Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwirizana Kumathandiza Kuti Banja Lizikula Mwauzimu

Kugwirizana Kumathandiza Kuti Banja Lizikula Mwauzimu

 Kugwirizana Kumathandiza Kuti Banja Lizikula Mwauzimu

KUGWIRIZANA n’kofunika kwambiri kuti banja likhale lokonda zinthu zauzimu. Yehova atalenga anthu awiri oyambirira, anasonyeza kuti kugwirizana n’kofunika kwambiri. Hava anayenera kugwira ntchito ndi Adamu monga “wom’thangatira.” (Gen. 2:18) Choncho mwamuna ndi mkazi wake ayenera kugwirizana komanso kuthandizana. (Mlal. 4:9-12) Kugwirizana n’kofunikanso kuti makolo ndiponso ana akwaniritse udindo umene Yehova wawapatsa m’banja.

Kulambira kwa Pabanja

Barry ndi mkazi wake Heidi, ali ndi ana asanu. Iwo amaona kuti kugwirizana pokonzekera phunziro la banja kumawathandiza kupita patsogolo mwauzimu. Barry anati: “Nthawi zonse ndimapatsa mwana aliyense kenakake koti adzachite tikamaphunzira. Nthawi zina ndimawauza kuti akonzekere ndemanga zina kuchokera m’nkhani za mu Galamukani! Timakonzekeranso utumiki wakumunda n’cholinga choti mwana aliyense adziwe zimene angakanene polalikira.” Heidi anawonjezera kuti: “Aliyense amalemba zolinga zauzimu zimene akufuna kukwaniritsa, ndipo nthawi zina timapeza mpata wokambirana pa phunziro lathu la banja kuti tione pomwe tafika pozikwaniritsa.” Banjali linaonanso kuti kukhala ndi masiku ena oti lisamaonere TV kumathandiza kuti aliyense m’banjamo azikhala ndi nthawi yowerenga.

Misonkhano ya Mpingo

Mike, ndi mkazi wake Denise, analera bwino ana awo anayi. Kodi banja lawo linapindula motani chifukwa chochitira limodzi zinthu? Mike anati: “Ngakhale kuti nthawi zina zinthu zinkavuta, kuchita zinthu mogwirizana kunkatithandiza kupezeka pamisonkhano pa nthawi yake.” Denise anati: “Ana athu atayamba kusinkhuka, mwana aliyense tinamupatsa ntchito yake. Mwana wathu wamkazi dzina lake Kim, ankatithandiza kuphika ndi kuika chakudya patebulo.” Mwana wawo wamwamuna, dzina lake Michael anati: “Lachiwiri madzulo tinkakhala ndi msonkhano wa mpingo kunyumba kwathu. Choncho, tinkakonza m’nyumba, kusesamo n’kuika bwino mipando.” Mwana wina dzina lake Matthew anati: “Bambo athu ankafika msanga kunyumba likakhala tsiku la misonkhano n’cholinga choti tonse tikonzekere kukapezeka kumisonkhano.” Kodi zotsatira zake n’zotani?

M’pakedi Kuchita Khama

Mike ananena kuti: “Mu 1987, ine ndi Denise tinayamba upainiya. Pa nthawiyi tinkakhalabe ndi ana athu atatu kunyumba. Awiri mwa ana athu anadzayambanso upainiya, ndipo awiri enawo agwira nawo ntchito yomanga nyumba za Beteli. Chosangalatsanso kwambiri n’chakuti banja lathu lathandiza anthu 40 mpaka kudzipereka n’kubatizidwa. Banja lathu lakhalanso ndi mwayi wogwira ntchito ya zomangamanga, ngakhale m’mayiko ena.”

Kugwirizana m’banja n’kofunika kwambiri ndipo m’pakedi kuchita khama. Kodi mungayesetse kupeza njira zina zolimbikitsira mgwirizano m’banja lanu? Mukatero, mudzaona kuti kugwirizana kudzathandiza kuti banja lanu lizikula mwauzimu.

[Chithunzi patsamba 28]

Kuyesera kulalikira, kumathandiza kuti tizipita patsogolo mu utumiki wakumunda