Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzipatsa Ena Ntchito Zina

Muzipatsa Ena Ntchito Zina

 Muzipatsa Ena Ntchito Zina

NKHANI yopatsa ena zochita inayamba kalekale dzikoli lisanalengedwe. Yehova atalenga Mwana wake wobadwa yekha, anamugwiritsa ntchito ngati “mmisiri” polenga zinthu zina zonse. (Miy. 8:22, 23, 30; Yoh. 1:3) Mulungu atalenga anthu awiri oyambirira anawauza kuti “mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Gen. 1:28) Mlengiyu anawapatsa anthu ntchito yokuza munda wa Edeni kukhala Paradaiso wa padziko lonse. Kuyambira kale, m’gulu la Yehova anthu amapatsana ntchito zina.

Kodi kupatsa ena ntchito zina kumatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani akulu achikhristu ayenera kupatsa ena ntchito zina, ndipo kodi angachite bwanji zimenezi?

Tanthauzo la Kupatsa Ena Ntchito Zina

Kupatsa ena ntchito kumaphatikizapo kupatsa mphamvu munthu wina kuti achite zinthu zina m’malo mwa ifeyo, kapena kuti atenge udindo wathu pa nthawi inayake. Motero munthu akapatsa ena ntchito zina amachititsa kuti anthu enawo athandize pokwaniritsa zolinga zinazake. Izi zimachititsa kuti munthu amene wapatsidwa ntchitoyo akhalenso ndi udindo.

Anthu amene apatsidwa ntchito inayake mumpingo wachikhristu amayenera kugwira bwino ntchito yawoyo komanso kupereka lipoti la mmene ntchitoyo ikuyendera kwa amene anawapatsa ntchitoyo. Amafunikanso azikambirana ndi munthu amene anawapatsa ntchitoyo. Ngakhale  zili choncho udindo waukulu umakhala wa m’bale amene wapereka ntchitoyo. Amafunika kuona mmene ntchitoyo ikuyendera komanso kupereka malangizo ofunika. Ndiyeno ena angafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani munthu ayenera kupatsa ena ntchito zimene akudziwa kuti iyeyo angazichite bwinobwino?’

Ubwino Wake

Taganizirani zimene Yehova anachita atalenga Mwana wake wobadwa yekha. Iye anamugwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse. Baibulo limati, “kudzera mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa, za kumwamba ndi pa dziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka.” (Akol. 1:16) Mlengi akanatha kugwira ntchito zonse yekha bwinobwino, koma anaganiza zopatsa Mwana wake ntchito zina n’cholinga choti nayenso asangalale chifukwa chogwira ntchito yabwino. (Miy. 8:31) Izi zinathandiza kuti Mwanayo adziwe bwino makhalidwe a Mulungu. Choncho tingati Atate anagwiritsa ntchito nthawi imeneyi kuti am’phunzitse Mwana wobadwa yekha ameneyu.

Yesu Khristu atabwera padzikoli, anatengera chitsanzo cha Atate wake chopatsa ena ntchito zina. Iye anaphunzitsa ophunzira ake pang’onopang’ono. Anatumiza atumwi 12 kenako anatumanso ophunzira ena 70 kuti akalalikire. (Luka 9:1-6; 10:1-7) Pamene Yesu ankafika kumadera amene anatumiza anthuwo anapeza kuti ntchito yaikulu yagwirika kale ndipo iye anangopitiriza. Pochoka padzikoli, Yesu anali ataphunzitsa bwino ophunzira ake ndipo anawapatsa udindo waukulu kwambiri kuphatikizapo ntchito yolalikira padziko lonse.​—Mat. 24:45-47; Mac. 1:8.

Mumpingo wachikhristu anthu amapatsa ena ntchito zina komanso kuwaphunzitsa mmene angachitire ntchitozo. Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti zinthu, “zimenezo, uziphunzitse kwa anthu okhulupirika amene nawonso, adzakhala oyenerera bwino lomwe kuphunzitsa ena.” (2 Tim. 2:2) Anthu amene amadziwa zinthu zina ayenera kuphunzitsa ena kuti nawonso adzaphunzitse anzawo.

Mkulu akamapatsa ena ntchito amawathandiza kuti nawonso azisangalala ndi ntchito yochita ubusa komanso yophunzitsa. Akulu amadziwa kuti pali zinthu zina zimene munthu payekha sangathe kuchita. Choncho ndi bwino kupempha ena kuti awathandize pa ntchito zina za mumpingo. Baibulo limanena kuti: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.” (Miy. 11:2) Munthu wodzichepetsa amazindikira kuti pali zina zimene sangathe kuchita. Ngati simupatsa ena ntchito zina, ntchito zizikupanikizani kwambiri moti simungakhale ndi nthawi yocheza ndi banja lanu. Choncho ndi nzeru ndithu kupatsako ena maudindo ena. Tiyerekezere kuti m’bale wina ndi wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu. Iye angapemphe akulu ena kuti awerengere maakaunti a mpingo. Kugwira ntchito imeneyi kungathandize abalewo kuti azidziwa bwino mmene ndalama za mpingo zikuyendera.

Kupatsa ena ntchito zina kumathandiza kuti anthuwo aphunzire zinthu zina komanso kuti akhale ndi luso linalake. Koma kuwonjezera pamenepo kumathandizanso kuti m’bale amene akupatsa ena zochitayo adziwe luso limene anthu ena ali nalo. Motero akulu akamapereka ntchito zoyenera kwa abale ena, zingathandize kuti akuluwo ayese abale amene angadzatumikire ngati atumiki othandiza n’kuona “ngati ali oyenerera.”​—1 Tim. 3:10.

Pomaliza, akulu akamapatsa ena ntchito zina amasonyeza kuti amawadalira anthuwo. Paulo anaphunzitsa Timoteyo umishonale pa nthawi imene ankagwira naye ntchito ya umishonaleyo. Anthu awiriwa anayamba kukondana kwambiri. Paulo anafika ponena kuti Timoteyo anali ‘mwana wake weniweni m’chikhulupiriro.’ (1 Tim. 1:2) Yehova ndi Yesu anafikanso pokondana kwambiri pa nthawi imene anali kuchitira limodzi ntchito yolenga zinthu zina zonse. Popereka ntchito zina  kwa ena, akulu nawonso angafike pokondana kwambiri ndi anthuwo.

N’chifukwa Chiyani Akulu Ena Sakonda Kupatsa Ena Ntchito Zina?

Ngakhale kuti amadziwa kuti ndi bwino kupatsa ena ntchito, akulu ena zimawavuta kutero. Iwo amachita zimenezi poganiza kuti mwina akatero mphamvu zawo zichepa. Iwo amafuna kuti nthawi zonse azikhala ndi mphamvu pa zinthu zimene zikuchitika. Komatu, kumbukirani kuti Yesu asanakwere kumwamba, anapatsa ophunzira ake udindo waukulu kwambiri ndipo ankadziwa kuti iwo adzachita ntchito zazikulu kuposa zimene Yesuyo anachita.​—Mat. 28:19, 20; Yoh. 14:12.

Palinso akulu ena amene kale anaperekapo ntchito kwa ena koma sanasangalale ndi mmene ntchitoyo inayendera. Motero, panopo amaona kuti ndi bwino kuchita okha ntchitoyo kuti iyende bwino komanso mwamsanga. Koma taganizirani chitsanzo cha Paulo. Iye ankadziwa kufunika kopatsa ena ntchito, koma ankazindikiranso kuti nthawi zina ophunzitsidwawo sangachite ntchitoyo ndendende mmene iyeyo angafunire. Paulendo wake woyamba waumishonale, Paulo anaphunzitsa mnyamata wotchedwa Maliko, amene ankayenda naye. Paulo anakhumudwa kwambiri Maliko atasiya ntchito imene anapatsidwa n’kubwerera kunyumba. (Mac. 13:13; 15:37, 38) Komabe Paulo sanasiye kuphunzitsa ena. Monga tanenera kale, iye anaitana Timoteyo kuti aziyenda naye limodzi. Timoteyo atafika poti angathe kusamalira maudindo akuluakulu, Paulo anamusiya ku Efeso, ndipo anam’patsa mphamvu zoika abale oyang’anira mipingo ndi atumiki othandiza.​—1 Tim. 1:3; 3:1-10, 12, 13; 5:22.

Akulunso masiku ano sayenera kusiya kuphunzitsa abale ena, chabe chifukwa choti m’bale mmodzi sanachite bwino pophunzitsidwa. N’chinthu chanzeru kuyamba kukhulupirira ena n’kumawaphunzitsa zinthu ndipo zimenezi n’zofunika kwambiri. Komabe, kodi akulu ayenera kukumbukira chiyani akamapereka ntchito kwa ena?

Mmene Mungapatsire Ena Ntchito Zina

Popatsa ena ntchito zina muyenera kuganizira zinthu zimene abale amene mukuwaganizirawo angakwanitse kuchita. Pa nthawi ina ku Yerusalemu kunafunika anthu oti agwire ntchito yogawira anthu chakudya. Zitatero, atumwi anasankha “amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi mzimu ndi nzeru.” (Mac. 6:1-3) Mukapereka ntchito kwa munthu wosadalirika, iye sangaichite bwino. Motero, muyenera kuyamba ndi kum’patsa ntchito zing’onozing’ono. Ngati munthuyo wagwira ntchitoyo mokhulupirika mukhoza kum’patsa ntchito zina zikuluzikulu.

Komatu pali zambiri zimene zimafunika. Anthufe tili ndi makhalidwe komanso maluso osiyanasiyana. Anthu ena amadziwa zambiri poyerekezera ndi ena. Mwachitsanzo, m’bale amene ali wansangala komanso wokonda kucheza ndi anthu angachite bwino ukalinde. Pamene m’bale amene amachita zinthu mwadongosolo angasankhidwe kukhala wothandizira ntchito za mlembi wa mpingo. Mlongo amene ali ndi luso lokongoletsa zinthu angasankhidwe kuti ayale maluwa pokonzekera Chikumbutso.

Mukamapatsa ena zochita, pamafunika kuwauza bwinobwino zimene akufunika kuchita. Yohane Mbatizi asanatume anthu kwa Yesu, anawafotokozera zimene iye ankafuna kudziwa komanso mafunso amene anthuwo angakafunse. (Luka 7:18-20) Komano Yesu atalangiza ophunzira ake kuti asonkhanitse zotsala zonse pa nthawi imene  anachulukitsa chakudya mozizwitsa, iye sanawauze tsatanetsatane wa chilichonse chimene ayenera kuchita potolera zotsalazo. (Yoh. 6:12, 13) Nkhani yagona pa mtundu wa ntchito imene ikufunika kuchitika komanso ziyeneretso za munthu amene mukufuna kum’patsa ntchitoyo. Amene wapereka komanso amene wapatsidwa ntchitoyo ayenera kudziwa mmene iyenera kuchitikira ndiponso ngati awiriwo azifunika kumadziwitsana za mmene ntchitoyo ikuyendera. Wopatsidwa ntchitoyo ayeneranso kudziwa ngati ali ndi ufulu wochita zinthu zina popanda kufunsa amene wam’patsa ntchitoyo. Ngati ntchitoyo iyenera kuchitika lisanafike tsiku linalake, zingakhale bwino kuti awiriwo akambirane n’kugwirizana za tsikulo, m’malo mongom’pangira wopatsidwa ntchitoyo.

Ngati pakufunikira kutero, munthu wopatsidwa ntchitoyo ayenera kupatsidwa ndalama zokwanira, zida ndiponso thandizo. Zingakhalenso zothandiza kuuza ena zimene mwagwirizanazo. Yesu anapatsa Petulo “makiyi a ufumu wa kumwamba,” pamaso pa ophunzira ake ena. (Mat. 16:13-19) Ngakhale mumpingo, nthawi zina ndi bwinonso kudziwitsa mpingo wonse za amene akusamalira maudindo osiyanasiyana.

Komabe pali mfundo ina yofunika kuikumbukira. Mukapereka ntchito kwa munthu muzipewa kulowerera kwambiri pa ntchitoyo, chifukwa mukamatero munthuyo angaganize kuti simum’khulupirira. N’zoona kuti nthawi zina mungakhumudwe ndi mmene munthuyo wachitira ntchitoyo. Komabe, tikalola kuti m’bale achite mwaufulu ntchito imene tam’patsa, amalimba mtima ndipo amaphunzirapo kanthu. Komabe, si kuti mungangom’siya kuti azichita zilizonse. Mwachitsanzo, ngakhale kuti polenga zinthu, Yehova anapatsa Mwana wake ntchito yoti achite, nayenso ankagwira nawo ntchitoyo. N’chifukwa chake polankhula ndi Mmisiri wake wamkuluyo, iye anati: “Tipange munthu m’chifanizo chathu.” (Gen. 1:26) Motero mwa mawu ndi zochita zanu, m’thandizeni munthuyo kuti alimbikire ntchitoyo, ndipo muzimuyamikira. Iye angalimbikitsidwe ngati mutatchulapo pang’ono zinthu zimene iye wakwaniritsa kale pa ntchito imene akuchitayo. Ngati ntchitoyo sakuichita bwino, musazengereze kum’patsa malangizo omuthandiza. Musaiwale kuti ngati zinthu zitalakwika, inuyo ndi amene mudzaimbidwe mlandu chifukwa ndi amene munam’patsa munthuyo ntchito.​—Luka 12:48.

Anthu ambiri athandizidwa chifukwa chopatsidwa ntchito zosiyanasiyana mumpingo ndi akulu owaganizira. Kunena zoona, potsanzira Yehova akulu onse azidziwa kuti pali zifukwa zomveka zopatsira ena ntchito zina ndiponso azidziwa mmene angachitire zimenezi.

[Bokosi patsamba 29]

KUPATSA ENA NTCHITO

• kumathandiza kuti enanso asangalale ndi ntchito imene yachitika

• kumathandiza kuti ntchito yambiri ichitike

• kumasonyeza nzeru ndi kudzichepetsa

• kumathandiza kuti ena aphunzitsidwe

• kumasonyeza kuti mumakhulupirira ena

[Bokosi patsamba 30]

KAGAWIDWE KA NTCHITO

• Sankhani anthu oyenerera kuchita ntchitoyo

• Afotokozereni mwatsatanetsatane zimene ayenera kuchita pogwira ntchitoyo

• Auzeni momveka bwino zimene mukufuna kukwaniritsa

• Perekani zinthu zonse zofunikira pa ntchitoyo

• Sonyezani kuti ntchitoyo ndi yofunika kwa inu, ndiponso kuti simukukayika kuti iwowo aichita bwino

• Ngati chinachake chitapanda kuyenda bwino pa ntchitoyo, muzikhala wokonzeka kuti inuyo ndi amene mudzaimbidwe mlandu

[Zithunzi patsamba 31]

Mukapatsa ntchito munthu wina muyeneranso kumaona mmene ikuyendera kuti muzidziwa pamene yafika