Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Lankhulani Zoona kwa Mnansi Wanu

Lankhulani Zoona kwa Mnansi Wanu

 Lankhulani Zoona kwa Mnansi Wanu

“Popeza tsopano mwataya chinyengo, aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnansi wake.”​—AEF. 4:25.

1, 2. Kodi anthu ali ndi maganizo otani pa nkhani ya kunena zoona?

KWA ZAKA zambiri, anthu akhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya kunena zoona. Cha m’ma 500 B.C.E., wolemba ndakatulo wina wa ku Greece, dzina lake Alcaeus, anati: “Munthu amanena zoona akaledzera basi.” Iye ankatanthauza kuti munthu akaledzera amanena zoona mwina chifukwa choti amakhala womasuka kulankhula. Nayenso bwanamkubwa wachiroma dzina lake Pontiyo Pilato anasonyeza kuti anali ndi maganizo olakwika pa nkhani yonena zoona. Iye anafunsa Yesu kuti: “Choonadi n’chiyani?”​—Yoh. 18:38.

2 Masiku anonso anthu ambiri ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya kunena zoona. Anthu ambiri amanena kuti zimene munthu wina amaona kuti ndi zoona, sizingakhale zoona kwa wina. Ena amangonena zoona pamene zinthu zili bwino. Buku lina limati: “Kunena zoona n’kwabwino. Koma kumavuta moyo ukakhala pa chiswe moti munthu amakakamizika kunama kuti apulumuke.”​—The Importance of Lying.

3. N’chifukwa chiyani tingati Yesu ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kulankhula zoona?

3 Komatu umu si mmene Akhristu amaonera nkhaniyi. Yesunso sankaona choonadi mwa njira imeneyi. Iye nthawi zonse ankalankhula zoona. Ndipo ngakhale adani ake ankadziwa zimenezi, moti ananena kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo mumaphunzitsa njira ya Mulungu m’choonadi.” (Mat. 22:16) Masiku anonso Akhristu oona amatsanzira Yesu. Iwo amalankhula zoona nthawi zonse. Amagwirizana kwambiri ndi malangizo amene Paulo anapereka kwa okhulupirira anzake, akuti: “Popeza tsopano mwataya chinyengo, aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnansi wake.” (Aef. 4:25) Tiyeni tikambirane mfundo zitatu zokhudza malangizo a Paulo amenewa. Tikambirana tanthauzo la m’nansi wathu, la kunena zoona komanso zimene tingachite kuti tizilankhula zoona pa zochita zathu zonse?

Kodi Mnansi Wathu Ndani?

4. Mosiyana ndi atsogoleri a chipembedzo achiyuda, kodi Yesu anasonyeza bwanji maganizo a Yehova pa nkhani ya mnansi wathu?

4 M’nthawi ya Yesu, atsogoleri a chipembedzo achiyuda ankaphunzitsa kuti Ayuda anzawo kapena anzawo apamtima okha ndiwo anansi awo. Koma Yesu anatengera Atate wake ndipo ankaiona nkhaniyi mmene Atate akewo amaionera. (Yoh. 14:9) Iye anasonyeza bwino ophunzira ake kuti Mulungu sakondera mtundu kapena fuko lina lililonse. (Yoh. 4:5-26) Komanso mzimu woyera unathandiza mtumwi Petulo kuzindikira kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu ulionse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Mac. 10:28, 34, 35) Choncho tiyenera kuona anthu onse ngati anansi athu n’kumawakonda ngakhale amene amachita zinthu ngati adani athu.​—Mat. 5:43-45.

5. Kodi kunena zoona kwa mnansi wathu kumatanthauza chiyani?

5 Ndiyeno kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene anati tiyenera kunena zoona kwa anansi athu? Kunena zoona kumatanthauza kufotokoza zinthu mmene zililidi popanda chinyengo. Akhristu oona sasintha kapena kupotoza mfundo n’cholinga choti ena asadziwe zoona zenizeni. Iwo ‘amanyansidwa ndi choipa,’ ndipo ‘amagwiritsitsa chabwino.’ (Aroma 12:9) Timatsanzira  “Mulungu wa choonadi” mwa kuyesetsa kunena zoona pa zochita zathu zonse. (Sal. 15:1, 2; 31:5) Ngati titasankha bwino mawu, tikhoza kunena zoona ndithu ngakhale pa nkhani zovuta kapena zooneka ngati zochititsa manyazi.​—Werengani Akolose 3:9, 10.

6, 7. (a) Kodi kunena zoona kumatanthauza kuti tiziulula chilichonse chimene tafunsidwa ndi aliyense? Fotokozani. (b) Tchulani anthu amene tiyenera kuwakhulupirira n’kumawauza zoona zokhazokha.

6 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kuulula chilichonse chimene tafunsidwa ndi aliyense? Ayi. Yesu ali padziko lapansi anasonyeza kuti pali anthu ena omwe si oyenera kuwauza tsatanetsatane wa zinthu zina. Atsogoleri achipembedzo omwe anali achinyengo atamufunsa Yesu za komwe kunkachokera mphamvu komanso ulamuliro wake wochitira zozizwitsa, iye anati: “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo inenso ndikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zinthu zimenezi.” Ndipo alembi ndi akulu atakana kupereka yankho la funso limene Yesu anafunsa, iye anati: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.” (Maliko 11:27-33) Iye anaona kuti si bwino kuwayankha chifukwa choti anali achinyengo komanso opanda chikhulupiriro. (Mat. 12:10-13; 23:27, 28) Masiku anonso anthu a Yehova ayenera kusamala ndi anthu ampatuko komanso anthu ena oipa amene amafunsa mafunso ndi zolinga zachinyengo kapena zadyera.​—Mat. 10:16; Aef. 4:14.

7 Paulo anasonyezanso kuti pali anthu ena omwe si oyenera kuwauza tsatanetsatane wa nkhani zina. Iye ananena kuti anthu ‘amiseche ndi olowerera nkhani za eni amalankhula zimene sayenera kulankhula.’ (1 Tim. 5:13) N’zoona kuti anthu sakonda kunena nkhani zachinsinsi kwa anthu amene amakonda kulowerera nkhani zosawakhudza ndiponso amene sasunga chinsinsi. Choncho ndi bwino kutsatira malangizo ouziridwa a Paulo akuti: “Muyesetse kukhala moyo wabata, kusamala zanuzanu.” (1 Ates. 4:11) Pofuna kusamalira nkhani inayake, nthawi zina akulu mumpingo angatifunse zinthu zina zokhudza ifeyo zoti sitingauze munthu wina. Ngati izi zitachitika tiyenera kukhala ogwirizanika n’kunena zoona zokhazokha.​—1 Pet. 5:2.

Lankhulani Zoona M’banja

8. Kodi kulankhula zoona kumathandiza bwanji kuti anthu azigwirizana m’banja?

8 Anthu am’banja amayenera kukhala ogwirizana kwambiri. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kunena zoona zokhazokha tikamalankhulana. Mavuto ambiri komanso kusamvana kungachepe kapenanso kutha kumene ngati polankhulana timakhala omasuka, okoma mtima ndiponso timanena zoona. Mwachitsanzo, kodi tikalakwitsa chinachake, zimativuta kuvomereza kwa mwamuna kapena mkazi wathu, ana athu kapena achibale athu? Kupepesa kochokera pansi pa mtima kumalimbikitsa umodzi ndiponso mtendere m’banja.​—Werengani 1 Petulo 3:8-10.

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kunena zoona sikutanthauza kuti tizilankhula mosaganizira kapena mwamwano?

9 Kulankhula zoona sikutanthauza kuti tizilankhula mosaganizira kapena mwamwano  chifukwa chongoti tikunena chilungamo. Kuchita zimenezi, sikuchititsa anthu kuganiza kuti tikunena zoona. Paulo ananena kuti: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse. Koma khalani okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso anakukhululukirani Mulungu ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.” (Aef. 4:31, 32) Tikamalankhula mokoma mtima komanso mwaulemu, anthu amaona kuti zimene tikulankhulazo n’zofunika komanso kuti tikulemekeza amene tikulankhula nawowo.​—Mat. 23:12.

Lankhulani Zoona Mumpingo

10. Popeza Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani ya kunena zoona, kodi akulu achikhristu angaphunzirepo chiyani?

10 Akamalankhula ndi ophunzira ake, Yesu ankagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva komanso ankalankhula mosapita mbali. Iye ankapereka malangizo mwachikondi koma sankachepetsa mphamvu ya uthenga wake pofuna kusangalatsa anthu. (Yoh. 15:9-12) Mwachitsanzo, ophunzira ake atakangana pa nkhani yoti wamkulu ndani, iye anawalangiza mwamphamvu kuti akhale odzichepetsa. Koma iye anachita zimenezo moleza mtima. (Maliko 9:33-37; Luka 9:46-48; 22:24-27; Yoh. 13:14) Masiku anonso ngakhale kuti akulu achikhristu amayesetsa kutsatira chilungamo, iwo amachita zimenezi popanda kuchita ufumu pa nkhosa za Mulungu. (Maliko 10:42-44) Iwo amatsanzira Yesu mwa kukhala “okomerana mtima wina ndi mnzake” komanso “achifundo chachikulu” akamachita zinthu ndi ena.

11. Ngati timakonda abale athu, kodi tiyenera kugwiritsa ntchito motani lilime lathu?

11 Tikamakhala omasuka ndi abale athu koma mosapitirira malire, tingathe kufotokoza maganizo athu popanda kuwakhumudwitsa. Sitimalola kuti lilime lathu likhale ngati “lumo lakuthwa” limene lingavulaze anzathu ndi mawu okhadzula. (Sal. 52:2; Miy. 12:18) Kukonda abale athu kungatithandize kuti ‘tiletse lilime lathu lisatchule zoipa, ndipo milomo yathu isalankhule chinyengo.’ (Sal. 34:13) Tikatero timalemekeza Mulungu komanso kulimbikitsa mgwirizano mumpingo.

12. Kodi nthawi zonse munthu akanena bodza amafunika kuweruzidwa? Fotokozani.

12 Akulu amayesetsa kuteteza mpingo kuti usaipitsidwe ndi anthu okonda kujeda ndi kuneneza anzawo. (Werengani Yakobe 3:14-16.) Munthu woneneza amafuna kuti mnzakeyo zinthu zisamuyendere bwino kapena kuti apeze mavuto. Iye amachita zambiri osati kungonena zinthu zing’onozing’ono, kungopotoza nkhani kapena kungoiwonjezera. N’zoona kuti kunama kulikonse n’koipa koma sikuti munthu akangopanda kunena zoona ndiye kuti akufunika kuweruzidwa. Choncho akulu asamachite zinthu monyanyira akamva kuti wina wanena zabodza. Iwo ayenera kukhala ololera komanso oganiza bwino. Zimenezi zingawathandize kuti adziwe ngati munthuyo akufunika chiweruzo chifukwa choti ali ndi chizolowezi chonena mabodza  kapena kunena zoipa za anthu ena. Nthawi zina munthuyo amangofunika kulangizidwa mwamphamvu koma mwachikondi pogwiritsa ntchito Malemba.

Lankhulani Zoona Kuntchito Komanso Pochita Malonda

13, 14. (a) Fotokozani zinthu zachinyengo zimene ena amachita kuntchito. (b) Kodi kugwira ntchito mwakhama komanso mokhulupirika kuli ndi ubwino wotani?

13 Masiku ano chinyengo chili ponseponse. Choncho zingakhale zovuta kunena zoona kwa anthu amene atilemba ntchito. Anthu ambiri amanama pofunsira ntchito. Mwachitsanzo anthu ena amatha kukokomeza maphunziro kapena luso lawo n’cholinga choti apeze ntchito yapamwamba. Palinso anthu ena amene amaswa malamulo a kampani mwa kuchita zinthu zawozawo pa nthawi yantchito. Iwo mwina amawerenga zinthu zosagwirizana ndi ntchito yawo, kuimba mafoni kwa anzawo, kutumizirana mauthenga ndi anzawo komanso kufufuza zinthu pa Intaneti.

14 Akhristu oona amadziwa kuti nthawi zonse ayenera kulankhula zoona ndiponso kukhala okhulupirika. (Werengani Miyambo 6:16-19.) Paulo anati: “Timafuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheb. 13:18) Motero Akhristu ayenera kugwira ntchito tsiku lonse mokhulupirika kuti asadzalandire malipiro a ntchito imene sanagwire. (Aef. 6:5-8) Tikamagwira ntchito mwakhama timalemekezanso Atate wathu wakumwamba. (1 Pet. 2:12) Chitsanzo pa nkhani imeneyi ndi m’bale wina wotchedwa Roberto wa ku Spain. Iye anayamikiridwa ndi abwana ake chifukwa cha khama komanso kukhulupirika kwake pa ntchito. Chifukwa cha zimenezi, kampaniyo inalembanso ntchito anthu ambiri a Mboni za Yehova. Nawonso ankagwira ntchito mokhulupirika kwambiri. Pakutha pa zaka zingapo, Roberto anali atapezera ntchito abale 23 komanso ophunzira Baibulo 8.

15. Kodi Mkhristu amene amachita bizinesi angasonyeze bwanji kuti amanena zoona?

15 Ngati sitili pa ntchito yolembedwa kodi timakhala oona mtima pochita malonda kapena nthawi zina timanamiza makasitomala athu? Anthu ena amakonda kunama potsatsa malonda awo kapena kuchemerera ntchito yawo n’cholinga choti ziwayendere. Ena amapereka kapena kulandira ziphuphu. Koma Mkhristu sayenera kuchita zimenezi. Timayesetsa kuchitira ena zimene timafuna kuti iwo atichitire.​—Miy. 11:1; Luka 6:31.

Lankhulani Zoona ndi Akuluakulu a Boma

16. Kodi ndi zinthu ziti zimene Akhristu amapereka kwa (a) akuluakulu a boma? (b) Yehova?

16 Yesu anati: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.” (Mat. 22:21) Kodi ndi “zinthu” ziti zimene tiyenera kupereka kwa akuluakulu aboma omwe ali ngati Kaisara? Yesu ananena mawu amenewa pamene ankakambirana za misonkho. Motero Akhristu amamvera malamulo kuphatikizapo okhudza misonkho, n’cholinga choti chikumbumtima chawo chikhale choyera pamaso pa Mulungu komanso anthu. (Aroma 13:5, 6) Koma timadziwa kuti Yehova ndiye Wolamulira wa chilengedwe chonse ndiponso Mulungu woona yekha, amene tiyenera kumukonda ndi mtima wathu wonse, ndi moyo wathu wonse, ndi maganizo athu onse, ndi mphamvu zathu zonse. (Maliko 12:30; Chiv. 4:11) Motero timagonjera Yehova Mulungu ndi mtima wathu wonse.​—Werengani Salmo 86:11, 12.

17. Kodi anthu a Yehova amaona bwanji nkhani yolandira chithandizo cha boma?

17 M’mayiko ambiri, boma limapereka chithandizo kwa anthu osauka. Ngati Mkhristu akuyenerera, palibe vuto ngati atalandira nawo.  Ngati timalankhula zoona ndi mnansi wathu, sitidzanamiza akuluakulu a boma ndi cholinga choti tilandire nawo chithandizocho.

Munthu Wolankhula Zoona Amadalitsidwa

18-20. Fotokozani madalitso amene amabwera tikamanena zoona kwa anansi athu.

18 Tikamalankhula zoona timadalitsidwa mu njira zambiri. Timakhala ndi chikumbumtima choyera ndiponso mtima wathu umakhala m’malo. (Miy. 14:30; Afil. 4:6, 7) Kukhala ndi chikumbumtima choyera ndi kofunika kwambiri pamaso pa Mulungu. Munthu akamachita zachinyengo, amakhala ndi nkhawa poopa kuti ena angatulukire zochita zakezo. Koma munthu woona mtima sakhala ndi nkhawa imeneyi.​—1 Tim. 5:24.

19 Ndipotu pali madalitso enanso. Paulo anati: “Tikudzichitira umboni mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu . . . olankhula zoona.” (2 Akor. 6:4, 7) Umboni wa zimenezi ndi nkhani ya m’bale wina wa ku Britain. Pogulitsa galimoto yake, iye anauza munthu amene ankafuna kuigula zonse zokhudza galimotoyo. Ananena ubwino wake komanso mavuto ake ngakhale kuti ena mwa mavutowo sanali oonekera. Munthu uja ataitenga n’kukaiyesa anaona kuti m’bale uja ananena zoona, ndipo anamufunsa ngati anali wa Mboni za Yehova. N’chifukwa chiyani anafunsa? Iye anadabwa chifukwa m’baleyo anali woona mtima komanso ankavala modzilemekeza. Zimenezi zinachitsa kuti m’baleyo amulalikire munthuyo.

20 Kodi nafenso timatamanda Mlengi wathu mwa kukhala oona mtima nthawi zonse? Paulo anati: “Tasiya zamanyazi zochitidwa mseri, ndipo sitikuyenda mwachinyengo.” (2 Akor. 4:2) Choncho tiyeni tiziyesetsa kulankhula zoona nthawi zonse. Tikatero, timalemekeza Atate wathu wa kumwamba komanso anthu ake.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi mnansi wathu ndani?

• Kodi kunena zoona ndi mnansi wathu kumatanthauza chiyani?

• Kodi kuona mtima kumalemekeza bwanji Mulungu?

• Tchulani madalitso amene amabwera tikamanena zoona.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi mumavomereza zimene mwalakwitsa, ngakhale zitakhala zazing’ono?

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi mumanena zoona mukamafunsira ntchito?