Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Yesu mwa Kulalikira Molimba Mtima

Tsanzirani Yesu mwa Kulalikira Molimba Mtima

 Tsanzirani Yesu mwa Kulalikira Molimba Mtima

“Tinalimba mtima . . . kulankhula kwa inu uthenga wabwino.”​—1 ATES. 2:2.

1. N’chifukwa chiyani uthenga wabwino wa Ufumu uli wosangalatsa kwambiri?

MUNTHU akamva uthenga wosangalatsa, amakondwera kwambiri. Koma pali uthenga wosangalatsa kwambiri kuposa uthenga wina uliwonse. Umenewo ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Uthenga umenewu umanena motsimikiza kuti matenda, chisoni, imfa ndiponso mavuto ena onse adzatha. Umatipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umatiuza cholinga cha Mulungu ndiponso umatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tikhale mabwenzi ake. Mwina mungaganize kuti aliyense angasangalale kumva uthengawu umene Yesu ankauza anthu. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ena amakana uthengawu.

2. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Ndinabwera kudzagawanitsa” anthu?

2 Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi; sindinabweretse mtendere, koma lupanga. Pakuti ndinabwera kudzagawanitsa, munthu kutsutsana ndi bambo wake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi wake, ndipo mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake. Kunena zoona, adani a munthu adzakhala am’banja lake lenilenilo.” (Mat. 10:34-36) M’malo mosangalala ndi uthenga wabwino, anthu ambiri amakana kumvetsera.  Ena amadana ndi anthu amene amalalikira uthengawo, ngakhale anthuwo atakhala abale awo enieni.

3. Kodi timafunikira chiyani kuti tigwire ntchito yolalikira?

3 Timalalikira choonadi chimenenso Yesu ankalalikira. Ndipo zimene anthu ambiri amachita akamva uthengawu, zimafanananso ndi zimene anthu ankachita m’nthawi ya Yesu. Izi siziyenera kutidabwitsa, chifukwa Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, adzakuzunzani inunso.” (Yoh. 15:20) Ngakhale kuti m’madera ambiri anthu satizunza, anthu ambiri sangalala nafe ndiponso sasonyeza chidwi. Motero, tifunika kukhala ndi chikhulupiriro komanso kulimba mtima kuti tilalikire uthenga wabwino.​—Werengani 2 Petulo 1:5-8.

4. N’chifukwa chiyani Paulo anafunika ‘kulimba mtima’ kuti alalikire?

4 Mwina inu nthawi zina zimakuvutani kuti mulalikire kapena mumachita mantha kuyesa njira zina zolalikirira. Ngati ndi choncho, dziwani kuti simuli nokha. Mtumwi Paulo anali mlaliki wolimba mtima ndiponso ankachidziwa bwino choonadi, koma nthawi zina ankalalikira movutikira. M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Tesalonika, Paulo anati: “Mukudziwa kuti, choyamba titavutika ndi kuchitidwa za chipongwe ku Filipi, tinalimba mtima mwa Mulungu wathu kulankhula kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.” (1 Ates. 2:2) Pa nthawi imene anali ku Filipi, akulu a boma anakwapula Paulo ndi Sila ndi zikoti, kuwaponya m’ndende ndi kumanga mapazi awo m’matangadza. (Mac. 16:16-24) Koma Paulo ndi Sila ‘analimba mtima’ n’kupitirizabe kulalikira. Kodi ifeyo tingawatsanzire bwanji? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione zimene zinathandiza kuti atumiki a Mulungu a m’nthawi za m’Baibulo alalikire choonadi chonena za Yehova molimba mtima. Tionanso zimene tingachite potengera chitsanzo chawo.

Atumiki Akale Anafunika Kulimba Mtima Chifukwa Ankadedwa

5. N’chifukwa chiyani kuyambira kale anthu a Yehova okhulupirika amafunika kulimba mtima?

5 Yesu Khristu ndiye chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kulimba mtima. Ndipotu kuyambira kale mpaka pano, anthu onse okhulupirika kwa Yehova amafunika kulimba mtima. N’chifukwa chiyani tikutero? Anthu atapanduka mu Edene, Yehova analosera kuti padzakhala udani pakati pa atumiki a Mulungu ndi atumiki a Satana. (Gen. 3:15) Sipanapite nthawi kuti udani umenewu uonekere chifukwa Abele, yemwe anali munthu wolungama, anaphedwa ndi m’bale wake. Patapita nthawi, anthu anayamba kudananso ndi Enoke, munthu wokhulupirika yemwe anakhalako Chigumula chisanachitike. Iye analosera kuti Mulungu adzabwera limodzi ndi zikwizikwi za oyera Ake kudzapereka chiweruzo kwa onse osaopa Mulungu. (Yuda 14, 15) Anthu ambiri sanasangalale ndi uthenga umenewu, ndipo ankadana ndi Enoke. N’zosakayikitsa kuti Yehova akanapanda kumugonetsa tulo ta imfa, anthuwo akanamupha. Enoke anasonyeza kulimba mtima kwambiri.​—Gen. 5:21-24.

6. N’chifukwa chiyani Mose anafunika kulimba mtima kuti alankhule ndi Farao?

6 Taganiziraninso za kulimba mtima kumene Mose anasonyeza. Iye analankhula ndi Farao, yemwe anthu ankamuona osati ngati woimira chabe milungu koma ngati mulungu amene, mwana wa Ra, mulungu dzuwa. N’zotheka kuti iye, mofanana ndi Afarao ena, ankalambira fano loimira iyeyo. Farao anali mfumu yoti ikanena yanena, ndipo palibe ankatsutsa zimene iye walamula. Popeza kuti Farao anali ndi mphamvu, anali wodzikuza ndiponso waliuma, sanazolowere kuuzidwa zochita. Ndiyeno Mose, m’busa wofatsa, anapita mobwerezabwereza kwa munthu ameneyu popanda kuitanidwa, ngakhale kuti sankamufunanso ngakhale pang’ono. Kodi kumeneko Mose anakalosera chiyani? Analosera miliri yoopsa. Nanga kodi anapempha chiyani? Anapempha kuti Farao alole akapolo ake mamiliyoni angapo kutuluka m’dzikolo. Kodi pamenepa Mose anafunika kulimba mtima? N’zosachita kufunsa.​—Num. 12:3; Aheb. 11:27.

7, 8. (a) Kodi anthu okhulupirika akale anakumana ndi mayesero otani? (b) Kodi n’chiyani chinathandiza anthu amene anakhalako Chikhristu chisanayambe kuti akhale olimba mtima pokweza ndi polimbikitsa kulambira koyera?

7 Nthawi imeneyi itadutsa, aneneri ndi atumiki  ena okhulupirika a Mulungu molimba mtima anakhalabe kumbali ya kulambira koona. Dziko la Satana linkadana nawo. Paulo anati: “Anaponyedwa miyala, anayesedwa, anachekedwa pakati ndi macheka, anafa mwa kuphedwa ndi lupanga, anayendayenda atavala zikopa za nkhosa, zikopa za mbuzi, pamene anali osowa, pamene anali m’chisautso, ndi pamene anali kuzunzidwa.” (Aheb. 11:37) Kodi n’chiyani chimene chinathandiza atumiki a Mulungu okhulupirika amenewo kukhala olimba? M’mavesi oyambirira, mtumwiyu anatchula chimene chinapatsa Abele, Abulahamu, Sara ndi ena mphamvu kuti apirire. Iye anati: “[Iwo] sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo. Koma [mwa chikhulupiriro] anawaona ali patali nawalandira.” (Aheb. 11:13) Mosakayika, aneneri monga Eliya, Yeremiya ndi anthu ena okhulupirika amene anakhalako Chikhristu chisanayambe, molimba mtima anakhala kumbali ya kulambira koona chifukwa chakuti nawonso ankakhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova.​—Tito 1:2.

8 Anthu okhulupirika amenewo, amene anakhalako Chikhristu chisanayambe, ankayembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo. Iwo akadzaukitsidwa, Khristu Yesu monga wansembe limodzi ndi a 144,000 omwe ndi ansembe aang’ono, adzawathandiza moti m’kupita kwa nthawi adzakhala angwiro ndipo ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda.’ (Aroma 8:21) Ndiponso, Yeremiya ndi atumiki ena a Mulungu kalelo analimba mtima chifukwa cha malonjezo a Yehova. Lina mwa malonjezo amenewa ndi limene anauza Yeremiya kuti: “Adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.” (Yer. 1:19) Masiku ano, tikamasinkhasinkha malonjezo a Mulungu a zimene iye adzatichitira m’tsogolo komanso kuti adzatiteteza mwauzimu, nafenso timalimbikitsidwa.​—Miy. 2:7; werengani 2 Akorinto 4:17, 18.

Yesu Ankalalikira Molimba Mtima Chifukwa cha Chikondi

9, 10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulimba mtima pamaso pa (a) atsogoleri achipembedzo, (b) gulu la asilikali, (c) mkulu wa ansembe, (d) Pilato?

9 Yesu, yemwe ndi chitsanzo chathu, anasonyeza kulimba mtima m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Yesu sanafewetse dala uthenga umene Mulungu anafuna kuti anthu adziwe, ngakhale kuti ankadedwa ndi olamulira amene anali ndi chikoka pa anthu. Iye mopanda mantha anavumbula khalidwe lodzilungamitsa ndiponso ziphunzitso zabodza za atsogoleri achipembedzo amphamvuwo. Anthu amenewo anali ndi mlandu, ndipo Yesu anawauza zimenezo momveka bwino komanso mosapita m’mbali. Pa nthawi ina, iye anati: “Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! chifukwa mumafanana ndi manda opaka laimu woyera, amene kunja kwake amaonekadi okongola, koma mkati mwake muli mafupa a anthu akufa ndi zonyansa za mitundu yonse. Mofananamo inunso, pamaso pa anthu, mumaonekadi ngati olungama koma mkati mwanu mwadzala chinyengo ndi kusamvera malamulo.”​—Mat. 23:27, 28.

10 Gulu la asilikali limene linali kumufunafuna litamupeza m’munda wa Getsemane, Yesu molimba mtima anadzidziwikitsa. (Yoh. 18:3-8) Kenako iwo anapita naye ku Bungwe Lalikulu la Ayuda kumene anakafunsidwa mafunso ndi mkulu wa ansembe. Ngakhale kuti anadziwa kuti mkulu wa ansembeyo ankafuna kupeza chifukwa chomuphera, Yesu sanaope kunena kuti Iyeyo anali Khristu komanso Mwana wa Mulungu. Iye ananenanso kuti iwo adzamuona ‘atakhala kudzanja lamanja lamphamvu [ndiponso] akubwera ndi mitambo yakumwamba.’ (Maliko 14:53, 57-65)  Atangochoka kumeneko ali womangidwa, Yesu anakaima pamaso pa Pilato, amene akanatha kumumasula. Koma apa Yesu anangokhala chete osanenapo chilichonse pa milandu imene anali kumuneneza. (Maliko 15:1-5) Zonsezitu zinafuna kulimba mtima kwambiri.

11. Kodi kulimba mtima kumagwirizana bwanji ndi chikondi?

11 Koma kwa Pilato yemwe uja, Yesu anati: “Chimene ndinabadwira, ndi chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.” (Yoh. 18:37) Yehova anali atatumiza Yesu kuti adzalalikire uthenga wabwino, ndipo iye ankasangalala kuchita zimenezo chifukwa chakuti ankakonda Atate wake wakumwamba. (Luka 4:18, 19) Yesu ankakondanso anthu. Ankadziwa kuti anthuwo anali m’mavuto. Ifenso timalalikira molimba mtima chifukwa chakuti timakonda kwambiri Mulungu ndi anansi athu.​—Mat. 22:36-40.

Mzimu Woyera Umatipatsa Mphamvu Kuti Tizilalikira Molimba Mtima

12. Kodi ophunzira oyambirira anasangalala chifukwa chiyani?

12 Patadutsa milungu ingapo kuchokera pamene Yesu anafa, ophunzira ake anasangalala kwambiri ataona kuti Yehova akuwonjezera anthu amene anali kupulumutsidwa. Inde, pa tsiku limodzi lokha, anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa. Anthu amenewa anali Ayuda komanso anthu olowa Chiyuda ochokera kumayiko ena, ndipo anabwera ku Yerusalemu ku chikondwerero cha Pentekosite. Ndipo nkhani imeneyi iyenera kuti inali ponseponse mumzindawo umene unali kuchimake kwa Chiyuda. Baibulo limati: “Anthu onse anayamba kuchita mantha, ndipo atumwiwo anayamba kuchita zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri.”​—Mac. 2:41, 43.

13. Kodi n’chifukwa chiyani abalewa anapemphera kuti akhale olimba mtima, ndipo chinachitika n’chiyani?

13 Atsogoleri achipembedzo atakwiya, anagwira Petulo ndi Yohane ndi kuwatsekera m’ndende usiku wonse, ndipo anawalamula kuti asalankhulenso za Yesu. Atawamasula, iwo anafotokozera abale zimene zinachitikazi, ndipo onse pamodzi anapemphera za chitsutso chimenechi kuti: “Yehova, . . . lolani akapolo anu alankhulebe mawu anu molimba mtima.” Kodi chinachitika n’chiyani? “Aliyense wa iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera, ndipo anali kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.”​—Mac. 4:24-31.

14. Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji pa ntchito yathu yolalikira?

14 Onani kuti mphamvu ya mzimu woyera wa Yehova ndi imene inathandiza ophunzirawo kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima. Kuti tilankhule choonadi kwa ena molimba mtima, ngakhale kwa amene amatsutsa uthenga wathu, sizidalira mphamvu zathu. Yehova amapereka mzimu woyera ndipo akhoza kutipatsa mzimuwo ngati timupempha. Mothandizidwa ndi Yehova, ifenso tingakhale olimba mtima ndipo tingapirire chitsutso chilichonse.​—Werengani Salmo 138:3.

Akhristu Masiku Ano Amalalikira Molimba Mtima

15. Kodi choonadi chikugawanitsa bwanji anthu masiku ano?

15 Masiku anonso, choonadi chikugawanitsabe anthu. Anthu ena amasangalala ndi choonadi, pamene ena samvetsa ndipo amaipidwa ndi kulambira kwathu. Enanso amatinena, kutiseka ngakhale kutida kumene, ndipo izi ndi zimene Yesu analosera. (Mat. 10:22) Nthawi zina, anthu amanena nkhani zabodza zokhudza ifeyo ndipo ena amafalitsa nkhani zoterezi chifukwa cha njiru. (Sal. 109:1-3) Ngakhale zili choncho, anthu a Yehova amalalikira uthenga wabwino molimba mtima padziko lonse.

16. Kodi ndi nkhani iti imene ikusonyeza kuti anthu amene timawalalikira angasinthe maganizo chifukwa cha kulimba mtima kwathu?

16 Chifukwa cha kulimba mtima kwathu, anthu angasinthe mmene amaonera uthenga wa Ufumu. Mlongo wina wa ku Kyrgyzstan anati: “Tsiku lina ndikulalikira, bambo wina anandiuza kuti: ‘Ndimakhulupirira Mulungu koma osati Mulungu wa Akhristu. Mukadzabweranso pano, ndidzakupsepsezerani galu.’ Kumbuyo kwake kunali chigalu chachikulu atachimangirira. Koma nthawi imene tinali kugawira Uthenga wa Ufumu Na. 37 wakuti, ‘Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!,’ ndinaganiza zopitanso kunyumba  yomwe ija kuti mwina ndikakumana ndi munthu wina wa m’banjamo. Komabe, amene anatsegula chitseko anali bambo yemwe uja. Nthawi yomweyo ndinapemphera kwa Yehova ndipo kenako ndinati: ‘Ndabweranso, ndipo ndikukumbukira zimene tinakambirana masiku atatu apitawa, komanso ndikukumbukira galu wanu uja. Koma ndati ndisangodutsa chifukwa inenso ndimakhulupirira kuti Mulungu woona ndi mmodzi yekha. Posachedwapa Mulungu adzawononga zipembedzo zimene sizimulemekeza. Kuti mudziwe zambiri, muwerenge kapepala aka.’ Ndinadabwa kwambiri bamboyu atalandira kapepala ka Uthenga wa Ufumu. Kenako, ndinapita kunyumba ina. Patangodutsa mphindi zowerengeka, bambo uja anandithamangira ali ndi Uthenga wa Ufumu m’manja. Ndipo anati: ‘Ndawerenga. Koma kodi ndingatani kuti Mulungu asadzandiwonge?’” Phunziro linayambika ndipo bamboyu anayamba kupezeka pamisonkhano.

17. Kodi kulimba mtima kwa mlongo wina kunamulimbikitsa bwanji wophunzira Baibulo amene ankachita mantha?

17 Kulimba mtima kwathu kungathandizenso anthu ena kukhala olimba mtima. Ku Russia, mlongo wina m’basi anafuna kugawira munthu wina magazini. Ndiyeno, bambo wina anangozambatuka pampando wake, kutsomphola magazini m’manja mwa mlongoyo, kuikwinyakwinya n’kuitaya pansi. Molalata, bamboyo anati mlongoyo amuuze kumene amakhala ndipo anamuchenjeza kuti asiye kulalikira m’mudziwo. Mlongoyo anapemphera kwa Yehova ndipo anakumbukira mawu a Yesu akuti: “Musachite mantha ndi amene amapha thupi.” (Mat. 10:28) Iye anaimirira ndipo modekha anauza bamboyo kuti, “Sindikuuzani kumene ndimakhala, ndipo sindisiya kulalikira m’mudzi uno.” Kenako anatsika m’basimo. Iye sanadziwe kuti m’basimo munalinso mayi yemwe ankaphunzira naye Baibulo. Mayi ameneyo ankalephera kusonkhana chifukwa choopa anthu. Ndiye ataona kulimba mtima kwa mlongo wathuyo, wophunzirayo anatsimikiza kuti ayamba kumasonkhana.

18. Kodi chingakuthandizeni n’chiyani kuti muzilalikira molimba mtima ngati Yesu?

18 M’dziko lotalikirana ndi Mulunguli, kulalikira ngati mmene Yesu anachitira kumafuna kulimba mtima. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuchita zimenezi? Muziganizira za chiyembekezo chanu. Muzilimbitsa chikondi chanu kwa Mulungu ndi anansi. Muzipemphera kwa Yehova kuti mukhale olimba mtima. Nthawi zonse muzikumbukira kuti simuli nokha, chifukwa Yesu ali ndi inu. (Mat. 28:20) Mzimu woyera udzakupatsani mphamvu. Ndipo Yehova adzakudalitsani ndi kukuthandizani. Choncho, tiyeni tikhale olimba mtima ndithu ndi kunena kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Angandichite chiyani munthu?”​—Aheb. 13:6.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi n’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amafunika kulimba mtima?

• Pa nkhani ya kulimba mtima, kodi tikuphunzira chiyani kwa . . .

anthu okhulupirika amene anakhalako Khristu asanabwere?

Yesu Khristu?

Akhristu oyambirira?

Akhristu anzathu masiku ano?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Yesu anavumbula atsogoleri achipembedzo mopanda mantha

[Chithunzi patsamba 23]

Yehova amatithandiza kukhala olimba mtima kuti tilalikire