Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani “Achangu pa Ntchito Zabwino”

Khalani “Achangu pa Ntchito Zabwino”

 Khalani “Achangu pa Ntchito Zabwino”

Yesu “anadzipereka m’malo mwa ife kuti atilanditse ku mkhalidwe wa kusamvera malamulo kwa mtundu uliwonse ndi kuti adziyeretsere anthu akeake, achangu pa ntchito zabwino.”​—TITO 2:14.

1. Fotokozani zimene zinachitika pa Nisani 10, m’chaka cha 33 C.E., Yesu atafika kukachisi.

PANALI pa Nisani 10, m’chaka cha 33 C.E., kutangotsala masiku owerengeka kuti tsiku la chikondwerero cha Pasika lifike. Anthu ambiri anasonkhana kukachisi wa ku Yerusalemu poyembekezera tsikuli. Kodi Yesu atafika kukachisiko anatani? Mateyo, Maliko ndi Luka analemba kuti Yesu kachiwirinso anathamangitsa anthu ogula ndi kugulitsa zinthu m’kachisi. Iye anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda. (Mat. 21:12; Maliko 11:15; Luka 19:45) Izi zinasonyeza kuti changu, chake chimene anachisonyeza zaka zitatu m’mbuyomo, chinalipobe.​—Yoh. 2:13-17.

2, 3. Tikudziwa bwanji kuti kuwonjezera pa kuyeretsa kachisi, Yesu anachitanso zinthu zina zosonyeza kuti anali wachangu?

2 Zimene Mateyo analemba zimasonyeza kuti kuwonjezera pa kuyeretsa kachisi, Yesu anachitanso zinthu zina zosonyeza kuti anali wachangu. Anachiritsanso akhungu ndi olumala amene anabwera kwa iye. (Mat. 21:14) Nayenso Luka ananena zinthu zina zimene Yesu anachita. Iye anati: “[Yesu] anayamba kuphunzitsa m’kachisimo tsiku ndi tsiku.” (Luka 19:47; 20:1) Motero utumiki wa Yesu unasonyeza kuti anali wachangu.

3 Kenako mtumwi Paulo analemba kalata yopita kwa Tito ndipo m’kalatayo ananena kuti  Yesu “anadzipereka m’malo mwa ife kuti atilanditse ku mkhalidwe wa kusamvera malamulo kwa mtundu uliwonse ndi kuti adziyeretsere anthu akeake, achangu pa ntchito zabwino.” (Tito 2:14) Kodi masiku ano tingakhale “achangu pa ntchito zabwino” m’njira ziti? Ndipo kodi zitsanzo za mafumu abwino a Yuda zingatithandize bwanji?

Khalani Achangu Polalikira ndi Kuphunzitsa

4, 5. Kodi mafumu anayi a Yuda anasonyeza bwanji kuti anali a changu pa ntchito zabwino?

4 Asa, Yehosafati, Hezekiya ndi Yosiya anachita zinthu zothandiza kuti mu Yuda musakhalenso kulambira mafano. Asa ‘anachotsa maguwa a nsembe achilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zawo, nalikha zifanizo zawo.’ (2 Mbiri 14:3) Chifukwa cha changu pa kulambira Yehova, Yehosafati “anachotsanso misanje ndi zifanizo m’Yuda.”​—2 Mbiri 17:6; 19:3. *

5 Pambuyo pa masiku 7 a chikondwerero cha Pasika chimene Hezekiya anakonza ku Yerusalemu, “Aisrayeli onse opezekako anatuluka kumka ku midzi ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe m’Yuda monse, ndi m’Benjamini, m’Efraimunso, ndi m’Manase, mpaka adaziononga zonse.” (2 Mbiri 31:1) Yosiya anakhala mfumu ali kamwana ka zaka 8. Ponena za iye, Malemba amati: “Atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga.” (2 Mbiri 34:3) Motero mafumu anayi onsewa anali a changu pa ntchito zabwino.

6. N’chifukwa chiyani utumiki wathu umafanana ndi ntchito imene mafumu okhulupirika a Yuda anagwira?

6 Ifenso masiku ano timagwira ntchito yaikulu yofanana ndi imeneyi. Timathandiza anthu kuti amasuke ku ziphunzitso zonyenga komanso kuti asiye kulambira mafano. Timatha kukumana ndi anthu osiyanasiyana tikamalalikira ku nyumba ndi nyumba. (1 Tim. 2:4) Mtsikana wina wa ku Asia amakumbukira kuti mayi ake ankalambira mafano ambirimbiri kunyumba kwawo. Iye ankadziwa kuti mafanowo sangaimire Mulungu woona choncho ankapemphera kuti amudziwe bwino Mulungu woona. Tsiku lina anamva kugogoda pachitseko ndipo atatsegula anapeza kuti ndi a Mboni za Yehova awiri. Iwo ananena kuti angamuthandize kudziwa dzina la Mulungu woona, lomwe ndi Yehova. Iye anasangalala kwambiri atayankhidwa mafunso ake okhudza mafano. Panopo amasonyeza changu chenicheni mwa kulalikira mwakhama ndipo n’kumathandiza ena mwauzimu.​—Sal. 83:18; 115:4-8; 1 Yoh. 5:21.

7. Kodi tingatsanzire bwanji zimene anthu ophunzitsa malamulo a Yehova m’nthawi ya Yehosafati anachita?

7 Kodi tikakhala mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba timayesetsa kufika paliponse m’gawo lathu? N’zochititsa chidwi kuti m’chaka chachitatu cha ulamuliro wake, Yehosafati anatumiza akalonga asanu, Alevi 9 ndi ansembe awiri kuti apite m’mizinda yonse kukaphunzitsa anthu malamulo a Yehova. Ntchito imeneyi inathandiza kwambiri chifukwa chakuti anthu a mitundu yowazungulira anayamba kuopa Yehova. (Werengani 2 Mbiri 17:9, 10.) Tikamasinthasintha masiku komanso nthawi imene timapitira mu utumiki, tingathe kulankhula ndi anthu osiyanasiyana panyumba iliyonse.

8. Kodi tingatani kuti tizichita zambiri mu utumiki?

8 Atumiki a Yehova ambiri masiku ano asamuka kwawo n’kupita kukalalikira kumene kulibe Mboni zambiri. Kodi nanunso mungakwanitse kuchita zimenezi? Mwina enafe sitingathe kusamukira kudera lina koma tikhoza kumalalikira kwa anthu a m’dera lathu amene amalankhula  chinenero china. M’bale wina dzina lake Ron, anaphunzira moni wa zinenero 32 ali ndi zaka 81. Iye anachita zimenezi ataona kuti kudera la kwawo kunkabwera anthu a zinenero zosiyanasiyana. Posachedwapa anakumana ndi banja lina la ku Africa ndipo analipatsa moni mu chinenero chawo chomwe ndi Chiyoruba. Iwo anamufunsa Ron ngati anakhalapo ku Africa. Iye anawayankha kuti sanakhalepo ndipo anamufunsa kuti anaphunzira bwanji chilankhulo chawo. Izi zinachititsa kuti ayambe kuwalalikira. Iwo analandira magazini moyamikira ndipo anamuuza kumene amakhala. Kenako Ron anadziwitsa mpingo wa kudera limene banjalo limakhala ndipo pano likuphunzira Baibulo.

9. N’chifukwa chiyani kuwerenga Baibulo tikakhala mu utumiki n’kofunika kwambiri? Perekani chitsanzo.

9 Aphunzitsi amene anatumidwa m’nthawi ya Yehosafati anali ndi “buku la chilamulo cha Yehova.” Padziko lonse, nafenso timayesetsa kuphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Tikakhala mu utumiki timathandiza anthu kudziwa kuti Baibulo ndi lofunika kwambiri mwa kuwerenga kuchokera m’Baibulo mwenimwenimo. Mlongo wina dzina lake Linda, atafika pa khomo lina mwininyumba anamuuza kuti akusamalira mwamuna wake yemwe ankadwala matenda opha ziwalo. Mayiyo anadandaula kuti: “Sindikudziwa chimene ndinalakwa kuti Mulungu alole kuti zimenezi zindichitikire.” Ndiyeno Linda anayankha kuti: “Mungandilole kuti ndikusonyezeni mfundo inayake yolimbikitsa?” Kenako anamuwerengera lemba la Yakobe 1:13 n’kumuuza kuti: “Tikamakumana ndi mavuto, sizitanthauza kuti Mulungu akutilanga.” Zitatero, mwininyumbayo anamukumbatira Linda chifukwa chosangalala ndi zimene anamvazo. Pambuyo pake Linda anati: “Chifukwa choti ndinamuwerengera lemba m’Baibulo, ndinamulimbikitsa kwambiri. Nthawi zina malemba amene timawerenga amakhala oti mwininyumbayo sanawamvepo chiyambire.” Zimene anakambirana pa tsikuli zinachititsa kuti ayambe kuphunzira Baibulo ndi mayiyu.

Achinyamata Amene Amatumikira Mwachangu

10. Kodi Yosiya anapereka chitsanzo chotani kwa Akhristu chinyamata masiku ano?

10 Taganiziraninso chitsanzo cha Yosiya chija. Iye anali ndi changu pa kulambira koona ali wamng’ono ndipo ali ndi zaka 20 anayamba ntchito yochotsa mafano. (Werengani 2 Mbiri 34:1-3.) Masiku ano pali achinyamata ambiri amene amasonyezanso changu mu utumiki.

11-13. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zitsanzo za achinyamata amene akutumikira Yehova mwachangu masiku ano?

11 Mtsikana wina wazaka 13 wa ku England dzina lake Hannah, anayamba kuphunzira Chifalansa kusukulu atamva zoti kagulu ka chinenero chimenechi kakhazikitsidwa m’tawuni ya pafupi ndi kwawo. Bambo ake anavomereza kuti azimuperekeza kutawuniyo kukachita nawo misonkhano. Panopa Hannah ali ndi zaka 18 ndipo ndi mpainiya wokhazikika. Iye amalalikira mwakhama mu Chifalansa. Kodi nanunso mungaphunzire chinenero  china n’cholinga choti muthandize anthu ena kudziwa za Yehova?

12 Mtsikana wina dzina lake Rachel, anasangalala kwambiri pamene anaonera mwachifatse vidiyo yonena za kukhala ndi zolinga zolemekeza Mulungu. (Pursue Goals That Honor God ) Ponena za nthawi imene anayamba kutumikira Yehova mu 1995, iye anati: “Ndinkaona ngati ndikuchita bwino m’choonadi.” Ndiyeno anapitiriza kuti: “Nditaonera vidiyoyi ndinazindikira kuti kwa zaka zonsezi sindinazike mizu m’choonadi. Ndiyenera kumenyera nkhondo choonadi n’kuchita khama kwambiri polalikira komanso kuphunzira Baibulo pandekha.” Panopa Rachel amaona kuti akutumikira Yehova mwachangu. Kodi zotsatira zake n’zotani? Iye anati: “Ubwenzi wanga ndi Yehova walimba kwambiri. Mapemphero anga amakhala ochokera pansi pa mtima. Ndimaphunzira Baibulo mozama ndipo ndimasangalala ndi kuphunzirako. Komanso nkhani za m’Baibulo ndimazimvetsa bwino kwambiri. Izi zachititsa kuti ndizisangalala mu utumiki komanso poona anthu akulimbikitsidwa ndi mawu a Yehova.”

13 Nayenso Luke analimbikitsidwa kwambiri ataonera vidiyo yonena zimene achinyamata ayenera kusankha pamoyo wawo. (Young People Ask​—What Will I Do With My Life? ) Ataonera vidiyoyi iye anati: “Panopo ndikufuna kuganiziranso bwino za moyo wanga.” Iye anatinso: “Poyamba ndinali ndi cholinga chochita maphunziro apamwamba kwambiri kuti ndidzakhale wachuma. Ndinkaganiza kuti pambuyo pake m’pamene ndidzachite zinthu zauzimu. Maganizo oterewa amachititsa munthu kupinimbira mwauzimu ndipo amasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova.” Achinyamata, bwanji osafufuza mmene mungagwiritsire ntchito zimene mwaphunzira kusukulu kuti muonjezere utumiki wanu ngati mmene anachitira Hannah? Mungachite bwinonso kutengera chitsanzo cha Rachel pokhala ndi zolinga zimene zingalemekezedi Mulungu. Tsanziraninso Luke ndipo pewani misampha imene achinyamata ambiri amakodwa nayo.

Mverani Machenjezo Mwachangu

14. Kodi Yehova amafuna kuti anthu omulambira akhale otani ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi sizophweka masiku ano?

14 Anthu a Yehova ayenera kukhala oyera kuti utumiki wawo ukhale wovomerezeka. Yesaya anati: “Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.” (Yes. 52:11) Zaka zambiri Yesaya asanalembe mawu amenewa, Mfumu Asa anagwira ntchito yothetseratu makhalidwe oipa mu Yuda. (Werengani 1 Mafumu 15:11-13.) Ndipo patapita zaka zambiri, mtumwi Paulo anauza Tito kuti Yesu anadzipereka kuti ayeretse otsatira ake n’cholinga choti akhale “anthu akeake, achangu pa ntchito zabwino.” (Tito 2:14) Masiku ano dzikoli ladzaza ndi anthu okonda zoipa, choncho sizophweka kuti achinyamata akhalebe oyera. Mwachitsanzo, atumiki onse a Mulungu, ana ndi akulu omwe, ayenera kuyesetsa kuti maganizo awo asaipitsidwe ndi zithunzi zoipa zimene zimapezeka m’zikwangwani zoitanira malonda, pa TV, m’mafilimu ndiponso makamaka pa Intaneti.

15. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizidana ndi choipa?

15 Kumvera mwachangu machenjezo a Mulungu, kudzatithandiza kudana ndi zoipa. (Sal. 97:10; Aroma 12:9) M’bale wina ananena kuti: “Tiyenera kudana kwambiri ndi zithunzi zolaula kuti tisamakopeke nazo, chifukwa zili ngati  maginito amphamvu kwambiri.” Chitsulo chikagwidwa ndi maginito, pamafunika kuchikoka mwamphamvu kuti muchichotse. Choncho pamafunikanso kuchita khama kwambiri kuti tisakhale ndi chizolowezi choonera zithunzi zolaula. Chimene chingatithandize kuti tizidana ndi zithunzi zolaula, ndi kuganizira mavuto amene angabwere chifukwa choonera zithunzi zimenezi. M’bale wina anachita khama kwambiri kuti asiye chizolowezi choonera zithunzi zolaula pa Intaneti. Iye anaika kompyuta yake pamalo oonekera kwa anthu onse a m’banja lake. Ndiponso anatsimikiza mumtima mwake kuti akhale woyera komanso wachangu pa ntchito zabwino. Anachitanso zinthu zina. Popeza ntchito yake imafunika kuti azigwiritsa ntchito kompyuta, iye anasankha kuti azigwiritsa ntchito kompyutayo mkazi wake ali pomwepo.

Ubwino Wosonyeza Makhalidwe Abwino

16, 17. Kodi khalidwe lathu labwino limakhudza bwanji anthu ena? Perekani chitsanzo.

16 Achinyamata ambiri m’gulu la Yehova amasonyeza makhalidwe abwino ndipo izi zimachititsa chidwi kwambiri anthu ena. (Werengani 1 Petulo 2:12.) Mwachitsanzo munthu wina anapita kukagwira ntchito yokonza makina osindikizira mabuku ku Beteli ya ku London. Atagwira ntchitoyo tsiku lonse, anazindikira kuti Mboni za Yehova ndi anthu abwino kwambiri. Mkazi wake, amene pa nthawiyi ankaphunziranso Baibulo ndi mlongo wina, anaona kuti mwamuna wakeyo wasintha kwambiri. Poyamba sankalola kuti Mboni ziziponda pakhomo pake. Koma atangobwera kokagwira ntchito ku Beteliko ankangonena zabwino zokhazokha zimene anam’chitira kumeneko. Iye anati palibe amene ankalankhula mawu oipa, aliyense anali woleza mtima ndipo malo onsewo anali abata. Iye anachitanso chidwi kwambiri kuona kuti achinyamata amagwira ntchito mwakhama popanda kulipidwa. Iwo amadzipereka kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zawo pa ntchito yolalikira uthenga wabwino.

17 Nawonso abale ndi alongo ena amene amagwira ntchito zolembedwa kapena kuchita bizinesi, amachita zimenezi moikirapo mtima. (Akol. 3:23, 24) Nthawi zambiri izi zimachititsa kuti asachotsedwe ntchito chifukwa mabwana awo amawakonda komanso amawaona kuti ndi okhulupirika.

18. Kodi tingatani kuti tikhale “achangu pa ntchito zabwino.”

18 Timasonyeza kuti ndife achangu pa nyumba ya Yehova mwa kukhulupirira Yehova, kumvera malangizo ake ndiponso kusamalira malo amene timachitira misonkhano yathu. Komanso tiyenera kuchita khama pa ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. Kaya ndife aakulu kapena ana, timapindula kwambiri tikamayesetsa kutsatira mfundo zolungama zogwirizana ndi kulambira kwathu. Tikatero tidzakhalabe anthu “achangu pa ntchito zabwino.”​—Tito 2:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 N’kutheka kuti Asa anachotsa misanje ya milungu yonyenga koma osati imene inali pamalo amene anthu ankalambirirapo Yehova. Apo ayi, ndiye kuti misanjeyo inamangidwanso pambuyo pa ulamuliro wa Asa, ndipo mwana wake Yehosafati atayamba kulamulira anachotsa misanjeyo.​—1 Maf. 15:14; 2 Mbiri 15:17.

Pa zitsanzo za m’Baibulo ndiponso za masiku ano, kodi mwaphunzira chiyani pa nkhani ya

• kusonyeza changu pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa?

• zimene Akhristu achinyamata angachite kuti akhale “achangu pa ntchito zabwino”?

• zimene tingachite kuti tipewe zizolowezi zoipa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi mumagwiritsa ntchito Baibulo nthawi zonse mu utumiki?

[Chithunzi patsamba 15]

Kuphunzira chinenero china kusukulu kungakuthandizeni kuchita zambiri mu utumiki