chakuti ndi anthu ochepa okha amene adzapita kumwamba, pamene anthu ambirimbiri adzakhala ndi moyo wangwiro padziko lapansi, n’chimene chinasiyanitsa Ophunzira Baibulo ndi Matchalitchi Achikhristu.

17. Kodi chidziwitso chinachuluka motani?

17 “Nthaŵi ya chimaliziro” imene inaloseredwa inayamba mu 1914. Kodi chidziwitso cha chiyembekezo cha anthu chinachulukadi? (Dan. 12:4) Pofika  mu 1913, nkhani za Russell zinasindikizidwa m’manyuzipepala okwana 2,000 ndipo anthu okwana 15 miliyoni ankawerenga nkhani zimenezi. Pofika kumapeto kwa chaka cha 1914, anthu oposa 9 miliyoni ochokera m’mbali zosiyanasiyana za dzikoli anaonera “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.” Sewero limeneli, linkasonyeza zithunzi zoyenda ndi zosayenda zofotokoza Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000. Kuyambira mu 1918 kudzafika mu 1925, nkhani yakuti “Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa,” yomwe inkafotokoza chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi, inakambidwa ndi atumiki a Yehova m’zinenero zoposa 30 padziko lonse. Podzafika mu 1934, Mboni za Yehova zinazindikira kuti anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi ayenera kubatizidwa. Kudziwa zimenezi kunawapatsa mphamvu yolalikira mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu. Masiku ano, anthu mamiliyoni ambiri amayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.

Posachedwapa Kudzakhala “Ufulu Waulemerero”

18, 19. Kodi ndi moyo wotani umene unaloseredwa pa Yesaya 65:21-25?

18 Mneneri Yesaya anauziridwa kulemba za moyo umene anthu a Mulungu adzasangalale nawo padziko lapansi. (Werengani Yesaya 65:21-25.) Maumboni amasonyeza kuti mitengo ina imene inalipo zaka 2,700 zapitazo, pamene Yesaya ankalemba mawu amenewa, idakalipobe. Ndiye tangoganizani inuyo mutakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali chonchi, muli ndi mphamvu ndiponso thanzi labwino.

19 M’malo mongokhala ndi moyo zaka zowerengeka chabe n’kufa, tidzatha kukhala ndi mwayi womanga nyumba, kubzala mbewu komanso kuphunzira zinthu mpaka muyaya. Ndiye taganizirani za mabwenzi amene mudzakhale nawo. Ubwenzi wapamtima umenewu udzapitirira kukula mpaka kalekale. Pa nthawi imeneyi, “ana a Mulungu” adzasangalala padziko lapansi ndi “ufulu waulemerero.”​—Aroma 8:21.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Augustine ankanena kuti Ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu wa Zaka 1,000 si wa m’tsogolo koma unayamba kale pamene tchalitchi [cha Katolika] chinayambika.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi zinatani kuti chiyembekezo cha anthu cha moyo wosatha padziko lapansi chisokonezeke?

• Kodi anthu ena owerenga Baibulo anamvetsa za chiyani m’zaka za m’ma 1600?

• Kodi zinatheka bwanji kuti anthu ayambe kumvetsa chiyembekezo chenicheni cha anthu pamene chaka cha 1914 chinkayandikira?

• Kodi chidziwitso chonena za chiyembekezo cha moyo wapadziko lapansi chachuluka motani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 13]

Wolemba ndakatulo dzina lake John Milton (kumanzere), ndi katswiri wa masamu dzina lake Isaac Newton (kumanja), ankadziwa za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi

[Zithunzi patsamba 15]

Ophunzira Baibulo oyambirira anazindikira kuchokera m’Malemba kuti nthawi inali itakwana yoti chiyembekezo chenicheni cha anthu chidziwike padziko lonse